Munthu Wopatsa Adzadalitsidwa
KUYAMBIRA kalekale anthu akhala akupereka nsembe polambira Yehova. Aisiraeli ankapereka nsembe za nyama ndipo Akhristu akhala akupereka nsembe zotamanda Mulungu. Koma palinso nsembe zina zimene Mulungu amasangalala nazo. (Aheb. 13:15, 16) Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza kuti munthu akapereka nsembe zoterezi amakhala wosangalala ndipo amadalitsidwa.
Hana ankatumikira Mulungu mokhulupirika ndipo ankafunitsitsa mwana wamwamuna koma anali wosabereka. Iye anapemphera kwa Yehova n’kulonjeza kuti akadzakhala ndi mwana wamwamuna adzamupereka “kwa Yehova masiku onse a moyo wake.” (1 Sam. 1:10, 11) Patapita nthawi, Hana anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina loti Samueli. Mwanayo atangosiya kuyamwa, anapita naye kuchihema mogwirizana ndi lonjezo lake. Yehova anadalitsa Hana chifukwa cha mtima wake wodzimana. Iye anakhalanso ndi ana ena 5 ndipo Samueli anakhala mneneri komanso wolemba Baibulo.—1 Sam. 2:21.
Masiku anonso Akhristu ali ndi mwayi wotumikira Mlengi wawo ndi moyo wawo wonse. Yesu ananena kuti anthu amene amalolera kudzimana zinthu zina n’cholinga choti atumikire Yehova adzadalitsidwa kwambiri.—Maliko 10:28-30.
Nthawi ya atumwi, panali Mkhristu wina dzina lake Dorika amene ankakonda “kuchita ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.” Koma kenako “anadwala n’kumwalira” ndipo mpingo wonse unadandaula kwambiri. Ndiyeno ophunzira atamva kuti Petulo ali m’deralo anamupempha kuti afike mwamsanga. Petulo atafika anaukitsa Dorika ndipo anthu anasangalala kwambiri. M’Baibulo, aka n’koyamba kuti mtumwi aukitse munthu. (Mac. 9:36-41) Mulungu sanaiwale nsembe zimene Dorika ankapereka. (Aheb. 6:10) Zimene ankachita pothandiza anthu zinalembedwa m’Baibulo kuti zikhale chitsanzo kwa ifeyo.
Mtumwi Paulo anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani yodzipereka kuti athandize anthu ena. Iye analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Ineyo ndidzagwiritsa ntchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipereka ndi moyo wanga wonse chifukwa cha miyoyo yanu.” (2 Akor. 12:15) Paulo anaona umboni wakuti munthu akamadzipereka kuti athandize ena amasangalala, koma chofunika kwambiri n’chakuti amasangalatsa Yehova ndipo amadalitsidwa.—Mac. 20:24, 35.
Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amasangalala tikamadzipereka kwambiri kuti timutumikire komanso tithandize anzathu. Koma kodi pali njira zina zimene tingathandizire pa ntchito yolalikira? Inde zilipo. Kuwonjezera pa ntchito zathu zachikondi, tikhoza kulemekeza Mulungu tikamapereka ndalama zathu. Ndalama zimenezi zimathandiza pa ntchito yolalikira komanso posamalira amishonale ndi atumiki ena a nthawi zonse. Zimathandizanso pokonza ndi kumasulira mabuku ndi mavidiyo, kusamalira amene akumana ndi ngozi zadzidzidzi komanso kumanga Nyumba za Ufumu. Choncho tisamakayikire kuti munthu wopatsa adzadalitsidwa kwambiri. Komanso tikamapereka zinthu zathu zamtengo wapatali kwa Yehova timasonyeza kuti timamulemekeza kwambiri.—Miy. 3:9; 22:9.