Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutsanzira Mulungu wa Choonadi

Kutsanzira Mulungu wa Choonadi

Kutsanzira Mulungu wa Choonadi

“Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.”​—AEFESO 5:1.

1. Kodi anthu ena amaganiza chiyani za choonadi, ndipo n’chifukwa chiyani maganizo awo ali olakwika?

“CHOONADI n’chiyani?” (Yohane 18:38) Funso limeneli, limene Pontiyo Pilato anafunsa monyoza pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, likupereka maganizo oti choonadi ndi chovuta ndipo n’chosatheka kuchipeza. Anthu ambiri masiku ano angavomereze maganizo amenewo. Choonadi chenichenicho akuchisokoneza. Mwina munamvapo anthu akunena kuti aliyense amakhala ndi choonadi chake, kapena kuti choonadi chimadalira mmene munthu akuonera, kapenanso kuti choonadi chimasinthasintha. Maganizo otero ndi olakwika. Anthu akamaphunzira kapena kuchita kafukufuku aliyense, cholinga chawo chachikulu chimakhala choti adziŵe mfundo zenizeni, kapena kuti choonadi, cha dziko limene tikukhalamoli. Choonadi sichidalira mmene munthu akuonera zinthu. Mwachitsanzo, mwina munthu ali ndi chinthu chimene sichifa iye akamwalira, kapena alibe. Mwina Satana alipo, kapena kulibe. Mwina moyo uli n’cholinga, kapena ulibe. Mu nkhani zonsezi, yankho lolondola ndi limodzi basi. Yankho lina n’loona, ndipo linalo n’lonama; mayankho aŵiri onsewo sangakhale oona.

2. Kodi Yehova ndi Mulungu wa choonadi m’njira ziti, ndipo kodi tikambirana mafunso ati?

2 Mu nkhani yapitayo, tinaona kuti Yehova ndi Mulungu wa choonadi. Amadziŵa zoona zake za chinthu chilichonse. Mosiyana kwambiri ndi mdani wake wonyenga Satana Mdyerekezi, Yehova nthaŵi zonse amanena zoona. Kuonjezera pamenepo, Yehova amauza ena choonadi mosaumira ndipo sabisa chilichonse. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Monga Mboni zake za Yehova, kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani ya kunena zoona ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi? Kodi n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika? Ndipo kodi tili ndi umboni wotani wosonyeza kuti Yehova amakondwera ndi anthu amene amakonda choonadi pa moyo wawo? Tiyeni tione.

3, 4. Kodi mtumwi Paulo ndi mtumwi Petro anafotokoza bwanji zinthu zimene zinali kudzachitika “masiku otsiriza”?

3 Tikukhala mu nthaŵi imene m’zipembedzo muli mabodza ambiri. Monga mmene mtumwi Paulo ananeneratu mouziridwa ndi Mulungu, anthu ambiri “masiku otsiriza” ano ali ndi maonekedwe a chipembedzo koma mphamvu yake adaikana. Ena amakana choonadi, chifukwa ndi anthu “ovunditsitsa mtima.” Kuonjezera apo, ‘anthu oipa ndi onyenga, akuipa chiipire, kusocheretsa ndi kusocheretsedwa.’ Ngakhale kuti anthu ameneŵa nthaŵi zonse amakhala akuphunzira, safika podziŵa “chizindikiritso cha choonadi.”​—2 Timoteo 3:1, 5, 7, 8, 13.

4 Mtumwi Petro anauziridwanso kulemba za masiku otsiriza. Mogwirizana ndi zimene ananeneratu, anthu sikuti amangokana choonadi basi, koma amanyozanso Mawu a Mulungu ndi anthu amene amalengeza choonadi chopezeka m’Mawuwo. Anthu onyozaŵa “aiwala dala” kuti dziko la masiku a Nowa linamizidwa ndi madzi, ndipo zimene zinachitikazo ndi chitsanzo cha zimene zidzachitike m’tsogolo muno pa tsiku lopereka chiweruzo. Maganizo awo onyengawo adzawadzetsera tsoka nthaŵi yoti Mulungu aononge anthu osapembedza ikadzafika.​—2 Petro 3:3-7.

