Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wonjezerani Chidwi Chofuna Kudziwa Zinthu Molondola

Wonjezerani Chidwi Chofuna Kudziwa Zinthu Molondola

Wonjezerani Chidwi Chofuna Kudziwa Zinthu Molondola

ATUMIKI onse a Yehova amafuna kuti Mulungu aziwakonda. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kum’tumikira mwakhama. Koma mtumwi Paulo anatchula vuto linalake limene Ayuda ena a m’nthawi yake anali nalo. Iwo anali “okangalika potumikira Mulungu; koma mosam’dziwa molondola.” (Aroma 10:2) Motero, tisakhulupirire komanso tisalambire Yehova mongotengeka maganizo. Tifunikira kumudziwa molondola Mlengi wathu ndi kuchita zimene amafuna.

M’kalata yake ina, Paulo anasonyeza kuti Mulungu amakonda anthu amene ali ndi chidwi chodziwa zinthu. Iye anapemphera kuti otsatira Khristu ‘adziwe molondola’ chifuniro cha Mulungu ‘kuti aziyenda moyenera Yehova ndi kum’kondweretsa kwathunthu.’ Angachite zimenezi pamene ‘akupitiriza kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezera kudziwa kwawo Mulungu molondola.’ (Akol. 1:9, 10) N’chifukwa chiyani tifunikira ‘kudziwa zinthu molondola’? Ndipo n’chifukwa chiyani tifunikira kuwonjezera zinthu zimene timadziwa?

Maziko a Chikhulupiriro

Kudziwa Mulungu molondola ndiponso zimene Iye amafuna, ndi maziko a chikhulupiriro chathu. Tikapanda kudziwa zinthu zimenezi molondola, chikhulupiriro chathu mwa Yehova chimakhala ngati nyumba yopanda maziko olimba imene sichedwa kugwa. Paulo anatilimbikitsa kutumikira Mulungu ndi ‘luntha lathu la kulingalira’ ndiponso “mwa kusintha maganizo athu.” (Aroma 12:1, 2) Kuphunzira Baibulo nthawi zonse kungatithandize kuchita zimenezi.

Ewa, mpainiya wokhazikika wa ku Poland anati: “Ndikanakhala kuti sindimaphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, bwenzi ndisakum’dziwa Yehova molondola. Makhalidwe anga achikhristu akanalowa pansi ndipo chikhulupiriro changa mwa Mulungu chikanakhala chosalimba moti ndikanawononga ubwenzi wanga ndi Mulungu.” Zimenezi siziyenera kutichitikira. Taganizirani za mwamuna wina amene anawonjezera kum’dziwa molondola Yehova ndipo anakondedwa kwambiri ndi Mulungu.

“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”

Salmo 119 yomwe ndi nyimbo yandakatulo imasonyeza mmene wamasalmo ankaonera malamulo, zikumbutso, malangizo, ndi maweruzo a Yehova. Wamasalmo analemba kuti: “Ndidzadzikondweretsa nawo malemba anu. . . . Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa.” Analembanso kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.”​—Sal. 119:16, 24, 47, 48, 77, 97.

Mawu akuti ‘kukondweretsa’ ndi ‘kulingirira’ amatanthauza kusinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso kusangalala ndi kusinkhasinkhako. Mawu amenewa amasonyeza kuti wamasalmo ankakonda kwambiri kuphunzira chilamulo cha Mulungu. Sanakonde Mawu a Mulungu mongotengeka maganizo. Koma ankafunitsitsa ‘kulingirira’ chilamulo, kuti apeze nzeru m’mawu a Yehova. Mtima umenewu ukusonyeza kuti ankafuna kudziwa Mulungu ndi chifuniro chake molondola.

N’zoonekeratu kuti wamasalmo ankakonda Mawu a Mulungu kuchokera pansi pamtima. Choncho, tingadzifunse kuti: ‘Kodi inenso ndimatero? Kodi ndimakonda kuwerenga ndiponso kuganizira Malemba tsiku ndi tsiku? Kodi ndimawerenga Mawu a Mulungu mwakhama ndiponso kupemphera ndisanayambe kuwerenga?’ Ngati tingayankhe kuti inde ku mafunso amenewa, ndiye kuti ‘tikuwonjezera kudziwa kwathu Mulungu molondola.’

