Kodi Mukufuna Moyo Kapena Ndalama?
Kodi Mukufuna Moyo Kapena Ndalama?
Mwina munamvapo kuti mbava zinalozetsa mfuti kumaso kwa munthu, zikumanena kuti: “Kodi mukufuna moyo kapena ndalama?” Lerolino, mawu otchuka ameneŵa akumveka m’vuto lothetsa nzeru limene limakhudza tonsefe makamaka amene akukhala m’mayiko olemera. Ulendo uno, si mbava zomwe zikunena mawu ameneŵa ayi. M’malo mwake, akunenedwa ndi mkhalidwe wokonda ndalama ndi chuma womwe anthu akuwutamanda mowonjezereka kwambiri.
KUKONDETSA chuma kotereku kwadzetsa mavuto atsopano ndiponso nkhaŵa zochuluka. Kodi tiyenera kulolera kutaya chiyani kuti tipeze ndalama ndi chuma? Kodi tingakhutire ndi chuma chochepa chabe? Kodi anthu akulolera kutaya “moyo weniweniwo” n’cholinga chopeza chuma chochuluka? Kodi ndalama ndizo njira yopezera moyo wachimwemwe?
Kukonda Ndalama Monkitsa
Pazinthu zomwe anthu amazifuna ndi kuzilakalaka, kaya mwachibadwa kapena ayi, kukonda ndalama kumaposa zonse. Mosiyana ndi chilakolako cha kugonana ndi kufuna chakudya, kukonda ndalama sikutha nthaŵi zonse. Ngakhale ukalamba sumathetsa kukonda ndalama. Nthaŵi zambiri munthu akamakalamba m’pamenenso amawonjezera kukonda kwake ndalama ndi kudera nkhaŵa kwambiri za katundu yemwe angagule.
Dyera landalama likukula mofulumira kwambiri. Munthu wina wa m’filimu ina yotchuka kwambiri ananena kuti: “Dyera landalama likugwiradi ntchito yake ndipo ndi lopindulitsa kwambiri.” Ngakhale kuti anthu ambiri amanena kuti zaka zapakati pa 1980 ndi 1990 zinali Zaka za Dyera Landalama, zomwe zinkachitika zakazi zisanafike ndiponso pambuyo pake, zikusonyeza kuti m’zaka zonsezi anthu sanasinthe kwenikweni zochita zawo pankhani ya ndalama.
Mwinamwake chomwe chasintha n’chakuti anthu ambiri akupeza mwayi wokhutiritsa chikhumbo chawo cha chuma mofulumira kwambiri. Zikuoneka kuti anthu ambiri padziko lapansi amathera nthaŵi komanso mphamvu zawo zochuluka popanga ndi kupeza chuma chochuluka m’moyo wawo. Mungavomereze kuti kukhala ndi chuma ndiponso kugwiritsa ntchito ndalama kwangosanduka chinthu chosangalatsa chomwe anthu akuyesetsa kupeza m’moyo wamasiku ano.
Koma kodi anthu akusangalala chifukwa cha zimenezi? Poyankha funso limeneli zaka 3,000 zapitazo, Mfumu yanzeru ndi yolemerayo Solomo inalemba kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.” (Mlaliki 5:10) Maphunziro amakono a chikhalidwe cha anthu amanenanso chimodzimodzi.
Ndalama Ndiponso Chimwemwe
Chodabwitsa kwambiri pa zomwe ena apeza chokhudza khalidwe la anthu n’chakuti, kupeza ndalama ndi kukundika chuma sikukhutiritsa kapena kubweretsa chimwemwe chowonjezereka mofanana n’chumacho. Ofufuza ambiri apeza kuti munthu akalemera kufika pamlingo winawake, kukhutira ndi chimwemwe chake zimadalira pa kuchuluka kwa chuma chomwe ali nacho.
