Sankhani Moyo Wosatha
Sankhani Moyo Wosatha
ANTHU ambiri sanakhalepo ndi zinthu zochuluka zoti asankhe ngati zimene ali nazo lerolino. Mwachitsanzo, timachita kusankha zovala zimene timavala, chakudya chimene timadya, ndi kumene timagwira ntchito, komanso kumene timakhala. M’madera ambiri a padziko lapansi, kusankha munthu woti udzakwatirane naye n’kofalanso. Koma m’Baibulo timapezamo chinthu choti tisankhe chimene chimaposa chinthu china chilichonse, ndipo munthu aliyense akhoza kusankha chinthu chimenechi.
Baibulo limati: “Wolimbikira chilungamo alandira moyo; koma wolondola zoipa adzipha yekha.” (Miyambo 11:19) Ndipo Yesu Kristu ananena kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”—Yohane 17:3.
Zoonadi, Mlengi wathu watipatsa mwayi woti tisankhe njira imene ingatibweretsere moyo wosatha! Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze moyo wosatha?
Malinga ndi zimene Baibulo limanena, “m’khwalala la chilungamo muli moyo.” (Miyambo 12:28) Tikhoza kukhala mmodzi wa anthu olungama amene ali panjira yopita ku moyo wosatha. Kodi tingatero motani? Mwa kuonetsetsa kuti moyo wathu ukugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndi malamulo ake. (Mateyu 7:13, 14) Choncho, tiyeni tisankhe mwanzeru kuti tidzalandire mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha.—Aroma 6:23.