Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 12

Kodi Mukuona Zimene Zekariya Anaona?

Kodi Mukuona Zimene Zekariya Anaona?

“‘Koma mzimu wanga,’ watero Yehova wa makamu.”​—ZEK. 4:6.

NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Ayuda omwe anali ku ukapolo ankayembekezera zinthu zosangalatsa ziti?

 AYUDA anasangalala kwambiri. Yehova “analimbikitsa mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya” kuti imasule Aisiraeli omwe anakhala zaka zambiri ku Babulo monga akapolo. Mfumuyo inalengeza kuti Ayuda angabwerere kwawo “n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (Ezara 1:1, 3) Zimenezitu zinali zosangalatsa kwambiri. Izi zinatanthauza kuti Ayuda akayambiranso kulambira Mulungu woona m’dziko limene iye anawapatsa.

2. Kodi Ayuda omwe anabwerera kuchoka ku ukapolo atangofika ku Yerusalemu anakwanitsa kuchita chiyani?

2 Mu 537 B.C.E., Ayuda oyambirira kuchoka ku ukapolo anafika ku Yerusalemu, likulu la ufumu wakum’mwera wa Yuda. Pasanapite nthawi, iwo anayamba kumanga kachisi ndipo pofika mu 536 B.C.E., anali atamaliza kale kumanga maziko ake.

3. Kodi Ayuda anatsutsidwa bwanji?

3 Komabe Ayudawo atangoyamba kumanganso kachisiyo, anthu anayamba kuwatsutsa kwambiri. Anthu owazungulira “anakhala akufooketsa manja a anthu a ku Yuda ndi kuwagwetsa ulesi pa ntchito yomanga.” (Ezara 4:4) Zimenezi zinali zovuta kwa Ayudawo, koma zinthu zinaipa kuposa pamenepa. Mu 522 B.C.E., mfumu yatsopano ya ku Perisiya dzina lake Aritasasita, inayamba kulamulira. * Otsutsawo anaona kusintha kwa ulamuliroko ngati mwayi wawo woti aletseretu ntchito yomangayo ‘poyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo.’ (Sal. 94:20) Iwo anauza Mfumu Aritasasita kuti Ayudawo ankapangana zoti aukire ufumu wake. (Ezara 4:11-16) Mfumuyo inakhulupirira mabodza a anthuwo ndipo inaletsa ntchito yomanga kachisiyo. (Ezara 4:17-23) Izi zinachititsa kuti Ayuda asiye ntchito imene ankasangalala nayo yomanga kachisi.​—Ezara 4:24.

4. Kodi Yehova anatani anthu atayamba kutsutsa ntchito yomanga kachisi? (Yes. 55:11)

4 Anthu a m’dzikolo omwe sankalambira Yehova komanso akuluakulu ena mu ulamuliro wa Perisiya, ankafunitsitsa kuletsa ntchito yomanga kachisi. Koma Yehova anali atatsimikiza kuti ntchito yomangayo isaime, ndipo nthawi zonse iye amakwaniritsa cholinga chake. (Werengani Yesaya 55:11.) Iye anawapatsa Ayuda mneneri wolimba mtima dzina lake Zekariya ndipo anamuonetsa masomphenya 8, ochititsa chidwi kuti awafotokozere n’cholinga choti awalimbikitse. Masomphenyawo anawathandiza kuona kuti sankafunika kuopa anthu omwe ankawatsutsa ndipo anawalimbikitsa kuti apitirize kugwira ntchito ya Yehova. M’masomphenya a nambala 5, Zekariya anaona choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi.

5. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

5 Tonsefe nthawi zina timakumana ndi zofooketsa. Choncho tingapindule poganizira mmene Yehova analimbikitsira Aisiraeli pogwiritsa ntchito masomphenya a a Zekariya a nambala 5. Kumvetsa masomphenyawa kungatithandize kuti tizitumikira Yehova mokhulupirika tikamatsutsidwa, zinthu zikasintha pa moyo wathu komanso tikalandira malangizo omwe sitikuwamvetsa.

