Kupirira Kumabweretsa Chimwemwe
Mbiri ya Moyo Wanga
Kupirira Kumabweretsa Chimwemwe
YOSIMBIDWA NDI MÁRIO ROCHA DE SOUZA
“Sizikudziwika ngati a Rocha apulumuke pa opaleshoniyi.” Ngakhale kuti dokotala ankaganiza choncho, lero ndidakali ndi moyo ndipo ndine mlaliki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova, pambuyo pa zaka 20 chichitikireni zimenezi. Kodi n’chiyani chimene chandithandiza kupirira kwa zaka zonsezi?
NDINAKULIRA pa famu ina yomwe inali pafupi ndi Santo Estêvão, mudzi wina wa m’boma la Bahia, kumpoto chakum’mawa kwa Brazil. Ndinayamba kuthandiza bambo anga kugwira ntchito za pafamu, ndili ndi zaka seveni. Tsiku lililonse ndikaweruka kusukulu, ankandipatsa ntchito yoti ndigwire. Patapita nthawi, bambo amati akapita kulikulu la bomalo ku Salvador, kukachita zina, ankandisiya pa famupo kuti ndiziyang’anira.
Tinkakhala mosangalala ngakhale tinalibe magetsi, madzi a pampopi, kapena zinthu zapamwamba zimene zili zotchuka masiku ano. Ndinkaulutsa ndege za mapepala zotchedwa kaiti kapena kuseweretsa magalimoto a matabwa amene ine ndi anzanga tinkapanga. Ndinkaimbanso chitoliro kutchalitchi tikamaguba. Komanso ndinali mnyamata wa kwaya kutchalitchi chakwathu, ndipo kumeneko n’kumene ndinaona buku lina lotchedwa História Sagrada (Mbiri Yopatulika), limene linandipatsa chidwi cha Baibulo.
M’chaka cha 1932 ndili ndi zaka 20, kumpoto chakum’mawa kwa Brazil kunagwa chilala choopsa ndiponso cha nthawi yaitali. Ng’ombe zathu zinafa, ndiponso mbewu zinauma, choncho ndinasamukira ku Salvador, kumene ndinapeza ntchito yoyendetsa sitima yaing’ono yonyamula anthu mumzinda. Kenako, ndinapeza nyumba imene ndinachita lendi ndipo ndinasamutsa abale anga onse n’kuyamba kukhala nawo limodzi. Bambo anamwalira mu 1944, ndipo anandisiyira udindo wosamalira amayi ndi azilongo anga eyiti, ndiponso azing’ono anga atatu.
Kusiya Ntchito Yoyendetsa Sitima N’kukhala Mlaliki
Chimodzi mwa zinthu zoyambirira zomwe ndinachita nditafika ku Salvador chinali kugula Baibulo. Nditapita kutchalitchi cha Baptist kwa zaka zowerengeka, Durval amene ndinkagwira naye limodzi ntchito yoyendetsa sitima, anakhala mnzanga. Ine ndi Durval tinkakambirana kwa nthawi yaitali za Baibulo. Ndipo tsiku lina anandipatsa kabuku kakuti Where Are the Dead? * (Kodi Akufa Ali Kuti?) Ngakhale ndinkakhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu wosafa, ndinali ndi chidwi chotsimikizira malemba a m’Baibulo amene anawalemba m’kabukuko. Komabe ndinadabwa kuona kuti Baibulo linatsimikiza kuti mzimu wa munthu umafa.
Durval ataona chidwi chimene ndinali nacho, anafunsa Antônio Andrade, mtumiki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova, kuti andipeze kunyumba. Pambuyo pa ulendo wake wachitatu, Antônio anandiuza kuti ndipite naye limodzi kokauza ena za ziphunzitso za m’Baibulo. Atalankhula pa nyumba ziwiri zoyambirira anati, “Tsopano ndi nthawi yoti iwenso ulankhulepo.” Ndinachita mantha, koma ndinasangalala chifukwa banja lina linamvetsera mwachidwi ndipo linalandira mabuku awiri omwe ndinawapatsa. Mpakana lero, ndimasangalalabe ndikakumana ndi munthu wina amene akufuna kudziwa choonadi cha m’Baibulo.
