“Mawu” a Yehova Azikutchinjirizani
“Mawu” a Yehova Azikutchinjirizani
M’CHAKA cha 490 B.C.E. pankhondo yosaiwalika ya ku Marathon, asilikali a mzinda wa Atene ku Girisi, omwe analipo pakati pa masauzande 10 kufika 20, anamenyana ndi asilikali a ku Perisiya omwe anali gulu la nkhondo lamphamvu kwambiri. Luso la Agirikiwo pankhondoyi linagona kwambiri pa mmene anayalirana m’magulu awo. M’gulu lililonse anayalana m’mizeremizere ndipo poyenda ankayenda moyandikana kwambiri. Zishango zawo zinkangokhala ngati khoma losabooleka lokhomerera mikondo italiitali. Izi zinathandiza asilikali a ku Atene kugonjetsa asilikali ankhaninkhaniwo a ku Perisiya. Ndipotu imeneyi inakhala nkhani yosaiwalika.
Akristu oona ali pankhondo yauzimu. Akulimbana ndi adani amphamvu kwambiri, omwe ndi olamulira osaoneka a dongosolo loipa lomwe lilipoli. Olamulira amenewa Baibulo limawafotokoza kuti ndi “akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, . . . a uzimu a choipa m’zakumwamba.” (Aefeso 6:12; 1 Yohane 5:19) Anthu a Mulungu akupitirizabe kupambana nkhondo imeneyi, komatu sikuti akutero mwa mphamvu zawo ayi. Yehova ndiye amene akuwathandiza. Iye ndiye amene amawatchinjiriza ndi kuwalangiza, monga mmene lemba la Salmo 18:30 limanenera kuti: “Mawu a Yehova n’ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.”
Inde, Yehova amateteza atumiki ake okhulupirika kuti asavulazidwe mwauzimu. Amachita zimenezi pogwiritsa ntchito “mawu” ake oyengeka, omwe ali m’Malemba Opatulika. (Salmo 19:7-11; 119:93) Ponena za nzeru yopezeka m’Mawu a Mulungu, Solomo analemba kuti: “Usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza.” (Miyambo 4:6; Mlaliki 7:12) Kodi nzeru za Mulungu zimatiteteza bwanji kuti tisavulazidwe? Taonani chitsanzo ichi cha Aisrayeli akale.
Anthu Amene Anatetezedwa ndi Nzeru za Mulungu
Chilamulo cha Yehova chinateteza ndi kutsogolera Aisrayeli pa mbali iliyonse ya moyo wawo. Mwachitsanzo, malamulo okhudza zakudya, ukhondo, ndi kubindikiritsa munthu anawateteza ku matenda ambiri amene anali kuvutitsa mitundu Deuteronomo 7:12, 15; 15:4, 5) Chilamulo cha Yehova chinathandizanso kusungitsa ngakhale nthaka ya ku Israyeli kuti ikhale yabwino. (Eksodo 23:10, 11) Malamulo oletsa kupembedza konyenga anateteza anthuwo mwauzimu, anawatchinjiriza kuti asaponderezedwe ndi ziwanda, kuti asapereke nsembe ana awo, ndi zoipa zina zambiri, kuwonjezera pa kuwatchinjiriza ku mchitidwe wochotsa anthu ulemu wogwadira mafano opanda moyo.—Eksodo 20:3-5; Salmo 115:4-8.
ina. Komatu ndi m’zaka za m’ma 1800 momwemu pamene asayansi anayamba kuona zinthu mofanana ndi Chilamulo cha Mulungu pambuyo poti atulukira tizilombo timene timayambitsa matenda. Malamulo okhudza kukhala ndi malo akoako, kuwombola munthu, kukhululukirana ngongole, ndi katapila anali kupindulitsa Aisrayeli chifukwa anali kupangitsa anthuwo kukhala mwabata ndiponso sanali kudyerana masuku pamutu pa zachuma. (Apatu n’zoonekeratu kuti “mawu” a Yehova sanali ‘opanda pake’ kwa Aisrayeli; koma kwa onse amene anamvera, kwa iwo mawuwo anali moyo wawo ndipo anachulukitsa masiku awo. (Deuteronomo 32:47) Zilinso chimodzimodzi masiku ano kwa anthu amene amasunga mawu anzeru a Yehova, ngakhale kuti Akristu salinso mu pangano la Chilamulo. (Agalatiya 3:24, 25; Ahebri 8:8) Ndipotu, m’malo mokhala ndi mpambo wa malamulo, Akristu ali ndi mfundo zambirimbiri za m’Baibulo zoti ziziwatsogolera ndi kuwatchinjiriza.
