Phunzirani ndi Kuphunzitsa Ena Makhalidwe Abwino Achikristu
Phunzirani ndi Kuphunzitsa Ena Makhalidwe Abwino Achikristu
“Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini?”—AROMA 2:21.
1, 2. Kodi pali zifukwa zotani zimene mungaphunzirire Baibulo?
PALI zifukwa zambiri zimene mungaphunzirire Mawu a Mulungu. Mosakayika, mukufuna mutadziŵa nkhani za m’Baibulo zokhudza anthu, zochitika, malo, ndi zinthu zina. Mufunika kudziŵa ziphunzitso zoona zomwe n’zosiyana kwambiri ndi ziphunzitso zolakwika za zipembedzo monga Utatu kapena moto wa helo. (Yohane 8:32) Mufunikanso kum’dziŵa bwino Yehova kuti mufanane naye ndi kuyenda molungama pamaso pake.—1 Mafumu 15:4, 5.
2 Chifukwa china chachikulu chophunzirira Mawu a Mulungu ndicho kuti mukhale wokonzeka kuphunzitsa ena. Mungaphunzitse anthu amene mumawakonda, amene mumawadziŵa ngakhalenso amene simuwadziŵa. Imeneyi si nkhani yoti Mkristu woona angasankhe kuchita kapena kusachita. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyu 28:19, 20.
3, 4. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti muziphunzitsa potsatira lamulo la Yesu?
3 Kuphunzira Baibulo n’cholinga choti muphunzitse ena n’chinthu chabwino
kwambiri ndipo zingakuchititseni kupeza chimwemwe chosatha. Ntchito ya uphunzitsi yakhala yolemekezeka kwa nthaŵi yaitali. Buku la Encarta Encyclopedia limati: “Makolo ambiri achiyuda ankaona aphunzitsi kukhala anthu omwe angathandize munthu kupulumuka ndipo ankalimbikitsa ana kuti azilemekeza aphunzitsi awo mwinanso kuposa mmene ankalemekezera makolo awo.” Makamaka Akristu afunika kudziphunzitsa okha mwa kuphunzira Baibulo ndiyeno n’kuphunzitsa ena.4 Buku lakuti The World Book Encyclopedia linati: “Ntchito imene ili ndi anthu ambiri kuposa ina iliyonse ndi ya uphunzitsi. Amuna ndi akazi pafupifupi 48 miliyoni padziko lonse ndi aphunzitsi.” Mphunzitsi wa kusukulu ali ndi udindo wolangiza achinyamata ndipo angakhudze moyo wawo kwa nthaŵi yaitali. Zotsatira za ntchito yophunzitsa zimakhala zopindulitsa kwambiri mukamvera lamulo la Yesu loti muziphunzitsa ena. Kuwaphunzitsa kwanu kungathandize kuti adzapeze moyo wosatha. Mtumwi Paulo anatsindika zimenezi pamene analimbikitsa Timoteo kuti: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Inde, kuphunzitsa kwanu n’kothandiza kuti munthu apulumuke.
5. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa kwa Mkristu n’kwapamwamba kwambiri?
5 Amene walamula ndi kulangiza kuti mudziphunzitse ndi kuphunzitsanso ena ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Mfundo imeneyi ikuchititsa ntchito yanu yophunzitsa kukhala yapamwamba kuposa ntchito yophunzitsa kaya maphunziro oyambirira a kusukulu, luso la zantchito, ngakhalenso ukatswiri wa zamankhwala. Kuphunzitsa kwa Mkristu kumatanthauza kuti wophunzirayo aphunzire kutsanzira Mwana wa Mulungu, Kristu Yesu, ndi kuphunzitsa ena kuchita chimodzimodzi.—Yohane 15:10.
N’chifukwa Chiyani Mufunika Kudziphunzitsa?
6, 7. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera choyamba kudziphunzitsa tokha? (b) Kodi Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino analephera bwanji kukhala aphunzitsi?
