Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anandithandiza Kum’peza

Yehova Anandithandiza Kum’peza

Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Anandithandiza Kum’peza

YOSIMBIDWA NDI FLORENCE CLARK

Ndinagwira dzanja la mwamuna wanga amene anali wodwala kwambiri. Poti ndinali wa chipembedzo cha Angilikani, ndinapemphera kwa Mulungu kuti mwamuna wanga achire, ndipo ndinalonjeza kuti ngati samwalira, ndidzafunafuna Mulungu mpaka ndidzam’peze. Ndipo ndidzakhala wake.

NDISANAKWATIWE dzina langa linali Florence Chulung ndipo ndinabadwa pa September 18, 1937, m’mudzi wa Oombulgurri wa anthu amtundu wa Aaborijini m’dera la Kimberley Plateau m’chigawo chakumadzulo kwa Australia.

Ndimakumbukira nthawi imene ndinali mwana m’masiku amenewo opanda mavuto ndi osangalatsa. Kutchalitchi cha mishoni, ndinaphunzira zinthu zofunika zochepa ponena za Mulungu ndi Baibulo, koma amayi anga ndi amene anandiphunzitsa khalidwe lachikristu. Ankandiwerengera Baibulo nthawi zonse, ndipo ndinayamba kukonda zinthu zauzimu kuyambira ndili wamng’ono. Ndinkasiriranso mmodzi wa azing’ono awo a mayi anga, amene anali mmishonale kutchalitchi kwawo. Ndinkalakalaka kuti ndidzakhale ngati iyeyo.

Dera lathu, limene kale linkatchedwa Forrest River Mission, kunali sukulu yoyambira giredi wani mpaka giredi faifi. Ndipo ndinkapita kusukulu maola awiri okha m’mawa uliwonse, kutanthauza kuti maphunziro anga anali osakwanira. Nkhani imeneyi inadetsa nkhawa abambo anga. Iwo ankafuna kuti ana awo akhale ophunzira bwino, choncho anaganiza zochoka ku Oombulgurri n’kusamutsira banja lawo ku tawuni ya Wyndham. Ndinali wokhumudwa pa tsiku lomwe tinasamuka, koma ku Wyndham, ndinkakwanitsa kupita kusukulu mokwanira kwa zaka folo zotsatira, kuyambira 1949 mpaka 1952. Ndimayamikira kwambiri abambo anga pondithandiza kuti ndiphunzire.

Amayi anga ankagwira ntchito kwa dokotala, ndipo pamene ndinamaliza sukulu ndili ndi zaka 15, dokotalayu anati andilembe ntchito yaunesi pa chipatala cha Wyndham. Ndinavomera mosangalala, chifukwa nthawi imeneyo kupeza ntchito kunali kovuta.

Patapita zaka zingapo ndinakumana ndi Alec, mzungu amene ankaweta ng’ombe pa famu. Tinakwatirana mu 1964 m’tawuni ya Derby. Kutawuni imeneyi n’kumene nthawi zonse ndinkapita ku Tchalitchi cha Angilikani. Tsiku lina a Mboni za Yehova anafika pakhomo panga ndipo ndinawauza kuti sindikufuna ndiponso kuti asadzabwerenso. Komabe, ndinachita chidwi ndi zomwe anandiuza zoti Mulungu ali ndi dzina, ndipo dzina lake ndi Yehova.

“Sungapemphere Wekha?”

M’chaka cha 1965 moyo unayamba kuvuta kwambiri. Mwamuna wanga anachita ngozi zitatu zoopsa ndithu, ziwiri ndi kavalo wake ndipo imodzi ndi galimoto. Mwamwayi, anachira ndipo anayambiranso kugwira ntchito. Patapita nthawi pang’ono, anachitanso ngozi ina ndi kavalo. Pangozi imeneyi anavulala kwambiri m’mutu. Nditafika kuchipatala, adokotala anandiuza kuti mwamuna wanga amwalira. Ndinali ndi chisoni chachikulu. Ndipo nesi anafunsa wansembe wakumeneko kuti ndionane naye, koma wansembeyo anati: “Lero sindibwera. Ndidzabwera mawa.”

