Kulalikira Ufumu ku Altiplano ku Peru
Ndife a Iwo Omwe Ali Ndi Chikhulupiriro
Kulalikira Ufumu ku Altiplano ku Peru
PAKATI pa mtandadza wa kum’maŵa ndi wa kumadzulo wa mapiri a Andes—m’malire a Bolivia ndi Peru—pali Altiplano. Dzina lakeli limatanthauza “chigwa cha pamalo okwera,” kapena kuti “malo athyathyathya a pamwamba paphiri.” Mbali yake yaikulu ili m’dziko la Bolivia.
Altiplano n’ngwautali wa makilomita 100 m’lifupi mwake ndi makilomita oposa 1,000 m’litali mwake, ndipo ali pamalo okwera, pa avareji mamita ngati 3,700 kuchokera pamwamba pa nyanja ya mchere. Mutakwera ndege kupita ku Altiplano kuchokera ku Lima, likulu la dziko la Peru, lomwe lili m’mphepete mwa nyanja, mudzadutsa pa phiri la El Misti. Phiri lavokano limeneli n’lokutidwa ndi chipale chofeŵa, ndipo n’lalitali kwambiri, mamita 5,822. Mudzaona nsonga zazitali zamapiri za mamita oposa 6,000 zokutidwa ndi chipale chofeŵa. Nsonga zimenezi n’zamapiri otalikirana a Nevado Ampato ndi Nevado Coropuna. Mwamsanga mudzaonano dambo lalikulu—Altiplano wa kum’mwera kwa Peru.
Likulu la Altiplano wa Peru ndilo Puno, ndipo lili kumpoto cha kumadzulo kwa Nyanja ya Titicaca, yomwe ndiyo nyanja yokhala pokwera kwambiri kuposa nyanja ina iliyonse padziko lapansi yotheka kuyendamo ndi sitima. Popeza kuti derali lili pamalo okwera kuposa makilomita atatu, alendo obwera kumeneku zimawatengera nthaŵi kuti agwirizane ndi mpweya wa kumeneku. M’mphepete mwa Nyanja ya Titicaca m’makhala amwenye amtundu wa Quechua ndi Aymara. Amwenye ameneŵa mungawaone akugwira ntchito m’minda yawo ing’onoing’ono, yotchedwa chacra, atavala zofiira, zobiriŵira, kapena zabluu. Ngakhale kuti Chisipanya ndicho chinenero chachikulu ku Peru, anthu a ku Altiplano amalankhulanso zinenero za Quechua ndi Aymara.
Kutsogolera Ntchito Yolalikira
Posachedwapa, anthu ambiri odzichepetsa ndi olimbikira ntchito olankhula zinenero za Quechua ndi Aymara adziŵa choonadi cha Baibulo. Mokulira, zimenezi zatheka chifukwa chakuti Yehova wadalitsa kwambiri khama la alaliki a Ufumu anthaŵi zonse omwe akutumikira ngati apainiya apadera.
Mwachitsanzo, José ndi Silvia omwe ndi apainiya apadera, anawatumiza kukatumikira ku tauni ya Putina, pafupifupi makilomita 50 kuchokera ku Nyanja ya Titicaca. M’miyezi iŵiri yokha, Silvia anayambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba okwana 16, ndipo José okwana 14. M’miyezi isanu ndi umodzi yokha, chiŵerengero cha ofalitsa a mumpingo chinakwera kuchoka pa 23 ndi kufika pa 41. Komanso chiŵerengero cha ofika m’misonkhano chakwera kuchoka pa 48 ndi kufika chiŵerengero chapamwamba cha 132.
José akuti: “Poyamba misonkhano yampingo m’midzi yotalikirana imeneyi, tinaona kuti n’kothandiza kuyamba ndi Msonkhano Wapoyera ndi Phunziro la Buku la Mpingo. Zimenezi zimathandiza osonyeza chidwi atsopano kuyamba kupezeka m’misonkhano mosavuta.”
