Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito ya Mboni za Yehova Ikupita Patsogolo Pachilumba Chokongola

Ntchito ya Mboni za Yehova Ikupita Patsogolo Pachilumba Chokongola

Ntchito ya Mboni za Yehova Ikupita Patsogolo Pachilumba Chokongola

ALENDO okacheza m’dziko la Taiwan amadabwa ndi kubiriwira kwa zomera za pachilumbachi. Mpunga womwe umakhala wobiriwira bwino, umasintha n’kumaoneka wofiirira panthawi yokolola. M’mphepete mwa mapiri muli nkhalango zowirira kwambiri. Koma anthu amatsitsimulidwa kwambiri akaona minda ya mbewu zobiriwira bwino komanso mapiri ake okongola kusiyana ndi mmene amachitira ndi mizinda ya pachilumbachi yomwe ili ndi anthu ambiri. Ndipotu, izi n’zimene zinapangitsa munthu woyambirira kuona chilumbachi wochokera ku dziko lina la kumadzulo, kuti achipatse dzina lakuti Ilha Formosa, kapena kuti “Chilumba Chokongola.”

N’zoona kuti Taiwan n’chilumba chokongola koma chaching’ono ndipo chili ndi makilomita 390 m’litali mwake ndi makilomita 160 m’lifupi mwake, pa malo ake aakulu kwambiri. Dera lalikulu la chilumbachi ndi la mapiri ataliatali. Phiri la Yü Shan (lomwe limadziwikanso ndi dzina lakuti Morrison) ndi lalitali kuposa phiri lalitali kwambiri ku Japan, la Fuji kapena phiri la Cook lomwe ndi lalitali kwambiri ku New Zealand. Mapiri a pakatikati pa chilumbachi azunguliridwa ndi zigwa zomwe zimakafika mpaka kunyanja, ndipo m’zigwa zimenezi ndi mmene anthu omwe tsopano akupitirira 22 miliyoni a m’dziko la Taiwan amakhala.

Kuwonjezeka Kwina

Komabe, m’dziko la Taiwan mukuchitika kuwonjezeka kwa mtundu winanso, komwe kukuonekera bwino kwambiri. Kuwonjezeka kumeneku n’kwauzimu. Zimenezi zimaonekera chifukwa cha changu chimene anthu, aakulu ndi aang’ono, amasonyeza akangodziwa Mulungu woona, Yehova. N’zochititsa chidwi kuona kuwonjezeka kwa chiwerengero cha anthu amene akugwira ntchito mwakhama kuthandiza anthu ena kuphunzira za Yehova ndi cholinga chake.

Chifukwa cha kuwonjezeka kwa anthu kumeneku, nthambi inafunika kukulitsidwa. Mu December 1990, anagula malo omangapo ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova yokulirapo. Nthambi yakale, imene inali ku Taipei, inali yaing’ono moti sikanatha kuyang’anira ntchito ya ofalitsa Ufumu okwana 1,777 omwe anali ku Taiwan panthawiyo. Zaka zingapo pambuyo pake, mu August 1994, anamaliza kumanga nyumba zatsopano komanso zokongola ku Hsinwu. Zimenezi zinatheka chifukwa cha khama la antchito odzipereka, amisinkhu yosiyanasiyana, ochokera m’mayiko ena komanso m’dziko lomwelo. Panthawiyi n’kuti kuli ofalitsa uthenga wabwino wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo, okwana 2,515. Tsopano, papita zaka zoposa teni, ndipo chiwerengerochi chawirikiza kuposa kawiri, moti kuli ofalitsa oposa 5,500, ndipo mwezi uliwonse ofalitsa pafupifupi 1,400 amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Amene amachititsa chidwi kwambiri ndi anyamata ndi atsikana amene amakhala ngati “mame” otsitsimula a m’mawa.​—Salmo 110:3.