Ewa anati: “Nthawi zonse ndimayesetsa kupeza njira zabwino zochitira phunziro langa la Baibulo. Kuyambira nthawi imene ndinalandira kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ ndimakagwiritsa ntchito nthawi zonse ndikamaphunzira. Ndimayesetsa kufufuza zinthu m’buku la Insight on the Scriptures komanso m’mabuku ena.”

Taganiziraninso chitsanzo cha Wojciech ndi mkazi wake Małgorzata amene ali ndi udindo waukulu wosamalira banja lawo. Kodi amapeza bwanji nthawi yophunzira Baibulo? “Aliyense amayesetsa kupeza nthawi yake yophunzira Mawu a Mulungu. Ndiyeno, paphunziro la banja ndiponso pocheza timakambirana mfundo zosangalatsa ndi zolimbikitsa zimene aliyense anapeza.” Kuphunzira mozama Mawu a Mulungu kumawasangalatsa ndiponso kumawathandiza ‘kuwonjezera kudziwa zinthu molondola.’

Muziphunzira Mwachidwi

Akhristufe timadziwa kuti Mulungu amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Mfundo imeneyi imagogomezera kufunika kowerenga Baibulo ndi kuyesetsa ‘kuzindikira tanthauzo lake.’ (Mat. 15:10) Chimene chingatithandize kuchita zimenezi ndicho kuphunzira mwachidwi. Anthu a ku Bereya anachita zimenezi Paulo atawalalikira uthenga wabwino. Baibulo limati: “Iwowa analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho.”​—Mac. 17:11.

Kodi timakhala ndi chidwi pophunzira Baibulo ndiponso timaika maganizo athu onse pa zimene tikuphunzirazo ngati Abereya? Mkhristu angayesetse kutsanzira Abereya ngakhale kuti poyamba sankakonda kuwerenga. Ndipo anthu ena akamakalamba sakonda kuwerenga ndi kuphunzira zinthu, koma zisakhale choncho kwa Akhristu. Kaya munthu ndi wamkulu bwanji, angathe kupewa zododometsa. Ndipo mukamawerenga muziyesetsa kupeza mfundo zouzako ena. Mwachitsanzo, muziyesetsa kuuza mkazi kapena mwamuna wanu kapenanso mnzanu wachikhristu zinthu zimene mwawerenga paphunziro lanu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musamaiwale zimene mwawerengazo komanso zingathandize anthu ena.

Tikamaphunzira tiyenera kutsatira chitsanzo cha Ezara, mtumiki wa Mulungu wakale amene “adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova.” (Ezara 7:10) Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muyenera kupeza malo abwino ophunzirira. Ndipo musanayambe kuphunzira pempherani kwa Yehova kuti akutsogolereni ndi kukupatsani nzeru. (Yak. 1:5) Kenako, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndiphunzira chiyani m’nkhani imene ndikufuna kuwerengayi?’ Pamene mukuwerenga pezani mfundo zazikulu. Mungalembe penapake mfundo zimene mwapeza kapena kudula mzere kunsi kwa mfundo zimene mukufuna kumazikumbukira. Onani mmene mungagwiritsire ntchito mfundozo polalikira, posankha zochita kapena polimbikitsa okhulupirira anzanu. Pomaliza yesani kuganiziranso zimene mwawerengazo. Zimenezi zidzakuthandizani kukumbukira zomwe mwaphunzira.

Ewa pofotokoza zimene amachita anati: “Ndikamawerenga Baibulo ndimagwiritsa ntchito malemba owonjezera a pa danga lapakati pa Baibulo, Watch Tower Publications Index ndi Watchtower Library ya pa kompyuta. Ndimalemba mfundo zimene ndikufuna kuzigwiritsa ntchito muutumiki.”

Anthu ena akhala akuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu kwa zaka zambiri. (Miy. 2:1-5) Ngakhale zili choncho, ali ndi maudindo ambiri ndipo zimawavuta kupeza nthawi yochitira phunziro laumwini. Ngati umu ndi mmene zinthu zilili pamoyo wanu, kodi mungatani kuti muzipeza nthawi yowerenga?

