Landirani Mzimu wa Mulungu Osati wa Dziko
Landirani Mzimu wa Mulungu Osati wa Dziko
“Tsopano sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu, kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.”—1 AKOR. 2:12.
1, 2. (a) Kodi Akhristu oona ali pa nkhondo yotani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
AKHRISTU oona ali pa nkhondo. Mdani wathu ndi wamphamvu, wochenjera ndiponso wokakala mtima chifukwa chozolowera nkhondo. Iye ali ndi chida champhamvu kwambiri chimene wagonjetsa nacho anthu ambirimbiri. Koma sitiyenera kuopa kuti atigonjetsa. (Yes. 41:10) Tili ndi chitetezo champhamvu kwambiri moti chida chilichonse sichingatigonjetse.
2 Nkhondo yathu si yakuthupi koma yauzimu. Mdani wathu ndi Satana Mdyerekezi ndipo chida china champhamvu chimene amagwiritsa ntchito ndi “mzimu wa dziko.” (1 Akor. 2:12) Koma chitetezo champhamvu kwambiri chimene tili nacho ndi mzimu wa Mulungu. Tingapulumuke pa nkhondoyi ndipo tingapitirize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu tikamapempha kuti Mulunguyo atipatse mzimu wake komanso tikamakhala ndi makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Koma kodi mzimu wa dziko n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani umatsogolera anthu ambiri? Kodi tingadziwe bwanji ngati mzimu wa dzikowu ukutitsogolera? Nanga tingaphunzire chiyani kwa Yesu pa nkhani yolandira mzimu wa Mulungu ndiponso yokana mzimu wa dziko?
N’chifukwa Chiyani Mzimu wa Dziko Wafalikira Kwambiri?
3. Kodi mzimu wa dziko n’chiyani?
3 Mzimu wa dziko umachokera kwa Satana, yemwe ndi “wolamulira wa dziko,” ndipo umatsutsana ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Yoh. 12:31; 14:30; 1 Yoh. 5:19) Mzimuwo umatanthauza mtima kapena maganizo amene ambiri ali nawo m’dzikoli ndipo umawalimbikitsa kuchita zinthu zosiyanasiyana. Mzimuwu umatsogolera anthu kuchita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Mulungu.
4, 5. Kodi zatheka bwanji kuti mzimu umene Satana amalimbikitsa ufalikire kwambiri?
4 Kodi zinatheka bwanji kuti mzimu umene Satana amalimbikitsa ufalikire kwambiri chonchi? Poyamba, Satana ananyengerera Hava m’munda wa Edeni. Satana anakopa Hava kuti azikhulupirira zoti akhoza kukhala ndi moyo wabwino popanda kulamuliridwa ndi Mulungu. (Gen. 3:13) Apatu Satana anasonyeza kuti ndi wabodza lamkunkhuniza. (Yoh. 8:44) Ndiyeno anagwiritsa ntchito mkaziyo pofuna kuti Adamu asamvere Yehova. Chifukwa cha zimene Adamu anasankha, anthu onse anakhala akapolo a uchimo ndipo onse anatengera mtima wofuna kutsogoleredwa ndi mzimu wosamvera umene Satana anauyambitsa.—Werengani Aefeso 2:1-3.
Chiv. 12:3, 4) Zimenezi zinachitika Chigumula cha masiku a Nowa chisanachitike. Angelowa ankaganiza kuti adzasangalala kwambiri ngati atasiya malo awo kumwamba, kuvala matupi a anthu, n’kubwera padziko lapansi kuti atsatire zilakolako zomwe sizinali zachibadwa kwa iwo. (Yuda 6) Satana limodzi ndi ziwanda zake, zomwe panopa zavalanso matupi auzimu, “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chiv. 12:9) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri adakali akhungu chifukwa chosazindikira mphamvu ya ziwanda.—2 Akor. 4:4.
5 Satana anachititsanso angelo ena ambiri ndithu kuti apanduke ndipo iwo anadzakhala ziwanda. (Kodi Inuyo Mukutsogoleredwa ndi Mzimu wa Dziko?
6. Kodi mzimu wa dziko ungatitsogolere pokhapokha titachita chiyani?
6 Anthu ambiri sazindikira mphamvu ya Satana koma Akhristu oona amaphunzitsidwa za ziwembu zake. (2 Akor. 2:11) Ndipotu mzimu wa dziko sungatitsogolere pokhapokha titaulola. Tiyeni tikambirane mafunso anayi amene angatithandize kudziwa ngati tikutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu kapena wa dziko.
