NKHANI YOPHUNZIRA 49
Timakhulupirira Kuti Anthu Amene Anamwalira Adzauka
“Ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka.”—MAC. 24:15.
NYIMBO NA. 151 Iye Adzaitana
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. Kodi atumiki a Yehovafe tili ndi chiyembekezo chotani?
KUKHALA ndi chiyembekezo n’kofunika kwambiri. Anthu ena amayembekezera kuti adzakhala ndi banja losangalala, adzakhala ndi ana a thanzi kapena adzachira matenda aakulu omwe ali nawo. Akhristufe tingayembekezerenso zinthu ngati zimenezi. Komabe timayembekezera zoposa pamenepa. Timayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha komanso kudzaonana ndi achibale athu amene anamwalira.
2 Mtumwi Paulo anati: “Ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Paulo sanali woyamba kufotokoza zokhudza kuuka kwa akufa. Yobu nayenso anafotokozapo za nkhani imeneyi. Iye sankakayikira kuti Mulungu adzamukumbukira n’kumuukitsa kuti akhalenso ndi moyo.—Yobu 14:7-10, 12-15.
3. Kodi chaputala 15 cha buku la 1 Akorinto, chingatithandize bwanji?
3 Nkhani ya “kuuka kwa akufa” ndi mbali ya “maziko” kapena kuti “chiphunzitso choyambirira” pa zonse zimene Akhristu amakhulupirira. (Aheb. 6:1, 2) Paulo anafotokoza za kuuka kwa akufa muchaputala 15 cha buku la 1 Akorinto. Zimene analemba ziyenera kuti zinalimbikitsa Akhristu a mu nthawi yake. Chaputala chimenechi chingatilimbikitsenso ifeyo komanso kulimbitsa chiyembekezo chimene takhala nacho kwa nthawi yaitali.
4. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti achibale athu amene anamwalira adzaukitsidwa?
4 Kuukitsidwa kwa Yesu Khristu kumatithandiza kuti tizikhulupirira kuti achibale athu amene anamwalira kapena ngati ifenso titamwalira tidzaukitsidwa. Nkhani imeneyi inali mbali ya “uthenga wabwino” umene Paulo analengeza kwa anthu a ku Korinto. (1 Akor. 15:1, 2) Ndipotu iye ananena kuti ngati Mkhristu sangakhulupirire kuti Yesu anaukitsidwa ndiye kuti chikhulupiriro chakecho chingakhale chopanda ntchito. (1 Akor. 15:17) Kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa n’kumene kumatithandiza kuti tizikhulupirira kuti anthu enanso adzaukitsidwa.
5-6. Kodi mawu opezeka pa 1 Akorinto 15:3, 4, amatanthauza chiyani kwa ife?
5 Paulo atangoyamba kulemba zokhudza kuuka kwa akufa, anatchula mfundo zitatu izi: (1) “Khristu anafera machimo athu.” (2) “Anaikidwa m’manda.” (3) “Anaukitsidwa tsiku lachitatu, mogwirizana ndi Malemba.”—Werengani6 Kodi imfa, kuikidwa m’manda komanso kuukitsidwa kwa Yesu zili ndi tanthauzo lotani kwa ife? Mneneri Yesaya ananeneratu kuti Mesiya ‘adzadulidwa m’dziko la amoyo’ ndipo “manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa.” Koma panalinso zina zimene zinkayenera kuchitika. Iye ananenanso kuti Mesiya adzanyamula “tchimo la anthu ambiri.” Yesu anachita zimenezi pamene anapereka moyo wake monga dipo. (Yes. 53:8, 9, 12; Mat. 20:28; Aroma 5:8) Choncho imfa, kuikidwa m’manda ndiponso kuukitsidwa kwa Yesu zimatipatsa zifukwa zamphamvu zokhulupirira kuti tidzamasulidwa ku uchimo ndi imfa komanso kuti tidzaonananso ndi achibale athu omwe anamwalira.
UMBONI WA ANTHU AMBIRI
7-8. Kodi n’chiyani chimathandiza Akhristu kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa?
7 Kuti tizikhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa, choyamba tiyenera kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yehova anaukitsa Yesu?