Atumiki a Yehova Amadziŵa Choonadi

5. Mogwirizana ndi zimene ananena mneneri Danieli, kodi n’chiyani chinali kudzachitika “nthaŵi ya chimaliziro,” ndipo kodi ulosi umenewu wakwaniritsidwa motani?

5 Pofotokoza za “nthaŵi ya chimaliziro,” mneneri Danieli anafotokoza zinthu zosiyana ndi zimene tatchula kale zija zomwe zidzachitike pakati pa anthu a Mulungu. Iye anafotokoza za kuyambikanso kwa choonadi m’chipembedzo. Iye analemba kuti: “Ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziŵitso chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Anthu a Yehova sasokonezeka kapena kunamizidwa ndi Wonyenga wamkuluyo. Chifukwa cha kuphunzira Baibulo, kumene kuli ngati “kuthamanga,” anthu a Yehova apeza chidziŵitso choona. M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Yesu anaunikira ophunzira ake. Iye “anawatsegulira mitima yawo, kuti adziŵitse malembo.” (Luka 24:45) Masiku athu ano, Yehova wachitanso chimodzimodzi. Mwa kugwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake, iye wathandiza anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi kumvetsetsa chinthu chimene iye akuchidziŵa kale​—choonadi.

6. Kodi anthu a Mulungu masiku ano amamvetsetsa mfundo zoona ziti za m’Baibulo?

6 Ife monga anthu a Mulungu, timamvetsetsa zinthu zambiri zimene sitikanatha kuzidziŵa patokha. Timadziŵa mayankho a mafunso amene anthu anzeru za dzikoli alimbana nawo kwa zaka mazana ambiri. Mwachitsanzo, timadziŵa chifukwa chake anthufe timavutika ndiponso kufa. Timadziŵanso chifukwa chake anthu sangakwanitse kukhazikitsa mtendere ndi mgwirizano padziko lapansili. Tadalitsidwanso mwa kusonyezedwa zinthu zimene zikubwera m’tsogolo muno​—Ufumu wa Mulungu, dziko lapansi la paradaiso, komanso moyo wosatha wangwiro. Tafika pomudziŵa Yehova, Wamkulukuluyo. Taphunzira za khalidwe lake lokopa komanso zimene tiyenera kuchita kuti tilandire madalitso ake. Kudziŵa choonadi kumatithandiza kuzindikira mabodza. Kugwiritsa ntchito choonadi kumatiteteza ku zinthu zopanda phindu zimene anthu amachita. Kumatithandiza kukhala ndi moyo wabwino kwambiri, komanso kumatipatsa chiyembekezo chosangalatsa kwambiri cha m’tsogolo.

7. Kodi ndi anthu otani amene amamvetsetsa choonadi cha m’Baibulo, ndipo ndi anthu otani amene sangachimvetsetse?

7 Kodi inu mumamvetsetsa choonadi chopezeka m’Baibulo? Ngati mumatero, ndinu odala kwambiri. Munthu wolemba mabuku akalemba buku, nthaŵi zambiri amalilemba kuti likakope gulu linalake la anthu. Mabuku ena amalembera anthu ophunzira kwambiri, ena amalembera ana, ndipo ena amalembera anthu odziŵa ntchito zina zapadera. Ngakhale kuti munthu aliyense akhoza kupeza Baibulo mosavutikira, linalembedwa m’njira yoti gulu linalake lapadera la anthu ndilo liyenera kulimvetsetsa ndi kulikonda. Yehova analikonzera anthu odzichepetsa ndi ofatsa a padziko lapansi. Anthu otereŵa angathe kulimvetsetsa Baibulo, ngakhale atakhala a maphunziro, chikhalidwe, moyo, kapena fuko lotani. (1 Timoteo 2:3, 4) Koma anthu a mtima wosafuna choonadi sangamvetsetse choonadi cha m’Baibulo, ngakhale atakhala anzeru kapena ophunzira motani. Anthu odzitukumula ndi onyada sangamvetsetse choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Mawu a Mulungu. (Mateyu 13:11-15; Luka 10:21; Machitidwe 13:48) Ndithudi, ndi Mulungu yekha amene akanatha kulemba buku loterolo.

Atumiki a Yehova Amanena Zoona

8. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anali choonadi chenichenicho?