Anthu Amene Amatetezedwa ndi Mfundo za M’Baibulo
Lamulo silingakhudze zinthu zambiri ndiponso lingagwire ntchito nthawi yochepa chabe. Koma mfundo za m’Baibulo, popeza kuti ndiwo maziko ake a malamulo, nthawi zambiri zimakhudza zinthu zambiri ndipo sizisintha. Mwachitsanzo, talingalirani mfundo imene ili pa lemba la Yakobo 3:17, lomwe mawu ake ena amati: “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere.” Kodi mfundo imeneyi ingateteze motani anthu a Mulungu masiku ano?
Kukhala woyera ndiko kukhala wodzisunga. Motero amene amaona kuti kukhala woyera n’kwaphindu amayesetsa kupewa osati chisembwere chokha, koma zinthunso zimene zimachititsa munthu kuchita chisembwerecho, monga kukonda kuganizira za kugonana ndi kukonda zinthu zolaula. (Mateyu 5:28) Mofananamo, mwamuna ndi mkazi amene ali pachibwenzi akakhala kuti mfundo ya pa Yakobo 3:17 inawalowa mu mtima, amapewa kuchita zinthu zosonyezana chikondi zimene zingawalepheretse kudziletsa. Popeza kuti iwo amakonda kutsatira mfundo za m’Baibulo, sapatutsidwa pa kukhala oyera, mwina mwa kuganiza kuti malinga ngati sakuphwanya lamulo lolembedwa, ndiye kuti khalidwe lawo Yehova amagwirizana nalo. Amadziwa kuti Yehova ‘amayang’ana mumtima’ ndipo amachitapo kanthu moyenerera. (1 Samueli 16:7; 2 Mbiri 16:9) Anthu anzeru oterowo amateteza thupi lawo ku matenda ochuluka opatsirana pogonana amene afala masiku ano ndiponso amapewa kudzivutitsa m’maganizo ndi m’mtima.
Lemba la Yakobo 3:17 limati nzeru yochokera kwa Mulungu ilinso “yamtendere.” Monga tikudziwa, Satana amayesa kutichititsa kuti tisamagwirizane ndi Yehova mwa kuika zachiwawa m’mitima yathu. Njira zina zimene amachitira zimenezi ndizo kudzera m’mabuku okayikitsa, mafilimu, nyimbo, ndi masewera a pakompyuta, ndipo ena mwa masewerawa amalimbikitsa osewerawo kuyerekeza kuti akuchitira anthu anzawo nkhanza zosaneneka kapenanso kuwapha kumene. (Salmo 11:5) Umboni wakuti Satana zikumuyendera pankhaniyi ndi kuchuluka kwa ziwawa. Zaka za m’mbuyomu, nyuzipepala ya ku Australia ya The Sydney Morning Herald inafotokoza mawu amene ananena bambo Robert Ressler pankhani imeneyi. A Ressler anati anthu opha anzawo amene anacheza nawo ndi kuwafunsa mafunso m’ma 1970 ankachita zimenezo chifukwa choonerera ndi kuwerenga zolaula zomwe “poziyerekezera ndi za masiku ano, sizinali zonyansa kwenikweni.” Choncho a Ressler anati akuona “tsogolo lopanda chabwino, koma nthawi imene anthu omwe amapha anthu ambiri azimka nachulukirachulukira.”