7. Kodi njira ina imene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kuti tisiye kutsatira Yehova ndi iti?
7 Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda zimasonyeza chiyani za ineyo? (Werengani Yakobo 3:14-18.) Satana amafuna kuti tisiye kutsatira Mulungu mwa kutichititsa kukonda zachiwawa. Mdyerekezi amadziwa kuti Yehova amadana ndi aliyense wokonda chiwawa. (Sal. 11:5) Choncho Satana amagwiritsa ntchito mabuku, mafilimu, nyimbo, ndi masewera a pa kompyuta kuti alimbikitse anthu kutsatira zilakolako za thupi. Mwachitsanzo masewera ena a pa kompyuta, wosewerayo amayerekezera akuchita zinthu zonyansa kwambiri zachiwerewere kapena zachiwawa. Satana sadandaula ngati timakonda zinthu zabwino malinga ngati mbali ina timakondanso zoipa zimene iye amalimbikitsa.—Sal. 97:10.
8, 9. Pa nkhani ya zosangalatsa, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
8 Mosiyana ndi mzimu wa dziko, mzimu wa Mulungu umalimbikitsa anthu kukhala oyera, amtendere ndiponso odzaza ndi chifundo. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda zimandilimbikitsa kukhala ndi makhalidwe abwino?’ Nzeru yochokera kumwamba ndi “yopanda chinyengo.” Anthu amene amatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu samangolalikira za kukhala oyera ndiponso amtendere koma kwinaku n’kumaonera zinthu zachiwawa ndiponso zachiwerewere akakhala kunyumba kwawo.
9 Yehova amafuna kuti anthu azilambira iye yekha. Koma Satana amafuna kuti tingomulambira ngakhale kamodzi kokha ndipo izi ndi zimene anafuna kuti Yesu achite. (Luka 4:7, 8) Choncho ndi bwino kudzifunsanso kuti: ‘Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda zimandithandiza kulambira Mulungu yekha? Kodi zimachititsa kuti ndizivutika kapena ndisamavutike kukana mzimu wa dziko? Kodi ndiyenera kusintha zosangalatsa zimene ndimakonda?’
10, 11. (a) Kodi mzimu wa dziko umalimbikitsa maganizo otani pa nkhani ya zinthu zakuthupi? (b) Kodi Mawu ouziridwa ndi mzimu wa Mulungu amatilimbikitsa kukhala ndi maganizo otani?
10 Kodi maganizo anga ndi otani pa nkhani ya chuma? (Werengani Luka 18:24-30.) Mzimu wa dziko umalimbikitsa “chilakolako cha maso” mwa kuchititsa anthu kukhala adyera ndiponso okonda chuma. (1 Yoh. 2:16) Mzimuwu walimbikitsa anthu ambiri kufunitsitsa kuti akhale olemera. (1 Tim. 6:9, 10) Mzimu umenewu ukhoza kutichititsa kuganiza kuti zinthu zingatiyendere bwino ngati tili ndi chuma chambiri. (Miy. 18:11) Koma tikayamba kukonda ndalama kuposa Mulungu ndiye kuti Satana wapambana. Ndiyeno tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi masiku ano ndimangoganizira zopeza chuma ndiponso kusangalala?’
11 Mosiyana ndi zimenezi, Mawu ouziridwa ndi mzimu wa Mulungu amatilimbikitsa kuti tizikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ndalama ndiponso kuti tizigwira ntchito mwakhama kuti tizipeza zofunikira pa moyo wathu komanso wa banja lathu. (1 Tim. 5:8) Mzimu wa Mulungu umathandiza anthu amene amaulandira kuti akhale ndi mtima wopatsa umene Yehova ali nawo. Anthu oterewa amakonda kupatsa osati kungolandira. Iwo amaona kuti anthu ndi ofunika kwambiri kuposa zinthu ndipo amagawana ndi anzawo zimene ali nazo, ngati angakwanitse. (Miy. 3:27, 28) Iwo salola kuti kufunafuna ndalama kuwalepheretse kutumikira Mulungu.
12, 13. Mosiyana ndi mzimu wa dziko, kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize bwanji?
12 Kodi khalidwe langa limasonyeza mzimu uti? (Werengani Akolose 3:8-10, 13.) Mzimu wa dziko umalimbikitsa ntchito za thupi. (Agal. 5:19-21) Kunena zoona, mzimu umene ukutitsogolera umaonekera pamene zinthu zavuta osati pamene zili bwinobwino. Mwachitsanzo, mzimuwu umaonekera pamene m’bale kapena mlongo watinyalanyaza, kutikhumudwitsa kapena kutichimwira. Ungaonekerenso pamene tili kwatokha m’nyumba mwathu. Tingachite bwino kudzifufuza pa nkhani imeneyi. Dzifunseni kuti, ‘Kodi pa miyezi 6 yapitayi ndasonyeza makhalidwe a Khristu kapena ndayambiranso kulankhula ndiponso kuchita zinthu zina zoipa?’