Achinyamata Olambira Yehova Akuwonjezeka

Ambiri omwe akufalitsa mwakhama uthenga wabwino ndi ana ang’onoang’ono. Ena ndi ana a kusukulu za pulayimale. Mwachitsanzo, m’tawuni ina imene ili kumpoto kwa Taiwan, banja lina linaitanidwa kuti likakhale nawo koyamba pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Pamsonkhano umenewu Mboni za Yehova zimaphunzira mmene zingaphunzitsire choonadi cha m’Baibulo. Banjalo linadabwa kuona mnyamata wamng’ono, dzina lake Weijun, akuwerenga Baibulo papulatifomu, mwaluso kwambiri kuposa mmene akuluakulu ena angawerengere. Kenako, pamisonkhano inanso yomwe iwo anapitako, anachita chidwi kwambiri kuona kuti ngakhale ana amene anali asanayambe sukulu akupereka mayankho ogwira mtima. Banja limeneli linafotokozapo mmene ana ang’onoang’ono amasonyezera khalidwe labwino pa Nyumba ya Ufumu.

N’chifukwa chiyani achinyamata amenewa aikira mtima kwambiri pa maphunziro a m’Baibulo, m’dziko limene anthu ambiri ndi a zipembedzo za Chibuda ndi Chitao? Chifukwa chakuti makolo awo achikristu atsatira malamulo a m’Baibulo ndipo achititsa moyo wa mabanja awo kukhala wosangalatsa chifukwa chokhala paubwenzi ndi Yehova. Chifukwa chakuti makolo a Weijun amayesetsa kuti phunziro la Baibulo la banja ndiponso utumiki wa kumunda ukhale wosangalatsa, mkulu wake wa Weijun limodzi ndi mchemwali wake ndi Mboni zobatizidwa. Posachedwapa, Weijun atapempha kuti achite nawo ntchito yolalikira, mayi ake ananena kuti, mnyamatayo anali atagawira kale magazini ambiri mwezi umenewo kuposa chiwerengero cha magazini onse amene banja lake linali litagawira. N’zoonekeratu kuti amakonda kwambiri kulankhula za choonadi, kuyankha pamisonkhano, ndiponso kuuza ena zimene waphunzira.

Achinyamatawa Akamakula

Kodi achinyamata oterewa akamakula amachita motani? Ambiri amapitirizabe kukonda kwambiri Yehova ndiponso utumiki. Mwachitsanzo, Huiping ali ku koleji. Tsiku lina aphunzitsi ake ananena kuti anthu a chipembedzo chinachake salandira magazi koma sankadziwa kuti anthu ake anali ndani. Ataweruka, Mkristu wachinyamatayu anafotokozera mphunzitsiyo kuti anthuwo ndi Mboni za Yehova ndipo anafotokozanso chifukwa chimene amachitira zimenezo.

Mphunzitsi wina anaonetsa vidiyo yonena za matenda opatsirana mwa kugonana. M’vidiyoyo anatchulamo lemba la 1 Akorinto 6:9, koma mphunzitsiyo ananena kuti Baibulo sililetsa kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Apanso, Huiping anauza mphunzitsiyo mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi.

Pamene mtsikana wina amene anali naye m’kalasi imodzi, dzina lake Shuxia, ankakonza lipoti lonena za chiwawa chochitika m’mabanja, Huiping anam’patsa Galamukani! ya November 8, 2001 yomwe pachikuto pake inali ndi mutu wakuti, “Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo” ndi kum’fotokozera kuti magaziniyo ili ndi mfundo zambiri za m’Baibulo pankhani imeneyo. Patapita nthawi, Shuxia anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Iye ndi Huiping tsopano amalalikira nawo uthenga wabwino kwa ena.

Akristu ambiri amene ali kusukulu amaona kuti n’zovuta kuti anthu aziwadziwa kuti amatsatira mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zimachitika makamaka m’matawuni ang’onoang’ono a kumidzi. Chifukwa cha chikhulupiriro chake ndiponso ntchito yake yolalikira, Zhihao ankafunika kulimbana ndi mtima wofuna kuchita zimene anzake akuchita. Iye anati: “Ndinathedwa nzeru kwambiri chifukwa chakuti ndinkaopa kukumana ndi anzanga a m’kalasi pamene ndili mu utumiki. Nthawi zina, pankakhala anzanga okwanira teni omwe amandinena.” Tsiku lina, aphunzitsi anamuuza Zhihao kuti akambe m’kalasi mwake nkhani yonena za chipembedzo chake. Iye anati: “Ndinaganiza zoyamba nkhani yanga ndi Genesis chaputala 1 ndiyeno kenako n’kufotokoza mayankho a mafunso monga: Kodi ndani analenga dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zili padziko? Ndipo kodi munthu anakhalako motani? Nditangoyamba kuwerenga Malemba, ena anayamba kundiseka, n’kumanena kuti ndimakhulupirira malodza. Komabe, ndinapitiriza mpaka kumaliza nkhani yangayo. Pambuyo pake, ndinali ndi mwayi wolankhula ndi ena mwa anzanga a m’kalasiwo za ntchito yathu ndiponso zimene timakhulupirira. Tsopano, akandiona muutumiki, sandisekanso.”