8 Mofanana ndi Yehova, Mboni zake zokhulupirika zimanena zoona. Yesu Kristu, Mboni yaikulu ya Yehova, anatsimikizira choonadi mwa zinthu zimene anaphunzitsa, moyo wake, komanso mmene anafera. Iye analimbikitsa choonadi cha mawu a Yehova ndi malonjezo ake. N’chifukwa chake Yesu anali choonadi chenichenicho, monga mmene ananenera mwiniwake.​—Yohane 14:6; Chivumbulutso 3:14; 19:10.

9. Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani ya kunena zoona?

9 Yesu anali “wodzala ndi chisomo ndi choonadi,” ndipo “m’kamwa mwake munalibe chinyengo.” (Yohane 1:14; Yesaya 53:9) Akristu oona amatsatira chitsanzo chimene Yesu anawasiyira chonena zoona kwa ena. Paulo analangiza okhulupirira anzake kuti: “Lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziŵalo wina ndi mnzake.” (Aefeso 4:25) Kalelo, Paulo asananene zimenezi, mneneri Zekariya anali atalemba kuti: “Nena choonadi yense ndi mnzake.” (Zekariya 8:16) Akristu amanena zoona chifukwa amafuna kusangalatsa Mulungu. Yehova amanena zoona ndipo amadziŵa mavuto amene amabwera chifukwa cha bodza. Ndiye mpake kuti iye amayembekezera atumiki ake kunena zoona.

10. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amanama, ndipo kodi zotsatirapo zake zoipa n’zotani?

10 Kwa anthu ambiri, kunama kumaoneka ngati njira yosavuta yopezera zinthu zinazake zimene akuzifuna. Anthu amanama kuti asalangidwe, kuti apeze phindu m’njira inayake, kapena kuti anthu ena awatamande. Koma chizoloŵezi chonama ndi khalidwe loipa. Kuonjezera apo, munthu wonama Mulungu sangakondwere naye. (Chivumbulutso 21:8, 27; 22:15) Ngati timadziŵika kuti timanena zoona, anthu ena amakhulupirira zimene timanena ndipo amatidalira. Koma tikadzangopezeka tikunama ngakhale kamodzi kokha, anthu adzayamba kukayikira chilichonse chimene tinganene m’tsogolo. Mwambi wina wa ku Africa kuno umati: “Kunama kamodzi kumafafaniza zoona zambirimbiri.” Wina umati: “Munthu wabodza sam’khulupirira, ngakhale pamene akunena zoona.”

11. Kodi kunena zoona kumatanthauza zambiri m’njira yotani?

11 Kunena zoona kumatanthauza zambiri. Kunena zoona ndi khalidwe la munthu. Kumasonyeza kuti ndife munthu wotani. Timauza anthu zoona osati chabe mwa zimene timanena komanso mwa zimene timachita. Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha?” (Aroma 2:21, 22) Ngati tikufuna kuphunzitsa ena choonadi, tiyenera kukhala oona mtima mu zonse. Mbiri yathu yoti ndife munthu wonena zoona komanso woona mtima idzathandiza kwambiri kuti anthu amvetsere zimene timaphunzitsa.

12, 13. Kodi mtsikana wina analemba chiyani pa nkhani yonena zoona, nanga chinamuthandiza n’chiyani kuti aziyendera mfundo zokhwima choncho pa moyo wake?

12 Atumiki a Yehova achinyamata nawonso amadziŵa kufunika kwa kunena zoona. Jenny, mtsikana amene panthaŵiyo anali ndi zaka 13, analemba m’nkhani yake ya kusukulu kuti: “Kuona mtima ndi khalidwe lofunika kwambiri kwa ine. Koma n’zomvetsa chisoni kuti si anthu ambiri amene amakhala oona mtima nthaŵi zonse masiku ano. Ndatsimikiza kuti pa moyo wanga nthaŵi zonse ndidzakhala woona mtima. Ndidzakhalanso woona mtima ngakhale pamene kunena zoona sikungandithandize kapena kuthandiza mabwenzi anga panthaŵi imeneyo. Ndimaonetsetsa kuti mabwenzi anga akhale anthu onena zoona komanso oona mtima.”

