Kodi Mungadalire Malonjezo a Ndani?
Kodi Mungadalire Malonjezo a Ndani?
“MALONJEZO ake anali amphamvu, monga momwe iye analili panthaŵiyo; koma palibe chimene anachitapo, monga mmene iye alili panopa, wopanda ntchito,” linatero buku lakuti King Henry the Eighth, la William Shakespeare.
Malonjezo amphamvu amene Shakespeare anali kunena anali a kadinala wachingelezi, Thomas Wolsey, amene anali wamphamvu kwambiri m’zandale ku England cha m’ma 1500. Ena anganene kuti zimene Shakespeare ananena zikufanananso ndi malonjezo ambiri amene amawamva masiku ano. Kaŵirikaŵiri, anthu amawalonjeza zinthu zambiri koma amawachitira zinthu zochepa. Choncho, sikovuta kumvetsa chifukwa chake amakayikira malonjezo aliwonse.
Kugwiritsidwa Mwala Kwachuluka
Mwachitsanzo, panthaŵi ya nkhondo yoopsa kwambiri ku Balkans cha m’ma 1990, nthambi ya zachitetezo ya bungwe la United Nations inalengeza kuti tauni ya Srebrenica, ku Bosnia, ikhala “malo abata.” Kwa mamembala a bungwe lapadziko lonse limeneli, lonjezoli linaoneka kuti ndi lodalirika. Asilamu ambiri amene anathaŵira ku Srebrenica anaganizanso chimodzimodzi. Koma mapeto ake, lonjezo lakuti tauniyi ikhala malo abata silinakwaniritsidwe n’komwe. (Salmo 146:3) Mu July 1995, zigaŵenga zinangothamangitsa asilikali a United Nations ndi kulanda tauniyo. Asilamu oposa 6,000 anathaŵa, ndipo Asilamu wamba 1,200 anaphedwa.
Kusakwaniritsa malonjezo ndi kofala pazochitika zambiri pamoyo wathu. Anthu amanyengedwa “kambirimbiri ndi anthu onama otsatsa malonda” amene alipo masiku ano. Amakhumudwa ndi “kusakwaniritsidwa kwa malonjezo amene anthu ambiri andale amapanga pochita misonkhano yawo yokopa anthu.” (The New Encyclopædia Britannica, Voliyumu 15, tsamba 37) Atsogoleri achipembedzo odalirika amene amalonjeza kuti asamalira nkhosa zawo amazizunza moipa kwambiri. Ngakhale pantchito monga zamaphunziro ndi zachipatala—zimene zimafunika kusonyeza chifundo ndi kudera nkhaŵa ena—anthu ena akhala osadalirika ndipo adyera masiku pamutu kapena kupha kumene anthu amene anali kuwasamalira. M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti tisakhulupirire mawu onse.—Miyambo 14:15.
Malonjezo Amene Amakwaniritsidwa
N’zoona kuti, anthu ambiri amasunga mawu awo, nthaŵi zina amachita zimenezi ngakhale kuti ziwatayitsa zinthu zambiri. (Salmo 15:4) Akanena chinthu amachikwaniritsa. Ena amafunitsitsa kusunga malonjezo amene amapanga ndi zolinga zabwino kwambiri. Amakhala okonzeka ndi ofunitsitsa kuchita zimene analonjeza koma kungoti amalephera kuchita zimenezo. Zochitika zingasokoneze ngakhale zolinga zabwino kwambiri.—Mlaliki 9:11.
Kaya anthu amalephera kukwaniritsa malonjezo awo pa zifukwa zotani, mfundo ndi yakuti anthu ambiri zimawavuta zedi kukhulupirira malonjezo a munthu aliyense. Choncho funso n’lakuti: Kodi pali malonjezo aliwonse amene tingadalire? Inde alipo. Tingadalire malonjezo a m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Bwanji osapenda zimene nkhani yotsatirayi ikunena pamfundoyi? Mungakhale ndi maganizo amene anthu ambiri ali nawo, akuti tingadaliredi malonjezo a Mulungu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
AP Photo/Amel Emric