Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• N’chifukwa chiyani “Chipangano Chakale” sichingathe ntchito?
Yehova Mulungu wachikondi ndi yemwe anachilemba, osati mulungu wosadziwika wankhanza. Yesu ndi otsatira ake oyambirira nthawi zonse ankagwira mawu m’Malemba Achiheberi. Malemba amenewa ali ndi malangizo othandiza pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndiponso amatipatsa chiyembekezo chabwino cham’tsogolo.—9/1, masamba 4 mpaka 7.
• Kodi n’chiyani chimene chakwaniritsidwa chifukwa cholola nthawi kudutsa kuchokera pamene Adamu ndi Hava anachimwa?
Pazaka pafupifupi 6,000 zomwe zadutsa zochitika zatsimikizira kuti Satana ndi wabodza chifukwa Adamu ndi Hava anafa komanso mbadwa zawo zambirimbiri zakhala zikufa. Zasonyezanso kuti anthu zinthu sizingawayendere bwino popanda kudalira Mulungu komanso kuti si oyenera kudzilamulira okha kapena kulongosola mapazi awo.—9/15, masamba 6 ndi 7.
• Kodi n’chifukwa chiyani Yakobo sanadzudzulidwe chifukwa chonamizira kuti anali Esau?
Yakobo ndi amene anali woyenerera kulandira madalitso a bambo ake chifukwa anagula ukulu kwa Esau. Ndipo Isake atazindikira kuti wadalitsa Yakobo, sanafune kusintha maganizo ake. Nayenso Mulungu sanalowerere pankhaniyi ndipo zimenezi zikuonetseratu kuti anafuna kuti madalitsowo apite kwa Yakobo.—10/1, tsamba 31.
• Kodi kukhala ndi chikumbumtima kumatsutsana bwanji ndi chiphunzitso chakuti anthu anachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina?
Anthu a mitundu yonse ndi zikhalidwe zosiyanasiyana amachita zinthu zofuna kuthandiza ena ngakhale kuti kuchita zimenezo kungaike moyo wawo pangozi. Anthu sangakhale okoma mtima chonchi akanakhala kuti anachokera ku nyama chifukwa choti nyamazo zimangochita zinthu zoti izo zokha zikhale ndi moyo basi.—10/15, tsamba 20.
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu ndi wodzichepetsa, ndipo amasonyeza motani khalidwe limeneli?
Popeza iye ndi Mlengi ndiponso Wolamulira Wamkulu, iye ndi wosiyana ndi anthu chifukwa palibe zinthu zimene angalephere kuchita. Koma malinga ndi lemba la 2 Samueli 22:36, Mulungu ndi wodzichepetsa m’njira yakuti amaganizira anthu otsika amene amayesetsa kum’tumikira ndipo amawasonyeza chifundo. Kunena mophiphiritsa, tingati iye amatsika pansi kuti akomere mtima anthu omwe amamuopa.—11/1, masamba 4 ndi 5.
• Kodi mapale akale amatsimikizira bwanji kuti nkhani za m’Baibulo n’zolondola?
Akatswiri okumba zinthu zakale anapeza mapale ku Samariya pomwe panalembedwa maina a mafuko 7 omwe ali pa Yoswa 17:1-6. Mapale amene anapezeka ku Aradi amatsimikizira nkhani zokhudza mabanja a ansembe ndipo alinso ndi dzina la Mulungu. Mapale a ku Lakisi amasonyeza bwino mmene nkhani zandale ndiponso chipwirikiti zinalili mu Yuda, Ababulo asanawononge mzindawu.—11/15, masamba 12 mpaka 14.
• N’chiyani chimene chimatitsimikizira kuti Luka ndi amene analemba buku la Machitidwe?
Uthenga Wabwino wa Luka ndiponso Machitidwe a Atumwi analembedwa kuti apite kwa Teofilo ndi zimenezi zikusonyeza kuti Luka ndi yemwe analemba mabuku onse awiri. Mawu akuti “ife,” “athu” ndi “ifeyo” akusonyeza kuti Luka ankachita nawo zinthu zina zolembedwa m’bukuli. (Machitidwe 16:8-15)—11/15, tsamba 18.
• Kodi Mkhristu aziona bwanji nkhani ya kusaka kapena kusodza?
Kuyambira nthawi ya Nowa, Mulungu walola anthu kupha ndi kudya nyama. Komano powauza kuti ayenera kukhetsa magazi, anasonyeza kuti moyo wanyama uyenera kulemekezedwa chifukwa ndi wochokera kwa Mulungu. Choncho Akhristu sayenera kupha nyama monga masewera kapena kuti asangalale. M’pofunika kumvera malamulo a Kaisara ndiponso kuganizira chikumbumtima cha anthu ena. (Aroma 14:13)—12/1, tsamba 31.