Malamulo a Mulungu Amatipindulitsa
Malamulo a Mulungu Amatipindulitsa
“Ha! Ndikondadi chilamulo chanu.”—SALMO 119:97.
1. Kodi anthu ambiri amakuona motani kumvera malamulo a Mulungu?
ANTHU ambiri masiku ano samvera malamulo a Mulungu. Amaona ngati kumvera wolamulira wosaoneka n’kupanda nzeru. Tikukhala m’nthaŵi imene anthu sakuona makhalidwe abwino kukhala ofunika kwenikweni koma kuti zimadalira kufuna kwa munthu kapena gulu la anthu amene akutsatira makhalidwe abwinowo. Anthu sasiyanitsa zabwino ndi zoipa ndiponso zoyenera ndi zosayenera. (Miyambo 17:15; Yesaya 5:20) Kufufuza kumene anachita posachedwapa pofuna kuona mmene anthu ambiri amaganizira anapeza kuti “anthu a ku America ambiri amafuna kusankha okha zimene akuona kuti n’zoyenera, zabwino ndiponso zaphindu.” Iwo amafuna “Mulungu wosakhwimitsa zinthu. Safuna malamulo okhwima. Safunanso atsogoleri okhulupirira kwambiri za makhalidwe abwino kapena zina zilizonse.” Katswiri wina wofufuza za chikhalidwe ananena kuti masiku ano, “munthu aliyense payekha amayembekezeka kudzisankhira moyo umene akuona kuti ndi wabwino ndiponso wotsatira makhalidwe abwino.” Anapitiriza kuti: “Wolamulira aliyense afunika kukonza malamulo ake kuti agwirizane ndi zofuna za anthu.”
2. Kodi kutchula koyamba za malamulo m’Baibulo kukugwirizana motani ndi madalitso ndiponso kuyanjidwa ndi Mulungu?
2 Popeza anthu ambiri akukayikira phindu la malamulo a Yehova, tifunika kulimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti miyezo ya Mulungu imatipindulitsa. N’zochititsa chidwi kuona nkhani imene malamulo anawatchula koyamba m’Baibulo. Pa Genesis 26:5, timaŵerenga Mawu a Mulungu kuti: “Abrahamu . . . [a]nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.” Yehova ananena zimenezi zaka zambirimbiri asanapereke Chilamulo cha Mose kwa mbadwa za Abrahamu. Kodi Mulungu anapatsa Abrahamu mphoto yotani chifukwa cha kumvera kwake, kuphatikizapo kumvera malamulo a Mulungu? Yehova Mulungu anam’lonjeza kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:18) Motero, kumvera malamulo a Mulungu n’kogwirizana kwambiri ndi madalitso ndiponso kuyanjidwa ndi Mulungu.
3. (a) Kodi wamasalmo wina anasonyeza maganizo otani pa malamulo a Yehova? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tifunika kuwaganizira?
3 Wamasalmo wina, yemwe mwinamwake anali kalonga wa Yuda amene kenako anadzakhala mfumu, anafotokoza maganizo osiyana ndi mmene anthu ambiri amaonera malamulo. Iye anauza Mulungu kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu.” (Salmo 119:97) Kumenekutu sikunali kungotengeka mtima chabe. Kunali kusonyeza kukonda chifuniro cha Mulungu chimene chili m’malamulo ake. Yesu Kristu, Mwana wangwiro wa Mulungu, analinso ndi maganizo ngati ameneŵa. Mawu olosera za Yesu amanena kuti iye anati: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.” (Salmo 40:8; Ahebri 10:9) Bwanji nanga ifeyo? Kodi timakonda kuchita zimene Mulungu amafuna? Kodi timakhulupirira kuti malamulo a Yehova ndi othandiza ndiponso opindulitsa? Kodi kumvera malamulo a Mulungu timakuika pati m’kulambira kwathu, pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, posankha zochita, ndiponso mmene timachitira zinthu ndi ena? Kuti tikonde malamulo a Mulungu tiyenera kudziŵa chifukwa chake Mulungu ali woyenerera kupanga malamulo ndi kuonetsetsa kuti tikuwatsatira.
