Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
“Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chimphona.”—SALMO 127:4.
1, 2. Kodi ana ali ngati ‘mivi m’dzanja la chimphona’ m’njira yotani?
MUNTHU woponya mivi akukonzekera kulasa chinthu chinachake. Akuika muvi wake bwinobwino pa uta wake, ndiyeno akuukoka mwamphamvu. Ngakhale kuti wachita zonsezi, iye sakupupuluma pofuna kuti achetekere bwinobwino muvi wakewo. Kenako, akuuponya. Kodi muviwo ulasa chinthu chimene akufunacho? Yankho la funsoli likudalira pa zinthu zosiyanasiyana, monga luso la woponya miviyo, mphepo, ndiponso mmene muviwo ulili.
2 Mfumu Solomo inayerekezera ana ndi ‘mivi m’dzanja la chimphona.’ (Salmo 127:4) Taonani mmene fanizoli lingagwiritsidwire ntchito. Muvi wa munthu woponya mivi sukhala nthawi yaitali pa uta. Kuti asaphonye, amafunika kuuponya mwamsangamsanga. Mofanana ndi zimenezi, makolo amakhala ndi nthawi yochepa yophunzitsira ana awo kukonda Yehova mochokera pansi pamtima. Zaka zimene zimaoneka ngati zochepa zikangotha, anawo amakhala atakula kenako amakakhala kwaokha. (Mateyo 19:5) Kodi anawo adzapitiriza kukonda ndi kutumikira Mulungu pambuyo pochoka panyumbapo? Apanso, yankho lake likudalira pa zinthu zosiyanasiyana. Zitatu mwa zinthu zimenezi ndi luso lophunzitsa limene makolowo ali nalo, mmene panyumba pomwe anawo akuleredwera palili, ndiponso mmene ‘muviwo,’ kapena kuti mwanayo, akugwiritsira ntchito zinthu zimene akuphunzitsidwa. Tiyeni tione mwatsatanetsatane mfundo zimenezi. Poyamba, tiona zina mwa zinthu zimene kholo lodziwa kuphunzitsa limachita.
Makolo Odziwa Kuphunzitsa Amapereka Chitsanzo Chabwino
3. N’chifukwa chiyani zonena za makolo ziyenera kugwirizana ndi zochita zawo?
3 Yesu anapereka chitsanzo kwa makolo chifukwa chakuti iye ankachita zimene anali kulalikira. (Yohane 13:15) Koma, anadzudzula Afarisi, amene ‘ankangonena’ zinthu “osachita.” (Mateyo 23:3) Kuti makolo alimbikitse ana awo kukonda Yehova, zonena zawo ziyenera kugwirizana ndi zochita zawo. Kungonena zinthu popanda kuchita n’kosathandiza, mofanana ndi uta wopanda chingwe.—1 Yohane 3:18.
4. Kodi makolo ayenera kudzifunsa mafunso ati, ndipo n’chifukwa chiyani?
1 Akorinto 15:33) Makolo ndi amene amakhala bwenzi lenileni la mwana kwa nthawi yaitali makamaka panthawi imene ali wamng’ono ndipo panthawiyi m’pamene amaphunzira zambiri pamoyo wake. Choncho makolo ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine bwenzi lotani? Kodi chitsanzo changa chimalimbikitsa mwana wanga kukhala ndi makhalidwe abwino? Kodi ndikupereka chitsanzo chotani pankhani zofunika kwambiri monga kupemphera ndi kuphunzira Baibulo?’
4 N’chifukwa chiyani chitsanzo cha makolo chili chofunika kwambiri? Popeza anthu akuluakulu amaphunzira kukonda Mulungu potsanzira Yesu, ana angaphunzire kukonda Yehova potsanzira makolo awo. Anthu amene mwana amacheza nawo angalimbikitse kapena ‘kuwononga makhalidwe abwino’ a mwanayo. (Makolo Odziwa Kuphunzitsa Amapemphera Pamodzi ndi Ana Awo
5. Kodi ana angaphunzire chiyani m’mapemphero a makolo?
5 Ana angaphunzire zinthu zambiri zokhudza Yehova akamamvetsera mapemphero anu. Kodi ana angaphunzire chiyani akamamva mukuthokoza Mulungu panthawi yachakudya, ndiponso mukupemphera pa phunziro la Baibulo? N’zodziwikiratu kuti adzaphunzira kuti Yehova amatipatsa zofunika pamoyo ndipo tiyenera kumuthokoza komanso amatiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Awatu ndi maphunziro ofunika kwambiri.—Yakobe 1:17.