TIKAMATSUTSIDWA

Zekariya anaona masomphenya a mitengo iwiri ya maolivi, yomwe inkathira mafuta muchoikapo nyale chomwe chinali ndi nyale 7 (Onani ndime 6)

6. Kodi masomphenya a choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi ofotokozedwa pa Zekariya 4:1-3, analimbikitsa bwanji Ayuda? (Onani chithunzi chapachikuto.)

6 Werengani Zekariya 4: 1-3. Masomphenya a choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi anathandiza Ayuda kukhala olimba mtima pamene ankatsutsidwa. Motani? Kodi mwaona kuti choikapo nyalecho chinkakhala ndi mafuta nthawi zonse? Mafuta ankachoka kumitengo ya maoliviyo n’kuthiridwa m’mbale yolowa ndipo kenako ankapita kunyale 7, zomwe zinali pa choikapo nyale. Mafuta amenewa ankachititsa kuti nyalezo zisamazime. Zekariya anafunsa kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani?” Mngeloyo anamuyankha pomuuza uthenga wochokera kwa Yehova kuti: “‘Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,’ watero Yehova wa makamu.” (Zek. 4:4, 6) Mafuta ochokera ku mitengoyo ankaimira mzimu woyera wa Yehova womwe ndi wamphamvu komanso suutha. Mphamvu za mzimu wa Mulungu zinali zochuluka kwambiri kuposa mphamvu za gulu la nkhondo la ufumu wa Perisiya. Mothandizidwa ndi Yehova, anthu omwe ankamanga kachisi akanagwira ntchito yawo mpaka kuimaliza ngakhale kuti ankatsutsidwa. Uthenga umenewu unali wolimbikitsa kwambiri. Zimene Ayudawo ankangofunika kuchita ndi kudalira Yehova n’kuyambiranso kugwira ntchito. Ndipotu zimenezi ndi zomwe anachitadi ngakhale kuti ntchitoyi inali idakali yoletsedwa.

7. Kodi ndi kusintha kuti kumene kunachititsa kuti mtima wa omanga kachisi ukhale m’malo?

7 Kusintha kwina kunachititsa kuti mtima wa omanga kachisiwo ukhale m’malo. Kusintha kotani? Mu 520 B.C.E., Dariyo Woyamba, anayamba kulamulira ku Perisiya. M’chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, iye anazindikira kuti kuletsa ntchito yomanga kachisiyo kunali kosemphana ndi malamulo. Choncho Dariyo anapereka chilolezo kuti ntchitoyo imalizidwe. (Ezara 6:1-3) Nkhani imeneyi inadabwitsa aliyense. Komatu panalinso zina zomwe zinachitika. Mfumu inalamula kuti anthu ozungulira kumeneko asiye kusokoneza komanso azipereka ndalama ndi zinthu zina zofunika pa ntchitoyo. (Ezara 6:7-12) Zotsatira zake, mu 515 B.C.E., Ayuda anamaliza kumanga kachisiyo patangopita zaka 4 zokha.​—Ezara 6:15.

Muzidalira mphamvu za Yehova mukamatsutsidwa (Onani ndime 8)

8. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala olimba mtima mukamatsutsidwa?

8 Masiku anonso atumiki a Yehova ambiri amatsutsidwa. Mwachitsanzo, ena amakhala m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. M’mayiko amenewa, abale athu akhoza kumangidwa ‘n’kutengeredwa kwa abwanamkubwa ndi mafumu’ kuti ukhale umboni kwa iwo. (Mat. 10:17, 18) Nthawi zina kusintha kwa ulamuliro kungachititse kuti zinthu zikhaleko bwino. Kapena woweruza wina wachifundo angapereke chiweruzo chomwe chingachititse kuti tikhale ndi ufulu wolambira. A Mboni ena amatsutsidwanso m’njira ina. Iwo amakhala m’mayiko amene kulambira Yehova si koletsedwa koma amatsutsidwa ndi achibale omwe amafunitsitsa kuti iwo asiye kulambira Mulungu. (Mat. 10:32-36) Nthawi zambiri, otsutsawo akazindikira kuti zomwe akuchita poyesetsa kufooketsa achibale awo omwe ndi a Mboni sizikuphula kanthu, amasiya. Ndipotu ena omwe ankatsutsidwa, pambuyo pake anakhala abale ndi alongo akhama kwambiri. Inunso mukamatsutsidwa musamafooke. Muzikhala olimba mtima. Yehova amakuthandizani ndi mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu. Choncho palibe choti muziopa.

