Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu

“Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu

“Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu

“Tsutsani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani.”​—YAK. 4:7.

1. Kodi Yesu ankadziwa kuti adzatsutsidwa ndi ndani, ndipo kodi ankadziwa kuti zotsatira zake zidzakhala zotani?

YESU KHRISTU anadziwa kuti adzatsutsidwa ndi Mdyerekezi. Mfundo imeneyi inaonekera m’mawu amene Mulungu ananena kwa njoka. Mawuwa kwenikweni ankauza mngelo woipa amene analankhula pogwiritsira ntchito njokayo. Mulungu anati: ‘Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo [mbali ya kumwamba ya gulu la Yehova], ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo iye [Yesu Khristu] adzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.’ (Gen. 3:14, 15; Chiv. 12:9) Palembali, mawu akuti Yesu adzalaliridwa chitende ankatanthauza kuti adzavutika kwakanthawi kochepa. Izi zinachitikadi, chifukwa iye ataphedwa padziko lapansi pano, Yehova anamuukitsa ndi kumupatsa ulemerero wakumwamba. Koma kulalira mutu wa njoka kukutanthauza kuti Mdyerekezi adzaphwanyidwa moti sadzakhalakonso.​—Werengani Machitidwe 2:31, 32; Aheberi 2:14.

2. N’chifukwa chiyani Yehova sanakayike kuti Yesu adzatha kutsutsa Mdyerekezi?

2 Yehova sankakayika kuti Yesu adzakwaniritsa ntchito imene iye anam’tuma padziko pano ndi kudzam’tsutsa Mdyerekezi. N’chifukwa chiyani Yehova sankakayika ngakhale pang’ono? N’chifukwa choti anam’lenga Yesuyo kalekale kumwamba, ndipo kwa nthawi yonseyo Yehova anaona kuti “mmisiri” ndiponso “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” ameneyu anali womvera ndiponso wokhulupirika. (Miy. 8:22-31; Akol. 1:15) Motero Yesu atatumizidwa padziko lapansi, Mulungu analola kuti Mdyerekezi amuyese mpaka imfa. Mulungu ankadziwa bwino kuti Mwana Wake wobadwa yekha ameneyu sangagonje ngakhale atayesedwa kwambiri.​—Yoh. 3:16.

Yehova Amateteza Atumiki Ake

3. Kodi Mdyerekezi amamva bwanji akaona atumiki a Yehova?

3 Yesu anati Mdyerekezi ndiye “wolamulira wa dzikoli,” ndipo n’chifukwa chake Yesuyo anazunzidwa. Motero anawauziratu ophunzira ake kuti nawonso adzazunzidwa. (Yoh. 12:31; 15:20) Dzikoli lili m’manja mwa Satana Mdyerekezi, motero limadana ndi Akhristu oona chifukwa iwo amatumikira Yehova ndipo amalalikira za chilungamo. (Mat. 24:9; 1 Yoh. 5:19) Mdyerekezi amalimbana makamaka ndi otsalira a odzozedwa amene m’tsogolo muno adzalamulire ndi Khristu mu Ufumu wake wakumwamba. Satana amalimbananso ndi Mboni za Yehova zina zambirimbiri zimene zili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.”​—1 Pet. 5:8.

4. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti anthu a Mulungu akwanitsa kutsutsa Mdyerekezi m’nthawi yathu ino?

4 Monga gulu timakwanitsa kutsutsa Mdyerekezi chifukwa chothandizidwa ndi Yehova Mulungu. Taganizirani mfundo zotsatirazi zotsimikizira mfundo imeneyi. Pazaka 100 zam’mbuyomu, olamulira ankhanza kwambiri ayesapo kuthetseratu gulu la Mboni za Yehova. Koma olamulira ankhanzawo ndi amene anatha, pamene Mboni zinapitirira kuwonjezeka moti panopo zatsala pang’ono kukwana 7,000,000, ndipo zili m’mipingo pafupifupi 100,000 padziko lonse.

5. Kodi lonjezo la pa Yesaya 54:17 lakwaniritsidwa motani kwa atumiki a Yehova?

5 Polankhula ndi Aisiraeli ngati kuti akulankhula ndi “mkazi” wake, Mulungu analonjeza kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chawo chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.” (Yes. 54:6, 11, 17) Padziko lonse anthu a Yehova “m’masiku otsiriza” ano, aona kuti Mulungu amakwaniritsa lonjezo limeneli. (2 Tim. 3:1-5, 13) Sitileka kutsutsa Mdyerekezi, ndipo chida chilichonse chimene angayese kugwiritsira ntchito kuti awononge anthu onse a Mulungu sichingaphule kanthu, chifukwa Yehova ali nafe.​—Sal. 118:6, 7.

