Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndikudwala Koma Ndikutumikira Yehova Mwachimwemwe

Ndikudwala Koma Ndikutumikira Yehova Mwachimwemwe

Mbiri ya Moyo Wanga

Ndikudwala Koma Ndikutumikira Yehova Mwachimwemwe

YOSIMBIDWA NDI VARNAVAS SPETSIOTIS

Mu 1990, ndili ndi zaka 68, ndinaferatu ziwalo zonse. Koma tsopano patha zaka pafupifupi 15 ndikuchita utumiki wa nthawi zonse m’chilumba cha Cyprus. Kodi n’chiyani chandipatsa mphamvu kuti nditumikirebe Yehova ngakhale ndikudwala chonchi?

NDINABADWA pa October 11, 1922, m’banja la ana naini, anyamata anayi ndi atsikana asanu. Tinkakhala m’mudzi wotchedwa Xylophagou, ku Cyprus. Ngakhale kuti makolo anga anali olemera ndithu, anafunika kuchita khama kwambiri kumunda kuti asamalire banja lalikulu chonchi.

Bambo anga dzina lawo anali Antonis, ndipo mwachibadwa anali munthu wokonda kuwerenga ndi kufuna kudziwa zinthu. Tsiku lina ine ndidakali kakhanda, bambo anaona kapepala kotchedwa kuti Peoples Pulpit, atapita kwa mphunzitsi wa m’mudzi mwathu. Kapepalako kanali kofalitsidwa ndi Ophunzira Baibulo (dzina la Mboni za Yehova panthawiyo). Anayamba kukawerenga, ndipo posakhalitsa mfundo zake zinawachititsa chidwi kwambiri. Motero, bambo ndi mnzawo wina dzina lake Andreas Christou, anali m’gulu la anthu oyamba kukhala a Mboni za Yehova pa chilumbachi.

Tinawonjezeka Ngakhale Tinali Kutsutsidwa

Patsogolo pake, bambo ndi mnzawoyo anapeza mabuku ofotokoza Baibulo kwa Mboni za Yehova. Posakhalitsa, bambo ndi Andreas anakhudzidwa mtima n’kuyamba kuuzako anzawo m’tauniyo zimene anali kuphunzirazo. Ntchito yolalikirayi inachititsa kuti abusa a chipembedzo cha Greek Orthodox komanso anthu ena alimbane kwambiri ndi bambo ndiponso mnzawo uja chifukwa ankaona kuti Mboni za Yehova zimasokoneza anthu.

Komabe anthu ambiri a m’derali ankawapatsa ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa anthu Baibulo. Bambo anali munthu wodziwika chifukwa cha kukoma mtima ndi kuwolowa manja. Nthawi zambiri ankathandiza mabanja osauka. Nthawi zina ankatuluka m’nyumba usiku mwakachetechete n’kukayika tirigu kapena buledi pakhomo pa mabanja osauka. Mtima wachikristu woganizira enawu unakometseranso kwambiri uthenga umene atumiki awiriwa anali kulalikira.​—Mateyu 5:16.

Zonsezi zinachititsa kuti anthu pafupifupi 12 ayambe kuchita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo. Anthuwa atayamba kukonda kwambiri choonadi, anaona kuti m’pofunika kumakumana m’nyumba zosiyanasiyana kuti aziphunzira Baibulo pagulu. Cha m’ma 1934, Nikos Matheakis, mtumiki wanthawi zonse wa ku Greece, anafika ku Cyprus n’kukumana ndi gulu la ku Xylophagou. Moleza mtima ndiponso mwakhama, Mbale Matheakis anathandiza kulinganiza gululo n’kulithandizanso kumvetsetsa Malemba. Gulu limeneli ndi limene linadzakhala mpingo woyamba wa Mboni za Yehova ku Cyprus.

Ntchito yachikristu itayamba kupita patsogolo anthu ambiri n’kuyamba kuvomereza choonadi cha m’Baibulo, abale anaona kuti m’pofunika kukhala ndi malo okhazikika ochitira misonkhano yawo. Mkulu wanga wamkulu kwambiri pa tonse, dzina lake George, pamodzi ndi mkazi wake Eleni, anapatsa abale nyumba imene ankasungiramo katundu wa kumunda. Nyumbayi inali moyandikana ndi nyumba yawo ndipo anaikonza bwinobwino n’kukhala malo oyenerera kuchitiramo misonkhano. Motero abalewo tsopano anali ndi Nyumba ya Ufumu yawoyawo yoyamba pachilumbacho. Anayamikira kwambiri. Ndipotu zimenezi zinathandiza kwambiri kuti Mboni ziwonjezeke pa chilumbacho.