6 N’chifukwa chiyani tikunena kuti choyamba tifunika kudziphunzitsa tokha? Chifukwa chakuti sitingathe kuphunzitsa bwino ena ngati sitinadziphunzitse kaye tokha. Paulo anatsindika mfundo imeneyi m’ndime yofuna kuiganizira imene inali yofunika kwa Ayuda kalelo yomwe ilinso ndi uthenga wofunika kwambiri kwa Akristu lerolino. Iye anafunsa kuti: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nawo mafano, umafunkha za m’kachisi Aroma 2:21-23.
kodi? Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo?”—7 Paulo pogwiritsa ntchito mafunso ofuna kuganiza, anatchula zolakwa ziŵiri zimene Malamulo Khumi analetsa mosapita m’mbali. Zolakwazo ndizo kuba ndi kuchita chigololo. (Eksodo 20:14, 15) Ayuda ena m’nthaŵi ya Paulo ankanyadira kuti anali ndi chilamulo cha Mulungu. Iwo ‘anaphunzitsidwa chilamulo ndipo analimbika mumtima kuti iwo okha anali otsogolera akhungu ndi nyali ya amene akhala mumdima, aphunzitsi a tiana.’ (Aroma 2:17-20) Komabe ena anali onyenga chifukwa anali kuba ndi kuchita chigololo mwamseri. Zimenezo zinatonzetsa Chilamulo ndiponso Amene anachilemba yemwe ali kumwamba. Mutha kuona kuti sanali oyenerera kuphunzitsa ena. Sanali kudziphunzitsa okha.
8. Kodi Ayuda ena a m’nthaŵi ya Paulo ayenera kuti ‘anafunkha za m’kachisi’ motani?
8 Paulo anatchula za kufunkha za m’kachisi. Kodi Ayuda ena anachitadi zimenezo? N’chiyani chinamuchititsa Paulo kunena zimenezo? Kunena zoona, sitingadziŵe bwinobwino mmene Ayuda ena ‘anafunkhira za m’kachisi’ chifukwa chakuti ndimeyi sikufotokoza zambiri. M’mbuyomo, mlembi wa mumzinda wa Efeso ananena kuti anzake a Paulo sanali “olanda za m’kachisi” zimene zikusonyeza kuti anthu ena ankaganiza kuti Ayuda ankachita zimenezi. (Machitidwe 19:29-37) Kodi anali kugwiritsa ntchito kapena kuchita malonda ndi zinthu za mtengo wapatali za mu akachisi achikunja zimene ankhondo kapena anthu achipembedzo ojijirika analanda? Lamulo la Mulungu linanena kuti golidi ndi siliva wa mafano anayenera kumuwononga osati kutenga n’kukagwiritsa ntchito. (Deuteronomo 7:25) * Motero, Paulo ayenera kuti anali kunena za Ayuda amene sanamvere lamulo la Mulungu n’kugwiritsa ntchito kapena kupindula ndi zinthu za mu akachisi achikunja.
9. Kodi ndi makhalidwe oipa ati okhudza kachisi ku Yerusalemu amene ayenera kuti anafanana ndi kulanda za pakachisi?
9 Komabe, Josephus anasimba za nkhani yochititsa manyazi imene anachita Ayuda anayi ku Roma ndipo mtsogoleri wawo anali mphunzitsi wa Chilamulo. Ayuda anayiwo anauza mkazi wachiroma amene anatembenukira kuchiyuda kuti awapatse golide ndi zinthu zina zamtengo wapatali kuti zikhale mphatso za pakachisi ku Yerusalemu. Mkaziyo atawapatsa, iwo anagwiritsa ntchito chumacho pa zofuna zawo, komwe kunali ngati kulanda za pakachisi. * Ena analinso kulanda za pakachisi wa Mulungu mwa kupereka nsembe zosayenera ndi kuchita malonda a dyera pa bwalo la kachisi, kuchititsa kachisiyo kukhala “phanga la achifwamba.”—Mateyu 21:12, 13; Malaki 1:12-14; 3:8, 9.
Phunzitsani Makhalidwe Achikristu
10. Kodi sitiyenera kuphonya mfundo iti ya mawu a Paulo pa Aroma 2:21-23?
10 Kaya ndi zochitika zotani zokhudza kuba, kuchita chigololo, ndi kufunkha za pakachisi za m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino zimene Paulo anali kunena, tisaphonye mfundo ya mawu ake. Iye anafunsa kuti: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini?” N’kofunika kudziŵa kuti zitsanzo zimene Paulo anapereka n’zokhudza makhalidwe abwino. Apa mtumwi Paulo sanatsindike pa ziphunzitso kapena zochitika za m’Baibulo. Anali kunena za kudziphunzitsa ndi kuphunzitsanso ena makhalidwe abwino achikristu.
