Mungathe Kugonjetsa Kusungulumwa
Mungathe Kugonjetsa Kusungulumwa
KODI ndani anganene kuti sanawawidwepo mtima chifukwa cha kusungulumwa? Pali zinthu zambiri zomwe zingatichititse kukhala osungulumwa. Komabe, makamaka kusungulumwa kwa akazi omwe sanakwatiwepo kapena amene amuna awo anamwalira kapena amene anasudzulidwa, kungakhale kopweteka kwambiri.
Mwachitsanzo, mtsikana wina wachikristu dzina lake Frances anasimba kuti: “Pamene ndimakwanitsa zaka 23, anzanga onse anali atakwatiwa ndipo ndinatsala ndekha.” * Pamene mwayi wokwatiwa ukunka nuchepa chifukwa cha kupita kwa zaka, kusungulumwa kungakule kwambiri. Sandra yemwe tsopano ali ndi zaka zothamangira m’ma 50, anati: “Sindinafune dala kukhala wosakwatiwa ndipo ndikufunabe n’takwatiwa ngati mwayi utapezeka.” Angela yemwe ali ndi zaka za m’ma 50 nayenso anati: “Sindinasankhe dala kukhala wosakwatiwa koma ndi mmene zinthu zakhalira. Abale osakwatira amene anali m’dera lomwe ndinkatumikira monga mpainiya wapadera anali ochepa chabe.”
Akazi ambiri achikristu tikuwayamikira chifukwa amasankha kukhala osakwatiwa potsatira mokhulupirika uphungu wa Yehova wa kukwatiwa “koma mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Ena amakhala bwinobwino osakwatiwa, koma ena zaka zikamapita chilakolako chofuna kukwatiwa ndi kukhala ndi ana chimakula. Sandra anavomereza kuti: “Nthaŵi zonse ndimavutika maganizo chifukwa choti ndilibe mwamuna.”
Zinthu zina monga ngati kusamalira makolo okalamba kungawonjezerenso kusungulumwa. Sandra anati: “Popeza ndine wosakwatiwa, banja lathu limayembekezera kuti ndizisamalira makolo athu okalamba. Ndasenza udindo umenewu kwa zaka 20 ngakhale kuti m’banja lathu tilimo ana asanu ndi mmodzi. Zinthu zikanakhala zopepukirapo ndikanakhala ndi mwamuna yemwe akanamandithandiza.”
Frances anatchula mbali inanso yomwe imawonjezera kusungulumwa kwake. Iye anati: “Nthaŵi zina anthu amandifunsa mwachindunji kuti, ‘N’chifukwa chiyani sukukwatiwa?’ Mawu ngati amenewo amandipatsa maganizo akuti sindikupeza banja chifukwa choti ndili ndi vuto. Pafupifupi ku ukwati kulikonse komwe ndapita, wina amandifunsa funso loumitsa pakamwa lakuti, ‘Kodi iwe ukwatiwa liti?’ Ndiyeno ndimayamba kuganiza kuti, ‘Ngati amuna okhwima mwauzimu sakundifunsira, ndiye kuti mwina ndilibe makhalidwe ofunika achikristu kapena mwina ndine wosakongola.’”
Kodi mungathetse bwanji maganizo akuti ena amakupatulani ndi kusungulumwa? Kodi ena angatani kuti athandize ngati n’kofunika kutero?
Dalirani Yehova
Wamasalmo anaimba kuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) M’Chihebri, mawu akuti “nkhaŵa” kwenikweni amatanthauza “mtolo” ndipo amanena za zovutitsa maganizo zomwe tingakhale nazo chifukwa cha zolemetsa m’moyo wathu. Yehova amadziŵa nkhaŵa zonsezi kuposa wina aliyense ndipo atha kutipatsa mphamvu zozithetsera. Kudalira Yehova Mulungu ndiko kwamuthandiza Angela kupirira vuto la kusungulumwa. Pa za utumiki wake wanthaŵi zonse, iye anati: “Pamene ndinkayamba upainiya, ine ndi mnzanga tinkakhala kutali ndi mpingo wathu. Tinaphunzira kudalira Yehova ndipo zimenezi zandithandiza kwambiri pa moyo wanga wonse. Ndikakhala ndi maganizo ofooketsa ndimauza Yehova ndipo amandithandiza. Lemba la Salmo 23 lakhala likundilimbikitsa nthaŵi zonse ndipo ndimaliŵerenga pafupipafupi.”
Mtumwi Paulo anali ndi vuto lalikulu kwambiri loti alipirire. Katatu konse ‘anapemphera kwa Ambuye kuti munga m’thupi uchoke kwa iye.’ Paulo sanathandizidwe mozizwitsa, koma analonjezedwa kuti chisomo cha Mulungu chidzamulimbikitsa. (2 Akorinto 12:7-9) Paulo anatulukiranso chinsinsi chokhala wokhutira. Kenako analemba kuti: “M’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:12, 13.
Kodi munthu angapeze bwanji mphamvu za Mulungu akataya mtima kapena kusungulumwa? Paulo analemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Sandra akugwiritsa ntchito langizo limeneli. Iye anati: “Popeza ndilibe mwamuna, nthaŵi zambiri ndimakhala ndekha. Zimenezi zimandipatsa mpata wokwanira wopemphera kwa Yehova. Ndimaona kuti ndili naye pafupi kwambiri ndiponso kuti nditha kumuuza momasuka mavuto anga ndiponso chimwemwe changa.” Frances nayenso anati: “Nthaŵi zonse pandekha ndimalimbana ndi maganizo ofooketsa, koma kuuza Yehova moona mtima mavuto anga kumandithandiza kwambiri. Ndimatsimikiza kuti Yehova amanditeteza ku zinthu zomwe zingandiwononge maganizo ndiponso mwauzimu.—1 Timoteo 5:5.