6. Kodi makolo angathandize motani ana kuona kuti Yehova amasamalira aliyense payekhapayekha?
6 Komabe, zingakhale zothandiza kwambiri mukamapemphera pamodzi ndi banja lanu panthawi zinanso kuwonjezera panthawi ya chakudya ndi yophunzira Baibulo, ndiponso mukamakambirana nkhani zimene zimakhudza inuyo ndi ana anuwo. Mukatero mudzathandiza ana anu kudziwa kuti banja lanu limadalira Yehova ndipo iye amasamalira aliyense payekhapayekha. (Aefeso 6:18; 1 Petulo 5:6, 7) Bambo wina anati: “Tinkapemphera ndi mwana wathu wamkazi kuyambira ali khanda. Pamene ankakula, m’mapemphero athu tinkatchula nkhani zimene zinkam’khudza monga za anzake ocheza nawo ndi zina. Nthawi yonse mpaka pamene analowa m’banja, palibe tsiku limene sitinapempherepo limodzi.” Kodi sizingakhale bwino kuti nanunso muzipemphera ndi ana anu tsiku lililonse? Kodi mungawathandize kuti aziona Yehova monga Bwenzi lawo, limene limamvetsa maganizo awo kuwonjezera pa kuwapatsa zofunika zakuthupi ndi zauzimu?—Afilipi 4:6, 7.
7. Kodi makolo ayenera kudziwa chiyani kuti mapemphero awo azikhala achindunji?
7 Kuti mapemphero anu azikhala achindunji, mumafunika kudziwa zimene zikuchitikira mwana wanu. Taonani zimene bambo wina wa ana awiri ananena: “Mlungu uliwonse ukamatha, ndinkadzifunsa mafunso awiri awa: ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene zadetsa nkhawa ana anga mlungu umenewu? Ndipo ndi zabwino ziti zimene zawachitikira?’” Makolo, kodi mungadzifunse mafunso ngati amenewa, ndiyeno ena mwa mayankho akewo n’kuwatchula m’mapemphero anu pamene muli limodzi ndi ana anuwo? Pochita zimenezi, mungaphunzitse anawo kuti azikonda Yehova, kuwonjezera pa kuwaphunzitsa kupemphera kwa Iye amene amamva mapemphero.—Salmo 65:2.
Makolo Odziwa Kuphunzitsa Amalimbikitsa Chizolowezi Chabwino Chophunzira
8. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuthandiza ana awo kukhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu?
8 Kodi mmene kholo limaonera kuphunzira Baibulo zingakhudze bwanji ubwenzi wa mwana ndi Mulungu? Kuti ubwenzi uliwonse wa anthu ukhale wolimba, anthuwo amayenera kulankhulana ndiponso kumvetserana. Tingamvetsere mawu a Yehova Mateyo 24:45-47; Miyambo 4:1, 2) Choncho, pofuna kuthandiza ana awo kuti azikonda Yehova nthawi zonse, makolo ayenera kulimbikitsa anawo kukhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu.
mwa kuphunzira Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo a “kapolo wokhulupirika.” (9. Kodi ana angathandizidwe bwanji kukhala ndi chizolowezi chabwino chophunzira?
9 Kodi ana angathandizidwe bwanji kukhala ndi chizolowezi chabwino chophunzira? Apanso, chitsanzo cha makolo n’chofunika kwambiri. Kodi ana anu amakuonani mukuwerenga kapena kuphunzira Baibulo nthawi zonse? N’kutheka kuti mumakhala wotanganidwa kusamalira ana anu, ndipo mwina mukuona kuti simungapeze nthawi yophunzira ndi kuwerenga. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi ana anga amandiona nthawi zonse ndikuonera TV?’ Ngati ndi choncho, kodi mungapatulepo nthawi ina n’cholinga choti muwasonyeze chitsanzo chabwino pankhani ya phunziro laumwini?
10, 11. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kumakambirana ndi ana awo za m’Baibulo nthawi zonse?
10 Kukambirana za m’Baibulo nthawi zonse ndi njira ina yabwino imene makolo angathandizire ana awo kumvetsera mawu a Yehova. (Yesaya 30:21) Ena angafunse kuti, ‘Kodi m’pofunikanso kuchita phunziro la banja ndi ana ngati makolo amapita ndi anawo kumisonkhano yampingo?’ Pali zifukwa zambiri zochitira phunziro la banja. Yehova wapereka kwa makolo udindo wophunzitsa ana. (Miyambo 1:8; Aefeso 6:4) Phunziro la banja limathandiza ana kuona kuti kulambira si mwambo chabe wongochita limodzi ndi anthu ena, koma ndi nkhani yomwe banja lililonse palokha limafunika kuchita.—Deuteronomo 6:6-9.