ZINTHU ZIKASINTHA

9. N’chifukwa chiyani Ayuda ena anakhumudwa maziko a kachisi watsopano atamangidwa?

9 Maziko a kachisi watsopano atangomangidwa, Ayuda ena achikulire anayamba kulira. (Ezara 3:12) Iwo anaona ulemerero wa kachisi yemwe Solomo anamanga ndipo ankaganiza kuti kachisi yemwe adzamangidweyo sadzakhala ndi ulemerero “poyerekeza” ndi kachisi woyamba. (Hag. 2:2, 3) Iwo anakhumudwa chifukwa choyerekezera kachisi wakale ndi watsopanoyo. Koma masomphenya a Zekariya akanawathandiza kuti ayambirenso kusangalala. Kodi zimenezi zikanatheka bwanji?

10. Kodi mawu a mngelo opezeka pa Zekariya 4:8-10, anathandiza bwanji Ayuda kuti asakhalenso okhumudwa?

10 Werengani Zekariya 4:8-10. Kodi mngelo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Ayuda “adzasangalala ndi ntchito imeneyi ndipo adzaona chingwe cha mmisiri womanga nyumba m’dzanja la [bwanamkubwa wa Ayuda] Zerubabele”? Chingwe cha mmisiri womanga nyumba chimathandiza mmisiriyo kudziwa ngati chinachake chawongoka. Choncho mngeloyo ankatsimikizira anthuwo kuti ngakhale kuti kachisiyo sankaoneka wogometsa kwa anthu ena, adzamalizidwa ndipo adzakhala wogwirizana ndi zimene Yehova amafuna. Yehova akanasangalala ndi kachisiyo, choncho iwonso ankafunika kusangalala naye. Chofunika kwambiri kwa Yehova chinali choti kulambira kochitika pakachisipo kukhale kovomerezeka kwa iye. Ayudawo akanamaganizira kwambiri zokhudza kulambira Yehova movomerezeka, komanso kuti iye azisangalala nawo, iwo akanayambiranso kukhala osangalala.

Muziona zinthu moyenera zinthu zikasintha (Onani ndime 11-12) *

11. Kodi n’chiyani chomwe chimakhala chovuta kwa atumiki ena a Yehova masiku ano?

11 Ambirife timavutika zinthu zikasintha. Ena omwe akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa nthawi yaitali, utumiki wawo unasintha. Chifukwa cha uchikulire, ena anafunika kusiya utumiki womwe ankaukonda. Si zachilendo kukhala wokhumudwa zinthu zikasintha chonchi pa moyo wathu. Mwina poyamba sitingamvetse bwinobwino kapena kuvomereza zomwe zachitika. Tikhoza kumaona kuti kale m’pamene zinthu zinali bwino. Mwina tingafooke n’kumaona kuti panopa sitingachitenso zambiri potumikira Yehova. (Miy. 24:10) Ndiye kodi masomphenya a Zekariya angatithandize bwanji kuti tizichita zonse zimene tingathe potumikira Mulungu?

