Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kondwerani ndi Mulungu Wachimwemwe

Kondwerani ndi Mulungu Wachimwemwe

Kondwerani ndi Mulungu Wachimwemwe

“Chotsalira, abale, kondwerani. . . . Ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.”​—2 AKORINTO 13:11.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anthu ambiri sakondwera m’moyo? (b) Kodi chimwemwe n’chiyani, nanga tingachikulitse motani?

M’MASIKU oopsa ano, anthu ambiri amaona kuti palibe chifukwa chokondwera. Tsoka likawagwera kapena likagwera wokondedwa wawo, amalingalira ngati Yobu wakaleyo, yemwe anati: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Akristu nawonso amavutika m’mtima chifukwa cha zochitika ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’ zino, ndipo si zodabwitsa kuti atumiki okhulupirika a Yehova nthaŵi zina amataya mtima.​—2 Timoteo 3:1.

2 Komabe, Akristu angakhale achimwemwe, ngakhale m’kati mwa chiyeso. (Machitidwe 5:40, 41) Kuti mumvetse mmene zimenezi zingathekere, choyamba lingalirani tanthauzo la chimwemwe. Chimwemwe ndicho “chisangalalo chimene munthu ali nacho mumtima chifukwa chakuti wapeza kapena akuyembekezera chinthu chinachake chosangalatsa.” * Chotero, pamene tikusinkhasinkha za madalitso omwe tikuyembekezera m’dziko latsopano la Mulungu, tingakondwere mwa kulingaliranso modekha za madalitso omwe tili nawo panopa.

3. Kodi tinganene kuti aliyense ali n’zifukwa zokhalira wokondwa m’lingaliro lotani?

3 Aliyense ali ndi mbali inayake yabwino yomwe amathokoza nayo Mulungu. Mwamuna m’banja atha kum’chotsa ntchito. Ndipo mwachibadwa amada nkhaŵa. Ali ndi udindo wopezera okondedwa ake zofunika. Koma ngati ali ndi nyonga komanso thanzi labwino, amanyadira kwambiri. Akapeza ntchito amatha kuigwira modzipereka chifukwa chakuti ndi wanyonga komanso wathanzi labwino. Chitsanzo china, mkazi wachikristu angathe kudwala mwadzidzidzi matenda opha ziwalo. Komabe, angathokoze anzake achikondi komanso am’banja lake omwe am’thandiza kuthetsa matenda akewo mwaulemu komanso molimba mtima. Ndipotu Akristu onse oona, kaya akukumana n’zotani, amakondwera pom’dziŵa Yehova, ‘Mulungu wachimwemwe,’ ndi Yesu Kristu, mwini Mphamvu wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11; 6:15) Inde, Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndi achimwemwe chochuluka. Akhalabe achimwemwe ngakhale kuti zinthu padziko lapansi n’zosiyana kwambiri ndi mmene Yehova anafunira pachiyambi. Chitsanzo chawo chingatiphunzitse zochuluka za mmene tingakhalirebe achimwemwe.

Sanasoŵepo Chimwemwe

4, 5. (a) Kodi Yehova anachitanji anthu oyambawo atapanduka? (b) Kodi Yehova anakhalabe ndi malingaliro abwino m’njira iti pochita ndi mtundu wa anthu?

4 M’munda wa Edene, Adamu ndi Hava anali ndi thanzi labwino ndipo maganizo awo anali angwiro. Anali ndi ntchito yopindulitsa yoti agwire ndipo anali ndi malo oyenera ogwirira ntchito imeneyo. Choposa zonsezi, anali ndi mwayi wolankhula ndi Yehova nthaŵi ndi nthaŵi. Cholinga cha Mulungu chinali chakuti anthu ameneŵa adzasangalale m’tsogolo mwawo monse. Koma makolo athu oyambawo sanakhutire ndi mphatso zabwino zonsezi; iwo anaba chipatso choletsedwa mu “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” Kusamvera kumeneku ndiko maziko a masoka onse omwe ife, mbadwa zawofe, tikukumana nawo lerolino.​—Genesis 2:15-17; 3:6; Aroma 5:12.