11 Komanso, phunziro la banja lochititsidwa mwaluso limathandiza makolo kudziwa maganizo a ana awo pankhani zauzimu ndiponso zamakhalidwe. Mwachitsanzo, kwa ana aang’ono, makolo angagwiritse ntchito mabuku monga Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. * Pafupifupi ndime iliyonse m’buku lophunzirira Baibulo limeneli, ili ndi funso limene lingathandize mwana kunena zimene akuganiza pankhani imene mukukambirana. Mwa kufotokoza malemba amene ali m’bukuli, makolo angathandize ana kukulitsa luntha la kuzindikira kuti ‘azisiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’—Aheberi 5:14.
12. Kodi makolo angatani kuti phunziro la banja lizigwirizana ndi zosowa za mwana, ndipo n’chiyani chimene inuyo mwaona kuti n’chothandiza pankhaniyi?
12 Anawo akamakula, phunzirolo lizigwirizana ndi zosowa zawo. Taonani mmene bambo ndi mayi wina anathandizira ana awo achinyamata kuganizira bwino za pempho la anawo loti apite ku dansi ya kusukulu. Bamboyo anati: Miyambo 23:15.
“Tinauza ana athuwo kuti pa phunziro lathu la banja lotsatira, ine ndi mkazi wanga tidzakhala ngati ana, ndipo iwo adzakhale ngati makolo. Wina adzakhale bambo ndipo wina adzakhale mayi, koma anafunika kuthandizana kufufuza nkhani ya madansi a kusukulu ndi kutipatsa malangizo.” Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Bamboyo anapitiriza kuti: “Tinadabwa kuona mmene anawo (monga makolo) anasiyanitsira choyenera ndi cholakwika. Anatifotokozera (monga ana) momveka bwino kwambiri zifukwa za m’Baibulo zimene zinawapangitsa kuona kuti si bwino kupita ku dansi. Chinanso chimene chinatichititsa chidwi ndi malingaliro amene anatipatsa a zinthu zina zimene tingachite m’malo mwa madansi. Izi zinatithandiza kwambiri kudziwa bwino maganizo ndi zofuna zawo.” Zoonadi, pamafunika khama ndiponso kuganiza bwino kuti phunziro la banja lizichitika nthawi zonse ndiponso lizikhala logwirizana ndi zosowa za pabanja, ndipo phindu lake n’lalikulu kwambiri.—Onetsetsani Kuti Panyumba Pali Mtendere
13, 14. (a) Kodi makolo angatani kuti pabanja pawo pazikhala mtendere? (b) Kodi ubwino woti makolo azivomereza zimene alakwitsa ndi wotani?
13 Nthawi zambiri muvi suphonya ngati woponyayo wachetekera ndi kuuponya pamene kuli bata. N’chimodzimodzinso ndi ana, iwo nthawi zambiri amaphunzira kukonda Yehova ngati makolo amayesetsa kuti panyumba pawo pazikhala mtendere. Yakobe analemba kuti: “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” (Yakobe 3:18) Kodi makolo angatani kuti panyumba pawo pazikhala mtendere? Mwamuna ndi mkazi wake amafunika kuonetsetsa kuti ukwati wawo ndi wolimba. Iwo akamakondana ndi kupatsana ulemu sizivuta kuti ana nawonso azikonda ndi kupatsa anthu ena ulemu, kuphatikizaponso Yehova. (Agalatiya 6:7; Aefeso 5:33) Chikondi ndiponso kupatsana ulemu zimalimbikitsa mtendere. Ndipo mwamuna ndi mkazi amene amakhala mwamtendere savutika kuthetsa mikangano yomwe ingabuke m’banja mwawo.
