Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsatirani Malangizo a Mulungu Wamoyo

Tsatirani Malangizo a Mulungu Wamoyo

Tsatirani Malangizo a Mulungu Wamoyo

‘Tembenukirani kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo.’​—MACHITIDWE 14:15.

1, 2. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuona Yehova kukhala “Mulungu wamoyo”?

MTUMWI Paulo ndi Barnaba atachiritsa munthu, Paulo anatsimikizira anthu a ku Lustra omwe anali kuonerera zomwe zinachitazo kuti: “Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo.”​—Machitidwe 14:15.

2 N’zoona kuti Yehova si fano lopanda moyo, koma ndi “Mulungu wamoyo.” (Yeremiya 10:10; 1 Atesalonika 1:9, 10) Kuwonjezera pa mfundo imeneyi yakuti Yehova ndi wamoyo, iyeyonso ndi Gwero la moyo wathu. “Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Iye amafuna kuti tizisangalala ndi moyo panopo ndiponso m’tsogolo. Paulo anawonjezera kuti Mulungu “sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.”​—Machitidwe 14:17.

3. N’chifukwa chiyani tingadalire malangizo a Mulungu?

3 Chidwi chomwe Mulungu ali nacho pa moyo wathu chimatipatsa chifukwa chodalirira malangizo ake. (Salmo 147:8; Mateyu 5:45) Ena sangaone choncho akapeza lamulo lina m’Baibulo limene sakulimvetsa kapena limene likuoneka kuti likuwamanitsa zinthu zina. Komatu ndi nzeru kudalira malangizo a Yehova. Tiyeni tiyerekezere motere: Ngakhale Mwisrayeli akanapanda kumvetsa kuti n’chifukwa chiyani pali lamulo loletsa kugwira mtembo, koma akanapindula nalo ndithu polimvera. Choyamba, kumvera kwake lamulo limenelo kukanam’thandiza kuti akhale paubwenzi wolimba ndi Mulungu wamoyo; ndipo chachiŵiri, kukanam’thandiza kupeŵa matenda.​—Levitiko 5:2; 11:24.

4, 5. (a) Chikristu chisanayambe, kodi Yehova anapereka malangizo otani okhudza magazi? (b) Kodi tikudziŵa bwanji kuti lamulo la Mulungu pankhani ya magazi limakhudzanso Akristu?

4 N’chimodzimodzinso ndi malangizo a Mulungu pankhani ya magazi. Mulungu anauza Nowa kuti anthu sayenera kudya magazi. Kenako m’Chilamulo, Mulungu anasonyeza kuti ntchito imodzi yokha yovomerezeka ya magazi ndiyo ya pa guwa la nsembe, pokhululukira machimo. Popereka malangizo ameneŵa, Mulungu anali kuyala maziko a ntchito yapamwamba kwambiri ya magazi, yopulumutsa miyoyo kudzera m’dipo la Yesu. (Ahebri 9:14) Inde Mulungu anapereka malangizo ake poganizira moyo wathu komanso kuti zinthu zitiyendere bwino. Pofotokoza lemba la Genesis 9:4, Adam Clarke, yemwe anali katswiri wa maphunziro a Baibulo wa m’zaka za m’ma 1800, analemba kuti: “Zipembedzo za Orthodox za m’mayiko a kum’maŵa zikutsatirabe kwambiri lamulo limeneli [lopita kwa Nowa] . . . Chilamulo chinaletsa kudya mwazi, chifukwa chakuti unali kuimira mwazi womwe unadzakhetsedwa patsogolo chifukwa cha machimo a dziko lonse; ndipo m’Mauthenga Abwino sunayenera kudyedwa, chifukwa nthaŵi zonse umafunika kuonedwa kuti ukuimira mwazi womwe unakhetsedwa kuti machimo akhululukidwe.”