Yehova Ndiye Wotipatsa Malamulo Woyenerera
4. N’chifukwa chiyani Yehova ndiye Wopereka Malamulo woyenerera kuposa wina aliyense?
4 Yehova monga Mlengi, ndiye Wopereka malamulo woyenerera kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse. (Chivumbulutso 4:11) Mneneri Yesaya anati: “Yehova ndiye wotipatsa malamulo.” (Yesaya 33:22) Iye wakhazikitsa amene tingati malamulo a chilengedwe amene amalamulira zinthu zamoyo ndi zopanda moyo. (Yobu 38:4-38; 39:1-12; Salmo 104:5-19) Munthu monga wolengedwa ndi Mulungu, amamvera malamulo a chilengedwe a Yehova. Ndipo ngakhale kuti munthu ali ndi ufulu wosankha ndipo amatha kuganiza mwanzeru payekha, amasangalala pokhapokha ngati agonjera malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino ndiponso auzimu.—Aroma 12:1; 1 Akorinto 2:14-16.
5. Kodi mfundo imene ili pa Agalatiya 6:7 ndi yoona motani pankhani ya malamulo a Mulungu?
5 Monga tikudziŵa, munthu sangaphwanye malamulo a Yehova a chilengedwe. (Yeremiya 33:20, 21) Ngati munthu satsatira malamulo a chilengedwe—mwachitsanzo, kukwera mumtengo wautali n’kudziponya—angaone zotsatira zake. Mofananamo, malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino n’ngosasinthika ndipo ngati munthu anyalanyaza kapena kuphwanya malamulowo amalandira chilango. Malamulo ameneŵa ngamphamvu monganso mmene alili malamulo ake achilengedwe, ngakhale kuti zotsatira zake mwina sizingaoneke msanga. “Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:7; 1 Timoteo 5:24.
Mbali Zimene Malamulo a Yehova Amakhudza
6. Kodi malamulo a Mulungu amakhudza mbali zotani?
6 Malamulo a Mulungu anawasonyeza bwino m’Chilamulo cha Mose. (Aroma 7:12) Patapita nthaŵi, Yehova Mulungu anaika “chilamulo cha Kristu” m’malo mwa Chilamulo cha Mose. * (Agalatiya 6:2; 1 Akorinto 9:21) Monga Akristu amene timatsatira “lamulo langwiro, ndilo laufulu,” timadziŵa kuti malangizo a Mulungu si ongokhudza mbali za moyo zochepa chabe, monga zikhulupiriro za chipembedzo kapena miyambo ayi. Miyezo yake imakhudza mbali zonse za moyo monga banja, zamalonda, mmene tingachitire zinthu ndi amene sali amuna kapena akazi anzathu, mmene timaonera Akristu anzathu, ndiponso kutenga nawo mbali pa kulambira koona.—Yakobo 1:25, 27.
7. Perekani zitsanzo za malamulo a Mulungu ofunika.
7 Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Inde, chigololo ndi dama sindizo “kusonyezana chikondi” chabe ayi.” Kugonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha sindiko “njira ina imene anthu angatsatire.” Kuchita zimenezi n’kuphwanya malamulo a Yehova. N’chimodzimodzinso ndi zinthu monga kuba, kunama, ndi kuneneza. (Salmo 101:5; Akolose 3:9; 1 Petro 4:15) Yakobo ananena kuti kudzikuza n’koipa ndipo Paulo anatilangiza kuti tipeŵe kulankhula zopanda pake kapena zopusa. (Aefeso 5:4; Yakobo 4:16) Kwa Akristu, malamulo a makhalidwe abwino onseŵa ali mbali ya malamulo olungama a Mulungu.—Salmo 19:7.
