Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mgonero wa Ambuye N’chiyani?

Kodi Mgonero wa Ambuye N’chiyani?

Kodi Mgonero wa Ambuye N’chiyani?

KODI Mgonero wa Ambuye n’chiyani, ndipo kodi uli ndi tanthauzo lotani kwa anthu amene tikukhala m’zaka za masiku anozi?

Mutafunsa Mkristu kuti “kodi Mgonero wa Ambuye n’chiyani?” angakuyankheni kuti ndi chakudya chimene Yesu Kristu anadya limodzi ndi atumwi ake usiku womaliza asanaphedwe kuti apereke moyo wake nsembe. Anthu ena amachitchanso Mgonero Womaliza chifukwa chinali chakudya chamadzulo chomaliza chimene Yesu anadyera limodzi ndi otsatira ake okhulupirika. Ndipo chifukwa chakuti chinakhazikitsidwa ndi Ambuye Yesu Kristu mwiniwakeyo, dzina loti Mgonero wa Ambuye n’loyenerera.

Kwa zaka zambiri m’mbuyo monsemu, anthu ambiri ataya miyoyo yawo pofera zinthu zimene ankaziona kuti n’zothandiza. Imfa ya ena mwa ameneŵa inathandizako anthu ena kwa kanthaŵi kochepa. Komabe, palibe imfa iliyonse ya anthu odzipereka ameneŵa, ngakhale kuti inali yothandizako pang’ono, imene phindu lake lingafanane m’pang’onong’ono pomwe ndi phindu la imfa ya Yesu Kristu. Ndiponso, palibe imfa ya munthu aliyense, m’mbiri yonse ya anthu yodzala ndi mavutoyi, imene ingakhudze anthu pa dziko lonse lapansi ngati mmene inachitira ya Yesu. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kuti tiyankhe funso limeneli komanso kuti tikuthandizeni kudziŵa tanthauzo limene Mgonero wa Ambuye uli nalo kwa inu, tikukupemphani kuti muŵerenge nkhani yotsatirayi.