6. Kodi ulosi wa Danieli umati ulamuliro wa Mdyerekezi uli ndi tsogolo lotani?

6 Mapeto a dongosolo lonse loipali atsala pang’ono kufika ndipo zinthu zonse zokhudzana ndi ulamuliro wa Satana zidzawonongedwa. Mneneri Danieli anauziridwa kulemba ulosi wakuti: “Masiku a mafumu aja [amene akulamulira masiku ano] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [amene alipowa]. Nudzakhala chikhalire.” (Dan. 2:44) Zimenezi zikadzachitika, ulamuliro wa Satana ndiponso wa anthu opanda ungwiro udzathetsedwa. Zinthu zonse zokhudzana ndi dongosolo la Mdyerekezi sizidzapezekanso, ndipo Ufumu wa Mulungu udzalamulira padziko lonse popanda aliyense woutsutsa.​—Werengani 2 Petulo 3:7, 13.

7. Kodi tikudziwa bwanji kuti mtumiki wa Yehova aliyense angathe kutsutsa Mdyerekezi?

7 N’zosakayikitsa ngakhale pang’ono kuti Yehova apitiriza kuteteza gulu lake kuti liziyenda bwino mwauzimu. (Werengani Salmo 125:1, 2.) Nanga bwanji aliyense payekha? Baibulo limati ifenso tingathe kutsutsa Mdyerekezi, monga Yesu anachitira. Ulosi umene Khristu ananena kudzera mwa mtumwi Yohane umasonyeza kuti ngakhale kuti Satana akutitsutsa, “khamu lalikulu” la anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi pano, lidzapulumuka mapeto a dongosolo lino la zinthu. Malemba amati khamuli likufuula kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa [Yesu Khristu].” (Chiv. 7:9-14) Baibulo limanena za odzozedwa kuti akugonjetsa Satana, ndipo limati a “nkhosa zina,” nawonso akum’tsutsa. (Yoh. 10:16; Chiv. 12:10, 11) Koma timafunika kuchita khama ndi kupemphera mochokera pansi pamtima kuti Mulungu ‘atilanditse kwa woipayo.’​—Mat. 6:13.

Chitsanzo Chabwino Kwambiri Potsutsa Mdyerekezi

8. Kodi mayesero oyamba olembedwa m’Baibulo, a Yesu ali m’chipululu, anali otani ndipo Khristu anam’yankha bwanji Mdyerekezi?

8 Mdyerekezi anayesa Yesu kuti achite zosakhulupirika. Yesu ali m’chipululu, Satana anamuyesa pofuna kuti achite zinthu zosamvera Yehova. Koma Yesu anam’tsutsa Satanayo ndipo anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Atakhala masiku 40 osadya, usiku ndi masana omwe, Yesu ayenera kuti anali ndi njala yadzaoneni. Satana anamuuza Yesu kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.” Koma Yesu anakana kugwiritsira ntchito mphamvu zimene Mulungu anam’patsa, pa zofuna zake. M’malomwake iye anayankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu asakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’”​—Mat. 4:1-4; Deut. 8:3.

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsutsa Mdyerekezi akamayesa kupezerapo mwayi pa zinthu zimene anthufe timalakalaka mwachibadwa?

9 Masiku ano, Mdyerekezi amafuna kusokoneza atumiki a Yehova pogwiritsira ntchito zinthu zimene anthufe timalakalaka mwachibadwa. N’chifukwa chake, tiyenera kukana motsimikiza tikamayesedwa kuti tichite zachiwerewere zimene zafala kwambiri m’dzikoli. Mawu a Mulungu amanena mosapita m’mbali kuti: “Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasochezedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna osungidwira kugonedwa ndi amuna anzawo, kapena amuna ogonana ndi amuna anzawo . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akor. 6:9, 10) Pamenepa n’zoonekeratu kuti anthu amene safuna kusintha makhalidwe awo oipa sadzaloledwa kukhala m’dziko latsopano la Mulungu.

