Ndinaphunzira Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse
Mbiri ya Moyo Wanga
Ndinaphunzira Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse
Yosimbidwa ndi Aubrey Baxter
Linali Loweruka madzulo, chaka cha 1940, pamene anthu awiri anandimenya mwamphamvu moti mpaka ndinagwa pansi. Apolisi awiri ankaona zimenezi ataima poteropo, koma m’malo mondilanditsa, anayamba kunditukwana n’kumachemerera anthu ondimenyawo. Zinthu zimene zinayamba kundichitikira zaka pafupifupi zisanu m’mbuyo mwake, n’zimene zinachititsa kuti ndifike pozunzidwa chonchi. Panthawiyo ndinkagwira ntchito pamgodi wina wamalasha. Talekani ndifotokoze bwinobwino.
M’BANJA mwathu tinalimo anyamata anayi ndipo ineyo ndinali wachitatu kubadwa. Ndinabadwa mu 1913 m’tawuni yotchedwa Swansea, yomwe ili m’mphepete mwa nyanja, m’chigawo cha New South Wales, m’dziko la Australia. Ndili ndi zaka zisanu, tonse m’banja mwathu tinadwala matenda oopsa kwambiri a fuluwenza ya ku Spain, omwe anapha anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse. Mwamwayi tonse tinapulumuka. Koma mu 1933, m’banja mwathu munagwa zovuta; mayi athu anamwalira ali ndi zaka 47. Mayi anali munthu wokonda Mulungu, ndipo m’mbuyomo analandira mabuku awiri ofotokoza Baibulo (otchedwa Light), omwe Mboni za Yehova zinkagawira.
Panthawiyo ndinkagwira ntchito pamgodi wamalasha. Ntchito yanga sinali yopanikiza nthawi zambiri, ndipo nthawi zina ndinkangokhala basi. Motero ndinkatenga mabukuwo kuntchito n’kumawawerenga pogwiritsira ntchito tochi younikira m’migodi imene ndinkavala pamutu. Sizinanditengere nthawi kudziwa kuti choonadi ndi chimenechi. Ndinayambanso kumvetsera nkhani zofotokoza Baibulo zomwe zinkaulutsidwa ndi Mboni pa wailesi. Chimwemwe changa chinafika podzaza tsaya pamene bambo, azichimwene anga, komanso mng’ono wanga anayamba kuchita chidwi ndi choonadi cha m’Baibulo.
Mu 1935, m’banja mwathu munagwanso zovuta zina; mng’ono wanga Billy, anadwala chibayo n’kumwalira. Machitidwe 24:15) Kenako, bambo anga ndi azichimwene anga, Verner ndi Harold, komanso akazi awo, anadzipereka kwa Mulungu. Panopo anthu ena onse m’banja mwanga anamwalira. Amene adakalipo ndi mkazi wa Verner, dzina lake Marjorie, ndi mkazi wa Harold, dzina lake Elizabeth. Iwowa akutumikirabe Yehova mwakhama.
Anamwalira ali ndi zaka 16 zokha basi. Komano panthawiyi banja lathu lonse linakhazika mtima pansi podziwa kuti pali chiyembekezo choti akufa adzauka. (Kuphunzira Kudalira Yehova
Nthawi yoyamba imene ineyo pandekha ndinakumanapo ndi Mboni za Yehova inali mu 1935, pamene mayi wina wa ku Ukraine anafika pakhomo pathu ali pa njinga. Lamlungu lake ndinapita kumsonkhano wachikhristu kwa nthawi yoyamba, ndipo patatha mlungu umodzi ndinakhala nawo pamsonkhano wokonzekera kulowa m’munda. Wamboni amene ankachititsa msonkhanowo anandipatsa timabuku tingapo, ndipo ndinadabwa kwambiri akundiuza kuti ndilowe ndekha m’munda. Nditafika pakhomo loyamba, ndinachita mantha kwambiri moti ndinkangolakalaka nthaka itatseguka n’kundimeza. Koma mwininyumbayo anali wansangala kwambiri mpaka analandira mabuku.