N’chifukwa chake kufunafuna chuma ndi ndalama monkitsa kumachititsa anthu ambiri kudzifunsa kuti: ‘Timaoneka ngati timasangalala ndi
chinthu chatsopano chilichonse chimene tagula, koma n’chifukwa chiyani tikaziganizira zonse pamodzi sizimatikhutiritsa mowonjezereka?’Wolemba mabuku wotchedwa Jonathan Freedman m’buku lake lakuti Happy People ananena kuti: “Munthu akangopeza phindu pang’ono, kuchuluka kwa ndalama zomwe ali nazo sikumam’patsa chimwemwe chokwanira ayi. Ndipo akafika poti walemera, chuma chomwe wapezacho sichigwirizana kwenikweni ndi chimwemwe.” Anthu ambiri azindikira kuti chofunika kwambiri kuti munthu akhale wachimwemwe ndicho kukhala ndi chuma chauzimu, kufunafuna zinthu zothandizadi pa moyo, ndiponso makhalidwe abwino. Chofunika chinanso ndicho kuyanjana ndi anzathu ndiponso kupeŵa mikangano kapena kaduka zomwe zingatilepheretse kusangalala ndi zomwe tili nazo.
Ambiri amaona kuti chizoloŵezi choyesa kuthetsa mavuto amumtima pogwiritsa ntchito ulemerero ndicho magwero a mavuto ambiri a chikhalidwe cha anthu masiku ano. Othirira ndemanga pa za chikhalidwe amanena za mtima woipa ndi wosakhutira. Iwo aonanso kuti chizoloŵezi chofunsira kwa madokotala kapena chofunafuna moyo wabwino ndi mtendere wamumtima kwa alangizi otchuka, magulu ampatuko, ndiponso odzinenera kuti amapereka thandizo chikukula kwambiri m’mayiko olemera. Zimenezi zikutsimikiza kulephera kwa chuma kubweretsa moyo weniweni.
Mphamvu Ndiponso Kupanda Mphamvu kwa Ndalama
Kunena zoona, ndalama zili ndi mphamvu. Zitha kugula nyumba yabwino, zovala zokongola, ndiponso mipando yooneka bwino. Zithanso kugula chikondi, mgwirizano, chinyengo, ngakhalenso mabwenzi akanthaŵi chabe. Ndalama zitha kuchita zonsezi. Koma ndalama sizingagule zinthu zomwe timafuna kwambiri monga chikondi cha bwenzi lenileni, mtendere wamumtima, chilimbikitso chochokera pansi pa mtima imfa ikayandikira. Ndipo kwa anthu amene amaonadi unansi wawo ndi Mlengi kukhala wamtengo wapatali, ndalama sizingagule chiyanjo cha Mulungu.
Mfumu Solomo imene inali ndi zinthu zonse zabwino zomwe ndalama zikanagula m’nthaŵi yake, inazindikira kuti kudalira chuma sikubweretsa chimwemwe chokhalitsa. (Mlaliki 5:12-15) Ndalama zitha kuwonongeka chifukwa cha kulephera kwa banki kapena kukwera mtengo kwa zinthu. Munda waukulu ungawonongeke ndi mvula ya mkuntho. Ngakhale kuti mainshuwalansi amabwezeretsa katundu wowonongeka kumlingo winawake, samathetsa kuvutika maganizo. Chuma ndi ndalama zosungidwa zingakhale zopanda phindu nkhani ya chuma itasokonezeka mwadzidzidzi. Ngakhale ntchito ya malipiro abwino ingathe kutha nthaŵi iliyonse.
Ndiyeno, kodi ndalama tingazione motani m’njira yoyenera? Kodi ndalama ndi chuma ziyenera kuchita mbali yotani pa moyo wathu? Chonde pitirizani kupenda nkhaniyi kuti muone mmene mungapezere chinthu chamtengodi wapatali—“moyo weniweniwo.”
[Zithunzi patsamba 4]
Chuma sichibweretsa chimwemwe chokhalitsa