8. (a) Kodi malamulo a Mulungu ndi otani? (b) Kodi tanthauzo lenileni la liwu la Chihebri lakuti “chilamulo” n’lotani?
8 Malamulo ofunika ameneŵa a m’Mawu a Yehova akusonyeza kuti malamulo ake sindiwo chabe malamulo okhwima, opanikiza. Malamuloŵa Salmo 119:72) Liwu lakuti “chilamulo” monga mmene analigwiritsira ntchito wamasalmo, alitembenuza kuchokera ku liwu la Chihebri lakuti toh·rahʹ. Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo anati: “Liwu limeneli likuchokera ku verebu limene limatanthauza kulangiza, kutsogolera, kulondolera. Motero, tanthauzo lake . . . ndilo lamulo la makhalidwe.” Kwa wamasalmoyo, chilamulo chinali mphatso ya Mulungu. Kodi sitiyenera kulemekeza malamulo a Mulungu moteromo, kuwalola kuti atitsogolere?
angachititse munthu kukhala ndi moyo wabwino, wopindulitsa, ndipo amathandiza m’mbali zonse za makhalidwe. Malamulo a Mulungu ndi omangirira, oyenera, ndiponso olangiza bwino. (9, 10. (a) N’chifukwa chiyani timafunikira malangizo odalirika? (b) Kodi kuti tikhale osangalala ndiponso kuti zinthu zitiyendere bwino n’chiyani chokha chimene tingachite?
9 Zolengedwa zonse zimafunikira malangizo odalirika. Yesu ndi angelo ena, omwe ndi apamwamba kuposa anthu, amafunikiranso zimenezi. (Salmo 8:5; Yohane 5:30; 6:38; Ahebri 2:7; Chivumbulutso 22:8, 9) Ngati zolengedwa zangwiro zimenezi zimapindula ndi malangizo a Mulungu kuli bwanji anthu opanda ungwirofe! Zochitika m’mbiri ya anthu komanso zimene ifeyo taziona zimatsimikizira kuti zimene mneneri Yeremiya ananena n’zoona. Iye anati: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
10 Ngati tikufuna kukhala osangalala ndiponso kuti zinthu zitiyendere bwino, tiyenera kulola Mulungu kutitsogolera. Mfumu Solomo inazindikira kuopsa kotsatira zimene munthu ukufuna, osalola kuti Mulungu akutsogolere. Iye anati: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”—Miyambo 14:12.
Zifukwa Zokondera Chilamulo cha Yehova
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kufunitsitsa kudziŵa chilamulo cha Mulungu?
11 Tiyenera kufunitsitsa kudziŵa chilamulo cha Yehova. Wamasalmo anasonyeza kufunitsitsa kumeneko pamene anati: “Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwiza za m’chilamulo chanu.” (Salmo 119:18) Tikamudziŵa kwambiri Mulungu ndi njira zake, tidzazindikira mokwanira kuti mawu a Yesaya ndi oonadi. Amati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga.” (Yesaya 48:17, 18) Yehova amafuna ndi mtima wonse kuti anthu ake apeŵe tsoka ndi kukhala osangalala mwa kumvera malamulo ake. Tiyeni tione zifukwa zina zazikulu zimene tingakondere chilamulo cha Mulungu.
12. N’chifukwa chiyani kutidziŵa kwa Yehova kumam’chititsa kukhala Wopereka Malamulo wabwino kuposa wina aliyense?
12 Chilamulo cha Mulungu chimachokera kwa Salmo 139:1, 2; Machitidwe 17:24-28) Anzathu apamtima, achibale, ngakhale makolo athu sangatidziŵe bwino kwambiri monga mmene Yehova amatidziŵira. Ee, Mulungu amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziŵira eni akefe! Amene anatipanga amadziŵa zosoŵa zathu zauzimu, maganizo athu, ndiponso zofunika pa moyo wathu kuposa wina aliyense. Pochita nafe zinthu, amasonyeza kuti amadziŵa bwino kwambiri mmene tilili, zimene timafuna, ndiponso zolinga zathu. Yehova amadziŵa zofooka zathu, koma amadziŵanso kuti tingathe kuchita zinthu zopindulitsa. Wamasalmo anati: “Adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Motero, tingatetezeke mwauzimu tikamatsatira malamulo ake ndiponso kumulola ndi mtima wonse kuti azititsogolera.—Miyambo 3:19-26.