Kutenga Choonadi Ngati Changachanga

Mu 1938, ndili ndi zaka 16, ndinaganiza zokhala kalipentala. Motero, bambo ananditumiza ku Nicosia, mzinda womwe uli likulu la Cyprus. Mwanzeru, iwo anakonza zoti ndikakhale ndi Nikos Matheakis. Ambiri pa chilumbachi amakumbukirabe mbale wokhulupirikayu chifukwa cha khama lake ndiponso mtima wake wochereza alendo. Anali munthu wochita zinthu motsimikiza ndiponso mosaopa ndipotu makhalidwe amenewa anali ofunika kwa Mkristu aliyense ku Cyprus m’masiku amenewo.

Mbale Matheakis anandithandiza kwambiri kuti ndilidziwe bwino Baibulo ndi kupita patsogolo mwauzimu. Ndikukhala panyumba pawo, ndinkapezeka pa misonkhano yonse yochitikira panyumbapo. Apa m’pamene ndinayamba kuona kuti ndayamba kum’konda kwambiri Yehova. Ndinayamba kufunitsitsa kukhala ndi ubwenzi weniweni ndi Mulungu. Patatha miyezi yochepa chabe, ndinapempha Mbale Matheakis kuti ndipita naye ku utumiki wa kumunda. Umu munali mu 1939.

Patapita kanthawi pang’ono ndinabwerera kwathu kukaona anthu. Kumeneko ndinakakhala ndi bambo anga kwa kanthawi ndipo izi zinandithandiza kutsimikiza mtima kwambiri kuti ndapezadi choonadi ndiponso ndadziwadi cholinga cha moyo. Mu September 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba. Achinyamata ambiri a msinkhu wanga anadzipereka kukamenya nkhondo, koma potsatira malangizo a m’Baibulo, ine ndinaganiza zosalowererapo pa nkhondoyi. (Yesaya 2:4; Yohane 15:19) Chaka chomwecho, ndinapereka moyo wanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa mu 1940. Kwa nthawi yoyamba ndinaona kuti ndilibe mantha alionse oopa munthu.

Mu 1948, ndinakwatira Efprepia. Tinadalitsidwa ndi ana anayi. Posakhalitsa tinazindikira kuti tinayenera kuchita khama kwambiri kuti anawo tiwalere “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Tinkapemphera ndiponso kuyesetsa kuphunzitsa ana athu kukonda kwambiri Yehova ndi kulemekeza malamulo ndiponso mfundo zake za makhalidwe abwino.

Kuvutika ndi Matenda

Mu 1964, ndili ndi zaka 42, ndinayamba kumva kuti mwendo wanga wa kumanja wachita ngati dzanzi. Zimenezi zinapitirira mpaka kumwendo wanga wa kumanzere. Nditapita kuchipatala anandipeza ndi matenda enaake osachiritsika ofooketsa minofu pang’onopang’ono mpaka kupheratu ziwalo zonse. Nditamva nkhaniyi, maganizo anangoti balala m’mutumu. Sindinayembekezere kuti zinthu zingasinthe chonchi ayi. Ndinakwiya komanso kukhumudwa kwambiri ndipo ndinadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani matendawa akugwira ineyo? Ndalakwa chiyani ine?’ Koma patapita nthawi, ndinakhazikika maganizo pang’ono. Komano ndinali ndi nkhawa kwambiri posadziwa kuti moyo wanga ukhala wotani. Ndinkadzifunsa mafunso ambiri. Kodi ziwalo zanga zonse zifa moti ndizingodalira ena? Kodi ndipirira bwanji matendawa? Kodi ndikwanitsa kusamalira banja langa, lokhala ndi mkazi komanso ana anga anayi? Mtima unandipweteka kwambiri poganizira zimenezi.