Malemba monga Mlaliki 12:1 ndi Mateyo 28:19, 20 anandikhudza mtima kwambiri, moti ndinayamba kulakalaka upainiya, kapena kuti utumiki wanthawi zonse. Bambo anga anasangalala ndi maganizo amenewa. Ndisanabatizidwe n’komwe, ndinakonzeratu zodzayamba upainiya pa July 15, 1936. Patsiku limenelo, ndinapita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Sydney, komwe anandiuza kuti ndikachite upainiya pamodzi ndi apainiya ena 12, m’dera la kunja kwa mzinda wa Sydney, lotchedwa Dulwich Hill. Apainiyawa anandiphunzitsa kugwiritsira ntchito chipangizo chogayira tirigu pamanja, chomwe ankagwiritsira ntchito panthawiyo pofuna kusinira ndalama zawo.
Kuchita Upainiya M’dera Lankhalango
Ndinabatizidwa chaka chomwecho ndipo ananditumiza ku dera lapakati m’chigawo cha Queensland pamodzi ndi apainiya ena awiri, Aubrey Wills ndi Clive Shade. Tinatenga zinthu zosiyanasiyana monga galimoto ya Aubrey, njinga zingapo, galamafoni ya m’manja youlutsirapo nkhani zofotokoza Baibulo, hema limene tinadzagonamo kwa zaka zitatu, mabedi atatu, tebulo, ndiponso poto wachitsulo, woti tiziphikira. Tsiku langa lophika litafika, ndinafuna kuphika chakudya chamadzulo chosiyana kwambiri ndi zakudya zimene ena ankaphika. Motero ndinatenga ndiwo zamasamba n’kusakaniza ndi phala la tirigu. Koma palibe aliyense amene anadya. Motero ndinatenga chakudyacho n’kupatsa hatchi yomwe inaima chapafupi. Hatchiyo itanunkhiza chakudyacho, inangopukusa mutu, basi n’kumapita! Apa m’pamene ndinasiyira kuphika zakudya m’njira zochita kupeka ndekha.
Kenako, tinaganiza zofulumizitsa ntchito yolalikira m’gawo lathu. Tinatero poligawa magawo atatu kuti aliyense azilowa m’gawo lakelake. Nthawi zambiri dzuwa linkandilowera kutali kwambiri moti nthawi zina ndinkangogona m’makomo mwa anthu ena achifundo, kumidzi imene ndinkalalikira. Tsiku lina ndinagona pabedi lawofuwofu, m’nyumba ya alendo pafamu ina yang’ombe. Tsiku lotsatira, ndinagona pansi m’kanyumba ka mlenje wina. M’kanyumbako munali fungo guu, chifukwa munadzaza ndi zikopa zosauma za nyama. Nthawi zambiri ndinkagona m’tchire. Tsiku lina usiku, ndinazindikira kuti mimbulu yazungulira malo amene ndinagona, ndipo phokoso la kulira kwake linadzaza dera lonseli. Usiku umenewu tulo sindinatione ayi, koma kutacha ndinazindikira kuti mimbuluyo sinkatsata ineyo ayi, koma inkatsata matumbo a nyama amene anatayidwa chapafupi pompo.
Kulalikira ndi Galimoto Yokhala ndi Zokuzira Mawu
Tinkagwiritsira ntchito galimoto yokhala ndi zokuzira mawu pofalitsa Ufumu wa Mulungu. Kumpoto kwa chigawo cha Queensland kuli mzinda wotchedwa Townsville, ndipo apolisi anatilola kuimika galimoto yathu m’dera la zamalonda mu mzindawo. Komabe nkhani yomwe tinkaulutsayo inakwiyitsa anthu achipembedzo china (chotchedwa Salvation Army), ndipo anatiuza kuti tichoke. Tinakana ndipo anthu asanu achipembedzocho anayamba kugunyuza galimotoyo mwankhondo. Apa n’kuti ineyo ndikuyang’anira zokuzira mawu m’kati mwa galimotoyo. Ngakhale kuti tinali ndi ufulu woimika galimoto yathu pamenepa, tinaona kuti si chinthu chanzeru kukakamira, motero anthuwo atasiya kugunyuzako, tinachokapo.