5 N’kutheka kuti katswiri ameneyu anali kunena za uthenga wabwino wofunika kwambiri wokhudza Yesu. Uthengawu umaphatikizapo zomwe Mulungu anachita potumiza Mwana wake kuti adzatifere ndiponso kuti adzakhetse mwazi wake kuti ife tithe kupeza moyo wosatha. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; Aroma 5:8, 9) Zimene katswiriyu ananena zimakhudzanso lamulo lomwe linadzaperekedwa pambuyo pake lakuti otsatira Kristu ayenera kusala mwazi.

6. Kodi Akristu anapatsidwa malangizo otani pankhani ya magazi, ndipo n’chifukwa chiyani?

6 Mukudziŵa inu kuti Mulungu anapatsa Aisrayeli malamulo ambirimbiri. Yesu atafa, ophunzira ake sanafunikire kutsatira malamulo onsewo. (Aroma 7:4, 6; Akolose 2:13, 14, 17; Ahebri 8:6, 13) Koma patapita nthaŵi, panabuka funso lokhudza lamulo lina lofunika kwambiri, lamulo la mdulidwe wa amuna. Kodi anthu omwe sanali Ayuda koma omwe nawo ankafuna kupindula ndi mwazi wa Kristu anafunikira kudulidwa posonyeza kuti anali kutsatirabe Chilamulo? M’chaka cha 49 Kristu Atabwera, bungwe lolamulira lachikristu linakambirana nkhani imeneyo. (Machitidwe, chaputala 5) Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, atumwi ndi amuna akulu anaona kuti lamulo loti mwamuna aliyense azidulidwa linatha pamene Chilamulo chinatha. Komabe, Akristu anafunika kupitiriza kutsatira zinthu zina zomwe Mulungu anali kufuna m’Chilamulocho. M’kalata yomwe inapita kumipingo, bungwe lolamuliralo linalemba kuti: “Chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu.”​—Machitidwe 15:28, 29.

7. Kodi ‘kusala mwazi’ n’kofunika motani kwa Akristu?

7 N’zoonekeratu kuti bungwe lolamulira linaona kuti ‘kusala mwazi’ ndi kofunika kwambiri mofanana ndi kukhala ndi makhalidwe abwino monga kupeŵa chiwerewere kapena kupeŵa kulambira mafano. Izi zikusonyeza kuti lamulo loletsa magazi siliyenera kuonedwa mopepuka. Akristu amene amalambira mafano kapena kuchita chiwerewere koma osalapa “sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu”; “cholandira chawo chidzakhala . . . imfa yachiŵiri.” (1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8; 22:15) Ndiye onani kuti ngati munthu samvera malangizo a Mulungu okhudza kupatulika kwa magazi mapeto ake ndi imfa yamuyaya, komano akamalemekeza nsembe ya Yesu angapeze moyo wamuyaya.

8. N’chiyani chikusonyeza kuti Akristu oyambirira sananyalanyaze malangizo a Mulungu pankhani ya magazi?

8 Kodi Akristu oyambirira anawamva motani malangizo a Mulungu okhudza magazi ndipo anawatsatira motani? Kumbukirani zimene Clarke ananena zakuti: “M’Mauthenga Abwino [mwazi] sunayenera kudyedwa, chifukwa nthaŵi zonse umafunika kuonedwa kuti ukuimira mwazi womwe unakhetsedwa kuti machimo akhululukidwe.” Zochitika zakale zimatsimikizira kuti Akristu oyambirira nkhaniyi ankaiona kuti n’njofunika kwambiri. Tertullian analemba kuti: “Talingalirani za anthu osusuka chifukwa cha ludzu, amene pachionetsero m’bwalo lamaseŵero, amatcherezera magazi a munthu wamlandu . . . kuti akachizire matenda awo a khunyu.” Mosiyana ndi akunja omwe ankadya magazi, Tertullian ananena kuti Akristu ‘ngakhale pakati pa zakudya [zawo] panalibe magazi a nyama . . . Pa ziyeso za Akristu mumawapatsa masoseji a magazi. Koma mumakhala mukudziŵiratu kuti kwa iwo [kuteroko] n’kuswa lamulo.’ Inde ngakhale kuti ankawaopseza kuti awapha, Akristu sankadya magazi. Kwa iwo, malangizo a Mulungu anali ofunika kwambiri.