13 Mzimu wa Mulungu ukhoza kutithandiza ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake’ n’kuvala “umunthu watsopano.” Zimenezi zingatithandize kukhala achikondi ndiponso okoma mtima kwambiri. Tidzakonda kukhululukira ena ndi mtima wonse ngakhale pamene tili ndi chifukwa chenicheni chodandaulira za iwo. Ngati taona kuti mwina pachitika zopanda chilungamo sitidzachita zinthu monga, ‘kuwawidwa mtima kwa njiru, kupsa mtima, kukwiya, kulalata ndiponso kulankhula mawu achipongwe.’ M’malomwake tidzayesetsa kukhala “achifundo chachikulu.”—Aef. 4:31, 32.
14. Kodi anthu ambiri m’dzikoli amaona bwanji Mawu a Mulungu?
14 Kodi ndimatsatira ndiponso kukonda makhalidwe abwino a m’Baibulo? (Werengani Miyambo 3:5, 6.) Mzimu wa dziko umalimbikitsa anthu kusamvera Mawu a Mulungu. Anthu amene amatsogoleredwa ndi mzimu umenewu amanyalanyaza mbali za Baibulo zimene siziwakomera, m’malomwake amatsatira miyambo ndi mfundo za anthu. (2 Tim. 4:3, 4) Ndiyeno pali anthu ena amene safuna kuganizira n’komwe Mawu a Mulungu. Anthu amenewa amakayikira zoti Baibulo ndi lothandiza kapena louziridwa ndi Mulungu, ndipo amadziona kuti ndi anzeru. Iwo amapeputsa mfundo za m’Baibulo zokhudza chigololo, kugonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha ndiponso kuthetsa banja. Anthu amenewa amaphunzitsa kuti “chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino.” (Yes. 5:20) Kodi ifenso tayamba kuyendera mzimu umenewu? Kodi tikakumana ndi mavuto timangodalira nzeru za anthu ndi mfundo zathuzathu? Kapena kodi timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo?
15. M’malo modalira nzeru zathu, kodi tiyenera kuchita chiyani?
15 Mzimu wa Mulungu umatithandiza kuti tizilemekeza mfundo za m’Baibulo. Mofanana ndi wamasalimo, timaona kuti Mawu a Mulungu ali ngati nyale younikira kumapazi athu ndi kuwala kounikira njira yathu. (Sal. 119:105) M’malo modalira nzeru zathu, timakhulupirira kwambiri Mawu olembedwa a Mulungu kuti atithandize kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Kuwonjezera pa kulemekeza mfundo za m’Baibulo timaphunziranso kukonda chilamulo cha Mulungu.—Sal. 119:97.
Zimene Tikuphunzira kwa Yesu
16. Kodi tingatani kuti tikhale ndi “maganizo a Khristu”?
16 Kuti tilandire mzimu wa Mulungu, tiyenera kukhala ndi “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:16) Kuti tikhale ndi “maganizo amene Khristu Yesu anali nawo” tiyenera kudziwa mmene iye ankaganizira ndiponso kuchitira zinthu, ndiyeno n’kumamutsanzira. (Aroma 15:5; 1 Pet. 2:21) Tiyeni tione njira zina zimene tingachitire zimenezi.
17, 18. (a) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu pa nkhani ya pemphero? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kupemphabe’?
17 Muzipempha mzimu wa Mulungu. Yesu asanakumane ndi mayesero ankapempha mzimu wa Mulungu kuti umuthandize. (Luka 22:40, 41) Ifenso tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera. Yehova amapereka mzimuwu mowolowa manja kwa anthu onse amene amapempha ndi chikhulupiriro. (Luka 11:13) Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.”—Mat. 7:7, 8.