13 Pothirirapo ndemanga pa nkhani imene Jenny analembayi, aphunzitsi ake anati: “Ngakhale uli wamng’ono kwambiri, uli ndi mfundo zokhwima zimene umayendera pa moyo wako. Ndikudziŵa kuti udzapitiriza kuyendera mfundo zimenezi chifukwa ndiwe wolimba mtima.” Kodi n’chiyani chinapangitsa mtsikanayu kukhala wolimba mtima chonchi? Kumayambiriro kwa nkhani yake, Jenny ananena kuti chipembedzo chake “chimamuikira mfundo zoti aziyendera pa moyo” wake. Patha zaka zisanu ndi ziŵiri kuyambira pamene Jenny analemba nkhani imeneyo. Monga mmene ananenera aphunzitsi ake, Jenny akupitirizabe kutsatira mfundo zokhwima pa moyo wake monga mmodzi wa Mboni za Yehova.

Atumiki a Yehova Sabisa Choonadi

14. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu makamaka ali ndi udindo waukulu kwambiri wolimbikitsa choonadi?

14 N’zoona kuti anthu ena amene si Mboni za Yehova angayesetse kunena zoona komanso kukhala oona mtima. Koma chifukwa chakuti ndife atumiki a Mulungu, tili ndi udindo waukulu wolimbikitsa choonadi. Tinaikizidwa choonadi cha m’Baibulo, chimene chingam’pezetse munthu moyo wosatha. Choncho, tili ndi udindo wogaŵana zimene tikudziŵazo ndi ena. Yesu anati: “Kwa munthu aliyense adam’patsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri.” (Luka 12:48) Indedi, anthu ‘amafuna zambiri’ kwa anthu amene ali ndi mwayi wamtengo wapatali wodziŵa Mulungu.

15. Kodi mumapeza chimwemwe chotani mukamaphunzitsa ena choonadi cha m’Baibulo?

15 Kuphunzitsa ena choonadi cha m’Baibulo kumabweretsa chimwemwe. Monga mmene anachitira ophunzira a Yesu m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, nafenso timalalikira uthenga wabwino, uthenga wosangalatsa wopatsa chiyembekezo, kwa anthu “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa,” ndi kwa anthu amene anamizidwa ndi kusokonezeka ndi “maphunziro a ziŵanda.” (Mateyu 9:36; 1 Timoteo 4:1) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Kukhulupirika kwa “ana” a Yohane, mwina amene anawaphunzitsa choonadi, kunam’bweretsera chimwemwe chambiri. Nafenso timasangalala tikamaona anthu akumvetsera ndi kuyamikira Mawu a Mulungu.

16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani si onse amene amakhulupirira choonadi? (b) Kodi ndi zinthu ziti zosangalatsa zimene mungapeze mukamalalikira choonadi cha m’Baibulo?

16 N’zoona kuti si onse amene adzakhulupirira choonadi. Yesu ananena zoona za Mulungu, ngakhale pamene ambiri sanasangalatsidwe nazo. Kwa Ayuda otsutsa, iye anati: “Simundikhulupirira Ine chifukwa ninji? Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.”​—Yohane 8:46, 47.

17 Monga mmene anachitira Yesu, ifenso sitileka kulankhula choonadi chamtengo wapatali chonena za Yehova. Sitiyembekezera kuti anthu onse adzakhulupirira zimene tikuwauza, chifukwa si onse amene anakhulupirira zimene Yesu ananena. Ngakhale zili choncho, timasangalala chifukwa chodziŵa kuti tikuchita zoyenera. Chifukwa cha kukoma mtima kwake, Yehova akufuna kuti anthu onse auzidwe choonadi. Chifukwa chokhala ndi choonadi, Akristu amanyamula kuunika m’dziko la mdima. Mwa kuwalitsa kuunika kwa choonadi kudzera m’mawu ndi ntchito zathu, tingathandize ena kulemekeza Atate wathu wakumwamba. (Mateyu 5:14, 16) Timaonetsa poyera kuti timakana mabodza a Satana ndipo timatsatira Mawu a Mulungu osaipitsidwa m’pang’ono pomwe. Choonadi chimene timadziŵa komanso kugaŵana ndi anthu ena chingawapatse ufulu weniweni anthu amene amachikhulupirira.​—Yohane 8:32.

Pitirizani Kunena Zoona pa Moyo Wanu

18. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anakonda Natanayeli, ndipo kodi anachita chiyani posonyeza kumukonda kumeneku?