9. Kodi kusala magazi kunaphatikizapo chiyani kuwonjezera pa kusadya magazi enieniwo?

9 Ena angaganize kuti bungwe lolamulira linali kungotanthauza kuti Akristu sanayenera kudya kapena kumwa magazi enieniwo kapena kudya nyama yosakhetsa magazi kapena chakudya chomwe asakanizamo magazi. N’zoona kuti limenelo ndilo linali tanthauzo loyambirira la lamulo lomwe Mulungu anapatsa Nowa. Ndipo lamulo la atumwi linauza Akristu kuti ‘asale zopotola,’ kutanthauza nyama yomwe sinakhetsedwe magazi. (Genesis 9:3, 4; Machitidwe 21:25) Komabe Akristu oyambirira anadziŵa kuti sizinali zokhazo. Nthaŵi zina anthu ankadya magazi monga mankhwala. Tertullian anafotokoza kuti anthu ena akunja ankadya magazi aaŵisi pofuna kuchiza matenda awo a khunyu. Ndipo n’kutheka kuti ankagwiritsanso ntchito magazi m’njira zina pofuna kuchiza matenda ena kapena pofuna kukhala ndi thanzi labwinopo. Motero, kwa Akristu, kukana magazi kunaphatikizapo kusadya magazi pazifukwa za “mankhwala.” Sanasinthe maganizo awo pankhaniyi ngakhale panthaŵi yomwe kuchita zimenezo kunkaika moyo wawo pangozi.

Kugwiritsa Ntchito Magazi Monga Mankhwala

10. Kodi magazi akugwiritsidwa ntchito m’njira zotani monga mankhwala, zomwe zikuchititsa kuti pakhale mafunso otani?

10 Masiku ano kugwiritsa ntchito magazi monga mankhwala n’kofala kwambiri. Kale anthu ankawaika magazi athunthu omwe awatenga m’thupi mwa wina, n’kuwasunga, kenaka n’kupatsa munthu wodwala, mwachitsanzo amene wavulala kunkhondo. M’kupita kwa nthaŵi, ofufuza anapeza njira zogaŵira magazi m’zigawo zake zikuluzikulu. Mwa kupatsa munthu chigawo chimodzi cha magazi, madokotala ankatha kupereka magazi womwewomwewo kwa odwala angapo. Ankatha kupereka madzi a m’magazi kwa munthu wina amene wavulala, ndipo maselo ofiira ankatha kuwapereka kwa munthu winanso. Popitiriza kuchita kafukufuku anapeza kuti angathenso kugaŵa chigawo chachikulu chilichonse cha magazi, monga madzi a m’magazi, n’kukhala tizigawo ting’onoting’ono tambiri, tomwe angapatsenso odwala ambirimbiri. Ntchito yoyesa kugaŵa magazi m’tizigawo ting’onoting’onoyi ikupitirira, ndipo akutulukiranso ntchito zina zatsopano za tizigawo ting’onoting’onoti. Kodi nkhani imeneyi Mkristu ayenera kuiona motani? Iye anatsimikiza mtima kuti sadzalola kuikidwa magazi, koma dokotala wake akum’kakamiza kuti alandire chigawo chachikulu chimodzi cha magazi, mwinamwake maselo ofiira okhaokha. Kapena mwina chithandizocho chingafune kuti apatsidwe kachigawo kakang’ono kamodzi kotengedwa m’chigawo chachikulu cha magazi. Kodi mtumiki wa Mulungu angasankhe motani zoti achite pankhanizi, pokumbukira kuti magazi ndi opatulika ndiponso kuti mwazi wa Kristu ndiwo wopulumutsadi moyo?