10. Kodi lemba la Mateyo 4:5, 6, limasonyeza kuti Satana anamuyesanso bwanji Yesu pofuna kuti achite zosakhulupirika?

10 Malemba amati Yesu adakali m’chipululu, anakumananso ndi mayesero otsatirawa: “Mdyerekezi anam’tenga kupita naye mu mzinda woyera, ndipo anamukweza pa tchinga la linga la kachisi ndi kumuuza kuti: ‘Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi; popeza Malemba amati, “Iye adzalamula angelo ake za inu, ndipo adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti musawombetse konse phazi lanu pamwala.”’” (Mat. 4:5, 6) Satana ankafuna kuti Yesu achite zinthu zogometsa, zodzionetsera kuti ndi Mesiya. Komatu Yesu akanatero akanachita zinthu zosalemekeza Mulungu ndipo Yehova sakanagwirizana nazo. Apanso Yesu anakhala wokhulupirika kwa Yehova ndipo anayankha pogwiritsira ntchito lemba. Iye anati: “Malemba amatinso, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”​—Mat. 4:7; Deut. 6:16.

11. Kodi Satana angatiyese motani ndipo chingachitike n’chiyani ngati titagonja?

11 Satana angatiyesenso kuti tizifuna ulemerero m’njira zosiyanasiyana. Angachititse kuti tizifuna kutsanzira mmene anthu a m’dzikoli amavalira ndi kudzikongoletsera, kapenanso kuti tizikonda zosangalatsa zowononga khalidwe. Koma tikamanyalanyaza malangizo a m’Baibulo n’kumatsanzira dzikoli, kodi tingayembekezere angelo kutiteteza ku mavuto amene angatigwere chifukwa cha kusamverako? Ngakhale kuti Mfumu Davide analapa machimo ake okhudza Bateseba, Mulungu sanam’teteze ku mavuto amene machimowo anam’bweretsera. (2 Sam. 12:9-12) Tisam’yese Yehova m’njira zolakwika, monga pokhala mabwenzi a dzikoli.​—Werengani Yakobe 4:4; 1 Yohane 2:15-17.

12. Kodi lemba la Mateyo 4:8, 9, limati Mwana wa Mulungu anayesedwanso bwanji ndipo kodi iye anatani?

12 Mayesero enanso amene Mdyerekezi anagwiritsira ntchito m’chipululu anali ofuna kum’patsa Yesu mphamvu zolamulira monga wandale. Satana anam’sonyeza Yesuyo maufumu onse a padziko lapansi ndi ulemerero wawo, n’kumuuza kuti: “Zinthu zonsezi ndikupatsani ngati mugwada pansi ndi kundilambirako ine.” (Mat. 4:8, 9) Apatu Mdyerekezi anasonyeza ukathyali wake wonse chifukwa anafuna kuti Yesu achite zinthu zosakhulupirika pom’lambira iyeyo m’malo molambira Yehova. Poganizira kwambiri zofuna kulambiridwa, Satana Mdyerekezi, yemwe poyamba anali mngelo wokhulupirika, anakhala wochimwa, wosirira, ndiponso mngelo woipa kwambiri wokonda kuyesa ena. (Yak. 1:14, 15) Koma mosiyana ndi Satana, Yesu anafunitsitsa kukhalabe wokhulupirika kwa Atate wake wakumwamba n’chifukwa chake ananena kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo utumiki wako wopatulika uyenera kupita kwa iye yekha basi.’” Pamenepa tingaone kuti Yesu anatsutsanso Mdyerekezi mwamphamvu komanso motsimikiza. Mwana wa Mulungu sankafuna kuti akhale mbali ya dziko la Satana, n’chifukwa chake anakana kumulambira Satanayo.​—Mat. 4:10; Deut. 6:13; 10:20.

“Tsutsani Mdyerekezi, Ndipo Adzakuthawani”

13, 14. (a) Pom’sonyeza Yesu maufumu onse apadziko, kodi kwenikweni Mdyerekezi ankafuna kum’patsa chiyani Yesuyo? (b) Kodi Satana amayesa bwanji kuwononga khalidwe lathu?

13 Pomuuza kuti am’patsa maufumu onse a padziko, Mdyerekezi anali kufuna kum’patsa Yesu mphamvu zolamulira zimene munthu aliyense sanakhalepo nazo. Satanayu ankaganiza kuti Yesu akopeka akaona maufumuwo ndipo avomera kukhala mtsogoleri wandale wamphamvu kwambiri padziko lonse. Masiku ano Mdyerekezi safuna kutipatsa maufumu, koma amayesa kuipitsa mitima yathu pogwiritsira ntchito zinthu zimene timaona, kumva, ndi kuganiza.

