Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Wokhutira ndi Zimene Mulungu Wandipatsa Kwandithandiza

Kukhala Wokhutira ndi Zimene Mulungu Wandipatsa Kwandithandiza

Mbiri ya Moyo Wanga

Kukhala Wokhutira ndi Zimene Mulungu Wandipatsa Kwandithandiza

YOSIMBIDWA NDI BENJAMIN IKECHUKWU OSUEKE

N’tangoyamba utumiki wanthaŵi zonse ndinapita ku nyumba ya makolo anga. Bambo anga atangondiona, anandigwira malaya ndi kuyamba kukuwa kuti, “Wakuba!” Iwo anatenga chikwanje ndi kundimenya nacho m’mbali mwake. Atamva phokoso, anthu ena a pamudzi anafika panyumba yathu. Kodi ndinali n’taba chiyani? Tandilolani ndifotokoze.

NDINABADWA mu 1930 pamudzi wa Umuariam kummwera koma chakum’maŵa kwa Nigeria, ndipo ndinali woyamba pa ana asanu ndi aŵiri. Yemwe anali wamkulu pa azichemwali anga anamwalira ali ndi zaka 13. Makolo anga anali achipembedzo cha Anglican. Bambo anga anali mlimi, ndipo mayi anali kuchita bizinesi yaing’ono. Ankayenda wapansi makilomita pafupifupi 30 kuchoka pamudzi wathu kupita ku misika ya m’deralo kukagula chidebe cha mafuta a mtengo wa mgwalangwa ndipo ankabwerako tsiku lomwelo madzulo. Ndiyeno, tsiku lotsatira m’maŵa kwambiri, ankayenda makilomita pafupifupi 40 kupita ku tauni yomwe inali ndi siteshoni ya sitima kukagulitsa mafutawo. Ngati apeza phindu, nthaŵi zambiri silinali kupitirira masenti 15 (U.S.), anali kugulira banja chakudya ndipo ankabwerako tsiku lomwelo. Anachita zimenezi kwa zaka pafupifupi 15 mpaka pamene anamwalira mu 1950.

Ndinayamba maphunziro anga m’mudzi wathu pa sukulu yomwe inkayendetsedwa ndi a Tchalitchi cha Anglican, koma kuti ndimalize maphunziro a pulayimale, ndinapeza nyumba ya lendi yomwe inali makilomita pafupifupi 35 kuchoka kumudzi kwathu. Popeza makolo anga analibe ndalama zopititsira maphunziro anga patsogolo, ndinayamba kufunafuna ntchito. Poyamba ndinagwira ntchito m’nyumba ya mlonda wa pakampani ya sitima ku Lagos, kumadzulo kwa Nigeria, kenako kwa mwamuna wina wogwira ntchito m’boma mu mzinda wa Kaduna, kumpoto kwa Nigeria. Mu mzinda wa Benin, kumadzulo chapakati pa dziko la Nigeria, ndinapeza ntchito ya ukalaliki kwa loya wina, ndipo patapita kanthaŵi ndinakagwira ntchito monga lebala pa kampani yocheka matabwa. Mu 1953 n’tachoka kumeneko, ndinapita ku Cameroon kukakhala ndi msuweni wanga amene anandithandiza kupeza ntchito pa munda wa mitengo ya mphira. Malipiro anga pamwezi anali pafupifupi madola 9 (U.S.). Ndinkapeza ntchito wamba zokhazokha, koma ndinali wokhutira malinga ndinkapeza chakudya chokwanira.

Munthu Wosauka Kwambiri Anandipatsa Chuma Chauzimu

Silvanus Okemiri, mnzanga wa kuntchito, anali wa Mboni za Yehova. Iye anagwiritsa ntchito mpata uliwonse kundiuza zimene anali kudziŵa m’Baibulo pamene tinali kumweta udzu ndi kuphimbira mitengo ya mphira. Ngakhale kuti ndinkamvetsera, sindinachitepo kanthu panthaŵiyo. Komabe, msuweni wanga atadziŵa kuti ndinkacheza ndi Mboni, anayesetsa kwambiri kundiletsa. Iye anandichenjeza kuti: “Benji, usamacheze ndi a Okemiri. Amakhulupirira Yehova ndipo ngosauka kwambiri. Aliyense amene akuyanjana nawo adzakhala ngati iwo.”

