Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yolalikira Ikupita Patsogolo ku Liberia Ngakhale Kuli Nkhondo

Ntchito Yolalikira Ikupita Patsogolo ku Liberia Ngakhale Kuli Nkhondo

Ntchito Yolalikira Ikupita Patsogolo ku Liberia Ngakhale Kuli Nkhondo

NKHONDO yapachiŵeniŵeni yakhala ikuchitika ku Liberia kwa zaka zoposa khumi. Pofika m’kati mwa chaka cha 2003, zigaŵenga zinali zitaloŵa mumzinda wa Monrovia womwe ndi likulu la dzikolo. Mboni za Yehova zambiri zinakakamizika kuthaŵa m’nyumba zawo, ndipo nthaŵi zina zimenezi zinachitika mobwerezabwereza. Katundu anali kulandidwa kaŵirikaŵiri.

N’zomvetsa chisoni kuti pa kumenyana kumene kunachitika mu likulu la dzikolo, anthu zikwi zambiri anaphedwa. Mwa anthu amene anaphedwawo panali Mboni ziŵiri, mbale ndi mlongo. Kodi abale ena anatani ndi mavuto oterowo, ndipo n’chiyani chinachitika pofuna kuwathandiza abale amene anali pa mavutowo?

Kuthandiza Anthu Ofunika Thandizo

M’nthaŵi yonse ya mavutoyi, nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Liberia inakonza zothandiza anthu amene anafunikira thandizo. Inali kupereka chakudya, zinthu zofunika panyumba, ndi mankhwala. Panthaŵi imene zigaŵenga zinalanda mbali ya ku doko, chakudya chinayamba kusoŵa. Nthambiyi inaoneratu zimenezo ndipo inasungiratu zinthu zofunika kuti ithandizire Mboni za Yehova zokwana 2,000 zimene zinathaŵira ku Nyumba za Ufumu za mu mzinda wonsewo. Abale anali kugaŵa chakudyacho moti chinakwanira mpaka pamene dokolo analitsegula. Nthambi za ku Belgium ndi ku Sierra Leone zinapititsa mankhwala pa ndege, pamene nthambi za ku Britain ndi ku France zinatumiza zovala.

Ngakhale kuti anali m’mavuto, abale athuwo sanataye mtima ndipo anali osangalala. Zimene ananena mbale wina amene anathaŵa kwawo katatu, zikuimira mmene enanso ambiri akuonera zinthu. Iye anati: “Zimene zikuchitikazi ndi zimene tikulalikira; tikukhala m’masiku otsiriza.”

Kumvetsera Uthenga Wabwino

Ngakhale kuti m’dziko lonselo muli chisokonezo, Mboni zikupitiriza kupeza zotsatira zabwino m’munda. Panali chiŵerengero chapamwamba kuposa china chilichonse cha ofalitsa Ufumu okwana 3,879 mu January, 2003, ndipo mu February anachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba okwana 15,227.

Anthu akumvetsera uthenga wabwino mofulumira. Chitsanzo cha zimenezi ndi zimene zinachitika m’mudzi wina kummwera chakummaŵa kwa dzikolo. Mpingo wina unakonza zochita Chikumbutso cha Imfa ya Kristu m’mudzi wina waukulu wotchedwa Bewahn, womwe uli pa mtunda woyenda maola asanu kuchokera pamalo amene amasonkhanira nthaŵi zonse. Abalewo asanapite kumudziko kukaitana anthu kuti afike pa Chikumbutso, anapatsa mfumu ya m’mudzimo pepala loitanira anthu ku Chikumbutso. Mfumuyo italandira, inatenga Baibulo lake, n’kupita kwa anthu a m’mudzimo, ndipo inaŵerenga lemba limene linasonyezedwa pa pepala loitaniralo, n’kuwalimbikitsa anthuwo kuti akapezeke pa Chikumbutsopo. Motero, pamene ofalitsawo amafika, anapeza kuti ntchito yawo anali atawachitira kale. Mfumuyo pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake aŵiri, anafika pa Chikumbutsocho. Onse amene anapezekapo anali 27. Kuyambira nthaŵi imeneyo, mfumuyo inachoka m’chipembedzo cha Methodist n’kuyamba kuphunzira ndi Mboni, ndipo inapereka malo oti pamangidwe Nyumba ya Ufumu.