Ndinkafuna kuti wansembe akhale pafupi nane kuti tipemphere limodzi, ndipo ndinamuuza sisitere. Sisitereyo anayankha kuti: “Kodi vuto lako n’chiyani? Sungapemphere wekha?” Choncho ndinayamba kupemphera kwa ziboliboli zimene zinali m’tchalitchimo kuti zindithandize, koma palibe chimene chinachitika. Mwamuna wangayo ankaoneka kuti amwalira. Ndinaganiza kuti, ‘Kodi ndidzatani mwamuna wanga akamwalira?’ Ndinkadanso nkhawa za ana anga atatu, Christine, Nanette, ndi Geoffrey, kuti kodi adzakhala ndi moyo wotani popanda bambo wawo? N’zosangalatsa kuti patapita masiku atatu mwamuna wanga anatsitsimuka, ndipo anamutulutsa m’chipatala pa December 6, 1966.

Ngakhale anali kuoneka kuti akuchira bwino, ubongo wa mwamuna wangayu unali utavulala. Anayamba kuiwalaiwala ndi kuchita chiwawa ndipo amati lero wadzuka wokwiya, mawa wosangalala, choncho. Zinkamuvuta kuti akhale bwino ndi ana ndipo ankakwiya ngati anawo sanachite zinthu ngati mmene wamkulu angachitire. Ndinkavutika kumusamalira. Ndinam’chitira pafupifupi chilichonse. Mpaka ndinamuphunzitsa kuti ayambirenso kuwerenga ndi kulemba. Ntchito yomusamalira ndi kusamaliranso ntchito zina za pakhomo inandikulira kwambiri moti ndinadwala matenda ovutika maganizo. Zaka seveni zitapita chichitikire ngozi ya mwamuna wanga, tinagwirizana zopatukana kwakanthawi kuti thanzi langa libwerere.

Ndinatenga ana anga n’kusamukira kum’mwera kwa mzinda wa Perth. Tisanasamuke, mng’ono wanga anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ku Kununurra, yomwe ndi tawuni yaing’ono m’chigawo chakumadzulo kwa Australia. Anandionetsa chithunzi m’buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, * cha dziko lapansi la paradaiso limene Baibulo limalonjeza. Anandionetsanso m’buku lomweli kuti Mulungu ali ndi dzina, lakuti Yehova, ndipo zimenezi zinandisangalatsa. Popeza kuti kutchalitchi kwanga sankatiuza zinthu zimenezi, ndinaganiza zokaimbira foni Mboni za Yehova ndikakakhazikika ku Perth.

Komabe, ndinali ndisanatsimikize zowaimbira foni. Ndiye tsiku lina madzulo, ndinamva kulira kwa belu la pakhomo. Mwana wanga wamwamuna anapita pakhomopo kenaka n’kubwera kwa ine akuthamanga, ndipo anati, “Amayi, anthu aja mumanena kuti mudzawaimbira foni aja abwera.” Ndinadabwa kenaka ndinati, “Auze kuti ine kulibe.” Koma mwanayo anayankha kuti, “Amayi, mukudziwa kuti sindiyenera kunena bodza.” Ndinamvera n’kutuluka. Mmene ndimapereka moni kwa anthuwo, ndinaona kuti ankaoneka odabwa. Anabwera kudzaona munthu wina amene ankakhala m’nyumba imene ndinkakhalayo, koma anasamuka. Ndinawauza kuti alowe m’nyumba ndipo ndinawafunsa mafunso. Anandiyankha mokhutiritsa kuchokera m’Baibulo.

Sabata yotsatira, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni mokhazikika, pogwiritsa ntchito buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Phunzirolo linandithandiza kuyambiranso kukonda zinthu zauzimu. Patapita milungu iwiri ndinakakhala nawo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu Yesu. Kenaka ndinayamba kusonkhana nawo Lamlungu lililonse, ndipo pasanapite nthawi yaitali ndinayamba kusonkhana nawonso m’misonkhano ya pakati pa mlungu. Ndinayambanso kuuza ena zimene ndinkaphunzira. Ndinaona kuti kuthandiza ena kuphunzira choonadi cha m’Baibulo kunandithandiza kuti ndiyambenso kupeza bwino. Patapita miyezi sikisi ndinabatizidwa pa msonkhano wachigawo ku Perth.

Nditapita patsogolo mwauzimu, ndinazindikira za mmene Yehova amaonera kupatulika kwa ukwati, kuphatikizapo mfundo ya m’Baibulo yopezeka pa 1 Akorinto 7:13, yomwe imati: “Mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.” Lemba limeneli linandithandiza kubwererana ndi Alec.

