Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Poti Alevi analibe choloŵa mu Israyeli wakale, kodi Hanameli yemwe anali Mlevi anagulitsa bwanji munda kwa msuweni wake Yeremiya yemwenso anali Mlevi, malinga ndi zimene zili pa Yeremiya 32:7?
Ponena za Alevi, Yehova anauza Aroni kuti: “Ulibe choloŵa m’dziko lawo, ulibe gawo pakati pawo [pa Aisrayeli].” (Numeri 18:20) Komabe, Alevi anapatsidwa midzi 48 pamodzi ndi mabusa ake, imene inali kupezeka m’Dziko lonse Lolonjezedwa. Kwawo kwa Yeremiya kunali ku Anatoti, umodzi wa midzi yomwe “ana a Aroni, ansembe,” anapatsidwa.—Yoswa 21:13-19; Numeri 35:1-8; 1 Mbiri 6:54, 60.
Pa Levitiko 25:32-34, timaona kuti Yehova anapereka malangizo osapita m’mbali okhudza mphamvu zowombola malo a Alevi. Zikuoneka kuti mabanja achilevi pawokhapawokha ankatha kugwiritsa ntchito ufulu umene munthu ankakhala nawo akalandira choloŵa, wokhudza kukhala ndi malo enaake, kuwagwiritsa ntchito kwake, ndiponso kuwagulitsa. Izi mwachidziŵikire zinkaphatikizapo kugulitsa ndi kuwombola malo. * Nthaŵi zambiri, Alevi ankakhala ndi malo ndiponso kuwagwiritsa ntchito m’njira zofanana ndi mmene Aisrayeli a mafuko ena ankachitira.
Mwachionekere, malo omwe Aleviwo ankakhala nawo ankawapeza mwa choloŵa cha banja. Koma pankhani ‘yokhoza kuwawombola,’ izo zinkaloledwa pakati pa Alevi okhaokha. Komanso zikuoneka kuti ankawombola ndi kugulitsa malo okhawo a m’kati mwa midzi, chifukwa chakuti “dambo la podyera pawo” silinkayenera kugulitsidwa popeza kuti linkakhala “lawolawo kosatha.”—Levitiko 25:32, 34.
Motero munda womwe Yeremiya anawombola kwa Hanameli ukuoneka kuti unali wotero moti ukanatha kukhala wa munthu wina mwa kuuwombola. N’kutheka kuti unali m’kati mwa mudzi. Yehova anasonyeza kuti “munda” womwe tikukambiranawu unalidi wa Hanameli ndi kuti Yeremiya anali ndi “mphamvu yakuombola.” (Yeremiya 32:6, 7) Yehova anagwiritsa ntchito malonda ameneŵa monga chizindikiro chotsimikizira lonjezo lake lakuti Aisrayeli adzakhalanso ndi malo amene anali choloŵa chawo nthaŵi ya ukapolo wa ku Babulo ikadzatha.—Yeremiya 32:13-15.
Palibe chilichonse chomwe chikusonyeza kuti Hanameli anapeza malo mu Anatoti m’njira yolakwika. Palibe chomwe chikusonyeza kuti anaswa lamulo la Yehova pouza Yeremiya kuti agule munda wa ku Anatotiwu kapenanso kuti Yeremiya sanagwiritse ntchito bwino mphamvu yake ya kuwombola katundu pogula mundawu.—Yeremiya 32:8-15.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Barnaba yemwe anali Mlevi anagulitsa malo ake ndi kupereka ndalama zake kuti zithandize otsatira a Kristu okhala ku Yerusalemu omwe ankafunika chithandizo. Mwina maloŵa anali ku Palestina kapena ku Kupro. Kapenanso mwina anali malo omwe ankafuna kuti adzakhale manda ake omwe Barnaba anagula mu Yerusalemu.—Machitidwe 4:34-37.