Ndinabatizidwa mu nyanja ya mchere ya Atlantic pafupi ndi Salvador pa April 19, 1943, tsiku lokumbukira imfa ya Kristu chaka chimenecho. Chifukwa chosowa amuna achikristu odziwa bwino ntchito yawo, ndinasankhidwa kuti ndizithandiza gulu la Mboni limene linkakumana kunyumba kwa Mbale Andrade yomwe inali pa umodzi mwa misewu yaing’ono, imene inkalumikiza chigawo cha kumtunda ndi chakumunsi cha mzinda wa Salvador.
Kukumana ndi Chitsutso
Zochitika zathu za Chikristu zinali zachilendo m’kati mwa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse (1939-45). Choncho akuluakulu ena a boma ankatiganizira kuti ndife akazitape a United States chifukwa chakuti zofalitsa zathu zambiri zinkachokera komweko. Chifukwa cha zimenezi kumangidwa ndi kufunsidwa mafunso sikunali kwachilendo. Mboni ikapanda kubwerera kuchokera ku utumiki wa kumunda, timadziwa kuti yatsekeredwa, ndipo timapita kupolisi kukapempha kuti aitulutse.
Mu August 1943, Adolphe Messmer, Mboni yachijeremani, inafika ku Salvador kuti idzathandize kukonza msonkhano wathu woyamba. Akuluakulu a boma atapereka chilolezo choti tipange msonkhano, tinaitanira anthu ku nkhani ya onse ya mutu wakuti “Ufulu M’dziko Latsopano” mwa kulemba m’nyuzipepala, ndipo tinamata zikwangwani m’mawindo a masitolo ndiponso m’mbali mwa sitima zonyamula anthu. Koma pa tsiku lachiwiri la msonkhanowo, wapolisi anatiuza kuti aletsa kuti tichite msonkhano. Bishopu wamkulu ku Salvador anakakamiza mkulu wa polisi kuti aletse msonkhano wathu. Komabe, mu April chaka chotsatira, anatipatsa chilolezo choti nkhani ya onse yomwe tinali titaitanira kale anthu ikambidwe.
Zimene Ndinafuna Kuchita
Mu 1946, anandiitana kuti ndikakhale nawo pa msonkhano wakuti Mitundu Yosangalala ku São Paulo. Mkulu wa sitima ya panyanja yonyamula katundu ku Salvador anatilola kuti tikwere nawo sitimayi ngati tingalole kugona pa bwalo la sitimayo. Ngakhale kuti tinakumana ndi namondwe amene anatidwalitsa, tinafika bwinobwino pa doko la Rio de Janeiro, titayenda panyanja kwa masiku anayi. Mboni za ku Rio zinatilandira m’nyumba zawo kuti tipumule kwa masiku owerengeka tisanapitirize ulendo wathu pa sitima ya pamtunda. Kagulu ka anthu konyamula zikwangwani za nsalu zolembedwa kuti “Takulandirani Mboni za Yehova” kanatilonjera sitima yathu itafika ku São Paulo.
Nditabwerera ku Salvador, ndinalankhula ndi Harry Black, mmishonale wochokera ku United States, kuti ndikufuna kukhala mpainiya, dzina limene atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova amatchulidwira. Harry anandikumbutsa kuti ndili ndi achibale oti ndiwasamalire ndipo anandilangiza kuti ndifatse kaye. Kenako, mu June 1952, azing’ono anga ndi azilongo anga aja anayamba kudzithandiza okha, ndipo ndinatumizidwa kukachita upainiya mu mpingo waung’ono ku Ilhéus, womwe unali pamtunda wa makilomita 210 kum’mwera kwa Salvador.