Zimene Mungachite Kuti Mupeze Nthawi

Tonse timadziwa kuti sizovuta kupeza nthawi yochita zinthu zimene timakonda. Anthu ambiri aona kuti kukhala ndi zolinga zimene angakwanitse monga kuwerenga Baibulo lonse, n’kothandiza kuti aziwerenga moikira mtima. N’zoona kuti zingaoneke zovuta kwambiri kuwerenga mndandanda wautali wa mayina a makolo a munthu winawake, nkhani zatsatanetsatane zofotokoza kachisi wakale kapena maulosi ovuta amene akuoneka kuti sakugwirizana ndi moyo wamasiku ano. Yesetsani kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa cholinga chanu. Mwachitsanzo, musanawerenge Malemba amene akuoneka ovuta, mungawerenge kaye mbiri ya nkhaniyo kapena mmene ikukuthandizirani m’buku la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” limene lili m’zinenero zoposa 50.

Kuganizira zimene mukuwerenga m’Baibulo n’kothandiza. Kungakuthandizeni kuona nkhaniyo m’maganizo mwanu. Kugwiritsa ntchito malingaliro amenewa kungapangitse kuti muzisangalala komanso kuti mupindule ndi zimene mukuwerenga. Motero, mudzakhala wofunitsitsa kupeza nthawi yophunzira. Ndipo simudzavutika kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.

Mfundo tafotokozazi zingathandize munthu aliyense payekha. Koma kodi mabanja amene amakhala ndi zochita zambiri angatani kuti azipeza nthawi? Bwanji osapeza nthawi yokambirana za phindu lokhala ndi phunziro la banja? Pokambiranapo mungapeze njira zina zothandiza, monga kudzuka m’mawa kwambiri tsiku lililonse, kapena masiku ena n’cholinga chowerenga Baibulo. Mwina mungaone kuti mufunika kusintha zinthu zina pabanjapo. Mwachitsanzo, mabanja ena aona kuti n’zothandiza kukambirana lemba la tsiku kapena kuwerenga Baibulo akangomaliza kudya. Iwo asanachotse mbale kapena asanayambe kuchita zinthu zina, amakambirana Malemba kapena kuwerenga Baibulo kwa mphindi 10 kapena 15. Poyamba zimenezi zingaoneke zovuta, koma m’kupita kwa nthawi amazolowera ndipo amayamba kusangalala nalo.

Wojciech ndi Małgorzata akufotokoza zimene zinathandiza banja lawo kuti: “Kale nthawi yathu inkangothera pa zinthu zosafunika. Kenako tinagwirizana zochepetsa nthawi imene timathera potumiza mauthenga a pa kompyuta. Tinachepetsanso nthawi imene timathera pocheza ndipo tinasankha tsiku ndi nthawi yophunzira.” Banja limeneli silinong’oneza bondo chifukwa chosintha zinthu ndipo inunso simunganong’oneze bondo.

Kudziwa Zinthu Molondola N’kofunika

Tikamaphunzira Mawu a Mulungu mozama ‘tingabale zipatso m’ntchito iliyonse yabwino.’ (Akol. 1:10) Mukamachita zimenezi pa moyo wanu, anthu onse adzaona kuti mukupita patsogolo. Mudzakhala munthu wokonda zinthu zauzimu ndiponso womvetsa bwino mfundo za m’Baibulo. Mudzasankha bwino zochita pa moyo wanu ndipo mudzatha kuthandiza ena komanso simudzachita zinthu monyanyira ngati mmene amachitira anthu osazindikira. Ndipo chofunika kwambiri, mudzayandikana kwambiri ndi Yehova. Mudzamvetsa bwino makhalidwe ake ndipo zimenezi zidzaonekera mukamauza ena za iye.​—1 Tim. 4:15; Yak. 4:8.

Kaya muli ndi zaka zambiri kapena mumadziwa zinthu zochuluka, yesetsani kukonda Mawu a Mulungu ndipo aphunzireni mozama ndi mtima wofuna kudziwa zinthu. Dziwani kuti Yehova sadzaiwala khama lanu ndipo adzakudalitsani kwambiri.​—Aheb. 6:10.

[Bokosi patsamba 13]

‘TIKAWONJEZERA KUDZIWA ZINTHU MOLONDOLA’. . .

Timalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndiponso timayenda moyenera Yehova.​—Akol. 1:9, 10

Timapeza nzeru, timakhala ozindikira ndipo timatha kusankha zochita mwanzeru.​—Sal. 119:99

Timasangalala kwambiri pothandiza ena kuyandikira kwa Yehova.​—Mat. 28:19, 20

[Chithunzi patsamba 14]

Kupeza malo abwino ophunzirira kungakhale kovuta koma n’kofunika

[Chithunzi patsamba 15]

Mabanja ena amawerenga Baibulo akangomaliza kudya