Titapita m’tawuni ya Bundaberg, munthu wina wachidwi anatibwereka boti kuti tigwiritsire ntchito pofalitsa uthenga tili mu mtsinje wa Burnett, womwe unadutsa m’kati mwa tawuniyo. Aubrey ndi Clive anakwera botilo atatenga zokuzira mawu zija, ndipo ine ndinatsala pa holo imene tinachita lendi. Usiku wa tsiku limenelo, mawu amphamvu a Joseph F. Rutherford, wa ku likulu la Mboni za Yehova, anamveka mu mzinda wonse wa Bundaberg, akulengeza uthenga wosapita m’mbali wa m’Baibulo. Kunena zoona, iyi inali nthawi yosangalatsa kwambiri, komabe anthu a Mulungu anafunika kulimba mtima ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.
Mavuto Anawonjezeka Chifukwa cha Nkhondo
Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itangoyamba mu September 1939, magazini ya Nsanja ya Olonda ya November 1 inalongosola zoti Akhristu sayenera kulowerera ndale kapena nkhondo. Nkhani imeneyi inadzandipindulitsa patsogolo motero ndinasangalala kwambiri kuti ndinaiwerenga. Ine, Aubrey, ndi Clive tinalalikira limodzi zaka zitatu, ndipo kenaka tinapatsidwa ntchito zimene zinatilekanitsa. Ndinasankhidwa kukakhala woyang’anira woyendayenda kumpoto kwa Queensland. Pochita ntchito imeneyi, ndinkakumana ndi zinthu zambiri zimene zinkayesa chikhulupiriro changa mwa Yehova.
Mu August 1940, ndinachezera mpingo wa ku Townsville, umene unali ndi apainiya anayi, Percy, ndi Ilma Iszlaub * komanso Norman Belloti ndi mchemwali wake Beatrice. Patatha zaka 6 Beatrice anadzakhala mkazi wanga. Tsiku lina Loweruka, nthawi ya madzulo, titamaliza ulaliki wa mumsewu, ndinakumana ndi zoopsa zimene ndatchula kumayambiriro zija. Komabe zimenezi zinangondilimbikitsa kwambiri kutumikira Yehova.
Kumpoto, kunali apainiya awiri, mayina awo Una Kilpatrick ndi mng’ono wake Merle. Ndipo iwo ankachita khama pantchito yolalikira. Tsiku lina ndinalowa nawo muutumiki, ndipo kenaka anandipempha kuti ndiwawolotse mtsinje paboti kuti apite ku nyumba ya banja lina lachidwi. Koma ndinafunikira kusambira kuti ndikatenge botilo, lomwe linali tsidya lina la mtsinjewo n’kubwera nalo pamene panali alongowo kuti akwere, kenaka n’kuwawolotsa. Koma nditasambira n’kufika pa botilo, ndinapeza kuti palibe zopalasira. Pambuyo pake tinamva kuti munthu wina amene ankadana nafe anabisa zopalasira botilo. Koma izi sizinandilepheretse kuthandiza alongowo. Kwa zaka zingapo, ineyo ndinali nditagwirapo ntchito yopulumutsa anthu kuti asamire, motero kusambira siinali nkhani kwa ine. Ndiye ndinatenga chingwe cha botilo n’kuchimangirira m’chiuno mwanga, n’kuyamba kusambira uku ndikukoka botilo mpaka kufika nalo pamene panali alongowo. Iwo atakwera, ndinachitanso chimodzimodzi n’kuwawolotsa kupita tsidya linalo. Yehova anatidalitsa chifukwa cha khama lathuli,
moti patsogolo pake banja lachidwilo linadzakhala la Mboni.Kutetezedwa ndi Dzanja la Yehova
Pofuna kukhazikitsa chitetezo, asilikali anaika malodibuloko chapafupi ndi tawuni ya Innisfail. Popeza ndinali wodziwika monga nzika ya m’deralo, ndinkatha kupeza mosavuta chilolezo cholowera m’deralo, ndipo zimenezi zinkandithandiza kwambiri kuti ndizitha kulowetsa abale odzacheza m’derali otumidwa ndi ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Komabe, kuti abalewo adutse pa malodibulokowo, ndinkawabisa penapake, chapansi pampando wakumbuyo wa galimoto yanga.
