Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mawu akuti “Mudzawayang’anira” opezeka pa Salimo 12:7, akunena za “ovutika” (vesi 5) kapena “mawu a Yehova” (vesi 6)?

Nkhani yonse ikusonyeza kuti mawu a muvesili akunena za anthu.

Pa Salimo 12:1-4, timawerenga kuti “anthu okhulupirika atheratu pakati pa anthu.” Tsopano tiyeni tikambirane Salimo 12:5-7, omwe ndi mavesi amene pachokera funsoli. Mawu ake amati:

Yehova wanena kuti: “‘Chifukwa chakuti ovutika akuponderezedwa

Chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,

Ndidzanyamuka nʼkuchitapo kanthu,

Ndidzawapulumutsa kwa anthu amene akuwanyoza.’

Mawu a Yehova ndi oyera.

Ali ngati siliva woyengedwa mungʼanjo yadothi nthawi zokwanira 7.

Inu Yehova mudzawayangʼanira.

Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.”

Vesi 5 likufotokoza zimene Mulungu adzachitire anthu “ovutika.” Iye adzawapulumutsa.

Vesi 6 limawonjezera kuti “Mawu a Yehova ndi oyera. Ali ngati siliva woyengedwa.” Izi zikusonyeza mmene Akhristu onse odzipereka amamvera ponena za Mawu a Mulungu.​—Sal. 18:30; 119:140.

Tsopano tiyeni tikambirane vesi lotsatira, la Salimo 12:7, lomwe limati: “Inu Yehova mudzawayangʼanira. Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.” Kodi mawu akuti “mudzawayang’anira” akunena za ndani?

Popeza mawu a muvesi 7 akubwera pambuyo pa mawu a muvesi 6 akuti, “mawu a Yehova,” ena angaganize kuti izi zikutanthauza kuti mawu akuti “mudzawayang’anira” akunena za mawu a Mulungu. Tikudziwa kuti iye wakhala akuyang’anira kapena kuti kuteteza Baibulo, ngakhale kuti anthu otsutsa ayesetsa kuliwononga komanso kuletsa kuti lisamapezeke.​—Yes. 40:8; 1 Pet. 1:25.

Komabe, zimenenso vesi 5 limafotokoza ndi zoona. Yehova wakhala akuthandiza komanso kupulumutsa “ovutika” ndi “oponderezedwa,” ndipo apitirizabe kuchita zimenezi.​—Yobu 36:15; Sal. 6:4; 31:1, 2; 54:7; 145:20.

Ndiye kodi mawu akuti “mudzawayang’anira” a muvesi 7 akutanthauza chiyani?

Nkhani yonse mu Salimoli ikusonyeza kuti mawu akuti “mudzawayang’anira,” akunena za anthu.

Pa Salimo 12:1, 2 akufotokoza za “anthu okhulupirika” omwe akhala akunamizidwa. Kenako muvesi lotsatira tikupezamo mawu osonyeza kuti Yehova adzalanga anthu omwe amagwiritsa ntchito lilime lawo kulankhula zinthu zoipa. Salimoli limatitsimikizira kuti Mulungu adzathandiza anthu ake chifukwa mawu ake ndi oyera.

Choncho vesi 7 likunena kuti Yehova ‘adzayang’anira’ kapena kuti kuteteza anthu amene akuvutitsidwa ndi anthu oipa.

Mawu akuti “Mudzawayang’anira” amapezekanso m’malemba a Chimasorete. Baibulo la Septuagint limagwiritsanso ntchito mawu akuti “mudzatiyang’anira” maulendo awiri muvesi 7, kusonyeza kuti akunenabe za anthu okhulupirika omwe akuvutika komanso kuponderezedwa. Pomaliza vesi 7 limanena kuti “aliyense” wa okhulupirikawo adzatetezedwa “ku m’badwo uwu,” omwe ndi anthu amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. (Sal. 12:7, 8) Baibulo la Chiaramu lomasulira Malemba a Chiheberi muvesi 7, anagwiritsanso ntchito mawu akuti “mudzawayang’anira,” ndipo limamveka kuti: “INU AMBUYE, mudzateteza olungama, mudzawayang’anira ku m’badwo woipawu mpaka kalekale.” Zimenezi zikupereka umboni winanso wosonyeza kuti Salimo 12:7, silikunena za mawu a Mulungu.

Pachifukwa chimenechi, vesili likupereka chiyembekezo kwa “anthu okhulupirika” kuti Mulungu adzachitapo kanthu kuti awathandize.