11. Kodi ndi maganizo olondola ati okhudza kulandira magazi amene Mboni zakhala nawo kwa nthaŵi yaitali?

11 Zaka zambiri zapitazo Mboni za Yehova zinamveketsa bwino maganizo awo. Mwachitsanzo, zinatumiza nkhani ku magazini ya The Journal of the American Medical Association (November 27, 1981; nkhani yomwe inasindikizidwanso mu kabuku kakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? masamba 27-9). * Nkhani imeneyo inagwira mawu m’mabuku a Genesis, Levitiko, ndi Machitidwe. Ndiyeno inati: “Pamene kuli kwakuti mavesiŵa sananenedwe m’mawu a zamankhwala, Mboni zimawalingalira kukhala oletsa kuthiridwa mwazi wathunthu, ma RBC [maselo ofiira okhaokha] ndi madzi a m’mwazi ndiponso WBC [maselo oyera a mwazi] ndi kupatsidwa zinthu za m’mwazi.” Buku la zachipatala lakuti Emergency Care la mu 2001, pamutu wakuti “Mmene Magazi Anapangidwira,” linati: “Magazi ali ndi zigawo zikuluzikulu zingapo: madzi, maselo ofiira ndi oyera, ndi maselo othandiza magazi kuundana.” Motero, mogwirizana ndi mfundo za achipatala, Mboni zimakana kuikidwa magazi athunthu kapena chigawo china chilichonse mwa zigawo zake zikuluzikulu zinayi.

12. (a) Kodi maganizo athu ndi otani pankhani ya tizigawo ting’onoting’ono totengedwa m’zigawo zikuluzikulu za magazi? (b) Kodi mungapeze kuti mfundo zina zowonjezera zokhudza nkhaniyi?

12 Nkhani yofotokoza za mankhwalayo inapitiriza motere: “Kuzindikira kwachipembedzo kwa Mboni sikumaletseratu kugwiritsiridwa ntchito kwa [tizigawo ting’onoting’ono ta magazi monga] albumin, immune globulins, ndi zosungunula mwazi; Mboni iliyonse iyenera kudzisankhira ngati ingavomereze zimenezi.” Kuchokera mu 1981, akatswiri apeza tizigawo ting’onoting’ono tambiri tomwe akutha kutigwiritsa ntchito kuchokera m’chigawo chilichonse cha zigawo zinayi zikuluzikulu zija. Motero, Nsanja ya Olonda ya June 15, 2000, inali ndi mfundo zabwino kwambiri zokhudza nkhaniyi m’nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga.” Pofuna kuthandiza anthu ambiri amene amaŵerenga magazini ano panopa, yankholo talisindikizanso pa masamba 29-31 a magazini ino. Likulongosola zinthu mwatsatanetsatane ndiponso lili ndi mfundo zofunika kuziganizira, komabe muona kuti mfundo zomwe zili m’nkhaniyi zikugwirizana ndi mfundo zikuluzikulu zomwe zinafotokozedwa mu 1981.

Ntchito ya Chikumbumtima Chanu

13, 14. (a) Kodi chikumbumtima n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani chimafunika kugwiritsidwa ntchito pankhani zokhudza magazi? (b) Kodi Mulungu anapereka kwa Israyeli malangizo otani pankhani yodya nyama, koma kodi n’kutheka kuti anthu ankakhala ndi mafunso otani?

13 Mfundo zimenezi zimafunika kugwiritsa ntchito chikumbumtima. Chifukwa chiyani tikutero? Akristu amavomereza kuti m’pofunika kutsatira malangizo a Mulungu, komabe pankhani zina munthu amafunika kudzisankhira zochita, ndipo apa m’pamene pamafunika chikumbumtima. Chikumbumtima ndi chibadwa chimene chimachititsa munthu kuganizira zinthu mosamala makamaka zokhudza khalidwe labwino. (Aroma 2:14, 15) Komatu mukudziŵa inu kuti chikumbumtima cha anthu chimasiyanasiyana. * Baibulo limanena kuti ena ali ndi ‘chikumbumtima chofooka,’ kusonyeza kuti chikumbumtima cha ena n’cholimba. (1 Akorinto 8:12) Akristu amasiyanasiyana pa zimene akudziŵa zokhudza zimene Mulungu amanena, mmene Mulungu amaganizira, ndiponso mmene angagwiritsire ntchito zimenezi pa zochita zawo. Apa tingapereke chitsanzo cha Ayuda pankhani ya kudya nyama.

