Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi njoka ija m’munda wa Edene inalankhula motani kwa Hava pom’chititsa kuti aswe lamulo la Mulungu lokhudza mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa?

Genesis 3:1 amati: “Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Pakhala maganizo osiyanasiyana onena za mmene njoka inalankhulira kwa Hava. Maganizo ena ndi oti njokayo inalankhula pogwiritsa ntchito zizindikiro mwa kugwedeza thupi. Mwachitsanzo, Mngelezi wina yemwe ndi mtsogoleri wachipembedzo, Joseph Benson anati: “Zikuoneka ngati inalankhula pogwiritsa ntchito zizindikiro zinazake. N’zoona kuti ena amakhulupirira kuti nthaŵi imeneyo njoka zimatha kuganiza ndiponso kulankhula, . . . koma palibe umboni wakuti zimenezi zinalidi choncho.”

Komabe, kodi njokayo ikanamuuza bwanji Hava kuti akadya chipatso choletsedwacho adzakhala ngati Mulungu wakudziŵa zabwino ndi zoipa ngati inangogwiritsa ntchito zizindikiro chabe? Ndiponso, Hava naye analankhulapo mwa kuyankha funso limene njokayo inafunsa. (Genesis 3:2-5) Ganizo lakuti njokayo inalankhula pogwiritsa ntchito zizindikiro zokha lingatanthauze kuti nayenso Hava anayankha mwa kulankhula ndi manja, koma Baibulo limanena kuti analankhula ndi mawu.

Mtumwi Paulo pogwirizanitsa ndi zimene zinachitika m’munda wa Edenezi, anachenjeza Akristu anzake kuti: “Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Hava ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe.” Ngozi imene Paulo anali kuifotokoza inali yochokera kwa “atumwi onyenga, ochita ochenjerera.” “Atumwi oposatu” amenewo sanabweretse chiopsezo mwa kungogwiritsa ntchito zizindikiro kapena kulankhula ndi manja basi. Anagwiritsanso ntchito mawu awo mochenjera, omwe anali kulankhula ndi cholinga choti asocheretse anthu ena.​—2 Akorinto 11:3-5, 13.

Ngakhale kuti Hava anamusocheretsa m’munda wa Edene mwa kugwiritsa ntchito mawu, sitinganene kuti njoka yeniyeniyo inali ndi kholingo kuti ithe kulankhula. Sinafunikire kukhala nalo. Pamene mthenga wa Mulungu analankhula ndi Balamu kudzera mwa bulu, nyamayo sinafunikire kholingo lofanana ndi la munthu kuti ithe kulankhula. (Numeri 22:26-31) N’zachidziŵikire kuti pamene ‘bulu wopanda mawu, analankhula ndi mawu a munthu,’ mthengayo ndi amene anamulankhulitsa.​—2 Petro 2:16.

Baibulo limafotokoza kuti cholengedwa chauzimu chimene chinachititsa kuti njoka ilankhule kwa Hava ndicho “njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana.” (Chivumbulutso 12:9) Mawu amene Hava anamva ndi kuyankha anachokera kwa Satana amene “adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.”​—2 Akorinto 11:14.

[Chithunzi patsamba 27]

“Mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa”