Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Landirani Moyamikira Ndipo Perekani ndi Mtima Wonse

Landirani Moyamikira Ndipo Perekani ndi Mtima Wonse

Landirani Moyamikira Ndipo Perekani ndi Mtima Wonse

ATATE wathu wakumwamba Yehova amakonda aliyense wa ife payekha. Mawu ake amatitsimikizira kuti iye amasamala kwambiri za atumiki ake onse. (1 Pet. 5:7) Choyamba, Yehova amasonyeza kuti amatikonda mwa kutipatsa thandizo m’njira zosiyanasiyana kuti tizimutumikira mokhulupirika. (Yes. 48:17) Yehova amafuna kuti tipindule ndi thandizo limene amapereka, makamaka tikakumana ndi mavuto amene akutisowetsa mtendere. Chilamulo cha Mose chimatsimikizira mfundo imeneyi.

Malinga ndi Chilamulo, Yehova anakonza dongosolo loonetsetsa kuti ‘anthu osauka’ monga ana amasiye, akazi amasiye komanso alendo, akuthandizidwa. (Lev. 19:9, 10; Deut. 14:29) Iye amadziwa kuti atumiki ake ena amafunika kuthandizidwa ndi olambira anzawo. (Yak. 1:27) Motero, si bwino kuti mtumiki wa Yehova azikana kulandira thandizo limene Yehova akumupatsa kudzera mwa anthu ena. Komabe, tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani yolandira thandizo.

Mawu a Mulungu amasonyezanso kuti anthu a Mulungu amakhalanso ndi mpata wopatsa. Kumbukirani nkhani ya “mkazi wina wamasiye wosauka” amene Yesu anamuona kukachisi wa ku Yerusalemu. (Luka 21:1-4) Iye ayenera kuti anapindula kwambiri ndi dongosolo lothandiza akazi amasiye limene Yehova anakonza lopezeka m’Chilamulo. Ngakhale kuti mkaziyu anali wosauka, amakumbukiridwa chifukwa cha zimene anapereka osati zimene analandira. Iye ayenera kuti anali wosangalala chifukwa cha mtima wake wopatsa. Tikutero chifukwa chakuti Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Tili ndi mfundo imeneyi m’maganizo, tiyeni tione zimene tingachite kuti ‘tikhale opatsa,’ n’kupeza chisangalalo.​—Luka 6:38.

“Ndidzabwezera Yehova Chiyani?”

Wamasalmo anafunsa kuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” (Sal. 116:12) Kodi ndi zinthu zokoma ziti zimene iye analandira? Yehova anamuthandiza kwambiri pa nthawi imene anali mu “nsautso ndi chisoni.” Yehova ‘analanditsanso moyo wake ku imfa.’ Ndipo nayenso anafuna kuchita zinazake kuti ‘abwezere’ Yehova. Ndiyeno kodi n’chiyani chimene wamasalmoyo akanachita? Iye anati: “Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova.” (Sal. 116:3, 4, 8, 10-14) Iye anatsimikiza kukwaniritsa zonse zimene anawinda kuti adzachitira Yehova ndipo anatsimikiza kupereka mangawa ake onse amene anali nawo kwa Yehova.

Nanunsotu mungathe kuchita zimenezi. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mungatero mwa kutsatira malamulo ndi mfundo za Mulungu pa moyo wanu wonse. Choncho, onetsetsani kuti pa moyo wanu mukuika kulambira Yehova patsogolo ndipo mukulola mzimu wa Mulungu kukutsogolerani pa zilizonse zimene mumachita. (Mla. 12:13; Agal. 5:16-18) Kunena zoona, simungakwanitse kubwezera Yehova zinthu zonse zimene wakuchitirani. Koma ngakhale zili choncho, mukamayesetsa kudzipereka ndi mtima wonse pomutumikira, ‘mumakondweretsa mtima wa Yehova.’ (Miy. 27:11) Ndi mwayitu waukulu kukondweretsa mtima wa Yehova mwa njira imeneyi.

Limbikitsani Mtendere wa Mpingo

N’zosachita kufunsa kuti inuyo panokha mwapindula m’njira zambiri chifukwa chokhala mumpingo wachikhristu. Yehova wapereka chakudya chauzimu chochuluka kudzera mumpingo. Munalandira choonadi chimene chinakumasulani ku mabodza a chipembedzo ndi mdima wauzimu. (Yoh. 8:32) Pamisonkhano yampingo, yadera ndiponso yachigawo imene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatikonzera, munaphunzira zinthu zimene zingakuthandizeni kupeza moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi mmene simudzakhala mavuto alionse. (Mat. 24:45-47) Madalitso amene mwalandira komanso amene mudzalandire kudzera mumpingo wa Mulungu, ndi ochuluka kwambiri moti simungakwanitse kuwatchula onse. Kodi pali zinthu zimene mungapatse mpingo chifukwa cha zimene wakuchitirani?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana mwa mfundo iliyonse yogwira ntchito yake yofunikira, malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.” (Aef. 4:15, 16) Ngakhale kuti lemba limeneli kwenikweni limanena za Akhristu odzozedwa, mfundo yake imagwiranso ntchito kwa Akhristu ena onse masiku ano. Munthu aliyense mumpingo angalimbikitse mtendere wa mpingo ndiponso kuthandiza kuti mpingowo ukule. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

Tingachite zimenezi mwa kuyesetsa kukhala anthu olimbikitsa komanso otsitsimula kwa ena. (Aroma 14:19) Tingathandizenso kuti ‘thupi lonse likule’ mwa kusonyeza chipatso cha mzimu wa Mulungu pochita zinthu ndi okhulupirira anzathu. (Agal. 5:22, 23) Komanso tiyenera kuyesetsa kupeza mipata yoti “tichitire onse zabwino, koma makamaka achibale athu m’chikhulupiriro.” (Agal. 6:10; Aheb. 13:16) Aliyense mumpingo, kaya m’bale kapena mlongo, kaya wamkulu kapena wamng’ono, akhoza kuthandiza kuti mpingo ‘ukule podzimanga mwachikondi.’