Kumayambiriro kwa 1954, ndinabwerera ku nyumba chifukwa ndinalephera kupirira kagwiridwe ka ntchito kozunza kwambiri. M’masiku amenewo a Tchalitchi cha Anglican anali kutsatira kwambiri miyezo ya makhalidwe abwino. Ndinkada kwambiri makhalidwe oipa pamene ndinkakula. Koma sipanapite nthaŵi yaitali, ndinali kuipidwa kwambiri ndi chinyengo cha omwe ndinkaloŵa nawo tchalitchi. Ngakhale ankanena kuti amatsatira kwambiri makhalidwe abwino a m’Baibulo, zochita zawo zinkatsutsana ndi zimene ankanena. (Mateyu 15:8) Nthaŵi zambiri ndinali kukangana ndi bambo anga, zimene zinachititsa kuti ubale wathu usokonekere. Usiku wina ndinangochoka panyumba.

Ndinasamukira ku Omoba, tauni yaing’ono imene ili ndi siteshoni ya sitima. Kumeneku ndinapezananso ndi Mboni za Yehova. Priscilla Isiocha, yemwe ndinkadziŵana naye kumudzi, anandipatsa timabuku ta “This Good News of the Kingdom” ndi After Armageddon​—God’s New World. * Ndinatiŵerenga ndi mtima wonse, ndikutsimikiza kuti ndapeza choonadi. Ku tchalitchi changa sitinali kuphunzira Baibulo; tinali kuumirira miyambo ya anthu. Koma mabuku a Mboni nthaŵi zambiri amagwira mawu Baibulo.

Mwezi usanathe, ndinafunsa Mbale ndi Mlongo Isiocha za nthaŵi imene amapita ku tchalitchi chawo. Pamene ndinapezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova nthaŵi yoyamba, sindinamve kanthu. Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda inali kunena za kuukira kwa ‘Gogi wa Magogi’ wotchulidwa mu buku laulosi la Ezekieli. (Ezekieli 38:1, 2) Mawu ambiri anali achilendo kwa ine, koma ndinasangalala kwambiri chifukwa anandilandira bwino kwambiri moti ndinaganiza kubwererako Lamlungu lotsatira. Pamsonkhano wachiŵiri, ndinamva za kulalikira. Chotero ndinafunsa Priscilla za tsiku limene amakalalikira. Pa Lamlungu lachitatu, ndinapita nawo, n’tanyamula Baibulo laling’ono. Ndinalibe chikwama chogwiritsa ntchito polalikira kapena mabuku alionse ofotokoza Baibulo. Komabe, ndinakhala wofalitsa Ufumu ndipo pamapeto pamwezi umenewo ndinapereka lipoti la utumiki wa kumunda.

Palibe amene anaphunzira nane Baibulo, koma nthaŵi iliyonse ndikachezera banja la a Isiocha, ndinali kuphunzira mawu achikhulupiriro ndiponso olimbikitsa ochokera m’Malemba komanso kutengako mabuku ena ofotokoza Baibulo. Pa December 11, 1954, pamsonkhano wachigawo mu mzinda wa Aba, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi. Msuweni wanga amene ndinkakhala naye ndipo yemwe ankandiphunzitsa ntchito anasiya kundipatsa chakudya ndiponso kundiphunzitsa ndipo sanandilipire ndalama iliyonse pa ntchito imene ndinagwira. Koma sindinam’sungire kanthu kukhosi; ndinangoyamikira kuti ndinali paubwenzi ndi Mulungu. Zimenezi zinandipatsa chitonthozo ndi mtendere wa maganizo. Mboni za m’derali zinandithandiza. Banja la a Isiocha linandipatsa chakudya, ndipo ena anandikongoza ndalama zoyambira bizinesi yaing’ono. Pakati pa 1955, ndinagula njinga yakapalasa yogwiritsidwapo kale ntchito, ndipo m’March 1956, ndinayamba ntchito ya upainiya wokhazikika. Patapita kanthaŵi, ndinabweza ngongole zanga. Phindu lomwe ndinkapeza pa bizinesi linali lochepa kwambiri, koma ndinkatha kudzisamalira. Zinthu zimene Yehova anali kupereka zinali zondikwanira.