Zhihao anapitiriza kuti: “Chifukwa chakuti makolo anga ndi Mboni, timakambirana lemba latsiku m’mawa uliwonse. Timaphunziranso Baibulo ndi kupezeka nthawi zonse pamisonkhano. N’chifukwa chake sindibwerera m’mbuyo munthu aliyense akamandinenabe pamene ndikuyesa kuuza ena choonadi chotsitsimula cha m’Baibulo.”

Tingmei akuphunzira pa sukulu ya atsikana okhaokha ya ntchito zamanja. Tsiku lina anaitanidwa kuti akayende limodzi ndi ena mwa anzake a m’kalasi ndiponso anyamata a pa sukulu ina ya anyamata okhaokha. Iye anaona kuti zimenezo zingathe kumulowetsa m’mavuto, ndipo anakana kupita nawo. Anzakewo anayesa kumuitana kambirimbiri, ngakhale kuti anali atalankhulapo nawo za mfundo zabwino za m’buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza. * Atsikanawo anamunyoza, n’kumanena kuti anali mtsikana wotsalira. Komabe, nzeru zake zotsatira malamulo a Baibulo zinaonekera pamene mmodzi wa atsikana aja anakhala ndi pakati kenako n’kuchotsa pakatipo. Tingmei anati: “Kuchita zinthu m’njira imene Yehova amafuna kwandithandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Chifukwa cha zimenezi, ndili ndi chimwemwe mumtima mwanga ndipo ndine wokhutira kwambiri.”

Kulimbana ndi Zolepheretsa Kupita Patsogolo

Ruiwen ndi mmodzi mwa anzake apamtima a Tingmei. Ali wamng’ono, Ruiwen ankaona kuti kupita ku misonkhano yachikristu ndiponso kulowa nawo muutumiki wa kumunda ndi chizolowezi chotopetsa. Koma ataona kusiyana pakati pa chikondi chenicheni cha anthu a mumpingo mwake ndi ubwenzi wachiphamaso chabe wa anzake a m’kalasi, anatsimikiza kuti akufunikira kusintha moyo wake. Ruiwen anayamba kulalikira kwa anzake akusukulu ndipo posapita nthawi anazindikira bwino chimene ankayenera kuchita. Anayamba upainiya wothandiza, n’kumathera maola oposa 50 pamwezi ali muutumiki. Kenako anakhala mpainiya wokhazikika, n’kumathera maola oposa 70 pamwezi ali muutumiki. Ruiwen anati: “Ndikum’thokoza kwambiri Yehova. Sanataye nane mtima ngakhale kuti ndinkachita zinthu zimene zinkamukhumudwitsa, iye ankandikondabe. Mayi anga ndiponso anthu ena mumpingo ankasonyeza mtima womwewo wachikondi. Popeza kuti tsopano ndikuchititsa maphunziro a Baibulo faifi, ndikudzimva kuti ndikuchita nawo ntchito yokhutiritsa kwambiri.”

Pasukulu ina yasekondale ya dera lakumidzi, ana awiri a Mboni anauzidwa kuti aimire sukuluyo pa mpikisano wa magule a makolo. Atadziwa mmene mpikisanowo udzakhalire, anyamatawo anaona kuti kuchita nawo mpikisanowo, kungawononge chikumbumtima chawo chachikristu. Atayesa kufotokoza mmene iwo ankaonera, ndi kupempha kuti asadzachite nawo mpikisanowo, anawakanira pempholo. M’malo mwake, aphunzitsi anawauza kuti chifukwa chakuti iwo anapatsidwa ntchito imeneyo, ndiye kuti ayenera kupita basi. Posafuna kugonja, achinyamata a Mboniwo anatsegula malo ena a pa Intaneti, amene amalembapo nkhani za dipatimenti ya zamaphunziro ya dzikolo, n’kutumiza kalata yofotokoza za vuto lawolo. Ngakhale kuti achinyamatawo sanayankhidwe mwachindunji, sukuluyo inalandira malangizo akuti isakakamize mwana aliyense kuchita nawo mpikisanowo. Achinyamata awiriwa anasangalala kwambiri kuona kuti kuphunzira Baibulo sikunangoumba chabe chikumbumtima chawo koma kunawapatsanso mphamvu yokhala anthu osasunthika pa zinthu zoona.

