Khirisimasi, Kodi Ikulowera Kuti?
Khirisimasi, Kodi Ikulowera Kuti?
M’MWEZI ngati uno zaka 10 zapitazo, pachikuto cha magazini ya U.S.News & World Report panali nkhani ya mutu wakuti “Kufunafuna Khirisimasi.” Nkhaniyi inaunika Khirisimasi ngati “ikutsatiridwa bwino kapena ikuchulukitsa malonda.” Kodi Khirisimasi ikutsatiridwadi bwino?
Nkhaniyo inafotokoza zifukwa zimene sitiyenera kuyembekezera zimenezo. Inati: “Palibe mbiri yokhudzana ndi kusunga tsiku limene Khristu anabadwa mpaka m’zaka za m’ma 300, pamene Constantine . . . anakhala mfumu ya Roma.” Zimenezi zinasonyeza “mbali ndithu ya umboni woti palibe aliyense amene ankadziwa bwino tsiku limene Yesu anabadwa.” Nkhaniyi inavomereza kuti, “mauthenga abwino, satchula chaka ngakhalenso mwezi weniweni kapena tsiku lenileni.” Mogwirizana ndi zimene wolemba mbiri wa pa yunivesite ya Texas ananena, “Akhristu oyambirira sankakondwerera kubadwa kwa Yesu.”
Pansi pa mutu waung’ono wakuti “Nkhani Yongoganiza,” nkhaniyo inafotokoza “chifukwa chimene tchalitchi chinasankhira tsiku la December 25.” Inavomereza kuti: “Maganizo a anthu ambiri ndi akuti, anapanga zimenezo mwadala kuti asandutse phwando la Saturnalia ndi mapwando ena achikunja kukhala ngati ndi Achikhristu.” “Poika tsiku la Khirisimasi kuti likhale kumapeto kwa mwezi wa December, nthawi imene anthu anali atazolowera kale kuchita chikondwerero, atsogoleri atchalitchi anatsimikiza kuti anthu ambiri adzakondwerera phwando la kubadwa kwa Mpulumutsi.” Pakatikati pa zaka za m’ma 1800, cholinga cha phwandolo chinasintha ndipo chinayamba kukhala cholimbikitsa kugula ndi kupatsana mphatso. “Mwambo watsopano wopatsana mphatso za pa Khirisimasi umenewu, unapereka mwayi woti malonda aziyenda, ndipo anthu amalonda ndiponso otsatsa malonda mwansanga anayamba kulimbikitsa nyengo imeneyi.”
Choncho palibe chifukwa chilichonse choyembekezera kuti Khirisimasi ingapite kwina kulikonse kupatulapo njira yosiyaniranatu ndi Chikhristu choona. Ngakhale kuti Khirisimasi ya masiku ano imalimbikitsa “malonda monyanyira,” mfundo ndi yakuti, Akhristu oona sanayembekezere kudzakondwerera kubadwa kwa Yesu. M’malo mwake, Baibulo limatsindika za dipo limene Khristu anapereka pa imfa yake ndi kuukitsidwa kwake kupita kumwamba. (Mateyo 20:28) Dipolo lidzakhala lofunika kwambiri kunthawi zonse za m’tsogolo.