11. N’chifukwa chiyani muyenera kuika mtima pa makhalidwe achikristu pamene mukuphunzira Mawu a Mulungu?
11 Kuti tigwiritse ntchito phunziro limene lili pa Aroma 2:21-23 tiyenera kuphunzira makhalidwe abwino achikristu m’Mawu a Mulungu, kutsatira zimene tikuphunzirazo, ndiyeno kuwaphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi. Motero pamene mukuphunzira Baibulo, onani miyezo ya Yehova, kumene kumachokera makhalidwe achikristu. Sinkhasinkhani malangizo ndi phunziro limene mukulipeza m’Baibulo. Ndiyeno gwiritsani ntchito ndi mtima wonse zimene mukuphunzirazo. Ndipo kuchita zimenezo kumafunadi kulimba mtima ndi kutsimikiza. Anthu opanda ungwirofe sizitivuta kupeza zifukwa zoganizira kuti malinga ndi mmene zinthu zilili pa zochitika zinazake, palibe kuchitira mwina koma kunyalanyaza makhalidwe abwino achikristu. Mwina Ayuda amene Paulo anawatchula ankakonda kupeza zifukwa zofuna kuchepetsa cholakwa kapena kusocheretsa ena. Koma mawu a Paulo akusonyeza kuti munthu sayenera kuchepetsa kapena kunyalanyaza makhalidwe achikristu malinga ndi mmene akufunira.
12. Kodi makhalidwe abwino kapena oipa amakhudza bwanji mmene anthu angaonere Yehova Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani n’kofunika kukumbukira mfundo imeneyi?
12 Mtumwi Paulo anasonyeza chifukwa chachikulu chophunzirira ndi kugwiritsa ntchito makhalidwe abwino amene ali m’Baibulo. Makhalidwe oipa a Ayuda anakhudza mmene anthu anaonera Yehova. Timaŵerenga kuti: “Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu.” (Aroma 2:23, 24) N’chimodzimodzinso lerolino kuti tikanyalanyaza makhalidwe abwino achikristu, timatonzetsa amene anapereka makhalidwe abwinowo. Koma ngati titsatira miyezo ya Mulungu, zimakhala bwino ndipo timamulemekezetsa iye. (Yesaya 52:5; Ezekieli 36:20) Kudziŵa zimenezi kungakulimbitseni mtima pamene mukumana ndi mayesero kapena zochitika zina pamene kungaoneke ngati kunyalanyaza makhalidwe abwino achikristu ndiko njira yachidule imene mungatsatire. Komanso, mawu a Paulo akutiphunzitsa chinachake. Kuwonjezera pa kudziŵa kuti makhalidwe anu amakhudza mmene anthu angaonere Mulungu, pamene mukuphunzitsa ena athandizeni kuona kuti mmene akugwiritsira ntchito miyezo ya makhalidwe abwino imene akuphunzira zidzakhudza mmene anthu angaonere Yehova. Makhalidwe abwino achikristu amachititsa munthu kukhala wosangalala ndiponso kuteteza moyo wake. Komanso amakhudza mmene anthu angaonere Amene anakhazikitsa ndi kulimbikitsa makhalidwewo.—Salmo 74:10; Yakobo 3:17.
13. (a) Kodi Baibulo limatithandiza bwanji pankhani ya makhalidwe? (b) Perekani mfundo yaikulu ya malangizo amene ali pa 1 Atesalonika 4:3-7.
13 Makhalidwe abwino amakhudzanso anthu ena. Mungaone zimenezi m’zitsanzo za m’Mawu a Mulungu zimene zimasonyeza phindu logwiritsa ntchito miyezo ya makhalidwe abwino ya Mulungu ndi zimene zimachitika munthu akanyalanyaza miyezoyo. (Genesis 39:1-9, 21; Yoswa 7:1-25) Mungapezenso malangizo osapita m’mbali oterowo pankhani ya makhalidwe monga akuti: “Ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeneretso ndi ulemu, kosati m’chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziŵa Mulungu; asapitirireko munthu, nanyenge [ndi kuphwanya ufulu wa, NW] mbale wake m’menemo, . . . pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso.”—1 Atesalonika 4:3-7.
