“Limodzi mwa Masiku Amene Ndinasangalala Kwambiri Pamoyo Wanga”
“Limodzi mwa Masiku Amene Ndinasangalala Kwambiri Pamoyo Wanga”
BUNGWE lina lothandizidwa ndi boma ku Australia, lotchedwa Beyondblue, linati: “Kuvutika maganizo ndi vuto limene anthu amalitchula kawirikawiri ndipo mwinanso lalikulu kwambiri pa mavuto a m’maganizo amene achinyamata akukumana nawo.” Kafukufuku akusonyeza kuti chaka ndi chaka achinyamata pafupifupi 100,000 ku Australia amavutika maganizo.
Vutoli limakhudzanso achinyamata achikristu. Koma kukhulupirira Yehova kwathandiza ambiri mwa achinyamatawa kuti athane ndi maganizo olefula ndi kusangalala ndi chinyamata chawo. Akamachita zimenezi, amachititsa chidwi kwambiri anthu ena. Motani?
Taonani nkhani ya mtsikana wina wa zaka 18, dzina lake Claire. Iye ndi mayi ake amapita ku mpingo wina wa Mboni za Yehova ku Melbourne. Bambo a Claire atathawa banjali, Claire anavutika nazo maganizo kwambiri. Koma anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Atate wake wakumwamba, Yehova. Tsiku lina dokotala wa banjali, dzina lake Lydia, anabwera kunyumba kwa Claire kudzaona mayi ake, omwe anali kudwala. Kenako chifukwa cha kukoma mtima kwake, dokotalayo anadzipereka kutenga Claire pagalimoto kupita naye kumsika. Ali m’njira, dokotalayo anafunsa Claire ngati ali ndi chibwenzi. Claire anafotokoza kuti monga wa Mboni za Yehova, sangakhale ndi chibwenzi popanda cholinga chodzakwatirana nacho. Izi zinam’dabwitsa dokotalayo. Kenako, Claire anafotokoza mmene Baibulo lam’thandizira kusankha mwanzeru zoti achite pamoyo wake. Pomaliza, Claire anauza dokotalayo kuti angathe kum’bweretsera buku lina lofotokoza za m’Baibulo limene linam’thandiza kwambiri iyeyo. Bukulo linali lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.
Patatha masiku atatu chilandirireni buku lija, Lydia anaimbira telefoni mayi a Claire kuti awafotokozere mmene bukulo likumusangalatsira. Kenako anapempha mabuku ena sikisi oti akapatse anzake kuntchito. Claire anapititsa mabukuwo, ndipo dokotalayo anafotokoza mmene wachitira chidwi ndi chikhulupiriro chake. Claire anafotokoza kuti angathe kumaphunzira Baibulo ndi dokotalayo, ndipo dokotalayo anavomera phunzirolo.
Claire anakhala akuchita phunziro ndi dokotalayo kwa miyezi ingapo ndipo linkachitika panthawi yopuma masana. Kenako, Lydia anapempha Claire ngati angafune kudzalankhula pamsonkhano wina wokambirana za kuvutika maganizo kwa achinyamata. Ngakhale kuti poyamba anali kuopaopa, Claire anavomera. Pamsonkhanowo panali anthu oposa 60. Akatswiri a zaubongo anayi, omwe onsewo anali achikulire, analankhula pamsonkhanowo. Kenako inafika nthawi yoti Claire alankhule. Iye anasonyeza kufunika koti achinyamata akhale paubwenzi ndi Mulungu. Anafotokoza kuti Yehova Mulungu amawakonda kwambiri achinyamata ndipo amathandiza anthu onse amene am’pempha kuti awathandize ndi kuwalimbikitsa. Kuwonjezera apo, anafotokozanso chikhulupiriro chake choti posachedwapa Yehova adzachotsa matenda onse, kuphatikizapo matenda a m’maganizo. (Yesaya 33:24) Kodi anthu anachita chiyani atamva umboni wogwira mtima umenewu?
Claire anati: “Chigawo cha msonkhano chimenechi chitatha, anthu anabwera kudzandiuza kuti achita chidwi kumva wachinyamata akulankhula za Mulungu. Ndinagawira mabuku 23 a Achichepere Akufunsa. Atsikana atatu omwe anali nawo pamsonkhanowo anandipatsa nambala za telefoni zawo. Panopa, mmodzi wa atsikanawo akuphunzira Baibulo. Limeneli linali limodzi mwa masiku amene ndinasangalala kwambiri pamoyo wanga.”