18 Yesu anakonda choonadi ndipo ananena zoona nthaŵi zonse. Panthaŵi ya utumiki wake padziko lapansi, iye anakonda anthu onena zoona. Ponena za Natanayeli, Yesu anati: “Onani, Mwisrayeli ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!” (Yohane 1:47) Kenaka, Natanayeli, amene zikuoneka ngati ankatchedwanso Bartolomeyo, anasankhidwa kuti akhale mmodzi wa atumwi 12. (Mateyu 10:2-4) Unali mwayi wapadera kwambiri!

19-21. Kodi munthu amene kale anali wakhungu anadalitsidwa motani chifukwa chonena zoona molimba mtima?

19 M’buku la m’Baibulo la Yohane muli chaputala chathunthu chokamba za munthu wina woona mtima amene anadalitsidwa ndi Yesu. Dzina lake sitikulidziŵa. Zimene tikudziŵa n’zoti munthuyo anali wopemphapempha ndipo anabadwa wakhungu. Anthu anadabwa pamene Yesu anamuchiritsa, iye n’kuyamba kuona. Nkhani ya kuchiza kodabwitsaku inafika kwa Afarisi ena, anthu odana ndi choonadi, amene anali atagwirizana kuti aliyense wokhulupirira Yesu anayenera kuchotsedwa m’sunagoge. Podziŵa zimene Afarisiwo anagwirizana, makolo amantha a munthu amene kale anali wakhunguyo ananama kwa Afarisiwo, n’kuwauza kuti sanali kudziŵa kuti zatheka bwanji kuti mwana wawo ayambe kuona ndiponso anati sanali kudziŵa munthu amene wamuchiritsa.​—Yohane 9:1-23.

20 Afarisi anamuitananso munthu wochiritsidwayo. Mosaopa kuti amuchita chiyani, anawauza zoona molimba mtima. Anawafotokozera mmene anachiritsidwira, ndipo anawauza kuti ndi Yesu amene anamuchiritsa. Podabwa ataona kuti anthu otchuka komanso ophunzira ngati amenewo sanali kukhulupirira kuti Yesu anachokera kwa Mulungu, munthu wochiritsidwayo mopanda mantha anawalimbikitsa kuti avomereze zinthu zimene zinali zachidziŵikire powauza kuti: “Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.” Posoŵa choyankha, Afarisiwo anamuuza munthuyo kuti anali wamwano n’kumutayira kunja.​—Yohane 9:24-34.

21 Yesu atamva zimenezi, mwachikondi anapatula nthaŵi n’kupita kukam’funa munthuyo mpaka kum’peza. Atam’peza, anamuuza zinthu zolimbikitsa chikhulupiriro chake chimene anali atasonyeza. Yesu anamuuza mosapita m’mbali kuti anali Mesiya. Munthuyo anadalitsidwa kwambiri chifukwa chonena zoona! Inde, Mulungu amadalitsa anthu onena zoona.​—Yohane 9:35-37.

22. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukonda choonadi pa moyo wathu?

22 Kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi kukhale chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu. Kumathandiza kwambiri kuti tikhale pa ubwenzi ndi anthu komanso ndi Mulungu, ndiponso kuti tisunge ubwenziwo. Munthu wonena zoona amakhala wosabisa kanthu, woona mtima, wochezeka, ndi wodalirika, ndipo Yehova amakondwera naye. (Salmo 15:1, 2) Munthu wabodza amakhala wachinyengo, wosadalirika, ndiponso amakhala kathyali, ndipo Yehova sakondwera naye. (Miyambo 6:16-19) Choncho, yesetsani kukonda choonadi pa moyo wanu. Inde, kuti titsanzire Mulungu wa choonadi, tiyenera kudziŵa choonadi, kunena zoona, ndi kutsata choonadi pa moyo wathu.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kuti tadziŵa choonadi?

• Kodi tingam’tsanzire bwanji Yehova pa nkhani ya kunena zoona?

• Kodi timapeza phindu lanji tikamaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo kwa ena?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukonda choonadi pa moyo wathu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 17]

Chifukwa chakuti Akristu anaikizidwa choonadi cha m’Baibulo, iwo amagaŵana choonadicho ndi ena mwachangu

[Zithunzi patsamba 18]

Munthu wakhungu amene anachiritsidwa ndi Yesu anadalitsidwa kwambiri chifukwa chonena zoona