5 Komabe, Yehova sanalole kuti mtima wosayamika wa Adamu ndi Hava um’chotsere chimwemwe chake. Anali wotsimikiza kuti mitima ya zina mwa mbadwa zawo ikawasonkhezera kumutumikira. Kunena zoona, anali wotsimikiza kwabasi, mwakuti Adamu ndi Hava asanabale n’komwe mwana wawo woyamba, Yehova analengezeratu chifuno chake chowombola mbadwa zawo zokhulupirika! (Genesis 1:31; 3:15) M’zaka mazana otsatira, anthu ambiri anatsatira mapazi a Adamu ndi Hava, koma Yehova sananyalanyaze mtundu wa anthu chifukwa cha kusamvera kosanenekako. Mmalo mwake, anasonyeza chidwi kwambiri mwa amuna ndi akazi omwe ‘anakondweretsa mtima wake,’ anthu amene anayesetsa mwakhama kuti amukondweretse chifukwa chakuti amam’konda.​—Miyambo 27:11; Ahebri 6:10.

6, 7. Kodi n’zinthu ziti zomwe zinam’thandiza Yesu kukhalabe wachimwemwe?

6 Nanga bwanji Yesu​—kodi anakhalabe wachimwemwe motani? Monga cholengedwa chauzimu champhamvu kumwamba, Yesu anali ndi mwayi wonse woona zochita za amuna ndi akazi padziko lapansi. Zochita zawo zopanda ungwiro sizinali zachilendo kwa iye, komabe Yesu anawakonda. (Miyambo 8:31) Pambuyo pake, atabwera padziko lapansi “nakhazikika pakati” pa anthu, anali kuwaonabe chimodzimodzi. (Yohane 1:14) N’chiyani chinathandiza Mwana wa Mulungu wangwiroyo kukhalabe ndi malingaliro ake abwinowo okhudza anthu ochimwa?

7 Choyamba, Yesu sanali kuchita zinthu kapena kuyembekezera kuti ena achite mopambanitsa. Ankadziŵa kuti si anthu onse apadziko lapansi omwe adzawatembenuza mitima. (Mateyu 10:32-39) Chotero anali kukondwera munthu mmodzi yekha wokhulupirika akalandira uthenga wa Ufumu. Ngakhale kuti makhalidwe komanso malingaliro a ophunzira ake nthaŵi zina sanali oyenera, Yesu ankadziŵa kuti kwenikweni mtima wawo unali wofunitsitsa kuchita chifuno cha Mulungu, ndipo ankawakonda pachifukwa chimenechi. (Luka 9:46; 22:24, 28-32, 60-62) Komanso, popemphera kwa Atate wake wakumwamba, Yesu anatchula mwachidule zabwino zomwe ophunzirawo anali atachita podzafika nthaŵiyo. Iye anati : “Anasunga mawu anu.”​—Yohane 17:6.

8. Tchulani zina mwa njira zomwe tingatsanzirire Yehova ndi Yesu pambali ya kukhalabe achimwemwe.

8 Mosakayika, tonsefe tingapindule ngati titalingalira mosamalitsa zitsanzo zomwe Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anasonyeza pambali imeneyi. Kodi tingam’tsanzire kwambiri Yehova mwinamwake mwa kusadera nkhaŵa mopambanitsa ngati zinthu sizikuchitika monga momwe timayembekezera? Kodi tingalondole mapazi a Yesu mosamala kwambiri mwa kukhalabe ndi malingaliro abwino pamene tikuona mmene zinthu zilili panopa, komanso mwa kusayembekezera kuchita kapena kuti ena achite zinthu zomwe sangakwanitse? Tiyeni tione mmene tingagwiritsire bwino ntchito zina mwa mfundo zimenezi m’ntchito yomwe Akristu achangu kwina kulikonse amaikonda kwambiri​—utumiki wakumunda.

Khalanibe ndi Malingaliro Abwino Okhudza Utumiki

9. Kodi Yeremiya anayambanso motani kukondwera, ndipo kodi chitsanzo chake chingatithandize motani?

9 Yehova amafuna kuti tikhale okondwa pomutumikira. Chimwemwe chathu sichiyenera kungodalira zotsatira zimene timapeza. (Luka 10:17, 20) Mneneri Yeremiya analalikira m’gawo losapindula kwa zaka zambiri. Atalingalira za kusamvera kwa anthu, Yeremiya sanalinso wachimwemwe. (Yeremiya 20:8) Koma atasinkhasinkha za ubwino wa uthengawo, Yeremiya anayambanso kukondwera. Yeremiya anauza Yehova kuti: “Mawu anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mawu anu anakhala kwa ine chikondwerero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova.” (Yeremiya 15:16) Inde, Yeremiya anakondwera m’ntchito yake yolalikira Mawu a Mulungu. Nafenso tingatero.