Kuwonjezera pamenepa, tikhoza kugwiritsa ntchito luso lathu, mphamvu zathu komanso chuma chathu, pogwira nawo ntchito yopulumutsa moyo imene mpingo ukugwira. Yesu Khristu anati: “Munalandira kwaulere.” Ndiye kodi nafenso tiyenera kutani? “Patsani kwaulere,” anatero Yesu. (Mat. 10:8) Motero chitani zonse zimene mungathe pa ntchito yofunika kwambiri yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kodi muli ndi vuto lina limene limakulepheretsani kuchita zimenezi? Kumbukirani mkazi wamasiye wofotokozedwa ndi Yesu uja. Iye anapereka zochepa kwambiri. Koma Yesu ananena kuti iye anapereka zochuluka kuposa ena onse. Iye anapereka zonse zimene akanatha kupereka.​—2 Akor. 8:1-5, 12.

Khalani ndi Maganizo Oyenera pa Nkhani Yolandira Thandizo

Zingachitike nthawi zina kuti inuyo mungafunike thandizo lochokera kumpingo. Zikatere, si bwino kukana thandizo limene mpingo ungapereke ngati mwapanikizika ndi mavuto a m’dongosolo lino. Yehova waika amuna oyenerera komanso achikondi kuti ‘awete mpingo,’ ndipo amuna amenewa angakuthandizeni ngati mwakumana ndi mavuto kapena mayesero. (Mac. 20:28) Akulu komanso anthu ena mumpingo ndi okonzeka kukutonthozani, kukulimbikitsani ndiponso kukutetezani mukakumana ndi mavuto.​—Agal. 6:2; 1 Ates. 5:14.

Koma polandira thandizo limene mukufunikira, muyenera kukhala ndi maganizo oyenera. Nthawi zonse muziyamikira mukalandira thandizolo. Muziona kuti thandizo limene mwalandira kuchokera kwa okhulupirira anzanu ndi umboni wa kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu. (1 Pet. 4:10) N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Chifukwa chakuti sitifuna kukhala ngati anthu ambiri m’dzikoli omwe amalandira zinthu mosayamikira.

Khalani Anzeru ndi Oganiza Bwino

M’kalata yake yopita kumpingo wa ku Filipi, Paulo ananena za Timoteyo kuti: “Ndilibe wina wa mtima ngati iye amene angasamaledi za inu moona mtima.” Kenako Paulo anati: “Ena onse akungofuna za iwo eni, osati za Khristu Yesu.” (Afil. 2:20, 21) Poganizira za mfundo yofunika kwambiri imene Paulo ananenayi, tiyeni tione mmene tingapewere kumangoganizira ‘zofuna zathu.’

Si bwino kukakamiza anthu ena mumpingo kupatula nthawi ndi kusiya zinthu zawo kuti atithandize pa vuto linalake. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchita zimenezi? Taganizirani mfundo iyi: Ngati m’bale wina watipatsa zinthu zina pofuna kutithandiza pa nthawi imene tagweredwa vuto linalake, timayamikira kwambiri. Koma kodi tingayerekeze n’komwe kumukakamiza kuti atipatse zinthuzo? Ayi sitingatero. Ndi mmene zililinso ndi thandizo limene abale athu amatipatsa. Iwo nthawi zonse amafuna kutithandiza, koma tiyenera kukhala anzeru ndi oganiza bwino tikamafuna kuti apeze nthawi yodzatithandiza. Pajatu timafuna kuti zilizonse zimene okhulupirira anzathu angatichitire tikakhala pa mavuto, azichita mwa kufuna kwawo osati mokakamizika.

N’zosachita kufunsa kuti abale ndi alongo anu amakhala okonzeka nthawi zonse kukuthandizani. Koma nthawi zina sangakwanitse kukuthandizani. Ngati izi zitachitika, dziwani kuti Yehova adzakuthandizani pa vuto lililonse limene mungakumane nalo, ngati mmene anachitira ndi wamasalmo.​—Sal. 116:1, 2; Afil. 4:10-13.

Motero musazengereze kulandira moyamikira thandizo lililonse limene Yehova angakupatseni, makamaka pa nthawi imene mwapanikizika ndi mavuto. (Sal. 55:22) Yehova amafuna kuti muzichita zimenezi. Komatu iye amafunanso kuti mukhale munthu “wopereka mokondwera.” Choncho ‘tsimikizani mumtima mwanu’ kupereka zilizonse zimene mungathe pochirikiza kulambira koona. (2 Akor. 9:6, 7) Mukatero, mudzatha kuchita zonse ziwiri, kulandira moyamikira ndi kupereka ndi mtima wonse.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 31]

“Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?”​—Sal. 116:12

▪ Tiziyesetsa kupeza mipata yoti “tichitire onse zabwino”

▪ Yesetsani kukhala anthu olimbikitsa komanso otsitsimula mwauzimu kwa ena

▪ Yesetsani mmene mungathere kugwira ntchito yopanga ophunzira