“Kuba” Azichimwene ndi Azichemwali Anga

N’tangokhala ndi nyumba yanga, nkhaŵa yanga yoyamba inali kuthandiza azichimwene ndi azichemwali anga mwauzimu. Bambo anatsutsa kwambiri kukhala kwanga Mboni chifukwa anali ndi tsankhu ndiponso wokayikira kwambiri zochita za ena. Chotero, ndikanawathandiza bwanji azibale angaŵa kuphunzira choonadi cha Baibulo? Ndinapempha kuti ndizithandiza mng’ono wanga Ernest, ndipo bambo anam’lola kuti azikhala nane. Mwamsanga Ernest anaphunzira choonadi ndipo anabatizidwa mu 1956. Kusintha kwake kunachititsa bambo kukhala wotsutsa kwambiri. Ngakhale zinali choncho, mchemwali wanga amene anali wokwatiwa nayenso anaphunzira choonadi limodzi ndi mwamuna wake. Pamene ndinalinganiza kuti mchemwali wanga wachiŵiri, Felicia, adzakhale nane akatsekera sukulu, bambo anavomera monyinyirika. Sipanapite nthaŵi kwambiri, Felicia nayenso anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova.

Mu 1959, ndinapita ku nyumba kukatenga Bernice, mchemwali wanga wachitatu kuti adzakhale ndi Ernest. Imeneyi inali nthaŵi yomwe bambo anandigwira, kundiimba mlandu woba ana awo. Iwo sanathe kumvetsa kuti ana awo anasankha okha kutumikira Yehova. Bambo analumbira kuti sadzandilola kutenga Bernice. Koma dzanja la Yehova linathandiza chifukwa chaka chomwe chinatsatira, Bernice atatsekera sukulu anabwera kudzakhala ndi Ernest. Mofanana ndi alongo ake, iyenso anaphunzira choonadi ndipo anabatizidwa.

‘Kuphunzira Chinsinsi’

Mu September 1957, ndinayamba kutumikira monga mpainiya wapadera, kuthera maola pafupifupi 150 mwezi uliwonse m’ntchito yolalikira. Ineyo ndi Sunday Irogbelachi, yemwe ndinkagwira naye ntchitoyi tinatumikira gawo lalikulu mu mzinda wa Akpu-na-abuo ku Etche. Pa msonkhano wadera woyamba womwe tinapezekapo tili komweko, anthu 13 ochokera ku gulu lathu anabatizidwa. Ndifetu osangalala kwambiri tsopano kuona mipingo 20 m’dera limeneli!

Mu 1958, ndinadziŵana ndi Christiana Azuike, mpainiya wokhazikika yemwe anali kusonkhana ndi mpingo wa Aba East. Changu chake chinandisangalatsa kwambiri ndipo mu December chaka chomwecho tinakwatirana. Kumayambiriro a 1959, ndinaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda, kuchezera ndi kulimbikitsa mipingo ya abale athu auzimu. Kuchokera nthaŵi imeneyo mpaka 1972, ine ndi mkazi wanga tinachezera pafupifupi mipingo yonse ya anthu a Yehova kum’maŵa ndiponso kumadzulo chapakati pa dziko la Nigeria.

Mipingo inali patalipatali ndipo njinga yakapalasa ndi yomwe tinkagwiritsa ntchito kwambiri kuyendera. Pamene tinali kutumikira mipingo mu matauni akuluakulu, abale athu anali kuchita hayala takisi kutipititsa ku mpingo wotsatira. Nthaŵi zina zipinda zomwe tinali kukhalamo zinali zozira ndipo zopanda siling’i. Tinkagona pa mabedi opangidwa ndi mitengo ya mgwalangwa. Mabedi ena anali ndi matiresi audzu okhutidwa ndi mphasa; ena analibe matiresi n’komwe. Kuchuluka ndiponso kukoma kwa chakudya silinali vuto kwa ife. Popeza tinali titaphunzira kale m’mbuyomu kukhala wokhutira ndi zinthu zochepa, tinakonda chakudya chilichonse chimene anatikonzera, ndipo eninyumba anayamikira zimenezi. Mu masiku ameneŵa mizinda ina inalibe magetsi, chotero nthaŵi zonse tinkanyamula nyali yathu yamafuta a palafini. Komabe, mosasamala za mikhalidwe yovuta, nthaŵi zambiri tinali kusangalala kwambiri ndi mipingo.