Kubwerera ku Derby

Ndinabwerera ku Derby pa June 21, 1979, pambuyo popatukana ndi mwamuna wanga kwa zaka zoposa faifi, ndipo sindinkadziwa kuti mwamuna wanga akachita chiyani ndikakafika. Koma ndinadabwa kuona kuti anasangalala nditabwerera, ngakhale kuti anakhumudwa atamva zoti ndine wa Mboni za Yehova. Nthawi yomweyo ananena kuti ndizipita kutchalitchi kwake, kumene ndinkapita ndisanapite ku Perth. Ndinalongosola kuti sindingachite zimenezo. Ndinayesetsa kwambiri kulemekeza umutu wake ndipo ngati mkazi wachikristu ndinachita zomwe ndingathe. Ndinayesa kulankhula naye za Yehova ndi malonjezo Ake odabwitsa onena za m’tsogolo, koma sanalabadire.

Patapita nthawi, Alec anavomereza kusintha kwa zinthuku, ndipo mpaka anayamba kundipatsa ndalama kuti ndizikapezeka pa misonkhano yachigawo ndi misonkhano ina, ngakhalenso misonkhano ya mlungu ndi mlungu. Ndinayamikira kwambiri pamene anagula galimoto, yomwe inali chinthu chamtengo wapatali kumudzi ngati kumeneku, kuti ndizigwiritsa ntchito muutumiki wachikristu. Abale ndi alongo, kuphatikizapo woyang’anira dera, kawirikawiri ankakhala kunyumba kwathu masiku angapo. Zimenezi zinathandiza Alec kudziwa Mboni zosiyanasiyana, ndipo zikuoneka kuti zimenezo zinam’sangalatsa.

Ndinakhala Ngati Ezekieli

Ndinasangalala pamene abale ndi alongo ankandichezera, koma ndinkakumana ndi mavuto. M’tawuni ya Derby ndinali ndekha wa Mboni. Ndipo mpingo umene unali pafupi unali ku Broome, pa mtunda wa makilomita 220. Choncho ndinaganiza kuchita zotheka kuti ndilengeze uthenga wabwino. Ndi thandizo la Yehova, ndinakonzekera n’kuyamba kulalikira khomo ndi khomo. Ntchitoyi inkandivuta, koma ndinakumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.

Atsogoleri achipembedzo sanasangalale ndi ntchito yanga, makamaka kulalikira Aaborijini anzanga. Anayesa kundiopseza ndi kundiletsa kulalikira. Koma kutsutsa kwawoko kunandithandiza kulimbikira, ndipo ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Kawirikawiri ndinakumbukira mawu olimbikitsa amene Mulungu anauza Ezekieli, akuti: “Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zawo; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yawo. Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pawo.”​—Ezekieli 3:8, 9.

Maulendo angapo, amuna awiri atchalitchi anandipeza ndikugula zinthu ndipo anayamba kundinyoza mokweza mawu komanso mwamtopola, kuti andichititse manyazi kwa anthu ena amene ankagulanso zinthu. Koma ine sindinayankhe chilichonse. Nthawi ina, pa ulendo wobwereza kwa munthu wachidwi, mbusa anabwera pomwepo n’kuyamba kundinena kuti sindikhulupirira Yesu. Ananditsomphola Baibulo n’kumandiloza nalo kumaso, kenaka anandibwezera Baibulolo mwachipongwe. Ndinamuyang’anitsitsa, ndipo mofatsa koma mwamphamvu ndinanena mawu amene amapezeka pa Yohane 3:16 ndi kumutsimikizira kuti ndimakhulupirira Yesu. Anasowa chonena chifukwa cha yankho langa losapita m’mbalilo ndipo anangochoka osalankhula china chilichonse.

Ndinasangalala kulalikira kwa Aaborijini a m’dera la Derby. Wansembe anayesa kundiletsa kuti ndisakafikire anthu a m’mudzi wina wake koma wansembeyo anasamutsidwa. Choncho, ndinawauza uthenga wa m’Baibulo. Nthawi zonse ndinkafuna nditakhala mmishonale ngati ang’ono awo a mayi anga aja, ndipo apa ndinali kugwira ntchito ngati ya mmishonale, kuthandiza anthu kuphunzira Mawu a Mulungu. Aaborijini ambiri anavomera, ndipo ndinayambitsa maphunziro angapo a Baibulo.