Alongo aŵiri—mmodzi mpainiya—anali oyamba kutengera uthenga wabwino ku mudzi wakutali wa kwawokha wa Muñani, pafupifupi makilomita 20 kuchokera ku Putina. Kumeneko anayamba kuphunzira Baibulo ndi mwamuna wina wosaona wotchedwa Lucio. * Anaitanira mng’ono wake Miguel, mmishonale wakatolika wopanda udindo wina uliwonse m’tchalitchi komanso mtsogoleri wam’mudzimo yemwe amakhala m’dera lina lapafupi. Anthu akam’funsa Miguel chifukwa chimene amapitira ku Muñani mlungu uliwonse, amati amapita kukaphunzira za Yehova ndi Mawu ake. Ndiyeno panabuka funso lakuti: “N’chifukwa chiyani ife kuno sitiphunzira Baibulo?” Chifukwa cha chidwi chomwe anthu am’mudzi wa Miguel anasonyeza, posapita nthaŵi, Mbonizo zinakonza zomakachitira misonkhano kumeneko.
Miguel anayamba kuuza ena zomwe amaphunzirazo. Koma bwanji za ntchito yake ija monga mmishonale wakatolika wopanda udindo wina uliwonse m’tchalitchi komanso wachiŵiri kwa bwanamkubwa? Pamsonkhano womwe unachitikira m’holo ina yam’mudzimo, Miguel analengeza kuti watula pansi ntchito yake monga mmishonale wakatolika. Kodi anaika munthu wina m’malo mwake? Munthu wina m’khamu la anthulo anati: “Tifuniranjinso
mmishonale wina pamene tikuphunzira choonadi?” Inde, choonadicho amanena zinthu zomwe Mboni za Yehova zimaphunzitsa. Munthu winanso anati: “Sitikugwirizana n’zoti iwe wekha uchoke m’Katolika. Ena tonsefe tilekeranji kuchokamo?” Onse amene analipo panthawiyo anafuula mogwirizana kuti: “Tonsefe tachokamo!”Zitangotha zimenezi, pamsonkhano womwe unachitika m’mudzimo panakambidwa nkhani yokhudza mafano ndi mtanda. Mwamuna wina anapempha osonkhana onse kuŵerenga Deuteronomo 7:25, lomwe limati: “Mafano osema a milungu yawo muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golidi zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.”
Kenako mwamunayu anapempha omwe anagwirizana ndi mfundo yotentha mafano onse kuti aimike manja awo. Nthaŵi yomweyo anthu onse anaimika manja. (Machitidwe 19:19, 20) Panopa mabanja 23 mwa mabanja 25 am’mudzimo akuphunzira Mawu a Mulungu. Anthu aŵiri ndi ofalitsa osabatizidwa, ndipo mabanja asanu akukonzekera zokalembetsa ukwati wawo mwalamulo n’cholinga chakuti akhale oyera pamaso pa Yehova.—Tito 3:1; Ahebri 13:4.
Kuphunzitsa ndi Nkhani za Pakaseti
Popeza kuti odziŵa kuŵerenga n’ngochepa ku Altiplano, nkhani za m’mavidiyo ndi m’makaseti a Watch Tower za m’zinenero zakomweko n’zothandiza kwambiri—ngakhale pochititsa maphunziro a Baibulo a panyumba. Pogwiritsa ntchito makaseti a wailesi, mpainiya wina wapadera wotchedwa Dora amachititsa maphunziro m’bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Akamvetsera ndime imodzi pakaseti, amafunsa wophunzira Baibuloyo mafunso kuchokera m’nkhani imene wamvetserayo.
Nyumba youlutsa mawu pawailesi yakomweko kaŵirikaŵiri imaulutsa nkhani zotengedwa m’zigawo zina za bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji la m’chinenero cha Quechua. Imateronso ndi zigawo zina za m’magazini ya Galamukani! ya Chisipanya. Chotero, anthu ambiri amamva uthenga wa Ufumu ndipo amafunitsitsa kuphunzira zambiri Mboni za Yehova zikafika panyumba pawo.
Anthu ambiri sadziŵa n’komwe kuti kuli Altiplano koma Mulungu akudziŵa. Tim’thokoze Yehova chifukwa chakuti amakonda anthu, anthu ambiri okhala m’malo okwera pa Altiplano wa Andes akukhala mbali ya namtindi wa anthu olemekeza nyumba yake yaikulu ya kulambira koona.—Hagai 2:7.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Tagwiritsa ntchito mayina ena ongoyerekezera m’nkhani ino.