Anandikomera Mtima
Chaka chotsatira, anandisamutsira ku Jequié, tawuni yaikulu imene inali pakatikati pa boma la Bahia komwe kunalibe Mboni. Munthu woyamba kufika pakhomo pake anali wansembe. Iye anati tawuni yonseyo inali m’manja mwake ndipo anati ndisalalikire m’tawuniyo. Anachenjeza anthu am’tchalitchi chake kuti kwabwera “mneneri wonyenga” ndipo anaika anthu ozonda m’tawuni yonse kuti aziona zomwe ndikuchita. Komabe, tsiku limenelo ndinagawira mabuku ofotokoza za m’Baibulo 90 ndipo ndinayambitsa maphunziro a Baibulo anayi. Patapita zaka ziwiri, tawuni ya Jequié inali ndi Nyumba ya Ufumu, ndi Mboni zokwanira 36. Lero m’tawuni ya Jequié muli mipingo eyiti ndiponso Mboni pafupifupi 700.
M’miyezi yoyambirira ku Jequié, ndinkachita lendi kachipinda kakang’ono kunja kwa tawuniyi. Kenaka ndinakumana ndi Miguel Vaz de Oliveira, mwini wake wa hotela ina yotchedwa Hotel Sudoeste (Southwest Hotel), imene inali imodzi mwa mahotela abwino kwambiri mu mzinda wa Jequié. Miguel anavomera kuti ndiziphunzira naye Baibulo ndipo anandikakamiza kuti ndisamukire m’chipinda cha m’hotela yakeyo. Kenako Miguel ndi mkazi wake anakhala Mboni.
Chinthu china chosaiwalika pa masiku anga amene ndinakhala ku Jequié chimakhudza Luiz Cotrim, mphunzitsi wina wa sukulu ya sekondale amene ndimaphunzira naye Baibulo. Luiz anadzipereka kuti andithandize kuphunzira Chipwitikizi ndi masamu. Chifukwa chakuti ndinangophunzira sukulu ya pulaimale basi, ndinavomera kuti ayambe kundiphunzitsa. Maphunziro amenewo amene amachitika ndikamaliza kuphunzira Baibulo ndi Luiz mlungu uliwonse, anandithandiza kuti ndikonzekere ntchito zowonjezereka zimene ndinalandira m’gulu la Yehova.
Kuchita Ntchito Yovuta
Mu 1956, ndinalandira kalata yondiitana kuti ndipite ku nthambi yathu, imene pa nthawiyi inali ku Rio de Janeiro, kuti ndikaphunzire kukhala woyang’anira dera, dzina la atumiki oyendayenda a Mboni za Yehova. Sukuluyi, imene anthu enanso eyiti ankaphunzira nawo inatenga masiku opitirira mwezi umodzi. Sukuluyi ikupita chakumapeto, anandiuza kuti ndikatumikira ku São Paulo, ndipo zimenezi zinandidetsa nkhawa. Ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi munthu wakuda ngati ine, ndikachita chiyani pakati pa Ataliyana amenewo? Kodi akandilandira?’ *
Pa mpingo woyamba umene ndinakachezera m’boma la Santo Amaro, ndinalimbikitsidwa kuona kuti Nyumba ya Ufumu inadzadza ndi Mboni zinzanga ndiponso anthu ena okondwerera. Chimene chinanditsimikizira kuti mantha anga anali opanda pake chinali chakuti anthu onse 97 a mumpingomo analowa nane m’munda Loweruka ndi Lamlungu. ‘Amenewa ndi abale angadi,’ ndinaganiza choncho. Chikondi cha abale ndi alongo anga okondedwa amenewo n’chimene chinandipatsa mphamvu zoti ndipirire mu utumiki wanga woyendayenda.
Abulu, Mahatchi, ndi Nyama Zodya Chiswe
Chimodzi mwa zinthu zothetsa nzeru zimene oyang’anira oyendayenda ankakumana nazo kalelo, zinali kutalika kwa maulendo oti akafike komwe kunali mipingo ndi magulu ang’onoang’ono a Mboni kumidzi. M’malo oterowo, mathiransipoti anali osadalirika, kapena samapezeka n’komwe, ndipo misewu yambiri inali yaing’onoing’ono ndiponso yafumbi.