Panthawi imeneyi, kuposa kale lonse, m’pamene ndinaona kuti m’pofunika kupemphera kwa Yehova n’kumuuza nkhawa zanga zonse moonadi mtima. Ndinkapemphera usana ndi usiku womwe, misozi ili chuchuchu. Posakhalitsa mtima unakhala m’malo. Mawu olimbikitsa a pa Afilipi 4:6, 7 anandithandiza kwambiri. Mawu ake ndi akuti: “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”

Kulimbana ndi Matenda Ofa Ziwalo

Matenda angawo anapitirira. Ndinazindikira kuti ndiyenera kuyesetsa kuzolowera msanga vuto langali. Popeza sindikanathanso kuchita ntchito ya ukalipentala, ndinaganiza zopeza ntchito yofewerapo, yogwirizana ndi thanzi langa, komanso yoti indithandize kupeza ndalama zokwanira kusamalira banja langa. Poyamba ndinkagulitsa zakudya zozizira zotchedwa ayisikilimu pa galimoto yaing’ono. Ndinachita zimenezi kwa zaka sikisi mpaka pamene matendawa anandifikitsa pomayendera njinga ya opuwala. Kenaka ndinayamba kuchita ntchito zina zing’onozing’ono zimene ndikanatha kukwanitsa.

Kuyambira mu 1990 matendawa andifoola kwambiri moti sindithanso kugwira ntchito ina iliyonse. Tsopano ndimangodalira anthu ena basi, ngakhale pochita zinthu zimene munthu wabwinobwino amachita mosavutikira n’komwe. Ndimachita kugonekedwa, kusambitsidwa, ndi kuvekedwa. Popita ku misonkhano yachikristu, amandiyendetsa pa njinga ya opuwala kuti ndikakwere galimoto ndipo amachita kundinyamula kuti ndilowe m’galimotomo. Ku Nyumba ya Ufumuyo, amandinyamula pondichotsa m’galimotomo n’kundikhazika pa njinga ya opuwala ija kenaka n’kundiyendetsa kulowa m’Nyumba ya Ufumuyo. Kenaka amandiikira mbaula ya magetsi pafupi kuti ndisazizidwe miyendo misonkhano ikamachitika.

Koma ngakhale ndili ndi matenda opha ziwalo, ndimapezeka ku misonkhano yonse mokhazikika. Ndimadziwa kuti uku n’kumene Yehova amatiphunzitsira, ndiponso kuti kukhala ndi abale ndi alongo anga auzimu kumanditeteza ndiponso kundilimbikitsa. (Ahebri 10:24, 25) Abale ndi alongo okhwima mwauzimu amandiyendera kawirikawiri ndipo zimenezi zakhala zikundilimbikitsa kwabasi. Mumtima mwanga ndimamva mmene Davide anamvera ponena kuti: “Chikho changa chisefuka.”​—Salmo 23:5.

Mkazi wanga wakhala akundithandiza kwambiri zaka zonsezi. Ana anganso akhala akundithandiza kwambiri. Patha zaka zambiri ndithu akundithandiza pa moyo wanga wa tsiku ndi tsiku. Ntchito akuchitayi si yophweka ayi, ndipo ikuvutiravutira poti matenda angawa akuipiraipira. Iwo ndi chitsanzo chabwino zedi cha kudzipereka ndiponso kuleza mtima, ndipo ndimapemphera kuti Yehova apitirize kuwadalitsa.

Mphatso ina yabwino kwambiri imene Yehova wapereka kwa atumiki ake pofuna kuwalimbikitsa ndiyo mwayi wopemphera. (Salmo 65:2) Poyankha mapemphero anga ochoka pansi pa mtima, Yehova wandipatsa mphamvu zoti ndikhalebe wokhulupirika zaka zonsezi. Kupemphera kumandithandiza makamaka ndikayamba kutaya mtima ndipo kumandithandiza kukhalabe wachimwemwe. Kulankhula ndi Yehova nthawi zonse kumanditsitsimula ndi kundipatsa mphamvu zina zoti ndisabwerere m’mbuyo. Sindikayika m’pang’ono pomwe kuti Yehova amamva mapemphero a atumiki ake ndi kuti amawapatsa mtendere wa m’maganizo umene iwo amafunikira.​—Salmo 51:17; 1 Petro 5:7.

Koposa zonse, ndimalimbikitsidwa nthawi iliyonse ndikakumbukira kuti m’tsogolo muno Mulungu adzachiritsa anthu onse amene adzawapatse moyo m’paradaiso, mu ulamuliro wa Ufumu wa Mwana wake, Yesu Kristu. Nthawi zingapo ndithu ndakhala ndikukhetsa misozi poganizira chiyembekezo chosangalatsa chimenechi.​—Salmo 37:11, 29; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4.