10. Kodi tingakondwerebe motani muutumiki ngakhale kuti panopa gawo lathu n’losapindula?

10 Ngakhale anthu ambiri akane kumvetsera uthenga wabwino, ife tili ndi chifukwa chabwino zedi chokhalira okondwa pamene tili muutumiki wakumunda. Kumbukirani kuti Yehova anali wotsimikizira ndi mtima wonse kuti anthu ena adzasonkhezereka kumutumikira. Mofanana ndi Yehova, nafenso tisataye mtima, tikhalebe otsimikiza kuti nthaŵi inayake ena adzaona kufunika kwa nkhani ya ufumu wapadziko lonse ndipo adzamvera uthenga wa Ufumu. Tisaiwale kuti zinthu zimasintha m’moyo wa anthu. Akagwa m’tsoka kapena m’mavuto osayembekezeka, ngakhale munthu womva zake zokha angayambe kuganizira mwakuya za tanthauzo la moyo. Kodi ndinu wokonzeka kuthandiza pamene anthu oterowo ‘azindikira kusoŵa kwawo kwauzimu’? (Mateyu 5:3) Inde, n’kutheka kuti winawake m’dera lanulo ndi wokonzeka kumvetsera uthenga wabwino mukam’fikiranso kachiŵiri!

11, 12. Kodi m’tauni ina kunachitika zotani, nanga zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

11 Gawo lathu lingathenso kusintha. Lingalirani chitsanzo ichi. M’tauni inayake yaing’ono, munkakhala kagulu ka mabanja achinyamata ogwirizana kwabasi ndipo anali ndi ana. Mboni za Yehova zikafika, pakhomo lililonse zimalandira yankho limodzimodzi lakuti, “Sitikufuna kumvetsera zimenezo!” Wina akangosonyeza chidwi ndi uthenga wa Ufumu, mofulumira anzake amamufooketsa ndi kumuuza kuti alekeretu kugwirizana ndi Mboni. N’zodziŵikiratu kuti kulalikira m’dera limeneli kunali kovuta. Ngakhale zinali choncho, Mbonizo sizinagwe mphwayi, zinapitirizabe kulalikira. Zotsatira zake zinali zotani?

12 Patapita nthaŵi, ana ambiri m’tauni imeneyo anakula, kukwatira, ndi kumanga nyumba zawo komweko. Pozindikira kuti zochitika m’moyo wawo sizinawapatse chimwemwe chenicheni, ena mwa achinyamata ameneŵa anayamba kufunafuna choonadi. Anapeza choonadicho, atamvetsera mwachidwi uthenga wabwino umene Mboni zinali kulengeza. Chotero pambuyo pa zaka zambiri, mpingo waung’onowo unayamba kukula. Tangoganizani mmene ofalitsa Ufumu amene anachitabe khamawo anasangalalira! Nafenso tipitirizebe mwakhama kuuza ena uthenga waulemerero wa Ufumu ndipo zidzatidzetsera chimwemwe!

Okhulupirira Anzanu Adzakuthandizani

13. Kodi tiyenera kudalira yani ngati chinachake chatifooketsa?

13 Mavuto akachuluka kapena mukagwa m’masoka, kodi mungadalire ndani kuti akulimbikitseni? Choyambirira atumiki odzipereka a Yehova mamiliyoni ambiri amamfikira Yehova m’pemphero, ndipo pambuyo pake amafikira abale ndi alongo awo achikristu. Ali padziko lapansi, Yesu mwiniyo anaona kufunika kwa thandizo la ophunzira ake. Usiku wa tsiku la imfa yake, anauza ophunzira akewo kuti “ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga.” (Luka 22:28) N’zoona kuti ophunzirawo anali opanda ungwiro, koma kukhulupirika kwawo kunalimbikitsa Mwana wa Mulungu. Nafenso olambira anzathu angatilimbikitse.

14, 15. Kodi n’chiyani chinathandiza banja lina kupirira, mwana wawo atamwalira, nanga kodi mukuphunzira chiyani pa zomwe zinawachitikirazo?