12. Kodi masomphenya a Zekariya angatithandize bwanji ngati takhumudwa chifukwa cha zomwe zasintha pa moyo wathu?

12 N’zosavuta kuvomereza zinthu zikasintha ngati tikuona zinthu mmene Yehova akuzionera. Iye akuchita zinthu zambiri masiku ano, ndipo tili ndi mwayi waukulu wokhala antchito anzake. (1 Akor. 3:9) Utumiki wathu ungasinthe koma Yehova sasiya kutikonda. Choncho ngati kusintha kwina m’gululi kwakukhudzani, musamachedwe n’kuganizira chifukwa chake zinthu zasintha choncho. M’malo momalakalaka ‘zinthu zakale’ muzipemphera kwa Yehova n’kumaona zabwino zomwe zachitika chifukwa cha kusinthako. (Mlal. 7:10) M’malo moganizira zimene simungakwanitsenso kuchita, muziganizira zomwe mungathe kuchita. Masomphenya a Zekariya akutiphunzitsa kufunika kokhala ndi maganizo oyenera. Choncho tidzapitiriza kukhala osangalala komanso okhulupirika ngakhale zinthu zitasintha pa moyo wathu.

ZIKAKHALA ZOVUTA KUTSATIRA MALANGIZO

13. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ena akanaganiza kuti malangizo oti ayambirenso kumanga kachisi anali osamveka?

13 Ntchito yomanganso kachisi inali italetsedwa. Komabe amuna amene ankatsogolera ntchitoyo, omwe ndi mkulu wa ansembe Yesuwa (Yoswa) ndi Bwanamkubwa Zerubabele, “ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu.” (Ezara 5:1, 2) Kwa Ayuda ena, zimenezi zikanaoneka zosamveka. Adani awo akanadziwa kuti iwo ayambiranso ntchito yomanga kachisi ndipo akanachita chilichonse kuti awalepheretse kugwira ntchitoyi. Amuna awiriwa, Yoswa ndi Zerubabele, ankafunika umboni wowatsimikizira kuti Yehova akuwathandiza. Iwo anapezadi umboni umenewu. Motani?

14. Mogwirizana ndi Zekariya 4:12, 14, kodi mkulu wa ansembe Yoswa ndi Bwanamkubwa Zerubabele anapatsidwa umboni wotani?

14 Werengani Zekariya 4:12, 14. M’masomphenyawa, mngelo anafotokozera mneneri wokhulupirika wa Mulungu kuti mitengo iwiri ya maolivi ikuimira “odzozedwa awiri,” omwe ndi Yoswa ndi Zerubabele. Mngeloyo ananena kuti zinali ngati amuna awiriwa amaimirira “kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi,” Yehova. Umenewutu unali mwayi waukulu kwambiri chifukwa zinkasonyeza kuti Yehova ankawadalira. Choncho Aisiraeli akanatha kukhulupirira malangizo alionse amene amunawa akanawapatsa chifukwa Yehova ankawagwiritsa ntchito kuti aziwatsogolera.

15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza malangizo a Yehova opezeka m’Mawu ake?

15 Njira imodzi imene Yehova amaperekera malangizo kwa atumiki ake masiku ano ndi kudzera m’Mawu ake, Baibulo. M’buku lopatulikali, iye amatifotokozera zimene tingachite kuti tizimulambira movomerezeka. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza malangizo amene timapeza m’Mawu a Mulungu? Tingatero tikamayesetsa kupeza nthawi yowawerenga komanso kuwamvetsa bwino. Dzifunseni kuti, ‘Ndikamawerenga Baibulo kapena mabuku athu, kodi ndimaima kaye n’kuganizira mozama zomwe ndawerengazo? Kodi ndimafufuza tanthauzo la mfundo za m’Baibulo zomwe ndi “zovuta kuzimvetsa”? Kapena kodi ndimangoziwerenga mothamanga?’ (2 Pet. 3:16) Tikamayesetsa kupeza nthawi yoganizira zimene Yehova akutiphunzitsa, tidzatha kutsatira malangizo ake komanso kukwanitsa kugwira ntchito yolalikira.​—1 Tim. 4:15, 16.

Muzikhulupirira malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” (Onani ndime 16) *

16. Ngati sitikumvetsa bwino malangizo amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watipatsa, kodi n’chiyani chingatithandize kuwatsatira?

