Musalekerere Mtima wa Mwana Wanu!
Musalekerere Mtima wa Mwana Wanu!
DONGO lopanda ntchito limene lili m’manja mwa woumba waluso, angaliumbe chinthu chokongola kwambiri. Akatswiri pa zoumbaumba ochepa chabe amapanga zinthu zambiri kuchokera pa zinthu zochepa. Kwa zaka zambiri, anthu adalira oumba akafuna makapu, mbale, miphika, mosungira zinthu, ndiponso mitsuko yokongoletsera m’nyumba.
Makolonso amathandiza kwambiri dziko mwa kuumba zochita ndi mitima ya ana awo. Baibulo limayerekezera munthu aliyense ndi dothi, ndipo Mulungu wapatsa makolo ntchito yofunika youmba “dothi” lomwe ndi ana awo. (Yobu 33:6; Genesis 18:19) Mofanana ndi kuumba chinthu chokongola kwambiri, kuumba mwana kukhala munthu wamkulu wodalirika ndiponso wochita bwino zinthu si ntchito ya maseŵera. Kuumba kumeneko sikumangochitika kokha.
Pali zinthu zambiri zimene zimaumba mitima ya ana athu. Chomvetsa chisoni n’chakuti, zina mwa zimenezi n’zowononga. Choncho, m’malo mongolekerera mtima wa mwana, kholo lanzeru lidzaphunzitsa mwana mu “njira yake,” ndi chidaliro chakuti “atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.
Pantchito yolera mwana ya nthaŵi yaitali ndi yokondweretsa imeneyi, makolo achikristu anzeru afunika kukhala ndi nthaŵi yochotsa zinthu zoipa zimene zingaipitse mtima wa mwana wawo. Chikondi chawo chidzayesedwa kwambiri pamene akuyesetsa moleza mtima kumpatsa mwanayo “malangizo, ndiponso kumukonza, monga mwa maleredwe a Chikristu.” (Aefeso 6:4, The New English Bible) Kunena zoona, ntchito ya makolo imakhala yophwekerapo ngati ayamba anawo ali aang’ono.
Kuyamba Ali Aang’ono
Oumba amakonda kugwiritsa ntchito dongo lofeŵa bwino loti akaliumba likhala monga momwe aliumbiramo. Dongolo akalikonzakonza, amakonda kuligwiritsira ntchito pasanathe miyezi sikisi. Mofananamo, nthaŵi yabwino
kwambiri kwa makolo kuyamba kuumba mtima wa mwana wawo ndi pamene uli womvera ndiponso wosavuta kuwumba.Akatswiri pankhani za ana amanena kuti mwana akafika miyezi eyiti, amakhala ataphunzira kale kuzindikira chinenero cha makolo ake, amakhala paubwenzi wapamtima ndi makolo ake, amamva, ndiponso amayamba kutakataka m’mimbamo. Nthaŵi yabwino kuyamba kuumba mtima wake ndi pamene akadali wamng’ono. Si mmene mwana wanu adzapindulire ‘akadziŵa malembo opatulika kuyambira ukhanda’ monga Timoteo!—2 Timoteo 3:15. *
Mwachibadwa ana amatsanzira makolo awo. Kuwonjezera pa kutengera mawu, zochita ndiponso mmene makolowo akugwiritsira ntchito manja ndi nkhope polankhula, amaphunzira chikondi, kukoma mtima, ndiponso chifundo akamaona makolo awo akusonyeza makhalidwe ameneŵa. Ngati tikufuna kuphunzitsa mwana wathu motsatira malamulo a Yehova, malamulo a Mulungu ayenera kukhala kaye pa mitima yathu. Kuwakonda ndi mtima wonse kumeneku kudzalimbikitsa makolo kulankhula ndi ana awo nthaŵi zonse za Yehova ndiponso Mawu ake. Baibulo limalimbikitsa kuti: ‘Muziwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Francisco ndi Rosa akufotokoza momwe amachitira zimenezi ndi ana awo aang’ono aŵiri. *
“Kuphatikiza pa kucheza nawo tsiku ndi tsiku, timayesetsa tsiku lililonse kulankhula ndi mwana aliyense payekha kwa mphindi zosachepera 15. Tikaona vuto, timalankhula nawo kwanthaŵi yaitali ndipo pamapezekadi mavuto. Mwachitsanzo, posachedwapa mwana wathu wamwamuna wa zaka zisanu atabwera ku sukulu anatiuza kuti sakhulupirira Yehova. Mwachionekere, mnzake wina wa m’kalasi ankamuseka ndipo ankati kulibe Mulungu.”