“Nyamuliranani Zothodwetsa”
M’gulu la abale achikristu, munthu safunika kunyamula yekha zothodwetsa. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.” (Agalatiya 6:2) Kucheza ndi Akristu anzathu kudzatithandiza kumva mawu abwino olimbikitsa omwe angachepetse kusungulumwa kwathu.—Miyambo 12:25.
Taganiziraninso zomwe Malemba amanena za mwana wamkazi wa Yefita, Woweruza wa Israyeli. Yefita asanapambane nkhondo yake yolimbana ndi magulu ankhondo a Amoni, analonjeza kuti adzapereka kwa Yehova chilichonse chomwe chidzayambe kutuluka m’nyumba yake kudzamulandira. Zinachitika kuti woyamba kutuluka anali mwana wake wamkazi. (Oweruza 11:30, 31, 34-36) Ngakhale kuti mwana wamkazi wa Yefita tsopano anali kudzakhala wosakwatiwa ndiponso kuchotsa cholinga chake chachibadwa chofuna kukhala pabanja, iye mofunitsitsa anatsatira lonjezo limenelo ndipo anatumikira ku malo opatulika ku Silo moyo wake wonse. Kodi kudzipereka kwakeko kunali kopanda phindu? Ayi, kunali kwaphindu kwambiri, moti “ana aakazi a Israyeli ankamuka chaka ndi chaka kum’lirira [“kumuyamikira,” NW] mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anayi pa chaka.” (Oweruza 11:40). Inde, kuyamikira kumalimbikitsa amene akuyamikiridwayo. Choncho, tiziyamikira anthu amene afunika kuwayamikira.
Ndibwinonso kuganizira chitsanzo cha Yesu. Ngakhale kuti sichinali chikhalidwe cha Ayuda kuti amuna azicheza ndi akazi, Yesu anacheza ndi Mariya ndi Marita. Iwo mwachionekere Luka 10:38-42) Tingatsatire chitsanzo cha Yesu mwa kuitana alongo athu auzimu osakwatiwa kuti adzasangalale nafe pamodzi komanso kukalalikira nawo. (Aroma 12:13) Kodi iwo amayamikira zimenezo? Mlongo wina anati: “Ndimadziŵa kuti abale onse amandikonda ndipo amandiona kukhala wofunika, koma ndimayamikira kwambiri ngati iwo paokha akusonyezadi chidwi chenicheni ndi ine.”
anali akazi amasiye kapena osakwatiwa. Yesu anafuna kuti onse aŵiri apindule mwauzimu kuchokera kwa iye. (Sandra anafotokoza kuti: “Popeza tilibe amuna, timafuna kwambiri kuti tizikondedwa, tizidziona kuti tili m’banja la abale ndi alongo auzimu.” N’zodziŵikiratu kuti Yehova amawasamalira anthu oterewa, ndipo timagwirizana naye pamene tikuwachititsa kudziona kukhala ofunika ndi okondedwa. (1 Petro 5:6, 7) Yehova amaona kuwaganizira koteroko, popeza kuti “wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.”—Miyambo 19:17.
“Yense Adzasenza Katundu Wake”
Ngakhale kuti ena angathandize ndipo thandizo lawolo lingakhale lolimbikitsa kwambiri, “yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Komabe, polimbana ndi vuto la kusungulumwa pali ngozi zomwe tiyenera kusamala nazo. Mwachitsanzo, kusungulumwa kungatigonjetse ngati titakhala wosachezeka. Mosiyana ndi zimenezo, tingagonjetse kusungulumwa mwa kugwiritsa ntchito chikondi. (1 Akorinto 13:7, 8) Mulimonse mmene zinthu zilili, kupatsa ndi kugaŵa ndiyo njira yabwino yopezera chimwemwe. (Machitidwe 20:35) Mlongo wina yemwe ndi mpainiya wolimbikira ntchito kwambiri, anati: “Sindikhala ndi nthaŵi yaikulu yoganizira zoti ndili ndekha. Ndikamaona kuti ndine wofunika ndiponso kuti ndine wotanganidwa, sindisungulumwa.”
Tiyeneranso kusamala kuti kusungulumwa kusatichititse kuyamba chibwenzi ndi munthu wosayenera. Mwachitsanzo, zingakhaletu zomvetsa chisoni kwambiri ngati titalola chilakolako chofuna kukwatiwa kutiphimba m’maso kuti tisaone mavuto ambiri omwe amadza chifukwa chokwatiwa ndi wosakhulupirira, ndipo makamaka ngati titalephera kuona ubwino wa uphungu wa m’Malemba woti tipeŵe kumangidwa m’goli loterolo. (2 Akorinto 6:14) Mkazi wina wachikristu yemwe anasudzulidwa ananena kuti: “Kumanga banja ndi munthu wosayenera ndiko chinthu choipitsitsa kusiyana ndi kukhala mbeta.”
Pakadali pano, vuto lomwe silingathetsedwe tiyenera kungolipirira. Mothandizidwa ndi Mulungu tingapirire vuto la kusungulumwa. Pamene tikupitirizabe kutumikira Yehova, titsimikizetu mtima kuti tsiku lina zofuna zathu zonse zidzakwaniritsidwa m’njira yabwino koposa.—Salmo 145:16.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mayina a akazi omwe mawu awo tawalemba m’nkhani ino asinthidwa.
[Zithunzi patsamba 28]
Tingathetse kusungulumwa mwa kupatsa ndi kugaŵa