Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Yehova analoleza kuti atumiki ake akale, Aisrayeli, azichita mitala, koma masiku ano saloleza. Kodi mfundo zake zimasintha?
Maganizo a Yehova pa nkhani ya mitala sanasinthe. (Salmo 19:7; Malaki 3:6) Iye sanafune kuti anthu azichita mitala kuyambira pachiyambi, ndipo mpaka pano safunabe. Pamene Yehova analenga Hava kuti akhale mkazi wa Adamu, anafotokoza kuti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi. “Chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.”—Genesis 2:24.
Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, anabwerezanso mfundo imeneyi poyankha anthu amene anam’funsa za kusudzulana ndi kukwatiranso. Iye anati: “Kodi simunaŵerenga kuti iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi limodzi? Chotero kuti salinso aŵiri koma thupi limodzi.” Kenaka, Yesu ananenanso kuti: “Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo.” (Mateyu 19:4-6, 9) Pamenepa, n’zachionekere kuti kukwatira akazi aŵiri kapena oposa pamenepo n’kuchita chigololo.
Nanga n’chifukwa chiyani mitala inkaloledwa kalelo? Muyenera kukumbukira kuti si Yehova amene anayambitsa mitala. Munthu woyamba kutchulidwa m’Baibulo kuti anali ndi akazi oposa mmodzi anali Lameke, mbadwa ya Kaini. (Genesis 4:19-24) Pamene Yehova anabweretsa Chigumula mu nthaŵi ya Nowa, Nowa ndi ana ake aamuna atatu anali ndi mkazi mmodzimmodzi. Anthu amitala onse anaphedwa pa Chigumulacho.
Patatha zaka mazana angapo, pamene Yehova anasankha Aisrayeli kuti akhale anthu ake, anthu ena pakati pawo anali ali kale ndi mitala, ngakhale zikuoneka kuti kukhala ndi mkazi mmodzi n’kumene kunali kofala. Mulungu sanafune kuti mabanja amene anali ndi akazi oposa mmodzi athe. M’malo mwake, anaika malamulo okhwima okhudza mitala.—Eksodo 21:10, 11; Deuteronomo 21:15-17.
Zimene zikusonyeza kuti Mulungu analoleza mitala kwa nthaŵi yochepa chabe n’zimene Yesu ananena zokhudza mfundo ya Yehova yoyambirira ya ukwati komanso zimene mtumwi Paulo analemba mouziridwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Iye analemba kuti: “Munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.” (1 Akorinto 7:2) Paulo anauziridwanso kulemba kuti mwamuna aliyense woikidwa kukhala woyang’anira kapena mtumiki wotumikira mu mpingo wachikristu ayenera kukhala “mwamuna wa mkazi mmodzi.”—1 Timoteo 3:2, 12; Tito 1:6.
Choncho, Yehova analeka kuloleza mitala pamene mpingo wachikristu unapangidwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Pa nthaŵi imeneyo, ukwati unakhalanso ngati mmene unalili pamene Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi: mwamuna mmodzi, mkazi mmodzi. Imeneyi ndi mfundo imene anthu a Mulungu padziko lonse lapansi amayendera masiku ano.—Marko 10:11, 12; 1 Akorinto 6:9, 10.