amene amatidziŵa bwino kwambiri. Popeza Yehova ndi amene anatilenga, n’zomveka kuti angatidziŵe bwino kwambiri. (13. N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti Yehova amadziŵa bwino kwambiri zinthu zimene zingatipindulitse?
13 Malamulo a Mulungu amachokera kwa amene amatikonda kwambiri. Mulungu amafunitsitsa kuti tidzakhale ndi moyo kosatha. Kodi sanalolere kupereka Mwana wake “dipo la anthu ambiri” ngakhale kuti zinali zopweteka? (Mateyu 20:28) Kodi Yehova sanalonjeze kuti ‘sadzalola kuti tiyesedwe koposa kumene tikhoza’? (1 Akorinto 10:13) Kodi Baibulo silimatitsimikizira kuti ‘amatisamalira’? (1 Petro 5:7) Palibe amene amakonda anthu ndi kuwafunira zabwino mwa kuwapatsa malangizo opindulitsa kwambiri kuposa mmene Yehova wachitira. Amadziŵa zinthu zimene zingatipindulitse ndiponso amadziŵa zimene zingatibweretsere chimwemwe ndi zimene zingatibweretsere chisoni. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro ndipo timalakwa, ngati tichita chilungamo, iye amatisonyeza chikondi m’njira zimene zingatithandize kukhala ndi moyo ndi kulandira madalitso.—Ezekieli 33:11.
14. Kodi chilamulo cha Mulungu chimasiyana ndi malangizo a anthu m’njira yofunika iti?
14 Chilamulo cha Mulungu n’chosasinthika. M’nthaŵi zovuta zimene tikukhala zino, Yehova ndiye mwala wosasunthika, amene alipo kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha. (Salmo 90:2) Anadzinena yekha kuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Miyezo ya Mulungu imene ili m’Baibulo ndi yodalirika kwambiri osati monga malangizo a anthu amene amasinthasintha. (Yakobo 1:17) Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri akatswiri a zamaganizo ankalimbikitsa kuti anthu azilera ana mowalekerera, koma kenako akatswiri ena anasintha maganizo awo n’kuvomereza kuti malangizowo anali olakwika. Miyezo ndi malangizo a anthu m’dzikoli pankhani imeneyi amapita uku ndi uku ngati kuti akuwombedwa ndi mphepo. Koma, Mawu a Yehova sasintha. Kwa zaka zambirimbiri, Baibulo lapereka malangizo a mmene makolo angalerere ana mwachikondi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) N’zosangalatsa kudziŵa kuti tingadalire miyezo ya Yehova; siidzasintha!
Phindu Limene Anthu Omvera Malamulo a Mulungu Amapeza
15, 16. (a) N’chiyani chingachitike ngati tigwiritsa ntchito miyezo ya Yehova? (b) Kodi malamulo a Mulungu angathandize bwanji m’banja?
15 Mulungu ananena kudzera mwa mneneri wake Yesaya kuti: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga . . . adzakula m’mene ndinawatumizira [“adzapambana,” NW].” (Yesaya 55:11) N’chimodzimodzinso ndi ife. Ngati tiyesetsa ndi mtima wonse kutsatira miyezo imene ili m’Mawu ake, tidzapambana, tidzachita zinthu zopindulitsa, ndipo tidzapeza chimwemwe.