Kuchita Utumiki wa Nthawi Zonse

Cha m’ma 1991, ndinaganizira bwinobwino za moyo wanga ndipo ndinaona kuti njira yabwino kwambiri yopewera mzimu wodzimvera chisoni ndiyo kukhala wotanganidwa nthawi zonse pouza ena uthenga wabwino wa Ufumu, womwe ndi uthenga wamtengo wapatali kwambiri. M’chaka chimenecho, ndiyamba kuchita utumiki wa nthawi zonse.

Chifukwa cholemala, nthawi zambiri ndimalalikira polemba makalata. Komano, kwa ineyo kulemba n’chintchito chachikulu kwambiri; moti ndimafunika kuchita khama kwambiri. Ndimavutika kugwira bwinobwino bopeni ndi dzanja langa, chifukwa choti matendawa anafooketsa minofu ya manja. Komabe chifukwa chopirira ndiponso pemphero, tsopano ndatha zaka 15 ndikulalikira polemba makalata. Ndimalalikiranso anthu powaimbira telefoni. Abale anga, anzanga, ndi anansi ena amene amadzandizonda kunyumba kwanga, sindilephera kuwauza za dziko latsopano ndi paradaiso wa padziko lapansi.

Motero, pali nkhani zambiri zolimbikitsa zokhudza anthu amene ndacheza nawo m’njira imeneyi. Mwachitsanzo, ndinasangalala kwambiri kuona mdzukulu wanga, amene ndinaphunzira naye Baibulo zaka 12 zapitazo, akupita patsogolo mwauzimu n’kuyamba kuyamikira choonadi cha m’Baibulo. Chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo, wakhala wokhulupirika ndiponso wosasunthika pa mfundo yachikristu yosalowerera m’ndale.

Anthu amene ndawalembera kalata akandiyankha pofuna kudziwa zambiri zokhudza Baibulo, ndimasangalala kwambiri. Nthawi zina anthu ena amafuna kuti ndiwapatse mabuku ena ofokotoza Baibulo. Mwachitsanzo, mayi wina anandiimbira foni n’kundithokoza chifukwa cholemba kalata yolimbikitsa yopita kwa mwamuna wake. Mayiyo anati mfundo za m’kalatayo zinam’chititsa chidwi kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti iyeyo ndi mwamuna wake abwere kunyumba kwathu n’kukambirana nane nkhani zambirimbiri zokhudza Baibulo.

Ndili ndi Chiyembekezo

Pa zaka zonsezi, ndaona chiwerengero cha olengeza Ufumu chikukwera m’dziko lino. Nyumba ya Ufumu yaing’ono yoyandikana ndi nyumba ya mchimwene wanga George tsopano anaikulitsa ndipo akhala akuikonzanso kwa nthawi zingapo. Tsopano ndi malo okongola kwambiri olambirirapo ndipo mumasonkhana mipingo iwiri ya Mboni za Yehova.

Bambo anamwalira m 1943, ali ndi zaka 52. Komatu anatisiyira cholowa chauzimu chamtengo wapatali zedi. Ana awo eyiti anaphunzira choonadi ndipo akutumikirabe Yehova. M’tauni ya Xylophagou, kumene bambo anabadwira, komanso m’matauni ena apafupi, tsopano muli mipingo itatu, ndipo tikaphatikiza ofalitsa a Ufumu onse m’mipingoyi alipo 230.

Ndimasangalala kwambiri kuona zolimbikitsa ngati zimenezi. Tsopano ndili ndi zaka 83, ndipo ndimamva mmene ananenera wamasalmo kuti: “Misona ya mkango isowa nimva njala: koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.” (Salmo 34:10) Ndikudikirira mwachidwi nthawi imene ulosi wa pa Yesaya 35:6 udzakwaniritsidwe. Ulosiwo umati: “Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala.” Podikirira nthawi imeneyi, ndikufuna kuti ndipitirizebe kutumikira Yehova mosangalala ngakhale ndikudwala.

[Mapu patsamba 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

TURKEY

CYPRUS

SYRIA

LEBANON

Nicosia

Xylophagou

Nyanja ya Mediterranean

[Chithunzi patsamba 17]

Nyumba ya Ufumu yoyamba ku Xylophagou, imene akuigwiritsabe ntchito panopo

[Zithunzi patsamba 18]

Ndili ndi Efprepia mu 1946 ndiponso panopa

[Chithunzi patsamba 20]

Ndimasangalala chifukwa cholalikira pa telefoni ndi kulembera anthu makalata