Nthawi imeneyi mafuta a galimoto anali osowa, choncho galimoto zambiri sizinkayendera mafuta okha ayi komanso makala. Makalawo akakolera moto ankatulutsa gasi amene ankagwiranso ntchito ngati mafuta a galimoto. Motero galimoto yangayo ndinkadutsa nayo usiku, nditaunjika matumba a makala pamwamba pampando umene ndabisapo m’baleyo. Ndiyeno, poima pa lodibuloko ndinkapemerera kwambiri galimotoyo kuti makalawo akolere kwambiri. Ndinkatero pofuna kuti asilikaliwo agwe ulesi n’kusiya kufufuza kwambiri galimotoyo. Tsiku lina usiku, ndinawauza asilikali mokuwa kuti: “Ndikangosiya kupemerera, galimotoyi izima chifukwa cha kuchepa kwa gasi mu injini ndipo ikazima ivuta kuti ilirenso.” Chifukwa cha kutentha, phokoso, ndiponso utsi umene galimotoyi inkatulutsa, asilikaliwo anangofufuza galimotoyi mwapatalipatali n’kundiuza kuti ndizipita.
Panthawi imeneyi ndinapemphedwa kuyang’anira ntchito yokonzekera msonkhano wa Mboni ku Townsville. Chakudya chinali chosinira, motero tinachita kupita ku khoti kuti tikapeze chilolezo chogula chakudya choti chikwanire pamsonkhanowo. Panthawiyi, abale athu achikhristu ankamangidwa chifukwa chokana kulowerera ndale. Motero nditakonza zopita kukhoti kukaonana ndi mkulu wa zamalamulo, ndinadzifunsa chamumtima kuti, ‘Kodi ndikuchita zanzeru kapena ndikupalamula mavu pachisa?’ Ndinalimba mtima n’kupita monga anandiuzira.
Ndinaonekera pamaso pa mkulu wa zamalamuloyo, iye atakhala mu ofesi yolemekezeka zedi, ndipo anandiuza kuti ndikhale pansi. Nditamuuza zimene ndabwerera, anasintha nkhope n’kukhala kwa nthawi yaitali atangoti maso dwii pa ine. Kenaka anasinthanso n’kukhala bwinobwino, n’kundifunsa kuti: “Ukufuna chakudya chochuluka motani?” Ndinamupatsa mndandanda womwe tinalembapo mitundu ya zakudya zomwe tinkafuna. Pamtundu uliwonse wa chakudya tinalemba zochepa zedi. Atayang’ana mndandandawo ananena kuti: “Zakudya zimenezitu sizingakwanire ayi. M’pofunika tiwonjezere.” Ndinachoka mu ofesiyo ndikuthokoza kwambiri Yehova, chifukwa chondipatsa phunziro linanso pankhani yomukhulupirira.
Mu January 1941 ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa ku Australia. Anthu ambiri anayamba kutikayikira mpaka kufika pomanena kuti ndife akazitape a dziko la Japan. Panthawi ina, apolisi ndi asilikali odzaza magalimoto awiri anafika pa famu yomwe Mboni za Yehova zinagula ku Atherton, kuti zizilimako zakudya. Iwowa akuti anabwerera kudzafufuza chizindikiro chimene tinkagwiritsira ntchito polankhulana ndi adani awowo. Anthu ena ankanenanso kuti tinabzala chimanga m’njira yopereka uthenga winawake kwa munthu amene ali m’ndege. Koma zinadziwika kuti zinthu zonsezi zinali zabodza.