14 Michel ndi Diane omwe ndi banja lachikristu, anaona kufunika kwa thandizo la abale ndi alongo awo achikristu. Mwana wawo wa zaka 20, Jonathan, yemwe anali wamphamvu komanso wa ziyembekezo zabwino zam’tsogolo, anamupeza ndi matenda otupa ubongo. Madokotala anayesetsa kumuthandiza, koma matendawo anakula kwambiri mwakuti tsiku lina madzulo, Jonathan anamwalira. Michel ndi Diane anali achisoni kwambiri. Anadziŵa kuti Msonkhano wa Utumiki womwe unali m’kati madzulo amenewo unali utatsala pang’ono kutha. Popeza kuti ankafuna kwambiri woti awalimbikitse, anapempha mkulu yemwe anali nawo limodzi kuti atsagane nawo ku Nyumba ya Ufumu. Anafika kumeneko mpingo utangouzidwa kumene za imfa ya Jonathan. Msonkhano utatha, makolo achisoniwo anazingidwa ndi abale ndi alongo awo, ndipo anawakumbatira ndi kuwauza mawu otonthoza. Pokumbukira Diane anati: “Pofika kunyumba yaufumu tinali otaya mtima kwabasi, koma abale kumeneko anatilimbikitsa zedi! Ngakhale kuti sanathe kuchotseratu chisoni chathucho, koma anatithandiza mwa kutilimbikitsa m’nthaŵi yachisoniyo!”​—Aroma 1:11, 12; 1 Akorinto 12:21-26.

15 Tsoka linachititsa Michel ndi Diane kuyandikira abale ndi alongo awo. Linachititsanso aŵiriwo kudalirana kwambiri. Michel anati: “Ndaphunzira kudalira mkazi wanga wokondedwa mowonjezereka. Tikakumana ndi zofooketsa, timakambirana za choonadi cha Baibulo komanso mmene Yehova akutisamalira.” Powonjezera Diane anati: “Chiyembekezo cha Ufumu chikutithandiza kwambiri panopa.”

16. N’chifukwa chiyani kuuza abale athu za mavuto athu mosazengereza kuli kofunika?

16 Inde, abale ndi alongo athu achikristu angakhale ‘chotonthoza mtima’ kwa ife m’nthaŵi zovuta m’moyo ndipo mwakutero angatithandize kukhalabe achimwemwe. (Akolose 4:11) Komatu sangadziŵe zomwe zili m’maganizo mwathu. Choncho pamene tikufuna kuti atithandize, ndi bwino kuwauza mavuto athu. Mwa kutero tidzayamikira kuchokera pansi pamtima chilimbikitso chilichonse chimene abale athu adzatha kutipatsa, ndipo tidzachiona monga chochokera kwa Yehova.​—Miyambo 12:25; 17:17.

Yang’anani Mumpingo Wanu

17. Kodi nakubala wina yemwe alibe mwamuna amakumana ndi mavuto otani, nanga kodi anthu otereŵa timawaona motani?

17 Mukayang’anitsitsa olambira anzanu, mudzazindikira kuti ngofunika kwabasi ndipo mudzasangalala kucheza nawo. Yang’anani mumpingo wanu. Kodi mukuonamo chiyani? Kodi muli kholo lopanda mwamuna lomwe likuyesetsa kulera ana ake m’njira yachoonadi? Kodi mwaganizirapo mozama za chitsanzo chabwino chimene mlongoyo akusonyeza? Yesani kuganiza mavuto ena amene akukumana nawo. Mayi wopanda mwamuna yemwe dzina lake ndi Jeanine anatchula ena mwa mavuto ameneŵa: kusukidwa, kuumirizidwa kuchita zoipa ndi amuna kuntchito, kuchepa kwa ndalama. Koma iye anati chovuta kwambiri pazonsezi ndi kukwaniritsa zosoŵa zam’maganizo za mwana aliyense, chifukwa chakuti mwana aliyense amalingalira mosiyana ndi anzake. Jeanine anatchulanso vuto lina: “N’zovuta zedi kupeŵa chizoloŵezi choona mwana wamwamuna ngati mutu wabanja, kuloŵa m’malo mwa bambo amene kulibe. Ndili ndi mwana wamkazi, koma nthaŵi zambiri zimandivuta kukumbukira kuti sindiyenera kumulemetsa mwa kumuunjikira mavuto anga achinsinsi.” Mofanana ndi anakubala masauzande ambiri oopa Mulungu omwe akulera okha ana, Jeanine ali pantchito ndipo amasamalira banja lake. Amaphunziranso Baibulo ndi ana ake, kuwaphunzitsa utumiki, ndi kupita nawo kumisonkhano yampingo. (Aefeso 6:4) Yehova ayeneratu kuti akusangalala zedi kuona banja limeneli tsiku ndi tsiku likuyesetsa kuchitabe mokhulupirika! Kodi sitikukondwera mumtima kukhala ndi anthu otereŵa pakati pathu? Inde, timakondwera kwabasi.

