Kodi Mukumanga pa Maziko Otani?
Kodi Mukumanga pa Maziko Otani?
MOKULIRA, kulimba kwa nyumba kumadalira kulimba kwa maziko ake. Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mfundo imeneyi mophiphiritsira.
Mwachitsanzo, mneneri Yesaya ananena kuti Yehova Mulungu “[a]nakhazika maziko a dziko lapansi.” (Yesaya 51:13) Maziko ophiphiritsira amenewa ndi malamulo osasinthika a Mulungu omwe amalamulira kayendedwe ka dziko lapansi ndi kuligwira kuti lisachoke pamalo ake. (Salmo 104:5) Mawu a Mulungu, Baibulo, amanenanso kuti anthu ali ndi “maziko.” Maziko amenewa ndi chilungamo, malamulo, ndi kutsatira dongosolo lokhazikitsidwa. Mazikowa “akapasuka,” kapena kuti akatha mphamvu, chifukwa cha kupanda chilungamo, ziphuphu, ndi chiwawa, anthu sakhalanso mwabata.—Salmo 11:2-6; Miyambo 29:4.
Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pa munthu aliyense payekha. Chakumapeto kwa ulaliki wake wotchuka wa pa phiri, Yesu Kristu anati: “Yense amene akamva mawu anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzam’fanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mawu anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.”—Mateyu 7:24-27.
Kodi moyo wanu mukuumanga pamaziko otani? Kodi mukuumanga pa mchenga umene uli maziko osalimba a nzeru za anthu osaopa Mulungu, omwe angawonongetse moyo wanu? Kapena kodi mukuumanga pa thanthwe lolimba lomwe ndi kumvera mawu a Yesu Kristu, kumene kudzakuthandizani kupirira mkuntho wophiphiritsira pa moyo wanu?