Patangotha miyezi ingapo nkhani imeneyi itatuluka m’nyuzipepalayo, munthu wina wamfuti anapha ana 16 limodzi ndi mphunzitsi wawo pa sukulu yamkaka m’tauni ya Dunblane, ku Scotland. Atatero iyenso anadzipha. Mwezi wotsatira munthu winanso wosokonezeka mutu amene anali ndi mfuti anapha anthu 32 m’tauni ya Port Arthur, pa chisumbu chabata cha Tasmania, ku Australia. M’zaka zaposachedwapa, ku United States ana a sukulu ambiri akhala akuphedwa m’sukulu zawo, ndipo zimenezi zachititsa anthu ku America kufunsa kuti, N’chifukwa chiyani? Mu June 2001, nkhani ya munthu winawake wosokonezeka bongo ku Japan inali
m’kamwam’kamwa padziko lonse. Munthuyo anafika pa sukulu ina ndi kubaya ndi mpeni mpaka kupheratu ana 8 a sitandade 1 ndi 2 ndiponso anachekacheka anthu ena 15. Zonsezi zikungophera mphongo mawu aja amene ananena bambo Ressler. N’zoona kuti pali zifukwa zambirimbiri zimene zimapangitsa anthu kuchita zoipa zoterezi, komabe nthawi zambiri zikuoneka kuti zina zimene zikuchititsa zimenezi ndi zinthu zachiwawa zosonyezedwa m’ma TV, m’mavidiyo, ndi m’makompyuta. Bambo Phillip Adams, womwe amalemba nkhani mu nyuzipepala inayake ku Australia, anati: “Ngati malonda omwe amawatsatsa kwa masekondi 60 amachititsa anthu ambiri kukagula malondawo, musandiuze kuti filimu yotchuka kwambiri ya maola awiri singasinthe maganizo a anthu.” Ndiye kodi mungadabwe kuti apolisi analanda matepi a vidiyo 2,000 a zachiwawa ndi zolaula m’nyumba ya munthu wamfuti uja wa ku Port Arthur?Amene amatsatira mosamalitsa mfundo za m’Baibulo amateteza maganizo awo ndi mitima yawo ku zinthu za mtundu uliwonse zimene anthu amasangalala nazo koma zomwe zimalimbikitsa zachiwawa. Motero, “mzimu wa dziko lapansi” supeza mpata uliwonse pa kaganizidwe kawo ndi zokhumba zawo. M’malo mwake, iwo ‘amaphunzitsidwa ndi Mzimu [wa Mulungu],’ ndipo amayesetsa kuti azikonda zipatso za mzimuwo zomwe zimaphatikizapo mtendere. (1 Akorinto 2:12, 13; Agalatiya 5:22, 23) Amachita zimenezi mwa kuphunzira Baibulo nthawi zonse, kupemphera, ndi kusinkhasinkha pa zinthu zabwino. Amapewanso kuyanjana ndi anthu okonda zachiwawa, ndipo amasankha kuti azigwirizana ndi anthu amene mofanana ndi iwowo amalakalaka kudzakhala m’dziko latsopano lamtendere la Yehova. (Salmo 1:1-3; Miyambo 16:29) Ndithudi, nzeru za Mulungu zimatiteteza kwambiri.
Mawu a Yehova Azitchinjiriza Mtima Wanu
Pamene Yesu anayesedwa m’chipululu, anatsutsa zonena za Satana mwa kutchula molondola zimene Mawu a Mulungu amafotokoza. (Luka 4:1-13) Komabe, sikuti iye anakambirana ndi Mdyerekezi pofuna kungoona kuti wanzeru ndani. Mwa kuzika zonena zake m’Malemba, Yesu analankhula zimene zinali mumtima mwake, ndipo n’chifukwa chake machenjera a Mdyerekezi, omwe anagwira ntchito bwino kwambiri mu Edene, analephera kukola Yesu. Nafenso Satana sadzatikola ndi zochita zake zochenjera ngati tidzaza mawu a Yehova m’mitima yathu. Kuchita zimenezi ndiko chinthu chofunika kwambiri, chifukwa ‘magwero a moyo amatuluka’ mumtima.—Miyambo 4:23.
Ndiponso, tiyenera kupitirizabe kuteteza mtima wathu nthawi zonse. Satana atalephera kuyesa Yesu m’chipululu sanalekere pomwepo. (Luka 4:13) Nafenso sadzatileka msanga, koma adzayesa njira zosiyanasiyana kuti atichititse kukhala osakhulupirika. (Chivumbulutso 12:17) Choncho tiyeni titsanzire Yesu mwa kukonda kwambiri Mawu a Mulungu, panthawi yofananayo tikumapemphera mosaleka kuti atipatse mzimu woyera ndi nzeru. (1 Atesalonika 5:17; Ahebri 5:7) Kumbali yake, Yehova amalonjeza onse othawira kwa iye kuti sadzavulazidwa konse mwauzimu.—Salmo 91:1-10; Miyambo 1:33.
Mawu a Mulungu Amateteza Mpingo
Satana sangalepheretse “khamu lalikulu” lomwe linanenedweratu kuti lipulumuke chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 7:9, 14) Komabe iye amayesetsa mwamtima bii kuti aipitse Akristu n’cholinga chakuti ena a iwo Yehova aleke kuwayanja. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, zinthu zinamuyendera mu Israyeli wakale, moti anthu 24,000 anafa pa khomo lenileni lolowera m’Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 25:1-9) Inde, Akristu ochita zolakwa amene amalapa moona mtima amathandizidwa mwachikondi kuti akhalenso olimba mwauzimu. Koma ochimwa amene salapa, mofanana ndi Zimiri wakale, angathe kuipitsa makhalidwe a ena ndiponso moyo wawo wauzimu. (Numeri 25:14) Monga asilikali amene akuyenda ndi anzawo pa mizere ngati ija ya Agiriki koma ataya zishango zawo, iwo amaika anzawo pangozi kuwonjezera pa kudziika iwo eni pangozi.
