Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinthu Zimene Mungakondwere Nazo

Zinthu Zimene Mungakondwere Nazo

Zinthu Zimene Mungakondwere Nazo

ZINTHU zonse m’chilengedwe, kaya ndi kaselo kakang’ono kamodzi kapena ndi gulu la milalang’amba yambirimbiri, zinalengedwa mwadongosolo. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Mlengi wake “si Mulungu wachisokonezo.” (1 Akor. 14:33) Dongosolo la Mulungu pa nkhani ya kulambira ndi lochititsanso chidwi. Taganizirani zimene Yehova wachita. Iye wasonkhanitsa m’gulu limodzi angelo ndi anthu ambirimbiri, amene ali ndi ufulu wosankha, kuti azimulambira mogwirizana. Izitu n’zogometsa kwabasi.

Kale ku Isiraeli, mzinda wa Yerusalemu unkaimira mbali ya padziko lapansi ya gulu la Mulungu. Mumzindawu munali kachisi wa Yehova ndiponso n’kumene kunkakhala mfumu yodzozedwa ya Mulungu. Mwisiraeli wina amene anali ku ukapolo ku Babulo anafotokoza mmene ankaonera mzinda wopatulikawu ponena kuti: “Lilime langa limamatire m’kamwa mwanga ngati sindingakukumbukire, ngati sindingakweze iwe Yerusalemu pamwamba pa chilichonse chimene chimandikondweretsa.”​—Sal. 137:6.

Kodi mumamva choncho mukaganiza za gulu la Mulungu masiku ano? Kodi gulu lake limakukondweretsani kuposa chinthu china chilichonse? Kodi ana anu amadziwa mbiri ya mbali ya padziko lapansi ya gulu la Mulungu ndiponso mmene mbaliyi imayendera? Kodi amadziwa kuti iwowo ali m’gulu la Mboni za Yehova lomwe lili pa ubale wa padziko lonse? (1 Pet. 2:17) Mungachite bwino kugwiritsa ntchito mfundo zotsatirazi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja n’cholinga choti banja lanu lidziwe bwino ndiponso kuyamikira gulu la Yehova.

Muzikambirana za ‘Masiku Akale’

Kale, chaka chilichonse mabanja achiisiraeli ankasonkhana kuti achite Pasika. Pamene chikondwererochi chinakhazikitsidwa, Mose analangiza anthuwo kuti: “Mwana wanu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mudzamuyankhe kuti, ‘Yehova anatitulutsa ndi mphamvu ya dzanja lake mu Iguputo, m’nyumba ya ukapolo.’” (Eks. 13:14) Aisiraeli sanayenere kuiwala zimene Yehova anawachitira. N’zosakayikitsa kuti azibambo ambiri achiisiraeli ankatsatira zimene Mose ananena. Patapita zaka zambiri, Mwisiraeli wina anapemphera kuti: “Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu, makolo athu anatifotokozera ntchito zimene inu munachita m’masiku awo, m’masiku akale.”​—Sal. 44:1.

Masiku ano, wachinyamata angaone kuti mbiri ya Mboni za Yehova pa zaka zoposa 100 zapitazi ndi ya ‘masiku akale.’ Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti amvetse ndiponso kuti achite chidwi ndi zinthu zimenezi? Makolo ena amagwiritsa ntchito mabuku monga Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, Yearbook, mbiri ya moyo wa anthu imene imapezeka m’magazini athu, ndiponso nkhani zina zofotokoza mbiri ya gulu la Mulungu. Amagwiritsanso ntchito DVD yathu yatsopano imene imafotokoza bwino kwambiri za mbiri ya anthu a Mulungu masiku ano. Mavidiyo osonyeza kuzunzidwa kwa abale a ku Germany m’nthawi ya chipani cha Nazi ndiponso kumayiko amene anali mu Soviet Union amathandiza mabanja kuti azidalira Yehova pokumana ndi mayesero. Nanunso mungachite bwino kugwiritsa ntchito zinthu ngati zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja. Kuchita zimenezi kungalimbitse chikhulupiriro cha ana anu ngati atakumana ndi mayesero.