14. Kodi mungadzifunse mafunso otani pa malangizo amene ali pa 1 Atesalonika 4:3-7?
14 Pafupifupi aliyense angaone m’ndime imeneyi kuti chiwerewere chimaswa lamulo la makhalidwe abwino achikristu. Komabe, mungathe kuimvetsa mozama ndimeyi. Mawu ena pamenepa afunika kuwaphunzira mowonjezereka ndi kuwasinkhasinkha, zimene zingachititse kuti tiwamvetse bwino kwambiri. Mwachitsanzo, mungasinkhesinkhe zimene Paulo anatanthauza pamene anati munthu amene achita dama ‘amapitirira nanyenga ndi kuphwanya ufulu wa mbale wake m’menemo.’ Kodi ndi ufulu uti umene munthu angaphwanye, ndipo kodi kumvetsa bwino zimenezi kudzakulimbikitsani bwanji kusungabe makhalidwe abwino achikristu? Kodi zimene mungapeze mukafufuza zidzakukonzekeretsani bwanji kuphunzitsa ena ndi kuwathandiza kulemekeza Mulungu?
Kuphunzira N’cholinga Choti Muphunzitse
15. Kodi ndi zida ziti zimene mungagwiritse ntchito podziphunzitsa nokha pa phunziro laumwini?
15 A Mboni za Yehova ali ndi zida zimene amagwiritsa ntchito kufufuza nkhani kapena mafunso amene angapeze pamene akuphunzira komanso kuti akaphunzitse ena. Chida chimodzi chimene chikupezeka m’zinenero zambiri ndicho Watch Tower Publications Index. Ngati muli ndi chida chimenechi,
mungachigwiritse ntchito kupeza nkhani m’mabuku othandiza kuphunzira Baibulo a Mboni za Yehova. Mungafufuze malinga ndi mutu wa nkhani kapena pa m’ndandanda wa mavesi a m’Baibulo. Chida china chimene a Mboni za Yehova ali nacho m’zilankhulo zambiri zazikulu ndicho Watchtower Library. Imeneyi ndi pulogalamu ya pa kompyuta imene ili ndi zofalitsa zambiri. Pulogalamu imeneyi imathandiza munthu kufufuza nkhani ndiponso mmene anafotokozera malemba. Ngati muli ndi chimodzi mwa zida zimenezi kapena zonse, zigwiritseni ntchito nthaŵi zonse pamene mukuphunzira Mawu a Mulungu kuti muthe kuphunzitsa ena.16, 17. (a) Kodi mungapeze kuti ndemanga zothandiza kumvetsa ufulu umene autchula pa 1 Atesalonika 4:6? (b) Kodi dama lingaphwanye bwanji ufulu wa ena?
16 Tiyeni titenge chitsanzo chimene tachitchula pamwambapa cha 1 Atesalonika 4:3-7. Panali funso lokhudza ufulu. Kodi ndi ufulu wa ndani? Kodi munthu angapwanye bwanji ufulu umenewo? Pogwiritsa ntchito zida zimene tazitchulazi, mungapeze ndemanga zothandiza kumvetsa mavesi ameneŵa, ngakhalenso ufulu umene Paulo anatchula. Mungaŵerenge ndemanga zimenezo m’buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, masamba 863-4; Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?, tsamba 145; Nsanja ya Olonda, ya November 15, 1989, tsamba 31.
17 Popitiriza kuphunzira zimenezi, mudzaona kuti zofalitsazi zikusonyeza mmene mawu a Paulo alilidi oona. Wadama amachimwira Mulungu ndiponso angatenge matenda. (1 Akorinto 6:18, 19; Ahebri 13:4) Mwamuna amene wachita dama amaphwanya ufulu wa mkazi amene wagona nayeyo. Amawononga ufulu wake wokhala woyera ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Ngati ali wosakwatiwa, amamuphwanyira ufulu wake woloŵa m’banja ali namwali ndiponso amaphwanyira munthu yemwe adzakhale mwamuna wake ufulu wofuna kuti mkaziyo akhale namwali pamene akumukwatira. Ngati ali wokwatiwa, mwamuna wadamayo amavulaza maganizo a makolo a mkaziyo ndi mwamuna wake. Mwamuna wa makhalidwe oipayo amawononganso ufulu wa banja lake wokhala ndi mbiri yabwino. Ngati ali mumpingo wachikristu, amatukwanitsa mpingowo, ndi kuipitsa mbiri yake.—1 Akorinto 5:1.