14 N’zoona kuti panopa padziko lapansi palibe mabanja angwiro. Makolo nthawi zina angalephere kusonyeza chipatso cha mzimu pochita zinthu zosiyanasiyana ndi ana awo. (Agalatiya 5:22, 23) Zikatero, kodi makolo ayenera kuchita chiyani? Ngati iwo amavomereza kulakwa kwawo, kodi zingapangitse kuti anawo asamawapatse ulemu? Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye anali ngati bambo wauzimu kwa anthu ambiri. (1 Akorinto 4:15) Komabe, anavomera poyera kuti analakwitsapo zinthu zina. (Aroma 7:21-25) Komatu, timam’patsa ulemu kwambiri chifukwa choti anali wodzichepetsa ndiponso ankanena zoona. Ngakhale kuti anali ndi zophophonya, Paulo sanakayikire kuuza mpingo wa ku Korinto kuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.” (1 Akorinto 11:1) Ngati nanunso mumavomereza zophophonya zanu, mwachidziwikire ana anu angathe kunyalanyaza zophophonyazo.
15, 16. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kukonda abale ndi alongo awo achikhristu, ndipo angachite motani zimenezi?
15 Kodi n’chiyaninso chimene makolo angachite kuti ana awo asamavutike kukonda Yehova? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ngati wina anena kuti: ‘Ndimakonda Mulungu,’ koma amada m’bale wake, ndi wonama. Pakuti amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yohane 4:20, 21) Choncho, mukamaphunzitsa ana anu kukonda abale ndi alongo awo achikhristu, mumakhala mukuwaphunzitsa kukonda Mulungu. Motero, ndi bwino kuti makolo azidzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zokhudza mpingo zimene ndimalankhula kawirikawiri zimakhala zolimbikitsa kapena zonyoza?’ Kodi mungadziwe motani zimenezi? Muzimvetsera mwatcheru zimene ana anu amanena pankhani ya misonkhano ndiponso zokhudza abale ndi alongo a mu mpingo wanu. Mosakayikira mungamve anawo akubwereza zimene inuyo mumanena.
16 Kodi makolo angachite chiyani pofuna kuthandiza ana awo kuti azikonda abale awo auzimu? Peter, bambo wa ana awiri achinyamata, anati: “Kuyambira ana athu ali aang’ono, nthawi ndi nthawi tinkaitana abale ndi alongo okhwima mwauzimu kuti adzadye ndi kucheza kunyumba kwathu, ndipo tinkasangalala kwambiri kuchita zimenezi. Anawo anakula ndi anthu okonda Yehova, ndipo panopa amaona kuti kutumikira Mulungu n’kosangalatsa kwambiri.” Dennis, yemwe ndi bambo wa ana aakazi asanu, anati, “Tinkalimbikitsa ana athu kuti azigwirizana ndi apainiya achikulire mumpingo, ndipo zikakhala zotheka tinkachereza oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo.” Kodi nanunso mungaonetsetse kuti mukuthandiza ana anu kuona mpingo monga mbali ya banja lanu?—Maliko 10:29, 30.
Udindo wa Mwana
17. Kodi ana amafunika kusankha kuchita chiyani?
17 Taganiziraninso chitsanzo cha woponya mivi chija. Ngakhale kuti iye angakhale ndi luso loponya mivi, n’zokayikitsa kuti angalase chinthu chimene akufuna ngati muvi umene waponyawo ndi wokhota. Inde, makolo angayesetse kuthandiza mwana, yemwe ali ngati muvi wokhota, kuti asinthe maganizo ake olakwika. Komabe, m’kupita kwa nthawi anawo amafunika kusankha okha ngati akufuna kuti azichita zofuna za dzikoli kapena kulola Yehova kuti ‘awongole mayendedwe’ awo.—Miyambo 3:5, 6; Aroma 12:2.
18. Kodi ena angakhudzidwe bwanji ndi zosankha za mwana?
18 Ngakhale kuti makolo ali ndi ntchito yofunika kwambiri yolera ana awo “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake,” mwana aliyense payekha ali ndi udindo wosankha kuti adzakhale wotani. (Aefeso 6:4) Motero, ananu dzifunseni kuti, ‘Kodi ndidzatsatira malangizo achikondi a makolo anga?’ Ngati mungatsatire malangizowo, mudzasankha moyo wabwino koposa. Makolo anu adzasangalala kwabasi, ndipo chofunika kwambiri n’chakuti mudzakondweretsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi makolo angapereke motani chitsanzo chabwino pankhani ya pemphero ndi phunziro laumwini?
• Kodi makolo angatani kuti panyumba pawo pakhale mtendere?
• Kodi ana amafunika kusankha kuchita chiyani, ndipo kodi ena amakhudzidwa motani ndi zosankha zawozo?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 28]
Kodi mwana wanu mumam’patsa chitsanzo chabwino pankhani ya phunziro laumwini?
[Chithunzi patsamba 29]
M’banja mukakhala mtendere, mumakhalanso chimwemwe