Poti ntchito yathu inaletsedwa, tinayenera kusamala pokapereka mabuku kwa abale. Mwachitsanzo, kutatuluka buku la ana (lotchedwa Children), ndinatenga katoni ya mabukuwa ku Brisbane, n’kuyenda nayo pasitima molowera chakumpoto, n’kumasiya ena mwa mabukuwa m’mipingo yosiyanasiyana ya m’madera amene sitimayo inkaima. Pofuna kuti apolisi ndiponso asilikali ofufuza zinthu agwe ulesi kutsegula katoniyo, ndinayenda ndi sowo yozungulira yochekera matabwa ndipo ndinkaimangirira pa katoniyo ndisanatuluke msitimayo. Ngakhale kuti njirayi inali yosavuta, palibe anaitulukira. Anthu a Yehova anasangalala kwambiri pamene ntchito yawo inatsegulidwanso mu June 1943. Woweruza mlandu umenewu ananena kuti ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa pa zifukwa zosamveka ndiponso zopondereza.
Tinaitanidwa Kuti Tikalowe Usilikali
Chaka chotsatira, ineyo, Aubrey Wills ndiponso Norman Belloti, tinaitanidwa kuti tikalowe usilikali. Aubrey ndi Norman ataitanidwa, panangopita mlungu umodzi inenso n’kuitanidwa. Anthu awiriwa anaweruzidwa kuti akakhale m’ndende miyezi 6. Panthawiyi, magazini onse a Nsanja ya Olonda otumizidwa pa positi, omwe ankapita kwa Mboni zodziwika, ankasowetsedwa. Koma sankasowetsa magazini opita kwa anthu ena amene anangolembetsa kuti azilandira magaziniwa. Motero ifeyo tinapatsidwa ntchito yopeza mmodzi wa anthu amenewa, n’kukopera magazini imene walandirayo, kenaka n’kugawira makope a magaziniyo kwa Mboni zina. Mwanjira imeneyi, tinkalandira chakudya chauzimu nthawi zonse.
Zinali zodziwikiratu kuti adzandipatsa chilango
chokakhala m’ndende miyezi 6, motero atangopereka chilangochi, ndinachita apilo nthawi yomweyo, potsatira malangizo amene ndinapatsidwa ndi ofesi ya nthambi ku Sydney. Cholinga chathu chinali choti tichedwetse mlanduwu kuti ndisakalowe msanga m’ndende mpaka titapeza munthu wina woti asamalire ntchitoyi. Ndinagwiritsira ntchito nthawi imeneyi kuyendera ena mwa a Mboni 21 amene anali m’ndende kumpoto kwa Queensland. Ambiri mwa abale amenewa anali m’ndende imodzi, ndipo woyang’anira akaidiwo ankadana nafe kwambiri. Ndinamuuza kuti asatiletse kukumana ndi abale athuwo chifukwa abusa a zipembedzo zina amawalola kukaona anthu awo. Nditamuuza zimenezi anapsa mtima kwambiri n’kunena kuti: “Ndikanapatsidwa mphamvu, ndikanalamula kuti Mboni za Yehova zonse aziike pamzere n’kuziwombera.” Nthawi yomweyo asilikali olondera ndendeyo ananditulutsa mwamsangamsanga.Nthawi yomvanso mlandu umene ndinachita apilo uja itakwana, aboma anandipatsa munthu wondiimira pamlunduwo, mogwirizana ndi lamulo. Komabe, ngakhale zinali choncho ndinakayankha ndekha mlanduwo. Zimenezi zinandichititsa kuti ndidalire kwambiri Yehova. Ndipo Yehova anakhala nanedi. (Luka 12:11, 12; Afilipi 4:6, 7) Zinali zovuta kumvetsa kuti mlandu uja wandikomera. Izi zinatheka chifukwa choti pa chisamani chofotokoza mlandu umene ndinali kuimbidwa, analakwitsapo zina ndi zina.