14 Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti munthu womvera Mulungu sangadye nyama yosakhetsa magazi. Lamulo limeneli linali lamphamvu kwambiri moti ngakhale panthaŵi ina asilikali achiisrayeli zinthu zitawapanikiza n’kufika podya nyama yosakhetsa magazi, anachimwa kwambiri. (Deuteronomo 12:15, 16; 1 Samueli 14:31-35) Komabe, n’kutheka kuti anthu ankakhala ndi mafunso osiyanasiyana. Mwisrayeli akapha nkhosa, kodi anayenera kukhetsa magazi ake mwamsanga bwanji? Kodi ankafunika kuiboola nkhwiko kuti magaziwo atulukirepo? Kodi pankafunika kuikoloŵeka nkhosayo penapake ataimanga miyendo yam’mbuyo? Nanga akanatero kwanthaŵi yaitali motani? Kodi akanachita zotani ndi ng’ombe yaikulu kwambiri? Ngakhale pambuyo pokhetsa nyamayo, magazi ena angathe kutsalirabe m’minofu. Kodi iye akanadya nyama yoteroyo? Kodi ndani anafunika kusankha zochita pamenepo?

15. Kodi Ayuda ena ankachita chiyani ndi nkhani ya kudya nyama, koma kodi Mulungu anawalangiza chiyani?

15 Yerekezani kuti Myuda amene amatsatiradi chikhulupiriro chake akuganizira mafunso ngati ameneŵa. Mwina akanaona chinthu chanzeru kwambiri kusadya nyama yogulitsidwa pamsika, monganso momwe wina angakanire kudya nyama ngati akuiganizira kuti ingakhale itaperekedwa nsembe kwa mafano. N’kutheka kuti Ayuda ena ankadya nyama pokhapokha akatsatira mwambo wochotsera magazi m’thupi la nyama. * (Mateyu 23:23, 24) Kodi mukuganiza bwanji za kusiyanasiyana maganizo kumeneku? Komanso, popeza kuti Mulungu sanafune kuti anthu aganize moteromo, kodi kukanakhala koyenera kuti Ayuda atumize mafunso ambirimbiri ku bungwe la akuluakulu achipembedzo kuti ligamulepo pa nkhani iliyonse? Ngakhale kuti mwambo umenewu unayambika pakati pa Ayuda, n’zosangalatsa kudziŵa kuti Yehova sanalamule olambira oona kuti azichita zimenezo posankha zochita pankhani ya magazi. Mulungu anapereka mfundo zikuluzikulu zophera nyama zoyera ndi kukhetsa magazi ake, koma sanaperekenso malangizo ena kuwonjezera pa amenewo.​—Yohane 8:32.

16. Kodi n’chifukwa chiyani Akristu angasiyane maganizo pankhani yolandira jekeseni wa kachigawo kakang’ono kochoka m’chigawo chachikulu chimodzi cha magazi?

16 Monga momwe taonera m’ndime 11 ndi 12, Mboni za Yehova sizilola kuikidwa magazi athunthu kapena zigawo zake zikuluzikulu zinayi, zomwe ndi madzi a m’magazi, maselo ofiira, maselo oyera, ndi maselo othandiza magazi kuundana. Nanga bwanji za tizigawo ting’onoting’ono tochokera m’chigawo chachikulu chimodzi, monga tizigawo totengedwa m’madzi a m’magazi tokhala ndi chitetezo chothandiza thupi la munthu kulimbana ndi matenda kapena ululu wa njoka? (Onani tsamba 30, ndime 4.) Ena amaona kuti magazi akawagaŵa m’tizigawo ting’onoting’ono kwambiri toteroto, tizigawoto si magazi ayi motero sitikhudzidwa ndi lamulo ‘losala mwazi.’ (Machitidwe 15:29; 21:25; tsamba 31, ndime 1) Umenewo ndi udindo wawo. Chikumbumtima cha ena chimawaletsa kulandira chilichonse chotengedwa m’magazi (kaya a nyama kapena a munthu), ngakhale kachigawo kochepetsetsa ka chigawo chachikulu chimodzi chokha. * Ndiye pali ena amene amalola kulandira jekeseni wa mapuloteni a m’madzi a m’magazi kuti alimbane ndi matenda kapena ululu wa njoka m’thupi lawo, koma angakane tizigawo ting’onoting’ono tina tonse ta magazi. Komanso, tina mwa tizigawo ta m’magazi tingagwire ntchito mofanana kwambiri ndi chigawo chachikulu chonsecho n’kumuthandiza munthu kuti akhalebe ndi moyo moti Akristu ambiri angaone kuti tizigawo toteroto n’tosavomerezeka kwa iwowo.