M’zaka zimenezi, tinazindikira kufunika kwa malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:8) Chifukwa chokumana ndi mavuto, Paulo anaphunzira chinsinsi chimene chinam’thandiza kukhala wokhutira. Kodi chinali chiyani? Iye anafotokoza kuti: “Ndadziŵa ngakhale kupeputsidwa, ndadziŵanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo [“ndaphunzira chinsinsi,” NW] wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa.” Tinaphunzira chinsinsi chofananacho. Paulo ananenanso kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye [Mulungu] wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:12, 13) Mawu ameneŵa anakhaladi oona kwa ife! Tinali okhutira, tinali ndi zochita zolimbikitsa zokwanira zachikristu ndiponso mtendere wa maganizo.

Kutumikira Mipingo Pamodzi ndi Banja

Kumapeto kwa 1959, mwana wathu woyamba, Joel, anabadwa ndipo mu 1962, tinakhala ndi wachiŵiri, Samuel. Ineyo ndi Christiana tinapitiriza m’ntchito yoyendayenda, kuchezera mipingo limodzi ndi anyamata athu. Mu 1967, nkhondo yachiŵeniŵeni inayamba mwadzidzidzi m’dziko la Nigeria. Sukulu zinatsekedwa chifukwa cha kuwombera kosaleka kwa ndege zankhondo. Mkazi wanga anali mphunzitsi asanayambe kugwira nane ntchito yoyendayenda, chotero pamene nkhondo inali m’kati, anaphunzitsa ana panyumba. Atafika zaka zisanu ndi chimodzi, Samuel anadziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Pamene anayamba sukulu nkhondo itatha, anali patsogolo pa anzake ndi makalasi aŵiri.

Panthaŵi imeneyo sitinadziŵe kwenikweni mavuto akulera ana uku tili m’ntchito yoyendayenda. Komabe, atatiuza kukatumikira monga apainiya apadera mu 1972 zinakhala zothandiza kwa ife. Zimenezi zinachititsa kuti tikhale malo amodzi kotero kuti tithe kusamalira bwino moyo wauzimu wa banja lathu. Ana athu ali aang’ono tinawaphunzitsa kufunika kokhala wokhutira ndi zimene Mulungu watipatsa. Mu 1973, Samuel anabatizidwa ndipo Joel anayamba upainiya wokhazikika chaka chomwecho. Ana athu onse aŵiri anakwatira akazi achikristu ochita bwino mwauzimu ndipo tsopano akusamalira mabanja awo mu choonadi.

Kuipa kwa Nkhondo Yachiŵeniŵeni

Pamene nkhondo yachiŵeniŵeni inayamba, ndinali kutumikira mpingo mu mzinda wa Onitsha monga woyang’anira dera, limodzi ndi banja langa. Nkhondo imeneyinso inatisonyeza kwambiri kupanda pake kokhala ndi katundu wambiri kapena kudalira katundu. Ndinaona anthu akuthaŵa kuti apulumutse miyoyo yawo n’kusiya katundu wawo wamtengo wapatali mu misewu.

Pamene nkhondo inakula, amuna olimba onse analembedwa usilikali. Abale ambiri amene anakana kulembetsa anazunzidwa. Sitinali kuyenda momasuka. Kusoŵa kwa chakudya kunachititsa chipwirikiti m’dziko. Mtengo wa magalamu 500 a chinangwa unakwera kuchoka pa masenti 7 kufika pa madola 14 (U.S.) ndipo wa kapu ya mchere unakwera kuchoka pa madola 8 kufika pa madola 42 (U.S.). Mkaka, bata ndi shuga zinasiya kuoneka. Kuti tikhale ndi moyo tinali kusinja mapapaya osapsa ndi kuwasanganiza ndi ufa wachinangwa pang’ono. Tinali kudyanso ziwala, makoko achinangwa, masamba a hibiscus ndi nsenjere ndiponso masamba alionse amene tinkapeza. Nyama inali yodula kwambiri chotero tinkagwira abuluzi kuti ana azidya. Komabe, ngakhale zinthu zinaipa bwanji, Yehova anatisamalira nthaŵi zonse.

Komabe, kusoŵa chakudya chauzimu kunali chinthu choopsa kwambiri chimene nkhondo inachititsa. Abale ambiri anathaŵira ku nkhalango kuchoka kudera kumene kunali nkhondo kapena kuthaŵira ku midzi ina, ndipo pochita zimenezi anasoŵetsa mabuku awo ofotokoza Baibulo ambiri ndipo mwina onse. Ndiponso, asilikali aboma amene anatseka misewu anachititsa kuti mabuku atsopano ofotokoza Baibulo asaloŵe mu dera la Biafra. Ngakhale kuti mipingo yambiri inayesa kuchita misonkhano, abale anavutika mwauzimu chifukwa malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi sanali kuwafika.