Ana akhoza kutopa msanga mukamangowafotokozera nkhani yaitali yotere. Koma kuti asatope msanga muziwapatsa zochita. Mwachitsanzo, mungapemphe mwana wanu kuti asankhe dziko limene amachita nalo chidwi n’kufufuza mbiri ya anthu a Mulungu m’dzikolo, kenako n’kufotokozera banja lonse zinthu zina zimene wapeza. Ngati mu mpingo wanu muli Akhristu ena amene atumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri, mukhoza kuwaitana kudzakhala nanu pa kulambira kwa pabanja. Mwina mwana wanu angawafunse mafunso kuti afotokoze zimene akumana nazo. Kapena mungapemphe mwana wanu kuti ajambule zithunzi za zinthu zosaiwalika zimene zachitika m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, angajambule chithunzi cha anthu akumanga ofesi ya nthambi, ali pa msonkhano wa mayiko kapena akugwiritsa ntchito galamafoni polalikira kunyumba ndi nyumba.

Dziwani Mmene ‘Chiwalo Chilichonse Chimagwirira Ntchito Yake’

Mtumwi Paulo anayerekezera mpingo wachikhristu ndi ‘thupi lonse lolumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira, limene limakula ndi kudzilimbikitsa lokha mwa chikondi, pomwe chiwalo chilichonse chigwira ntchito yake.’ (Aef. 4:16, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Tikamaphunzira mmene thupi limagwirira ntchito, timayamikira ndiponso kulemekeza kwambiri Mlengi wathu. Izi n’zimene zimachitikanso tikamaphunzira mmene mpingo wa padziko lonse umayendera. Timagoma kwambiri ndi “mbali zambirimbiri za nzeru ya Mulungu.”​—Aef. 3:10.

Yehova amafotokoza mmene gulu lake limayendera. Iye amafotokoza ngakhale mmene mbali ya kumwamba ya gulu lake imachitira zinthu. Mwachitsanzo, iye amatiuza kuti poyamba anapereka chivumbulutso kwa Yesu Khristu amene kenako “anatumiza mngelo wake kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro kwa kapolo wake Yohane. Yohaneyo anachitira umboni.” (Chiv. 1:1, 2) Popeza Mulungu amafotokoza mmene mbali yosaoneka ya gulu lake imagwirira ntchito, ndiye kuti angafunenso kuti timvetse mmene ‘chiwalo chilichonse chimagwirira ntchito yake’ padziko lapansi.

Mwachitsanzo ngati posachedwapa woyang’anira dera adzachezera mpingo wanu, mungachite bwino kukambirana ndi banja lanu ntchito imene oyang’anira oyendayenda amagwira ndiponso madalitso amene amapeza. Kodi iwo amathandiza bwanji aliyense wa ife? Mungakambirane mafunso ena monga akuti: N’chifukwa chiyani tiyenera kupereka lipoti la utumiki wakumunda? Kodi ndalama zoyendetsera gulu la Mulungu zimapezeka bwanji? Kodi Bungwe Lolamulira limayendetsa bwanji ntchito zake ndipo limapereka bwanji chakudya chauzimu?

Tikamvetsa mmene gulu la anthu a Yehova limayendera, timapindula m’njira zingapo koma tingotchulapo njira zitatu. Choyamba, timayamikira kwambiri Akhristu anzathu amene amagwira ntchito mwakhama potitumikira. (1 Ates. 5:12, 13) Chachiwiri, timalimbikitsidwa kuti tizichirikiza dongosolo la m’gulu la Mulungu. (Mac. 16:4, 5) Chachitatu, timakhulupirira kwambiri anthu amene akutsogolera tikamamvetsa kuti zinthu zimene iwowo amasankha ndiponso dongosolo limene amakonza zimachokera m’Malemba.​—Aheb. 13:7.

“Yenderani Nsanja Zake Zokhalamo”

“Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo, werengani nsanja zake. Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba. Yenderani nsanja zake zokhalamo, kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.” (Sal. 48:12, 13) Pamenepa, wamasalimo analimbikitsa Aisiraeli kuti azikaona mzinda wa Yerusalemu. Kodi mukuganiza kuti mabanja achiisiraeli amene anapita kumzinda wopatulikawo kukachita nawo zikondwerero za pachaka ndiponso kuona kachisi wokongola kwambiri ankamva bwanji akabwerera kwawo? Iwo ayenera kuti ankalimbikitsidwa ‘kusimbira m’badwo wam’tsogolo’ zimene anaonazo.