17. (a) Kodi chikumbumtima chathu chingatithandize motani pamene tili ndi mafunso okhudza tizigawo ting’onoting’ono ta magazi? (b) N’chifukwa chiyani si nkhani yopepuka kusankha zochita pankhaniyi?

17 Zimene Baibulo limanena pankhani ya chikumbumtima ndi zothandiza pamene tikusankha zochita pambaliyi. Choyamba, m’pofunika kuphunzira zimene Mawu a Mulungu amanena ndi kuyesetsa kuzoloŵeretsa chikumbumtima chanu kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. Izi zidzakuthandizani kusankha zochita mogwirizana ndi malangizo a Mulungu m’malo mouza munthu wina kuti akusankhireni zochita. (Salmo 25:4, 5) Pankhani yolandira tizigawo ting’onoting’ono ta magazi, ena amaganiza kuti, ‘Iyi ndi nkhani ya chikumbumtima, motero ndi nkhani yochepa.’ Maganizo oterowo n’ngolakwika. Kunena kuti nkhani inayake ndi yoyendera chikumbumtima cha munthu sizikutanthauza kuti nkhaniyo ndi yochepa. Ingathe kukhala nkhani yaikulu kwambiri. Chifukwa chimodzi n’chakuti nkhaniyo ingathe kukhudza anthu ena amene chikumbumtima chawo chikusiyana ndi chathu. Timaona zimenezi m’malangizo a Paulo pankhani ya nyama yomwe ingakhale kuti inakaperekedwa nsembe kwa mafano ndipo kenako ikugulitsidwa pamsika. Mkristu afunika kudera nkhaŵa kuti ‘asalase chikumbumtima cha ofooka.’ Ngati akhumudwitsa ena, iye ‘angataye mbale wake amene Kristu anam’fera’ motero angachimwire Kristu. Chotero, ngakhale kuti nkhani zokhudza tizigawo ting’onoting’ono ta magazi zikudalira pa zimene munthu angasankhe payekha, zimenezo sizofunika kuziona mopepuka.​—1 Akorinto 8:8, 11-13; 10:25-31.

18. Kodi Mkristu angapeŵe motani kupha chikumbumtima chake posankha zochita pankhani yokhudza magazi?

18 Mbali inanso yofunika kuiganizira ikusonyeza kuti kusankha zochita pankhani ya magazi si nkhani yochepa. Iyi ndi mbali ya mmene zimene mungasankhezo zingakukhudzireni. Ngati mungavutike ndi chikumbumtima chanu chophunzitsidwa ndi Baibulo chifukwa cholandira kachigawo kakang’ono ka magazi, musachinyalanyaze chikumbumtimacho. Komanso simuyenera kupondereza chikumbumtima chanucho chabe chifukwa chakuti munthu wina wakuuzani kuti, “Palibe vuto kulandira kachigawo aka; anthu ambiri alandirapo.” Kumbukirani kuti anthu ambiri masiku ano amanyalanyaza zomwe chikumbumtima chawo chikuwauza, ndipo chimafa, n’kuwalola kuti azinama kapena kuchita zinthu zina zoipa thima lili zii. Akristu amafunika kupeŵeratu mtima wotero.​—2 Samueli 24:10; 1 Timoteo 4:1, 2.