16 Njira ina imene Yehova amatipatsira malangizo ndi kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Nthawi zina kapoloyu angatipatse malangizo omwe sitikuwamvetsa bwino. Mwachitsanzo, angatipatse malangizo enaake otikonzekeretsa kuti tidzapulumuke pa nthawi ya ngozi za m’chilengedwe zimene tikuona ngati sizingachitike m’dera lathu. Kapenanso tingaone ngati kapoloyu akukhwimitsa zinthu pa nthawi ya mliri winawake. Ndiye kodi tingatani ngati tikuona kuti malangizo amene tapatsidwa ndi osathandiza? Tiyenera kuganizira mmene Aisiraeli anapindulira chifukwa chotsatira malangizo amene anapatsidwa kudzera mwa Yoswa ndi Zerubabele. Tingaganizirenso nkhani zina za m’Baibulo zimene tinawerenga. Nthawi zina anthu a Mulungu ankapatsidwa malangizo ooneka ngati osathandiza koma akawatsatira ankapulumutsa moyo wawo.​—Ower. 7:7; 8:10.

MUZIONA ZIMENE ZEKARIYA ANAONA

17. Kodi masomphenya a choikapo nyali ndi mitengo iwiri ya maolivi, anathandiza bwanji Ayuda?

17 N’kutheka kuti masomphenya a nambala 5 amene Zekariya anaona anali aafupi. Koma anathandiza Ayuda kukhala ndi maganizo oyenera pa ntchito yawo komanso kulambira kwawo. Ndipo atachita zinthu mogwirizana ndi masomphenyawo, anaona kuti Yehova ankawathandiza mwachikondi komanso kuwatsogolera. Pogwiritsa ntchito mzimu wake womwe ndi wamphamvu, Yehova anawathandiza kuti apitirize kugwira ntchito yawo komanso kuti ayambirenso kusangalala.​—Ezara 6:16.

18. Kodi masomphenya a Zekariya angakuthandizeni bwanji?

18 Masomphenya a Zekariya a choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi, angakuthandizeni kwambiri pa moyo wanu. Monga mmene taonera, masomphenyawa angakuthandizeni kupeza mphamvu zimene mumafunikira mukamatsutsidwa, chimwemwe chimene mumafunikira zinthu zikasintha pa moyo wanu komanso chikhulupiriro chimene mumafunikira kuti mukhalebe omvera mukapatsidwa malangizo amene simukuwamvetsa. Kodi muyenera kutani mukakumana ndi mavuto? Choyamba, muziona zimene Zekariya anaona, zomwe ndi umboni wakuti Yehova akusamalira anthu ake. Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi umboniwo pokhulupirira Yehova komanso kupitirizabe kumulambira ndi mtima wanu wonse. (Mat. 22:37) Mukamachita zimenezi, Yehova adzakuthandizani kuti muzimutumikira mosangalala mpaka kalekale.​—Akol. 1:10, 11.

NYIMBO NA. 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

^ ndime 5 Yehova anaonetsa mneneri Zekariya masomphenya osiyanasiyana ochititsa chidwi. Zimene Zekariya anaona zinathandiza iyeyo komanso anthu a Mulungu kupeza mphamvu zowathandiza kulimbana ndi mavuto omwe ankakumana nawo, pomwe ankabwezeretsa kulambira koona. Masomphenyawo angatithandizenso ifeyo kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale tikukumana ndi mavuto. Munkhaniyi tikambirana mfundo zofunika zomwe tingaphunzire pa masomphenya a Zekariya okhudza choikapo nyale ndi mitengo ya maolivi.

^ ndime 3 Patapita zaka, munthawi ya Bwanamkubwa Nehemiya, wolamulira wina yemwenso dzina lake anali Aritasasita anachita zinthu mokoma mtima kwa Ayuda.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akuona kufunika kozolowera kusintha komwe kwachitika pa moyo wake chifukwa cha uchikulire komanso matenda.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akuganizira mfundo yakuti Yehova amathandiza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ngati mmene anathandizira Yoswa ndi Zerubabele.