Motero lamulo la m’Baibulo limati: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi. . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (1 Akorinto 5:11, 13) Kodi inu simukuvomereza kuti “mawu” anzeru amenewa amathandiza kutchinjiriza mpingo wachikristu kuti anthu mu mpingowo akhalebe ndi makhalidwe abwino ndiponso kuti mpingowo ukhale woyera mwauzimu?
Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, Matchalitchi Achikristu ambiri, ngakhalenso anthu ampatuko, amati mfundo za m’Baibulo zimene sizigwirizana 2 Timoteo 4:3, 4) Komabe, onani kuti mawu amene ali pa Miyambo 30:5, omwenso amanena za “mawu” a Yehova kuti ali ngati chikopa kaya kuti chishango, mu vesi 6 akutsatiridwa ndi lamulo lakuti: “Usawonjezere kanthu pa mawu [a Mulungu], angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti uli kunama.” Ndithudi, amene amasokoneza uthenga wa m’Baibulo amanama mwauzimu, ndipo ndiwo amene amanena bodza loipitsitsa pa mabodza onse. (Mateyu 15:6-9) Motero tiyeni tiziyamikira ndi mtima wathu wonse kuti tili m’gulu limene limalemekeza kwambiri Mawu a Mulungu.
ndi maganizo amakono ovomereza makhalidwe otayirira n’zachikale. Choncho saona vuto lililonse anthu akamachita machimo akuluakulu a mtundu wina uliwonse, ngakhale ochita zimenezowo akhale atsogoleri achipembedzo. (Kutetezedwa ndi “Fungo Labwino”
Chifukwa chakuti anthu a Mulungu amamamatira ku Baibulo ndipo amauza ena uthenga wake wotonthoza mtima, amatulutsa “fungo labwino” lopatsa moyo lokhala ngati chofukiza. Fungoli limasangalatsa Yehova. Koma kwa osalungama, anthu amene ali ndi uthenga umenewo amatulutsa “fungo la imfa ku imfa.” Inde, dongosolo la zinthu la Satanali lasokoneza kwambiri mphuno zophiphiritsa zomvera fungo za anthu oipa moti amakhala omangika kapenanso amanyansidwa kumene akakhala pafupi ndi amene amatulutsa “fungo labwino la Kristu.” Komano anthu amene amafalitsa mwakhama uthenga wabwino amakhala “fungo labwino la Kristu . . . mwa iwo akupulumutsidwa.” (2 Akorinto 2:14-16) Nthawi zambiri anthu oona mtima oterowo amaipidwa ndi chinyengo ndiponso mabodza achipembedzo zimene chipembedzo chonyenga chimadziwika nazo. Ndiye tikatenga Mawu a Mulungu n’kuwauza uthenga wa Ufumu, amamva kuti akukokedwera kwa Kristu ndipo amafuna kudziwa zambiri.—Yohane 6:44.
Ndiye musamagwe mphwayi munthu wina akakana kumvetsera uthenga wa Ufumu. M’malo mwake muziona “fungo labwino la Kristu” kukhala lokutetezani mwauzimu mwa njira yakuti, chifukwa cha fungoli, anthu ambiri amene angakhale ovulaza sayandikira munda wauzimu umene muli anthu a Mulungu, koma limakopa anthu a mitima yabwino.—Yesaya 35:8, 9.
Chifukwa chakuti asilikali a ku Girisi anali kuyenda moyandikana kwambiri pankhondo ija ya ku Marathon, ndiponso chifukwa chakuti zishango zawo anazigwirabe ndi mphamvu zawo zonse, iwo anapambana nkhondoyo ngakhale zinali zoonekeratu kuti gulu lawo linali losanunkha kanthu. Mofananamo, palibe kukayika kulikonse kuti Mboni zokhulupirika za Yehova zidzapambana kotheratu nkhondo yawo yauzimu, chifukwa ichi ndi “cholowa” chawo. (Yesaya 54:17) Motero tiyeni tonsefe tipitirize kuthawira kwa Yehova mwa ‘kugwirabe zolimba mawu a moyo.’—Afilipi 2:16, NW.
[Zithunzi patsamba 31]
‘Nzeru yochokera kumwamba ndi yoyera, nikhalanso yamtendere’