18, 19. Fotokozani mmene tingawonjezere kuyamikira kwathu anthu ena mumpingo.

18 Yang’ananinso mumpingo wanu. Muonamo akazi amasiye okhulupirika kapena amuna okhulupirika omwe akazi awo anamwalira, ameneŵa saphonya misonkhano. (Luka 2:37) Kodi amasukidwa nthaŵi zina? Amatero kumene. Amafunitsitsa ali limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wawo! Komabe amatanganidwa ndi kutumikira Yehova komanso amapanga ubwenzi ndi ena. Mtima wawo wabwino ndi wodekha umawonjezera chimwemwe mumpingo! Mkristu wina amene watumikira mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zoposa 30 anati: “Chimodzi mwa zinthu zomwe zimandikondweretsa kwambiri ndicho kuona abale ndi alongo achikulire amene akumana ndi ziyeso zambiri koma akutumikirabe Yehova mokhulupirika!” Inde, Akristu achikulire omwe ali pakati pathuwa amalimbikitsa kwambiri achinyamata.

19 Nanga bwanji za atsopano omwe angoyamba kumene kusonkhana ndi mpingo? Samatilimbikitsa kodi akamasonyeza chikhulupiriro chawo m’misonkhano? Taganizirani mmene apitira patsogolo kuchokera pamene anayamba kuphunzira Baibulo. Yehova akukondwera nawo ameneŵa. Kodi ife tikutero? Kodi timasonyeza kuyamikira kwathu, kuwathokoza chifukwa cha khama lawo?

20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti aliyense amachita mbali yofunika mumpingo?

20 Kodi ndinu wokwatira kapena wokwatiwa, mbeta, kapena ndinu kholo lopanda mwamuna kapena mkazi? Kodi ndinu mnyamata kapena mtsikana wopanda bambo (kapena mayi)? Kodi ndinu mkazi wamasiye kapena mwamuna amene mkazi wake anamwalira? Kodi mwagwirizana ndi mpingo kwa zaka zambiri kapena kodi mwangoyamba kumene kusokhana? Dziŵani tsono kuti chitsanzo chanu cha kukhulupirika n’cholimbikitsa kwa tonsefe. Ndipo mukamaimba nyimbo za Ufumu limodzi ndi ena, mukayankha kapena kukhala m’pulogalamu ya ophunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Teokalase, zonse zimene m’machita zimawonjezera chimwemwe chathu. Koposa zonse, zimakondweretsa mtima wa Yehova.

21. Kodi tili ndi zifukwa zambiri zochitira chiyani, koma kodi pali mafunso otani?

21 Inde, ngakhale m’nthaŵi yamavuto ino, tingakhale okondwa polambira Mulungu wathu wachimwemwe. Tili ndi zifukwa zambiri zolabadirira mawu olimbikitsa a Paulo akuti: “Kondwerani. . . . Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.” (2 Akorinto 13:11) Nanga bwanji ngati takumana ndi tsoka lachilengedwe, mazunzo, kapena mavuto aakulu azachuma? Kodi n’zotheka kukhalabe achimwemwe m’mikhalidwe ngati imeneyi? Yesani kupeza nokha yankho pamene mukuphunzira nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 119, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungathe Kuyankha?

• Kodi chimwemwe tanthauzo lake n’chiyani?

• Kodi kukhalabe ndi malingaliro abwino kungatithandize motani kukhalabe achimwemwe?

• N’chiyani chomwe chingatithandize kukhala ndi malingaliro abwino okhudza gawo la mpingo wathu?

• Kodi abale ndi alongo m’mpingo wanu m’mawaona kukhala ofunika m’njira ziti?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Anthu a m’gawo lathu angasinthe

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi anthu mumpingo wanu akukumana ndi mavuto otani?