Makolo ameneŵa anazindikira kuti ana amafunika kukhulupirira Mlengi wawo. Kukhulupirira kumeneku angakhale nako posangalala ndi zinthu zimene Mulungu analenga. Si mmene ana amakondera kugwira nyama, kuthyola maluwa am’thengo, kapena kuseŵera pa mchenga m’mphepete mwa nyanja! Makolo angathandize ana kugwirizanitsa zinthu zachilengedwe ndi Mlengi. (Salmo 100:3; 104:24, 25) Mantha ndi ulemu umene amakhala nawo pa zimene Yehova analenga angakhale nawo kwa moyo wawo wonse. (Salmo 111:2, 10) Kuphatikiza pa kumvetsetsa kumeneku, mwana angafune kusangalatsa Mulungu ndiponso angaope kumukhumudwitsa. Izi zidzamulimbikitsa ‘kupatuka pa zoipa.’—Miyambo 16:6.
Ngakhale kuti ana ang’ono ambiri amafunitsitsa kuphunzira ndiponso sachedwa kuphunzira, zimawavuta kumvera. (Salmo 51:5) Nthaŵi zina angaumirire kuchita zofuna zawo kapena kukhala ndi chilichonse chimene akufuna. Makolo afunika kulimba, kuleza mtima, ndiponso kulanga kuti aletse makhalidwe ameneŵa kumera mizu. (Aefeso 6:4) Izi n’zimene aona a Phyllis ndi a Paul amene alera bwino kwambiri ana asanu.
A Phyllis akuti: “Ngakhale kuti mwana aliyense anali ndi mtima wapadera, aliyense ankafuna kuchita zofuna zake. Zinali zovuta, komabe m’kupita kwa nthaŵi anaphunzira tanthauzo la mawu akuti ‘ayi.’” A Paul, omwe ndi amuna awo, anati: “Nthaŵi zambiri, tinkawauza zifukwa zimene
tasankhira zimenezo ngati anali a msinkhu woti amvetsa. Ngakhale kuti nthaŵi zonse tinkayesetsa kukhala okoma mtima, tinawaphunzitsa kulemekeza udindo wathu umene Mulungu anatipatsa.”Ngakhale kuti mwana angakumane ndi mavuto m’zaka zake zoyambirira, makolo ambiri amaona kuti vuto lalikulu limabwera paunyamata pamene mtima wanthete umakumana ndi mavuto ambiri atsopano.
Kumufika Pamtima Wachinyamata
Woumba ayenera kuyamba ntchito yake dongo lisanaume. Kuti adzipatse nthaŵi yokwanira, angawonjezere madzi ku dongolo kuti likhalebe lofeŵa. Mofananamo, makolo ayenera kulimbikira kuti atchinjirize mtima wa mwana wawo wachinyamata kuti ukhale womvera. Ndithudi, chida chawo chachikulu ndi Baibulo, limene ‘angatsutsire, kukonzera, ndi kukonzekeretsera mwana wawo kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Timoteo 3:15-17.
Komabe, wachinyamata, sangamvere malangizo a makolo mwamsanga monga anali kuchitira ali wamng’ono. Achinyamata angayambe kumvera kwambiri achinyamata anzawo, choncho kulankhulana ndi makolo awo momasuka ndiponso mochokera pansi pamtima kungachepe. Ndi nthaŵi yofunika kuleza mtima kwambiri ndiponso luso lochuluka, popeza ntchito ya makolo ndiponso ana yafika pa msinkhu wina. Wachinyamata afunika kuzoloŵera kusintha kwa thupi lake ndiponso maganizo ake. Afunika kuyamba kusankha zochita ndiponso kukhala ndi zolinga zimene zingakhudze moyo wake wonse. (2 Timoteo 2:22) Panthaŵi yonse yovuta imeneyi, afunika kulimbana ndi mphamvu imene imawononga mtima wake yomwe ndi kufuna kuchita zimene anzake akuchita.