Mu 1944, ndinatumizidwa kukayang’anira dera lalikulu lomwe limafika m’chigawo chonse cha kum’mwera kwa Australia, kumpoto kwa Victoria, ndiponso mzinda wa Sydney, womwe uli m’chigawo cha New South Wales. Chaka chotsatira, padziko lonse panayambika ntchito yokamba nkhani kwa anthu, ndipo wokamba nkhani aliyense ankafunika kukonzekera yekha nkhani yonseyo, mogwirizana ndi mfundo zopezeka pa chipepala cha tsamba limodzi, chimene ankapatsidwa. Tinafunika nthawi kuti tizolowere kukamba nkhani kwa ola lathunthu, koma tinachita khama kutero podalira Yehova ndi mtima wonse, ndipotu anatidalitsa.
Ndinakwatira N’kukhala ndi Maudindo Atsopano
Mu July 1946, ndinakwatira Beatrice Bellotti, ndipo tinayamba kuchitira limodzi upainiya. Tinkagona mu kalavani yamatabwa, kapena nyumba yokoka ndi galimoto. Tili ndi mwana mmodzi yekha, dzina lake Jannyce (mwachidule timam’tchula kuti Jann), ndipo anabadwa mu December 1950. Tinachita upainiya m’madera angapo, kuphatikizapo tawuni ya Kempsey, ku New South Wales. Kumeneku kunalibe Mboni kupatulapo ifeyo basi. Lamlungu lililonse tinkapita ku holo yomwe anthu am’derali amaloledwa kugwiritsira ntchito, ndipo ndinkakhala nditakonzeka kukamba nkhani. Tinkalengeza za nkhaniyi kwa anthu powagawira timapepala. Kwa miyezi ingapo, anthu amene ankamvetsera nkhani yangayi anali mkazi wanga Beatrice ndi mwana wathu wakhanda, Jann basi. Koma posakhalitsa, kunayamba kubwera anthu ena. Tikunena pano ku Kempsey kuli mipingo iwiri yolimba.
Jann ali ndi zaka ziwiri, tinapita kukakhala ku Brisbane. Atamaliza sukulu, banja lathu lonse linachita upainiya kwa zaka zinayi m’tawuni ya Cessnock, ku New South Wales. Kenaka tinabwerera ku Brisbane kukathandiza mayi a mkazi wanga, omwe ankadwala. Panopo, ndikutumikira monga mkulu mumpingo wa Chermside.
Ineyo ndi mkazi wanga timathokoza kwambiri Yehova chifukwa chotidalitsa m’njira zosawerengeka. Dalitso lina ndi loti tathandiza anthu 32 kum’dziwa Yehova. Ineyo ndimathokozanso Yehova, chifukwa chondipatsa mkazi wofatsa, koma wolimba mtima kwambiri polengeza choonadi cha m’Baibulo. Iyeyu wakhaladi mkazi wangwiro komanso mayi wabwino kwambiri chifukwa amakonda ndi kukhulupirira Mulungu, ndipo ali ndi ‘diso lolunjika chimodzi.’ (Mateyo 6:22, 23; Miyambo 12:4) Ine limodzi ndi mkazi wanga timanena moyamikira kuti: “Wodala munthu amene akhulupirira Yehova.”—Yeremiya 17:7.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 19 Mbiri ya moyo wa Percy Iszlaub inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya May 15, 1981.
[Chithunzi patsamba 9]
Tinkayendera galimoto yokhala ndi zokuzira mawu iyi kumpoto kwa Queensland
[Chithunzi patsamba 10]
Apa, ndikuthandiza Mlongo Kilpatrick ndi mng’ono wake kusuntha galimoto yawo m’nyengo yamvula, kumpoto kwa Queensland
[Chithunzi patsamba 12]
Tsiku la ukwati wathu