Kusintha Maganizo

Khalidwe la abale athu lathandizanso kwambiri kusintha mmene anthu ena otsutsa ankaonera choonadi. Taonani chitsanzo cha munthu wina wotchedwa Opoku. Mpainiya wina wapadera anakumana naye mu utumiki wakumunda ndipo anam’patsa magazini ya Nsanja ya Olonda. Opoku anachita chidwi ndi nkhani ina imene inali m’magaziniyo koma analibe ndalama. Atafotokoza kuti inalibe mtengo, mpainiyayo anampatsa magaziniyo ndipo anakonza zoti adzacheze nayenso ulendo wina. Pa ulendo wobwerezawo, Opoku anafunsa mpainiyayo kuti: “Kodi umandidziŵa? Ambiri mwa anthu a m’gulu lanu a m’tauni ya Harper amandidziŵa. Ndinkakonda kuchotsa sukulu ana a Mboni.” Ndiyeno anafotokoza kuti anali mkulu wa pa sukulu ina ya sekondale m’tauniyo ndipo anali kuzunza ana a Mboni za Yehova chifukwa chosachitira sawatcha mbendera.

Komabe, zitsanzo zitatu zimene Opoku anaona zosonyeza chikondi chachikristu chimene Mboni za Yehova zimaonetsa, zinamuchititsa kuganiziranso bwino mmene amaonera Mboni. Choyamba, iye anaona Mboni zikusamalira mbale wawo wauzimu amene anali kudwala mwakayakaya. Mbonizo mpaka zinakonza zoti mbale wawoyo akalandire chithandizo ku dziko lakunja loyandikana nalo. Opoku ankaganiza kuti amene anali kudwalayo anali “munthu waudindo waukulu” pa gulu la Mbonizo koma anamva kuti anali Mboni wamba. Chachiŵiri, m’zaka za m’ma 1990, Opoku anali ku Côte d’Ivoire monga wothaŵa kwawo. Tsiku lina ali ndi ludzu, anapita kukagula madzi kwa mnyamata wina. Opoku anali ndi ndalama yaikulu yokha basi, ndipo mnyamatayo analibe ndalama zoti asinthe ndalama yaikuluyo, motero anangom’patsa Opoku madziwo kwaulere. Atam’patsa madziwo, mnyamatayo anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti idzafika nthaŵi imene anthu ngati ine ndi inu tidzapatsana zinthu popanda kulipiritsana?” Opoku anaganiza kuti anali wa Mboni za Yehova, ndipo mnyamatayo anavomera. Kuwoloŵa manja ndi kukoma mtima kwa mbale ameneyu kunamuchititsa chidwi Opoku. Ndiyeno pomaliza, zimene mpainiya wapaderayo anachita pom’patsa magazini kwaulere zinam’patsa Opoku umboni wokwanira woti anali kuziona Mboni molakwika ndipo anafunika kusintha. Anapita patsogolo mwauzimu ndipo tsopano ndi wofalitsa wosabatizidwa.

Ngakhale kuti abale ku Liberia akukumanabe ndi mavuto adzaoneni, akukhulupirira Mulungu ndipo akulengeza mokhulupirika uthenga wabwino woti zinthu zidzakhala bwino mu Ufumu wa Mulungu wachilungamo. Yehova sadzaiŵala ntchito yawo yaikulu imene akuchita ndi chikondi chimene amachisonyeza pa dzina lake.​—Ahebri 6:10.

[Mapu patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MONROVIA

[Zithunzi patsamba 31]

M’nthaŵi zamavuto, anthu a Yehova amapereka thandizo la zinthu zofunika pamoyo ndi lauzimu kwa anthu amene akufunikira thandizolo