Kuzindikira Chosowa Changa Chauzimu

Kwa zaka zisanu, ndine ndekha amene ndinali Mboni ya Yehova ku Derby. Kunali kovuta kuti ndikhale wolimba mwauzimu popanda kulimbikitsidwa ndi misonkhano ndi olambira anzanga. Nthawi ina, ndinali wokhumudwa ndipo ndinangokwera galimoto n’kuchoka. Madzulo nditabwera kunyumba, ndinapeza mlongo wina ndi ana ake seveni akundidikirira. Anandibweretsera mabuku kuchokera ku mpingo wa Broome, kutali kwambiri. Kuyambira nthawi imeneyo, mlongoyu, Betty Butterfield, anakonza zomabwera ku Derby kamodzi pamwezi n’kudzakhala nane Loweruka ndi Lamlungu. Tinkalalikira limodzi kenako tinkaphunzira limodzi Nsanja ya Olonda kunyumba kwanga. Ndiyeno, ine ndinkapitanso ku Broome kamodzi pa mwezi.

Abale a ku Broome anali othandiza kwambiri ndipo nthawi zina ankatha kuyenda ulendo wautali kubwera ku Derby kuti adzandithandize mu utumiki wa kumunda. Anauzanso abale ndi alongo onse ochokera m’matawuni ena kuti akamadutsa ku Derby azindizonda ndi kupita nane muutumiki. Abale apaulendo amenewa ankandibweretsera matepi a nkhani za onse. Ena anayambanso kuphunzira nane Nsanja ya Olonda. Ndinalimbikitsidwa chifukwa cha kundichezera kwa nthawi yaifupi kumeneku.

Ndinalandiranso Thandizo Lina

Kwa zaka zambiri, ndinkalimbikitsidwa Arthur ndi Mary Willis, banja limene linapuma pa ntchito lochokera kum’mwera kwa chigawo chakumadzulo kwa Australia, akabwera kudzandithandiza, ndipo ankakhala miyezi itatu m’nyengo yozizira iliyonse. Mbale Willis ankachititsa misonkhano yambiri ndi kutsogolera muutumiki wa kumunda. Tinkapita tonse ku malo akutali kwambiri m’dera Kimberley Plateau. Kumeneko, tinkapita m’mafamu owetako n’gombe. Nthawi iliyonse Mbale ndi Mlongo Willis akapita kwawo, ndinkasungulumwa kwambiri.

Pomaliza, chakumapeto kwa chaka cha 1983, ndinalandira uthenga wosangalatsa wakuti banja la Danny ndi Denise Sturgeon ndi ana awo folo aamuna, akubwera kudzakhala ku Derby. Atafika, tinayamba kuchita misonkhano ya nthawi zonse mlungu uliwonse ndi kulowa limodzi mu utumiki wa kumunda. M’chaka cha 200l panapangidwa mpingo. Lero, mumzinda wa Derby muli mpingo wolimba umene uli ndi ofalitsa 24, akulu awiri ndi mtumiki wothandiza mmodzi amene akutisamalira mwauzimu. Nthawi zina, timasonkhana anthu pafupifupi 30.

Ndikakumbukira zaka zambiri m’mbuyomu, ndimasangalala kuona mmene Yehova anandithandizira kuti ndimutumikire. Ngakhale kuti mwamuna wanga sanakhalebe Mboni, amapitirizabe kundichirikiza m’njira zina. Anthu okwana faifi a pabanja panga ndi Mboni zobatizidwa, ana anga aakazi awiri, zidzukulu zanga ziwiri zazikazi, ndi mwana wa mng’ono wanga. Komanso, achibale anga ena ambiri akuphunzira Baibulo ndi anthu a Yehova.

Ndikuyamikira ndi mtima wonse kuti Yehova anandithandiza kum’peza. Sindidzasiya kukhala wake mpaka kalekale.​—Salmo 65:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, koma tsopano anasiya kulisindikiza.

[Map/​Zithunzi patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AUSTRALIA

Wyndham

Kimberley Plateau

Derby

Broome

Perth

[Mawu a Chithunzi]

Kangaroo and lyrebird: Lydekker; koala: Meyers

[Chithunzi patsamba 14]

Ndikugwira ntchito yaunesi pachipatala cha Wyndham, mu 1953

[Chithunzi patsamba 15]

Mpingo wa Derby, mu 2005