Madera ena anathetsa vutoli pogula bulu kapena hatchi kuti woyang’anira dera azigwiritsa ntchito. Lolemba, ndimaika chokhalira chachikopa pa msana pa bulu kapena hatchi, kumanga katundu wanga, n’kukwera bulu kapena hatchiyo kwa maola 12 kupita ku mpingo wotsatira. Mu mzinda wa Santa Fé do Sul, Mboni zinagula bulu dzina lake Dourado (Goldie) amene ankadziwa njira yopita ku magulu a maphunziro a Baibulo amene anali kumidzi. Dourado amaima pa geti la mafamu n’kumadikirira mofatsa kuti ine nditsegule getilo. Tikatha kucheza, ine ndi Dourado timapitiriza ulendo wathu wopita ku gulu lotsatira.
Chinthu chinanso chimene chinkapangitsa kuti ntchito yoyang’anira dera ikhale yovuta, chinali kusowa kwa njira zodalirika zoperekera uthenga. Mwachitsanzo, kuti ndithe kuyendera gulu la Mboni zimene zimakumana pa famu ina m’boma la Mato Grosso, ndinkayenera kuwoloka mtsinje wa Araguaia pa bwato kenako n’kukwera bulu kwa mtunda wokwana makilomita 25 kudutsa m’nkhalango. Pa ulendo wina, ndinalemba kalata kudziwitsa gululi kuti ndikubwera, koma kalatayo mwachidziwikire sinafike, chifukwa nditawoloka mtsinjewo sindinapeze munthu aliyense amene ankandidikirira. Unali madzulo, choncho ndinafunsa mwini sitolo ina yaing’ono yomwe amagulitsiramo zakumwa kuti andisamalire katundu wanga ndipo ndinayamba kuyenda ndi chikwama chonyamulira mabuku basi.
Posapita nthawi kunada. Ndikuyenda movutikira mumdima, ndinamva kulira kwa nyama ina yake imene imadya chiswe. Ndinali nditamvapo kuti nyama imeneyi ikakwiya, ingaphe munthu ndi manja ake amphamvu. Choncho ndimati ndikamva phokoso la chinthu chilichonse m’tchire, mosamala ndimapita kutsogolo pang’onopang’ono nditaika chikwama cha mabuku patsogolo panga kuti chinditeteze. Nditayenda kwa maola ambiri, ndinafika pa mtsinje wina waung’ono. Mwatsoka, chifukwa cha mdima sindinaone kuti kutsidya kwa mtsinjewo kunali mpanda wa waya wamingaminga. Ndinadumpha mtsinjewo kamodzin’kamodzi, ndipo ndinagwera pa mpandawo, n’kudzicheka.
Pomaliza nditafika pa famuyo, agalu anayamba kuuwa. Anthu ankakonda kuba nkhosa usiku, choncho pamene chitseko chinatseguka, mofulumira ndinazidziwikitsa. Ndiyenera kuti ndinamvetsa chifundo chifukwa cha zovala zanga zong’ambika komanso za magazi, koma abale anali osangalala kundiona.
Mosasamala kanthu za zovuta, amenewo anali masiku osangalatsa. Ndinkasangalala kuyenda ulendo wautali pa hatchi ndiponso pansi. Nthawi zina ndimapuma pamthunzi pansi pa mtengo, kumvetsera kuimba kwa mbalame, ndiponso kuona nkhandwe zikudutsa m’misewu ya m’chipululu. Chinanso chimene chinali kundipatsa chimwemwe n’choti ndinkadziwa kuti maulendo anga amathandizadi anthu ambiri. Ambiri ankandilembera makalata ondiyamikira, ndipo ena amandithokoza ndikakumana nawo m’misonkhano. Ndinali wosangalala kuona anthu akupirira mavuto ndiponso kupita patsogolo mwauzimu.
Ndinapeza Wondithangatira
Kwa zaka zonsezo nthawi zambiri ndinkakhala ndekhandekha m’ntchito yoyendayenda ndipo ndinaphunzira kudalira Yehova monga “thanthwe langa, ndi linga langa.” (Salmo 18:2) Kuphatikiza apo, ndinazindikira kuti kukhala wosakwatira kunandithandiza kusamalira zinthu za Ufumu popanda chododometsa.