Kulimbana ndi Njala Yauzimu

Oyang’anira oyendayenda anayesetsa kwambiri kupitiriza makonzedwe ochezera mpingo uliwonse. Popeza abale ambiri anali atathaŵa m’matauni, ndinakawafunafuna kulikonse kumene akanapezeka. Panthaŵi ina, ndinasiya mkazi wanga ndi ana pamalo osungika ndipo ndinayenda ndekha kwa milungu isanu ndi umodzi, kupita midzi yosiyanasiyana ndiponso mbali zina za nkhalango kufunafuna abale.

Pamene ndinali kutumikira mpingo mu mzinda wa Ogbunka, ndinamva kuti Mboni zambiri zinali m’dera la Isuochi m’chigawo cha Okigwe. Chotero, ndinapempha wina kuti auze abale a m’deralo kukumana pa munda wa mtedza wa mkolosa ku mudzi wa Umuaku. Ineyo ndi mbale wina wachikulire tinapalasa njinga zathu makilomita pafupifupi 15 kupita ku mundawu kumene Mboni pafupifupi 200 kuphatikizapo akazi ndi ana zinasonkhana. Chifukwa chothandizidwa ndi mlongo wina amene anali mpainiya, ndinatha kupeza gulu lina la Mboni pafupifupi 100, zimene zinabisala m’nkhalango ya Lomara.

Lawrence Ugwuegbu anali mmodzi wa abale olimba mtima okhala mu tauni yosakazidwa ndi nkhondo ya Owerri. Iye anandiuza kuti m’dera la Ohaji munali Mboni zambiri. Izo sizinali kuyenda momasuka chifukwa asilikali anali m’dera limenelo. Aŵirife tinapita komweko usiku panjinga ndipo tinakumana ndi Mboni pafupifupi 120 mu mpanda wa mbale. Tinagwiritsanso ntchito mpata umenewu kuchezera Mboni zina zimene zinali m’malo awo obisika.

Mbale Isaac Nwagwu anaika moyo wake pangozi kundithandiza kupeza abale ena omwe anali atathaŵa kwawo. Anandiolotsa mtsinje wa Otamiri m’bwato kukakumana ndi Mboni zoposa 150 zomwe zinasonkhana mu mudzi wa Egbu-Etche. Mbale wina kumeneku anafuula kuti: “Lero ndi tsiku labwino koposa pamoyo wanga! Sindinkaganiza kuti ndidzatha kuonananso ndi woyang’anira dera. Ngati ndingamwalire tsopano pamene nkhondoyi ikuchitika, ndine wokhutira.”

Ndinali pangozi yolembedwa usilikali, koma nthaŵi zambiri Yehova ankanditeteza. Tsiku lina madzulo, n’tamaliza kukumana ndi abale pafupifupi 250, pamene ndinkabwerera kumene ndinali kukhala, gulu la asilikali linandiimitsa pamalo ofufuzira a pamsewu. Iwo anandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani sunaloŵe usilikali?” Ndinawauza kuti ndine mmishonale wolalikira Ufumu wa Mulungu. Ndinazindikira kuti atsimikiza mtima kundimanga. N’tapemphera mwamsanga cha m’mtima, ndinati kwa mkulu wawo: “Ndisiyeni ndizipita.” Modabwitsa kwambiri, anandiyankha kuti: “Kodi ukuti tikusiye?” “Inde, ndisiyeni,” ndinayankha motero. Iye anati: “Zipita.” Palibe msilikali ananena mawu ena.​—Salmo 65:1, 2.

Kukhala Wokhutira Kubweretsa Madalitso Ena

Nkhondo itatha mu 1970, ndinapitiriza kutumikira m’ntchito yadera. Unali mwayi kuthandiza kukonzanso mipingo. Ndiyeno, ineyo ndi Christiana tinatumikira monga apainiya apadera mpaka 1976, pamene ndinaikidwanso kukhala woyang’anira dera. Chapakati pa chaka chimenechi, ndinapatsidwa ntchito yachigawo. Zaka zisanu ndi ziŵiri zitapita, ine ndi mkazi wanga tinapemphedwa kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Nigeria, kumene tikukhala tsopano. Kuno ku nthambi, nthaŵi zonse timasangalala kwambiri kuonanso abale ndi alongo amene tinkakumana nawo panthaŵi yankhondo yachiŵeniŵeni ndiponso panthaŵi zina, amene akutumikirabe Yehova mokhulupirika.