Zimenezi sizimabwera m’njira imodzi yodziŵika. M’malo mwake, nthaŵi zambiri zimaonekera m’mawu ambiri kapena m’zochitika zambiri zofooketsa. Zimenezi zimakhudza kwambiri mbali yofooka ya achinyamata ambiri yomwe ndi mantha aakulu akuti achinyamata anzawo aziwapatula. Wachinyamata pofuna kuoneka kuti ndi wofunika ndiponso kuti ena azim’konda, angayambe kuchita “za m’dziko lapansi” zimene achinyamata ena amalimbikitsa.—1 Yohane 2:15-17; Aroma 12:2.
Poipitsanso zinthu kuposa pamenepa, zofuna za mtima wopanda ungwiro zingalimbikitse kuchita zonena za anzake. Mawu onga akuti “Sangalala” ndiponso “Chita zofuna zako” angaoneke osangalatsa kwambiri. María akukumbukira motere zimene zinam’chitikira: “Ndinamvera achinyamata anzanga amene ankakhulupirira kuti achinyamata ali ndi ufulu wosangalala kwambiri, mosaganizira zotsatira zake. Popeza ndinkafuna kuchita zimene
anzanga akusukulu ankachita, ndinatsala pang’onong’ono kugwera m’mavuto aakulu.” Monga kholo, mumafuna kuthandiza wachinyamata wanu kuthana ndi vuto limeneli, koma kodi mungachite bwanji?Mwa mawu anu ndi zochita zanu, mtsimikizireni nthaŵi zonse kuti mumam’konda. Yesetsani kudziŵa momwe amaonera zinthu, ndipo yesani kumvetsa mavuto ake, amene angakhale ovuta kwambiri kuposa mavuto amene munkakumana nawo ku sukulu. Makamaka panthaŵi imeneyi, mwana wanu afunika kumakuonani monga munthu amene angamuthere zakukhosi. (Miyambo 20:5) Mwa zochita zake kapena mmene alili, mungaone kuti akuvutika maganizo kapena waima mutu. Muthandizeni mavuto ake ngakhale kuti sanawanene, ndipo ‘tonthozani mtima wake.’—Akolose 2:2.
Ndithudi, n’kofunika kulimba poumirira chinthu chabwino. Makolo ambiri aona kuti nthaŵi zina pamakhala kulimbana kwa kholo ndi mwana, koma sangagonjere ngati zosankha zawo zili za zanzeru. Komanso, onetsetsani kuti mukumvetsa nkhani yonse bwinobwino musanaganize ngati n’kofunika kupereka chilango chachikondi ndiponso momwe mungachitire zimenezo ngati n’kofunika.—Miyambo 18:13.
Ngakhale mu Mpingo
Mtsuko ungaoneke kuti watha, koma ngati sanauwotche, utha kusweka ndi madzi amene asungiramo. Baibulo limayerekezera ziyeso ndiponso mavuto ndi ntchito yowotcha imeneyi, popeza zimasonyeza kuti ndife anthu amtundu wanji kwenikweni. N’zoona kuti Baibulo likunena makamaka ziyeso za chikhulupiriro chathu, koma mfundoyi imagwiranso ntchito pa ziyeso zina. (Yakobo 1:2-4) Chodabwitsa n’chakuti, ziyeso zina zovuta zimene achinyamata amakumana nazo zimachokera mu mpingo.
Ngakhale wachinyamata wanu akuoneka ngati wanthanzi labwino mwauzimu, angakhale akuvutika mkati ndi mitima iŵiri. (1 Mafumu 18:21) Mwachitsanzo, Megan anatengera maganizo adziko kwa achinyamata ena amene ankabwera ku Nyumba ya Ufumu, ndipo anati:
“Zochita za gulu la achinyamata amene ankaona Chikristu monga chotopetsa ndiponso monga chinthu cholepheretsa kusangalala, zinandikhudza. Ankanena zinthu monga izi: ‘Ndikadzangofika zaka 18, ndidzasiya choonadi,’ kapena ‘Ndikufunitsitsa n’tasiya choonadi.’ Iwo ankapeŵa achinyamata amene anali kunena zosiyana ndi zimenezi, moti ankawatcha kuti oyera mtima.”