Komabe, mu 1978, ndinakumana ndi mlongo wina yemwe anali mpainiya dzina lake Júlia Takahashi. Mlongoyu anasiya ntchito yabwino ya unesi yomwe ankagwira ku chipatala china chachikulu cha ku São Paulo, kuti akatumikire kumalo kumene kunkafunika ofalitsa Ufumu. Akulu achikristu amene ankamudziwa mlongoyu ankamuyamikira chifukwa cha makhalidwe ake auzimu ndi luso lake monga mpainiya. Monga mmene mukudziwira, chosankha changa chokwatira pambuyo pa zaka zambiri chinadabwitsa anthu ena. Mnzanga wina wapamtima sanakhulupirire, ndipo anandilonjeza kuti ndikadzakwatira adzandipatsa ng’ombe yaimuna yolemera makilogalamu 270. Ng’ombeyo tinaiotcha pa phwando la ukwati wathu pa July 1, 1978.
Kupirira Matenda
Júlia anayamba kuyenda nane limodzi mu ntchito yanga yoyendayenda, ndipo kwa zaka eyiti tinayendera mipingo ya kum’mwera ndi ya kum’mwera cha kummawa kwa Brazil. Ndi nthawi imeneyi imene ndinayamba kudwala matenda a mtima. Ndinakomoka kawiri ndikulankhula ndi eni nyumba mu ntchito yolalikira. Poona za vuto langalo, tinavomera kukhala apainiya apadera mu mzinda wa Birigüi, m’boma la São Paulo.
Mboni za ku Birigüi zinadzipereka kunditenga pa galimoto kuti ndikaonane ndi dokotala ku Goiânia, mtunda wa makilomita 500. Nditapezako bwino, anandichita opaleshoni n’kundiika kachida kothandiza kuti mtima uzigwira ntchito. Zimenezo ndi zaka 20 zapitazo. Ngakhale kuti anandichitanso maopaleshoni a mtima ena awiri kuphatikiza pa yoyambayo, ndidakali wachangu muntchito yopanga ophunzira. Monga akazi ena ambiri achikristu ndiponso okhulupirika, Júlia nthawi zonse wakhala akundipatsa mphamvu ndi chilimbikitso.
Ngakhale kuti sinditha kuchita zambiri ndipo ndimakhumudwa nthawi zina chifukwa cha kudwala, ndimathabe kuchita upainiya. Ndimakumbukira kuti Yehova sanatilonjeze kuti moyo m’dziko lakaleli udzakhala wosavuta. Mtumwi Paulo ndi Akristu ena okhulupirika akale anayenera kupirira, ndiye zingatheke bwanji kuti zikhale zosiyana ndi ife?—Machitidwe 14:22.
Posachedwapa, ndinapeza Baibulo loyamba limene ndinagula m’ma 1930. M’kati mwa chikuto, ndinali nditalembamo 350, chiwerengerero cha anthu ofalitsa Ufumu ku Brazil panthawi imene ndinayamba kupita kumisonkhano yachikristu mu 1943. Zikuoneka ngati zovuta kukhulupirira chifukwa tsopano ku Brazil kuli Mboni zoposa 600,000. Ndili ndi mwayi kuti ndathandiza nawo pang’ono pa ntchito imeneyi! Yehova wandidalitsa kwambiri chifukwa cha kupirira. Monga wa masalmo, ndikuti: “Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.”—Salmo 126:3.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kusindikiza.
^ ndime 23 Ataliyana osamuka kwawo pafupifupi 1,000,000 anakhazikika ku São Paulo pakati pa 1870 ndi 1920.
[Chithunzi patsamba 9]
Mboni zikuitanira anthu ku nkhani ya onse pa msonkhano woyamba mu mzinda wa Salvaldor, mu 1943
[Chithunzi patsamba 10]
Mboni zikufika ku São Paulo ku msonkhano wa Mitundu Yosangalala, mu 1946
[Zithunzi pamasamba 10, 11]
Ndili mu ntchito yoyendayenda cha kumapeto kwa zaka za m’ma 1950
[Chithunzi patsamba 12]
Ndili ndi mkazi wanga, Júlia