19. Posankha zochita pankhani zachipatala zokhudza magazi, kodi chinthu chachikulu chomwe tiyenera kuchiganizira chiyenera kukhala chiyani?

19 Yankho lomwe talisindikizanso pamasamba 29-31, chakumapeto kwake likuti: “Kodi popeza kuti malingaliro ndiponso zosankha zachikumbumtima zimatha kusiyana ndiye kuti si nkhani yodetsa nkhaŵa? Iyayi. Ndi nkhanitu yaikulu.” Ndi nkhani yaikulu makamaka chifukwa chakuti ikukhudza ubwenzi wanu ndi “Mulungu wamoyo.” Ndi ubwenzi wokhawu womwe ungapezetse munthu moyo wosatha, chifukwa cha mphamvu yopulumutsa ya mwazi wokhetsedwa wa Yesu. Magazi muziwaona kuti n’ngolemekezeka kwambiri chifukwa cha mmene Mulungu akuwagwiritsira ntchito, kupulumutsa miyoyo. Paulo ananena zoona kuti: ‘Munali . . . opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m’dziko lapansi. Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Kristu.’​Aefeso 2:12, 13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 13 Panthaŵi ina Paulo ndi Akristu ena anayi anapita kukachisi kukadziyeretsa mwamwambo. Nthaŵiyi n’kuti Chilamulo chitatha ntchito, komabe Paulo anachita izi potsatira malangizo a amuna akulu a ku Yerusalemu. (Machitidwe 21:23-25) Koma n’kutheka kuti Akristu ena anaganiza kuti iwo sakanaloŵa m’kachisi kapena kuchita mwambo umenewo. Panthaŵiyo anthu anali ndi chikumbumtima chosiyanasiyana, ndipo ndi mmenenso zilili masiku ano.

^ ndime 15 Buku la Encyclopaedia Judaica limalongosola malamulo “ovuta ndiponso atsatanetsane” ofunika kutsatira kuti nyama ikhale yoyenera kudya mogwirizana ndi miyambo ya Ayuda. Limatchula mphindi zimene nyama iyenera kukhala m’madzi, mmene angaiumikire pa choyanikapo, mtundu wa mchere womwe angaipake, ndiponso maulendo amene angaitsuke m’madzi ozizira.

^ ndime 16 Nthaŵi zambiri, mankhwala enieni m’majekeseni ena kapena mankhwala ofunika kwambiri m’majekeseniwo sawatenga m’magazi. Koma nthaŵi zina mbali yochepa chabe ya mankhwalawo imatha kukhala kachigawo kakang’ono ka magazi, monga albumin.​—Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1994.

Kodi Mungakumbukire?

• Kodi Mulungu anapereka malangizo otani pankhani ya magazi kwa Nowa, Aisrayeli, ndiponso Akristu?

• Pankhani ya magazi, n’chiyani chimene Mboni za Yehova zimakaniratu kulandira?

• Kodi kulandira tizigawo ting’onoting’ono ta zigawo zikuluzikulu za magazi n’kodalira chikumbumtima cha munthu m’lingaliro lotani, koma kodi izi sizikutanthauza chiyani?

• Posankha zochita, n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira kwambiri za ubwenzi wathu ndi Mulungu?

[Mafunso]

[Tchati patsamba 22]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MMENE TIMAONERA MAGAZI

MAGAZI ATHUNTHU

ZOSALOLEKA

Maselo ofiira

Maselo oyera

Maselo othandiza magazi kuundana

Madzi a m’magazi

MKRISTU ASANKHE ZOCHITA

Tizigawo ta maselo ofiira

Tizigawo ta maselo oyera

Tizigawo ta maselo othandiza magazi kuundana

Tizigawo ta madzi a m’magazi

[Chithunzi patsamba 20]

Bungwe lolamulira linaona kuti Akristu ayenera ‘kusala mwazi’

[Chithunzi patsamba 23]

Musanyalanyaze chikumbumtima chanu ngati mukuganiza zochita pankhani yolandira kachigawo kakang’ono ka magazi