Munthu mmodzi yekha kapena aŵiri a khalidwe loipa akhoza kusonkhezera ena onse. Nthaŵi zambiri anthu pagulu amangochita zimene anthu ambiri pagululo akuchita. Kupusa komanso kudziona ngati wochenjera kungachititse munthu kunyalanyaza nzeru ndi makhalidwe abwino. M’mayiko ambiri, pakhala nkhani zomvetsa chisoni za achinyamata achikristu amene aloŵa m’mavuto chifukwa chotsatira zimene ambiri akuchita.
Aroma 12:13) Limbikitsani mwana wanu kufuna ntchito yabwino, monga kuphunzira kuimba ndi choimbira kapena kudziŵa kwambiri chinenero china kapena ntchito ya manja. Mbali yaikulu ya zimenezi, angachitire pakhomo pomwepo, pomwe ndi malo abwino kwambiri.
N’zoona kuti, achinyamata amafunika nthaŵi yocheza mosangalala. Kodi inu monga kholo mungachite bwanji zimenezi? Lingalirani kwambiri zosangalatsa zawo, ndipo konzani zinthu zosangalatsa pamodzi ndi banja kapena kagulu ka achinyamata ndi achikulire. Dziŵani anzake a mwana wanu. Aitanireni ku chakudya, kapena kudzacheza nawo madzulo. (Kuphunzira Kungakhale Chitetezo
Sukulu ingam’thandizenso wachinyamata kuika zosangalatsa pa malo ake. Loli, yemwe wakhala woyang’anira pa sukulu yaikulu kwa zaka 20, anati: “Ndaona achinyamata ambiri a Mboni akumaliza sukulu. Ana ambiri anali amakhalidwe abwino, koma ena sanali osiyana ndi ophunzira ena onse. Ana amakhalidwe abwino ndi amene ankalimbikira maphunziro awo. Ndikulangiza kwambiri makolo kuti azichita chidwi ndi mmene ana awo akuchitira ku sukulu, kudziŵa aphunzitsi awo, ndipo kutsimikizira ana awo kuti kukhoza bwino n’kofunika. Ena angakhoze kwambiri komabe onse angafike pamlingo wabwino ndipo angasangalatse aphunzitsi awo.”
Kuphunzira kotereko kungathandizenso achinyamata kupita patsogolo mwauzimu. Kungawaphunzitse njira zabwino zophunzirira, kudziletsa, ndiponso kudziona kuti ali ndi udindo woti angachite kanthu kena kaphindu. Mosakayikira kudziŵa kwawo kuŵerenga bwino ndiponso kumvetsa mfundo kudzawalimbikitsa kukhala ophunzira ndiponso aphunzitsi abwino a Mawu a Mulungu. (Nehemiya 8:8) Zofunika ku sukulu kwawo ndiponso maphunziro awo auzimu zingathandize kuchita zosangalatsa panthaŵi yake.
Inu Ndiponso Yehova Mudzalemekezedwa
Kale ku Greece mitsuko yambiri inkakhala ndi siginecha ya woumba ndiponso amene anaikongoletsa. Mofananamo, nthaŵi zambiri m’banja mumakhala anthu aŵiri amene amagwira ntchito youmba ana. Bambo ndi mayi amagwira ntchito youmba mtima wa mwana, ndipo mophiphiritsira mwana wanu amakhala ndi “siginecha” ya nonse aŵiri. Monga woumba waluso, ndiponso/kapena monga wokongoletsa, mungasangalale ndi ntchito yanu youmba mwana waphindu ndi wabwino.—Miyambo 23:24, 25.
Kuyenda bwino kwa ntchito yaikulu imeneyi kudzadalira kwambiri kuti mwafika pati poumba mtima wa mwana wanu. Tikukhulupirira mudzanena kuti: “Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka.” (Salmo 37:31) Mtima wa mwana ndi wofunika kwambiri wosati n’kungowulekerera.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Makolo ena amamuŵerengera Baibulo mwana wawo wobadwa kumene. Mawu osangalatsa ndiponso chinthu chabwino chimenechi chingam’limbikitse mwanayo kukonda kuŵerenga kwa moyo wake wonse.
^ ndime 9 Tasintha mayina ena.