18 Tikamapempha mzimu wa Yehova ndiponso thandizo lake sitiyenera kusiya msanga. Tiyenera kupemphera kawirikawiri ndiponso kutherapo nthawi. Nthawi zina Yehova asanayankhe mapemphero, amafuna kuti anthu asonyeze kuti akufunadi zimene akupemphazo ndiponso kuti ali ndi chikhulupiriro chenicheni. *
19. Kodi Yesu ankachita chiyani nthawi zonse ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kumutsanzira?
19 Muzimvera Yehova nthawi zonse. Yesu ankachita zinthu zokondweretsa Atate ake nthawi zonse. Koma pa nthawi ina, iye ankafuna kuchita zinthu mosiyana ndi mmene Atate ake ankafunira. Ngakhale zinali choncho, molimba mtima anauza Atate akewo kuti: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.” (Luka 22:42) Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimamvera Mulungu ngakhale pamene n’zovuta kutero?’ Kumvera Mulungu n’kofunika kuti tikhale ndi moyo. Iye ndi Mlengi wathu ndipo ndi amene amatisamalira. (Sal. 95:6, 7) Kuti tisangalatse Mulungu tiyenera kumumvera basi, palibenso china chimene tingachite.
20. Kodi cholinga chachikulu pa moyo wa Yesu chinali chiyani ndipo tingamutsanzire bwanji?
20 Lidziweni bwino Baibulo. Poyesedwa ndi Satana, Yesu anamutsutsa pogwira mawu a m’Malemba. (Luka 4:1-13) Poyankha atsogoleri achipembedzo amene ankamutsutsa, Yesu anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. (Mat. 15:3-6) Cholinga chachikulu pa moyo wa Yesu chinali kudziwa ndi kukwaniritsa chilamulo cha Mulungu. (Mat. 5:17) Nafenso tiyenera kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu amene amalimbitsa chikhulupiriro chathu. (Afil. 4:8, 9) Nthawi zina zimavuta kupeza nthawi yophunzira patokha kapena ndi banja lathu. Tiyenera kupatula nthawi yochita zimenezi m’malo mongodikira kuti nthawiyo ipezeke yokha.—Aef. 5:15-17.
21. Kodi ndi dongosolo liti limene lingatithandize kudziwa bwino Mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsa ntchito?
21 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watithandiza kuti tipeze nthawi yophunzira Baibulo patokha kapena ndi banja lathu. Kapoloyu wachita zimenezi mwa kukonza dongosolo loti tizikhala ndi Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse. (Mat. 24:45) Kodi mukuugwiritsa ntchito mwayi umenewu? Kuti mukhale ndi maganizo a Khristu, kodi mungamaphunzire zimene Yesu anaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana zimene mungasankhe? Kuti mupeze mfundo zothandiza pa nkhani iliyonse mukhoza kugwiritsa ntchito mlozera nkhani wa kumapeto kwa magazini a December kapena wa Watch Tower Publications Index. Mwachitsanzo, kuyambira mu 2008 mpaka 2010, mu Nsanja ya Olonda yogawira munatuluka nkhani 12 za mutu wakuti, “Zimene Tikuphunzira kwa Yesu.” Mwina mungamaphunzire nkhani zimenezi pa phunziro lanu. Kuyambira mu 2006, mu Galamukani! munkatuluka nkhani zakuti “Kodi Mungayankhe Bwanji?” Cholinga cha mafunso amenewa chinali kukuthandizani kudziwa bwino Mawu a Mulungu. Mwina nthawi zina mungamakambirane zinthu ngati zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja.
Tikhoza Kugonjetsa Dziko
22, 23. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tigonjetse dziko?
22 Kuti tizitsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu tiyenera kukana mzimu wa dziko. N’zoona kuti kukana mzimu wa dziko si nkhani yapafupi. Pamafunika khama ndiponso kumenya nkhondo mwamphamvu. (Yuda 3) Koma tikhoza kupambana. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.”—Yoh. 16:33.
23 Ifenso tikhoza kugonjetsa dziko ngati tikana mzimu wake ndiponso kuchita zonse zimene tingathe kuti tilandire mzimu wa Mulungu. Ndithudi, “ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?” (Aroma 8:31) Tikamalandira mzimu wa Mulungu ndiponso kuulola kuti uzititsogolera mwa kutsatira malangizo a m’Baibulo, tidzakhala pa mtendere ndiponso osangalala. Tidzakhalanso ndi chiyembekezo chodzalandira moyo wosatha posachedwapa m’dziko latsopano.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 18 Kuti mumve zambiri, werengani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? patsamba 170 mpaka 173.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani mzimu wa dziko wafalikira kwambiri?
• Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso anayi ati?
• Kodi taphunzira zinthu zitatu ziti kwa Yesu zotithandiza kulandira mzimu wa Mulungu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 8]
Kodi chinachitika n’chiyani kuti angelo ena akhale ziwanda?
[Chithunzi patsamba 10]
Satana amagwiritsa ntchito mzimu wa dziko kuti azilamulira anthu koma tikhoza kuukana