18. Kodi mumapindula chiyani pa phunziro la Baibulo pankhani ya makhalidwe abwino achikristu?
18 Kodi ndemanga zimenezo zokhudza ufulu sizikukuthandizani kumvetsa mozama mavesi amenewo? Kuphunzira koteroko n’kopindulitsa kwambiri. Pamene mukuchita zimenezi, mukudziphunzitsa nokha. Mumamvetsa bwino kwambiri choonadi cha Mawu a Mulungu ndipo chimakhudza kwambiri mtima wanu. Mumalimbitsa kutsimikiza mtima kwanu kutsatira makhalidwe abwino a Mulungu ngakhale mutakumana ndi mayesero otani. Ndiponso, mungakhale mphunzitsi wogwira mtima kwambiri. Mwachitsanzo, pophunzitsa ena choonadi cha Baibulo, mungafotokoze mmene angamvere mozama 1 Atesalonika 4:3-7 zimene zingawonjezere kumvetsa kwawo makhalidwe abwino achikristu ndi kuona kuti ndi ofunika kwambiri. Motero, kuphunzira kwanu kungakuthandizeni ndiponso kungathandize anthu ena ambiri kulemekeza Mulungu. Ndipo pano tangotchula chitsanzo chimodzi chokha cha m’kalata ya Paulo kwa Atesalonika. Pali mbali zina zambiri za makhalidwe abwino achikristu ndi zitsanzo zake za m’Baibulo ndiponso malangizo ake, zimene mungaphunzire, kuzigwiritsa ntchito ndi kuphunzitsa ena.
19. N’chifukwa chiyani mufunika kutsatira makhalidwe abwino achikristu?
19 N’zosachita kufunsa kuti n’kwanzeru kutsatira makhalidwe abwino achikristu. Pa Yakobo 3:17 amati “nzeru yochokera kumwamba,” ya Yehova Mulungu, “iyamba kukhala yoyera.” Zimenezi zikutanthauza kutsatira miyezo ya makhalidwe abwino ya Mulungu. Ndipotu, Yehova amafuna kuti amene akumuimira pophunzitsa Baibulo akhale zitsanzo zabwino “m’kuyera mtima.” (1 Timoteo 4:12) Mmene Paulo ndi Timoteo ankakhalira pa miyoyo yawo, zimachitira umboni kuti anali oyera. Anapeŵa makhalidwe oipa, moti Paulo mpaka analemba kuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa.”—Aefeso 5:3, 4.
20, 21. N’chifukwa chiyani mukugwirizana ndi zimene mtumwi Yohane analemba pa 1 Yohane 5:3?
20 Ngakhale kuti miyezo ya makhalidwe abwino ya m’Mawu a Mulungu ndi yomveka ndiponso yosapita m’mbali, iyo sili yolemetsa. Yohane, mtumwi amene anakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali kuposa atumwi ena onse, anachitira umboni zimenezi. Poona zimene anakumana nazo kwa zaka zambiri zimene anakhala ndi moyo, anadziŵa kuti makhalidwe abwino achikristu sanali ovulaza. M’malo mwake, iwo anali abwino ndiponso opindulitsa. Yohane anatsindika zimenezi pamene analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
21 Komabe onani kuti Yohane sananene kuti kumvera Mulungu mwa makhalidwe abwino achikristu ndiyo njira yabwino kokha chifukwa chakuti kumatithandiza kupeŵa mavuto amene tikanakumana nawo ngati sitikanamvera Mulungu. Anafotokoza bwino chifukwa chachikulu chomvera Mulungu mwa kusonyeza kuti kuchita zimenezi kumaonetsa chikondi chathu kwa Yehova Mulungu, mwayi wamtengo wapatali wosonyezera kuti timamukonda. Inde, kudziphunzitsa tokha kapena kuphunzitsa ena kukonda Mulungu kumafuna kuti tivomereze ndi kugwiritsa ntchito miyezo yake yapamwamba. Inde, kumatanthauza kudziphunzitsa tokha ndi kuphunzitsa ena makhalidwe abwino achikristu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Ngakhale kuti Josephus anafotokoza kuti Ayuda anali kulemekeza zinthu zopatulika, iye anafotokozanso lamulo la Mulungu motere: ‘Munthu aliyense asachitire mwano milungu imene anthu a mizinda ina amalambira, ndiponso asalande za mu akachisi, kapena kutenga chuma chimene anachipatulira kwa mulungu wina aliyense.’—Jewish Antiquities, Buku 4, mutu 8, ndime 10.
^ ndime 9 Buku lakuti Jewish Antiquities, Buku 18, mutu 3, ndime 5.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani tifunika kudziphunzitsa tokha tisanakaphunzitse ena?
• Kodi makhalidwe athu angakhudze bwanji mmene anthu angaonere Yehova?
• Kodi munthu wadama angaphwanye ufulu wa ndani?
• Kodi mwatsimikiza mtima kuchitanji pankhani ya makhalidwe abwino achikristu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 22]
“Malamulo ake sali olemetsa”