Ngakhale anthu olumala, amasangalala kuuza ena za chiyembekezo chawo cha m’Baibulo. Minyu anabadwa wolumala ndipo akafuna kupeza lemba lomwe akufuna kuwerenga, amatsegula Baibulo ndi lilime, chifukwa chakuti satha kugwiritsa ntchito manja ake. Akamakamba nkhani zake mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, pa Nyumba ya Ufumu, amagona pa sofa yaifupi kwambiri, ndipo mwininyumba wake amakhala pa mpando waufupi ndi kum’gwirira maikolofoni. N’zolimbikitsa kwambiri kuona khama limene Minyu amachita pokonzekera nkhani zimenezi.

Pamene Minyu ankafuna kukhala wofalitsa Ufumu, alongo ena a mumpingo anaphunzira kulalikira patelefoni kuti athe kum’thandiza. Amathabwanya mabatani a telefoni ndi lilime lake ndipo alongowo amalemba dzina ndi zilizonse zokhudza munthu amene akulankhula nayeyo. Amasangalala kwambiri ndi ntchito imeneyo moti tsopano ndi mpainiya wothandiza, ndipo amalankhula pafoni ndi anthu za Ufumu wa Mulungu, maola 50 mpaka 60 mwezi uliwonse. Anapeza anthu ena amene amawagawira mabuku ofotokoza za m’Baibulo ndipo amalola kuti azipitiriza kukambirana nawo. Tsopano akuchititsa maphunziro a Baibulo atatu ndi anthu amene anawapeza mwanjira imeneyi.

Inde, monga mame otsitsimula, achinyamata a m’mipingo 78 ya Mboni za Yehova ku Taiwan, akufotokozera anthu mamiliyoni ambiri a pachilumbachi mwa kufuna kwawo ndiponso mwakhama, uthenga wabwino wa Ufumu, womwe ndi wopatsa moyo. Imeneyi ndi mbali yaing’ono chabe ya kukwaniritsidwa kochitika padziko lonse kwa ulosi wa m’Baibulo wakuti: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M’moyera mokometsetsa, mobadwira matandakucha, muli nawo mame a ubwana wanu.” (Salmo 110:3) Achinyamata amenewa amalimbikitsa anthu achikulire, omwe ndi ena mwa anthu amene akugwira nawo limodzi ntchito imeneyi, ndipo koposa zonse, amakondweretsa Atate wawo wakumwamba, Yehova Mulungu.​—Miyambo 27:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 10]

PAKUFUNIKA NYUMBA ZA UFUMU ZINANSO

Kuwonjezeka kwa ofalitsa ku Taiwan, kwachititsa kuti pakhale vuto lalikulu losakhala ndi Nyumba za Ufumu zokwanira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kupatulapo m’madera ena akumidzi, malo oyenera kumangapo Nyumba za Ufumu amasowa kwambiri. Kuphatikiza apo, malo ndi okwera mtengo kwambiri ndiponso malamulo ogawira malowo ndi okhwima. M’matawuni akuluakulu ndiponso m’mizinda, njira yokhayo imene ilipo ndi yogula nyumba zimene anazimanga kuti zikhale maofesi, n’kuzisintha kukhala Nyumba za Ufumu. Ngakhale zili choncho, maofesi ambiri ali ndi siling’i zammunsi kwambiri, mitengo yake yokonzetsera ndi yokwera, kulowa m’nyumbazo n’kovuta, ndiponso pali zinthu zina zimene zimapangitsa kuti nyumba zotero zikhale zosayenera kukhala Nyumba za Ufumu.

Komabe, zaka zaposachedwapa, Mboni za Yehova ku Taiwan zapeza Nyumba za Ufumu zingapo zatsopano. Ntchito yofunafuna malo atsopano ikupitirirabe ndipo Mbonizi n’zokonzeka kupereka ndalama zogulira malowo ndiponso n’zofunitsitsa kukulitsa luso lawo pantchito ya zomangamanga.