Taganizirani za mfumukazi ya ku Sheba imene poyamba inkakayikira zimene inamva zokhudza ulamuliro wapamwamba wa Solomo ndiponso nzeru zake zodabwitsa. Kodi n’chiyani chinathandiza mfumukaziyi kukhulupirira zimene inamvazo? Mfumukaziyi inati: “Sindinakhulupirire mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga.” (2 Mbiri 9:6) N’zoona kuti zimene timaona ndi ‘maso athu’ zimatikhudza kwambiri.

Kodi mungathandize bwanji ana anu kuona ndi ‘maso awo’ zinthu zochititsa chidwi m’gulu la Yehova? Ngati pali ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova pafupi ndi kwanu, mungachite bwino kukaiona. Mwachitsanzo, Mandy ndi Bethany ndi atsikana amene anakulira m’dera lomwe lili pa mtunda wa makilomita 1,500 kuchokera ku Beteli ya m’dziko lawo. Koma makolo awo ankakonza zoti azikaona malowo makamaka pamene anawa ankakula. Atsikanawo anati: “Tisanapite ku Beteli tinkaganiza kuti ndi malo osasangalatsa a anthu okalamba okhaokha. Koma tinakumana ndi achinyamata amene ankatumikira Yehova mwakhama ndiponso mosangalala. Tinaona kuti gulu la Yehova silinkangopezeka m’dera lathu lokha ndipo ulendo uliwonse umene tinkapita ku Beteli tinkalimbikitsidwa kwambiri mwauzimu.” Mandy ndi Bethany ataona bwinobwino gulu la Mulungu analimbikitsidwa kuchita upainiya ndipo kenako anaitanidwa kukatumikira ku Beteli kwa kanthawi.

Ifeyo tili ndi njira ina imene ingatithandize ‘kuona’ gulu la Yehova ndipo njirayi kunalibe pa nthawi ya Aisiraeli akale. Posachedwapa, anthu a Mulungu alandira mavidiyo ndi ma DVD amene amasonyeza zinthu zosiyanasiyana za m’gulu la Mulungu. Mwachitsanzo, tili ndi ma DVD akuti Jehovah’s Witnesses​—Organized to Share the Good News, Our Whole Association of Brothers, To the Ends of the Earth, ndiponso United by Divine Teaching. Inu ndi banja lanu mukamaona khama la atumiki a ku Beteli, abale ndi alongo othandiza pakagwa zamwadzidzidzi, amishonale ndiponso abale amene amakonza ndi kuyendetsa misonkhano yachigawo, mumayamikira ubale wa padziko lonse ndi mtima wonse.

Mpingo uliwonse wa anthu a Mulungu umachita zambiri pa ntchito yolalikira uthenga wabwino ndiponso yothandiza Akhristu a m’gawo lake. Koma muyenera kupatula nthawi kuti muziganizira ‘gulu lonse la abale anu m’dzikoli.’ Zimenezi zingathandize inu ndi ana anu kuti mukhalebe “olimba m’chikhulupiriro” n’kuzindikiranso kuti pali zinthu zimene mungakondwere nazo.​—1 Pet. 5:9.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 18]

Gulu la Mulungu Nkhani Yofunika Kuiphunzira

Tili ndi zinthu zambiri zothandiza anthu onse kuphunzira zambiri za mmene gulu la Yehova limayendera ndiponso mbiri yake. Mafunso amene ali m’munsiwa angakuthandizeni kuyamba kuphunzira zimenezi:

Kodi ntchito ya oyang’anira oyendayenda a masiku ano inayamba bwanji?​Nsanja ya Olonda, November 15, 1996, tsamba 10 mpaka 15.

Kodi chinali chapadera n’chiyani ndi “Tsiku la Ana” pa Msonkhano Waukulu mu 1941?​Nsanja ya Olonda, July 15, 2001, tsamba 8.

Kodi Bungwe Lolamulira limasankha bwanji zinthu?​“Bearing Thorough Witness” About God’s Kingdom, tsamba 108 mpaka 114; Nsanja ya Olonda ya May 15, 2008, tsamba 29 ndiponso ya April 1, 2007, tsamba 23, ndime 10 ndi 11.