14 Dzikoli lili m’manja mwa Mdyerekezi. Motero zinthu zomwe zimafalitsidwa zilinso m’manja mwake. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti zoonera, zomvetsera ndiponso zowerenga, zambiri masiku ano zimalimbikitsa zachiwerewere ndiponso zachiwawa. Otsatsa malonda amafuna kutilimbikitsa kuti tizifuna kugula zinthu zambirimbiri zosafunika kwenikweni. Nthawi zonse Mdyerekezi amayesa kutikopa ndi zinthu zimene tingakopeke nazo tikaziona, kuzimva kapena kuziganizira. Tikamakana kuonera, kumvetsera ndiponso kuwerenga, zinthu zotsutsana ndi Malemba, timakhala ngati tikunena kuti: “Choka Satana!” Tikamatero timakhala tikutsanzira Yesu posalola ngakhale pang’ono kutengera makhalidwe oipa a dziko la Satanali. Tikakhala kunyumba, kuntchito, kusukulu, ndiponso pakati pa achibale athu, timaonetsanso kuti sitili mbali ya dziko la Satana tikamachita zinthu zosonyeza kuti ndife Mboni za Yehova komanso kuti timatsatira Khristu.​—Werengani Maliko 8:38.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala tcheru nthawi zonse kuti tithe kum’tsutsa Satana?

15 Atamuyesanso kachitatu n’kulephera kumuchititsa zinthu zosakhulupirika kwa Mulungu “Mdyerekezi uja anamusiya” Yesu. (Mat. 4:11) Koma sikuti Satana anaganiza zoti sadzamuyesanso Yesu, chifukwa Baibulo limati: “Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo [m’chipululu], anam’siya kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Tikatsutsa Mdyerekezi, tiyenera kuthokoza Yehova. Komanso nthawi zonse tizipempha kuti Mulungu atithandize, chifukwa Mdyerekezi amabweranso panthawi imene iyeyo akuona kuti ndi yabwino kwambiri, osati kwenikweni panthawi imene ifeyo tikuyembekezera kuti angatiyese. Motero, nthawi zonse tiyenera kukhala tcheru, kuti tithe kupitiriza kuchitira Yehova utumiki wopatulika ngakhale titakumana ndi mayesero otani.

16. Kodi ndi mphamvu iti imene Yehova amatipatsa, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuipempha?

16 Kuti tikwanitse kutsutsa Mdyerekezi, tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro kuti Mulungu atipatse mphamvu yoposa ina iliyonse, yomwe ndi mzimu Wake woyera. Mphamvu imeneyi imatithandiza kuchita zinthu zimene sitingathe kuchita mwamphamvu zathu zokha. Yesu anauza anthu omutsatira kuti Mulungu angathe kuwapatsa mzimuwu. Iye anati: “Choncho ngati inu, ngakhale muli oipa [poyerekezera ndi munthu wangwiro], mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Choncho tisasiye kupemphera kuti Yehova atipatse mzimu woyera. Mothandizidwa ndi mphamvu yosagonjetseka imeneyi, tingathe kum’tsutsa Mdyerekezi ngati tatsimikizadi kutero. Kuti tithe “kuchirimika polimbana ndi machenjera a Mdyerekezi,” nthawi zonse tiyenera kupemphera mochokera pansi pamtima komanso tiyenera kuvala zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.​—Aef. 6:11-18.

17. Kodi n’chiyani chinam’patsa Yesu chimwemwe kuti athe kutsutsa Mdyerekezi?

17 Palinso chinthu china chimene chinamuthandiza Yesu kutsutsa Mdyerekezi, chimenenso chingatithandize. Baibulo limati: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, [Yesu] anapirira mtengo wozunzikirapo, nanyoza manyazi, ndipo wakhala pansi ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Aheb. 12:2) Nafenso tingathe kukhala achimwemwe pokhalabe okhulupirika ku ulamuliro wa Yehova, polemekeza dzina lake loyera, ndiponso poganizira kwambiri mphoto ya moyo wosatha umene ukubwera. Tidzasangalala mosaneneka Satana ndi ntchito zake zonse zikadzachotsedwa kosatha ndipo “ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Sal. 37:11) Motero, pitirizani kutsutsa Mdyerekezi, monga mmene Yesu anachitira.​—Werengani Yakobe 4:7, 8.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Perekani umboni wotsimikiza kuti Yehova amateteza anthu ake.

• Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pankhani yotsutsa Satana?

• Kodi inuyo mungatsutse Mdyerekezi m’njira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Tikakhala mabwenzi a dziko timasanduka adani a Mulungu

[Chithunzi patsamba 31]

Yesu anakana kulandira maufumu onse a padziko amene Satana anamupatsa