Kodi Mapemphero Anu Angasinthitse Zinthu?
Kodi Mapemphero Anu Angasinthitse Zinthu?
KODI ndani wa ife amene sanakumanepo ndi vuto lalikulu limene sakanatha kuchitapo chilichonse? Baibulo limasonyeza kuti mtumwi Paulo ankadziŵa kuti pemphero lingathe kusintha mathero a vuto lalikulu.
Paulo atatsekeredwa m’ndende popanda chifukwa ku Roma anapempha okhulupirira anzake kuti azim’pempherera, n’kupitiriza ndi kuti: “Ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.” (Ahebri 13:18, 19) Panthaŵi ina, Paulo anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Mulungu ayankha mapemphero akuti iye amasulidwe mwamsanga. (Filemoni 22) Motero, Paulo anamasulidwa mofulumira ndi kupitiriza ntchito yake yaumishonale.
Koma kodi pemphero lingasinthedi mathero a mavuto a inuyo? Mwina lingatero. Koma, kumbukirani kuti pemphero sichinthu chongochita potsatira mwambo wachipembedzo. Ndi kulankhulana ndi Atate wathu wachikondi ndiponso wamphamvu wakumwamba. Tiyenera kukhala omasuka kutchula zinthu mwachindunji m’mapemphero athu, komano kenako n’kudikira moleza mtima kuti tione mmene Yehova atiyankhire.
Mulungu sangayankhe mwachindunji pemphero lililonse, komanso sikuti nthaŵi zonse angayankhe pemphero mmene ifeyo tikufunira kapena panthaŵi yomwe tikufuna. Mwachitsanzo, Paulo anapemphera mobwerezabwereza za “munga m’thupi” mwake. Mulungu sanam’chotsere Paulo vuto lakelo. Sitikudziŵa kuti linali vuto lotani, koma Mulungu analimbikitsa Paulo pomuuza mawu aŵa: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.”—2 Akorinto 12:7-9.
Nafenso tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti ngakhale kuti Mulungu sakutichotsera vuto linalake, iye ‘angaike populumukirapo, kuti tithe kupirira.’ (1 Akorinto 10:13) Posachedwapa, Mulungu athetsa mavuto onse a anthu. Panopo, kuyang’ana kwa “Wakumva pemphero” kungasinthitse zinthu.—Salmo 65:2.