Pa zaka zapitazi, Christiana wakhala wochirikiza ndiponso wokhulupirika kwambiri kwa ine. Kukhala kwake ndi maganizo abwino ndiponso kulimba mtima, mosasamala za kudwaladwala kumene wapirira kuyambira mu 1978, kwandithandiza kuti ndipitirizebe kuchita ntchito yanga. Mawu a wamasalmo akuti: “Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira,” akhala oona kwa ife.​—Salmo 41:3.

Ndikayang’ana m’mbuyo pa zaka zimenezi zotumikira Mulungu, sindingachitire mwina koma kuyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha madalitso ake osangalatsa. Chifukwa chokhala wokhutira ndi zimene amapatsa, ndinganene mosakayikira kuti ndapeza chimwemwe chachikulu. Chimwemwe choona azichemwali ndi azichimwene anga, ana anga ndiponso mabanja awo, onse akutumikira Yehova limodzi nane ndi mkazi wanga ndi dalitso losayerekezeka. Yehova wandipatsa moyo wabwino ndiponso watanthauzo. Palibe zokhumba zanga zimene sizinakwaniritsidwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Tofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Tsopano sitikusindikizidwanso.

[Bokosi patsamba 27]

Makonzedwe Apanthaŵi Yake Athandiza Kulimbikitsa Abale

Chapakati pa m’ma 1960, chidani pakati pa mafuko a kumpoto ndi kum’maŵa kwa Nigeria chinachititsa msokonezo, kuukirana, chipwirikiti ndi chiwawa. Zochitika zimenezi zinabweretsera mavuto Mboni za Yehova, zimene zinali zotsimikiza kwambiri kusaloŵerera m’mikangano. Mboni pafupifupi 20 zinaphedwa. Zambiri zinatayikidwa katundu wawo yense.

Pa May 30, 1967, zigawo za kum’maŵa kwa Nigeria zinachoka mu boma la mgwirizano wa mayiko angapo ndipo zinapanga boma la Biafra. Asilikali aboma anapatsidwa malangizo okonzekera kuchita nkhondo ndipo anthu ochokera ku Biafra sanali kuloledwa m’zigawo zina. Nkhondo yachiŵeniŵeni yokhetsa mwazi ndiponso yachiwawa kwambiri inayamba.

Kusaloŵerera m’nkhondo kwa Mboni za Yehova zomwe zinali m’dera la Biafra kunapangitsa kuti zivutike. Mu nyuzipepala munkakhala ndemanga zoipa, zolimbikitsa anthu kuti azida Mboni. Koma Yehova anatsimikiza kuti atumiki ake akulandira chakudya chauzimu. Motani?

Kumayambiriro a 1968, mwamuna wina wogwira ntchito m’boma anapatsidwa ofesi ku Ulaya ndipo winanso anapatsidwa ofesi pa bwalo la ndege ku Biafra. Aŵiri onseŵa anali Mboni. Abale a ku Biafra ankadziŵa zochitika ku mayiko ena chifukwa cha abale aŵiri ameneŵa. Mboni ziŵirizi zinadzipereka kuchita ntchito yoopsa yoloŵetsa chakudya chauzimu ku Biafra. Izo zinathandizanso kupereka kwa anthu ovutika katundu wa chithandizo. Abale aŵiriŵa anayendetsa makonzedwe ofunika ameneŵa nthaŵi yonse ya nkhondoyo, imene inatha mu 1970. Mmodzi wa iwo panthaŵi ina anati, “Makonzedwe ameneŵa anali oposa chilichonse chimene anthu akanalinganiza.”

[Chithunzi patsamba 23]

Mu 1956

[Chithunzi patsamba 25]

Mu 1965, tili ndi ana athu, Joel ndi Samuel

[Chithunzi patsamba 26]

Ndi dalitsotu kutumikira Yehova monga banja!

[Chithunzi patsamba 27]

Lero, ineyo ndi Christiana tikutumikira pa nthambi ya ku Nigeria