Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti akazi akhale “chete m’Mipingo”?
Paulo anauza mpingo wachikristu wa ku Korinto kuti: ‘Monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima, akazi akhale chete m’Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula.’ (1 Akorinto 14:33, 34) Kuti timvetse bwino zimenezi, ndi bwino kuganizira nkhani yomwe inachititsa Paulo kupereka malangizo amenewa.
M’chaputala 14 cha buku la Akorinto Woyamba, Paulo anafotokoza za misonkhano ya mpingo wachikristu. Iye anafotokoza zoyenera kukamba pamisonkhano imeneyi ndiponso anasonyeza mmene iyenera kuchitikira. (1 Akorinto 14:1-6, 26-34) Komanso anatsindika cholinga cha misonkhano yachikristu, chomwe ndi ‘kuti Mpingo ulandire chomangirira,’ kapena kuti ulimbikitsidwe.—1 Akorinto 14:4, 5, 12, 26.
Mawu a Paulo olangiza anthu ‘kukhala chete’ akupezeka maulendo atatu m’chaputala 14 cha buku la Akorinto Woyamba. Paulendo uliwonse, malangizowa akupita kwa magulu osiyanasiyana mu mpingo, koma m’maulendo onsewo, cholinga chake n’chimodzimodzi, chakuti “zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.”—1 Akorinto 14:40.
Pamalo omwe malangizowa akupezeka koyamba, Paulo anati: ‘Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iyayi, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.’ (1 Akorinto 14:27, 28) Izi sizinatanthauze kuti munthu wotero sankayenera kulankhula m’pang’ono pomwe pamisonkhano, koma zinatanthauza kuti nthawi zina munthuyo ankafunika kukhala chete. M’pake kutero, chifukwa sizikanatheka kukwaniritsa cholinga cha misonkhanoyo, chomwe chinali kulimbikitsana, ngati munthu atalankhula chinenero chomwe palibe ndi mmodzi yemwe wochidziwa.
Kachiwiri, Paulo anati: ‘Aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. Koma ngati kanthu kavumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo.’ Izi sizinatanthauze kuti mneneri woyambayo ankafunika kusiyiratu kulankhula pamisonkhano, koma kuti 1 Akorinto 14:26, 29-31.
ankafunika kukhala chete nthawi zina. Zikatero, mneneri amene walandira vumbulutso mwa chozizwitsayo ankatha kulankhula kwa mpingo, ndipo cholinga cha msonkhanowo, choti “onse afulumidwe,” kapena kuti alimbikitsidwe, chinkatha kukwaniritsidwa.—Kachitatu, Paulo analankhula kwa akazi achikristu okha, kuti: ‘Akazi akhale chete m’Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula, koma akhale omvera.’ (1 Akorinto 14:34) N’chifukwa chiyani Paulo anawalamula zimenezi alongo? Anatero n’cholinga choti zinthu zizichitika mwadongosolo mu mpingo. Iye anati: “Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna awo a iwo okha kwawo; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.”—1 Akorinto 14:35.
N’kutheka kuti alongo ena ankatsutsa zimene zanenedwa mu mpingo. Malangizo a Paulowa anathandiza alongo kusakhala ndi mtima wachisokonezo ndiponso kuti adzichepetse ndi kuvomera udindo womwe anapatsidwa m’makonzedwe a Yehova a umutu, makamaka wokhudza amuna awo. (1 Akorinto 11:3) Komanso, mwa kukhala chete, alongo akanasonyeza kuti alibe mtima wofuna kukhala aphunzitsi mu mpingo. M’kalata yomwe Paulo analembera Timoteo, iye anasonyeza kuti sizingakhale bwino kuti akazi akhale aphunzitsi mu mpingo. Anati: “Sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.”—1 Timoteo 2:12.
Kodi izi zikutanthauza kuti mkazi wachikristu sayenera kulankhula m’pang’ono pomwe pamsonkhano wa mpingo? Ayi, si choncho. M’masiku a Paulo, pankakhala nthawi yomwe akazi achikristu, mwina mwa mzimu woyera, ankapemphera kapena kulosera mu mpingo. Nthawi yoteroyo, iwo ankasonyeza kuzindikira udindo wawo mwa kuvala cha kumutu. * (1 Akorinto 11:5) Komanso, m’masiku a Paulo, alongo ndi abale ankalimbikitsidwa kulengeza chiyembekezo chawo, ndipo ndi mmenenso zilili masiku ano. (Ahebri 10:23-25) Kuwonjezera pa kuchita zimenezi mu utumiki wa kumunda, alongo amalengeza za chiyembekezo chawo ndi kulimbikitsa ena pamisonkhano ya mpingo mwa kupereka ndemanga zokonzekeredwa bwino akapemphedwa kutero ndiponso mwa kuvomera kuchita nawo zitsanzo komanso kukamba nkhani za ophunzira.
Motero, akazi achikristu ‘amakhala chete’ mwa kusayesa kulanda maudindo a amuna ndi kumaphunzitsa mpingo. Safunsa mafunso ofuna kuyambitsa mikangano omwe angasonyeze kuderera mphamvu za anthu amene amaphunzitsa mu mpingo. Alongo achikristu akamakwaniritsa udindo wawo mu mpingo, iwo amalimbikitsa kwambiri mtendere ndipo chifukwa cha mtendere umenewu pamisonkhano ya mpingo ‘pamachitika zonse kukumangirira.’—1 Akorinto 14:26, 33.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Masiku ano, alongo okhwima maganizo amatsatira chitsanzo chimenechi akafunika kuchita zinthu zina mu mpingo m’malo mwa mwamuna wobatizidwa.—Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, tsamba 26.