16 Taonani mmene malamulo a Mulungu amathandizira kuti zinthu ziyende bwino m’banja. “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse; ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo Ahebri 13:4) Anthu okwatirana ayenera kulemekezana ndi kukondana. “Inu, yense payekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.” (Aefeso 5:33) Chikondi chimene chikufunika achifotokoza pa 1 Akorinto 13:4-8: “Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” Ukwati umene uli ndi chikondi choterechi sudzatha.
adzawaweruza Mulungu.” (17. Kodi tingapindule chiyani ngati tigwiritsa ntchito miyezo ya Yehova pankhani ya kumwa mowa?
17 Umboni winanso woti miyezo ya Yehova ndi yopindulitsa ndi woti amaletsa kuledzera. Amaletsanso ‘kumwetsa vinyo.’ (1 Timoteo 3:3, 8; Aroma 13:13) Anthu ambiri amene amanyalanyaza miyezo ya Mulungu pankhani imeneyi amadwala matenda amene amayamba kapena kukula chifukwa cha kumwetsa mowa. Anthu ena ponyalanyaza malangizo a Baibulo oletsa kumwa kwambiri, afika pokhala ndi chizoloŵezi cha kumwa kwadzaoneni kuti “asangalale.” Pali mavuto ambiri amene amabwera chifukwa cha kumwetsa mowa, monga kudzichotsera ulemu, kusoŵa mtendere pabanja kapena kutha kwa banja kumene, kuwononga ndalama, ndiponso kuchotsedwa ntchito. (Miyambo 23:19-21, 29-35) Motero, kodi miyezo ya Yehova pa nkhani ya kumwa mowa si yopindulitsa?
18. Kodi malamulo a Mulungu ndi othandiza pa nkhani ya zachuma? Fotokozani.
18 Miyezo ya Mulungu ndi yothandizanso Luka 16:10; Aefeso 4:28; Akolose 3:23) Akristu ambiri chifukwa chotsatira malangizo ameneŵa, awakweza pantchito kapena kupitiriza kugwira ntchito pamene anthu ena akuwachokocha. Munthu amapindulanso pankhani ya zachuma ngati apeŵa kuchita zinthu zimene Malemba amaletsa monga juga, kusuta, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Mosakayika, mungakhale ndi zitsanzo zina zosonyeza kuti miyezo ya Mulungu ndi yothandiza pankhani ya zachuma.
pankhani ya zachuma. Baibulo limalimbikitsa Akristu kukhala oona mtima ndiponso akhama. (19, 20. N’chifukwa chiyani n’kwanzeru kumvera ndi kutsatira malamulo a Mulungu?
19 N’kosavuta kwa anthu opanda ungwiro kupatuka pa malamulo ndi miyezo ya Mulungu. Taganizani za Aisrayeli pamene anali pa phiri la Sinai. Mulungu anawauza kuti: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu.” Anthuwo anayankha kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” Komatu sanachite zimenezo. (Eksodo 19:5, 8; Salmo 106:12-43) Mosiyana ndi amenewo, tiyeni timvere ndi kutsatira miyezo ya Mulungu.
20 N’kwanzeru ndiponso tingapeze chimwemwe ngati tipitiriza kutsatira malamulo apamwamba amene Yehova wapereka kuti atitsogolere. (Salmo 19:7-11) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tifunikanso kuzindikira kufunika kwa mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Imeneyi ndiyo mfundo yaikulu m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1996, masamba 14-24. M’menemo tinafotokoza mwatsatanetsatane “chilamulo cha Kristu.”
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti malamulo a Mulungu amatipindulitsa?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda chilamulo cha Yehova?
• Kodi malamulo a Mulungu ndi opindulitsa m’njira zotani?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 13]
Abrahamu anam’dalitsa kwambiri chifukwa chomvera malamulo a Yehova
[Zithunzi patsamba 15]
Nkhaŵa zobwera chifukwa cha moyo wotanganidwa wa masiku ano zimalepheretsa ambiri kutsatira malamulo a Mulungu
[Chithunzi patsamba 17]
Malamulo a Mulungu ndi okhazikika ndiponso osasinthika ngati nyumba yolondolera amalinyero yomangidwa pamwala