8 Panali anthu ambiri amene anaona Yesu ataukitsidwa ndipo anafotokozera ena zimenezi. (1 Akor. 15:5-7) Munthu woyamba amene Paulo anatchula kuti anaona Yesu ataukitsidwa anali mtumwi Petulo (Kefa). Ophunzira enanso anatsimikizira kuti Petulo anaona Yesu ataukitsidwa. (Luka 24:33, 34) Kuwonjezera pamenepo, Paulo ananena kuti atumwi 12, nawonso anaona Yesu ataukitsidwa. Kenako Khristu “anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.” Mwina apa panali pamsonkhano wosangalatsa wotchulidwa pa Mateyu 28:16-20, umene unachitikira ku Galileya. Kenako Yesu “anaonekera kwa Yakobo.” N’kutheka kuti Yakobo ameneyu anali m’bale wake wa Yesu yemwe poyamba sankakhulupirira kuti iye ndi Mesiya. (Yoh. 7:5) Koma ataona kuti waukitsidwa, Yakobo anayamba kukhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya. N’zochititsa chidwi kuti cha m’ma 55 C.E. pamene Paulo ankalemba kalatayi, anthu ambiri amene anaona Yesu ataukitsidwa anali adakali ndi moyo. Choncho aliyense amene akanakayikira akanatha kufunsa anthu odalirika omwe anaona Yesu ataukitsidwa.
9. Kodi lemba la Machitidwe 9:3-5, limasonyeza bwanji kuti Paulo akanatha kupereka umboni wina wotsimikizira kuti Yesu anaukitsidwa?
9 Patapita nthawi, Yesu anaonekeranso kwa Paulo. (1 Akor. 15:8) Paulo (Saulo) anali paulendo wopita ku Damasiko pamene anamva mawu a Yesu ndi kuona masomphenya a Yesuyo ali kumwamba. (Werengani Machitidwe 9:3-5.) Zimene zinachitikira Paulo zinapereka umboni winanso wotsimikizira kuti Yesu anaukitsidwadi.—Mac. 26:12-15.
10. Kodi Paulo ankachita chiyani chifukwa chokhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa?
10 Anthu ena akanachita chidwi kwambiri ndi umboni wa Paulo chifukwa choti poyamba iye ankazunza Akhristu. Paulo atakhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa, anayesetsa kuthandiza anthu ena kuti akhulupirirenso zimenezi. Pamene Paulo ankalalikira zoti Yesu anafa kenako n’kuukitsidwa, anakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kumenyedwa, kuikidwa m’ndende komanso kusweka kwa chingalawa. (1 Akor. 15:9-11; 2 Akor. 11:23-27) Paulo ankakhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa moti anali wokonzeka kufa chifukwa cholalikira zimene ankakhulupirirazo. Kodi umboni wochokera kwa Akhristu oyambirirawa, sukutithandiza kuti ifenso tizikhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa? Ndipotu umboni umenewu umatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti m’tsogolomunso amene anamwalira adzaukitsidwa.
PAULO ANATHANDIZA AMENE ANKAKHULUPIRIRA ZABODZA
11. N’chifukwa chiyani anthu ena ku Korinto ankakhulupirira zabodza pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa?
11 Anthu ena mumzinda wa Korinto ku Girisi, ankakhulupirira zinthu zabodza zokhudza kuuka kwa akufa. Ndipo ena anafika ponena kuti “akufa sadzaukitsidwa.” N’chifukwa chiyani ankakhulupirira zimenezi? (1 Akor. 15:12) Chifukwa akatswiri a nzeru za anthu a mumzinda wa Atene ku Girisi komweko, ankanyoza anthu omwe ankakhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa. Choncho, mwina anthu ena ku Korinto anatengera maganizo amenewa. (Mac. 17:18, 31, 32) N’kutheka kuti ena ankaganiza kuti anthu amaukitsidwa mophiphiritsa. Iwo ankaona kuti munthu amakhala wakufa chifukwa choti ndi wochimwa koma akakhala Mkhristu amakhala ndi moyo chifukwa machimo ake amakhululukidwa. Kaya sankakhulupirira pa zifukwa zotani, kukana kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa kunapangitsa kuti chikhulupiriro chawo chikhale chopanda ntchito. Ngati Mulungu sanaukitse Yesu ndiye kuti dipo silinaperekedwe ndipo machimo a anthu onse sanakhululukidwe. Choncho amene ankatsutsa zoti akufa adzaukitsidwa analibe chiyembekezo chenicheni.—1 Akor. 15:13-19; Aheb. 9:12, 14.
12. Mogwirizana ndi 1 Petulo 3:18, 22, kodi kuukitsidwa kwa Yesu n’kosiyana bwanji ndi kuukitsidwa kwa anthu ena komwe kunachitika m’mbuyomu?
12 Paulo ankadziwa kuti Khristu “anaukitsidwa kwa akufa.” Kuukitsidwa kumeneku kunali kwapadera kuposa kwa anthu amene anaukitsidwa m’mbuyomu chifukwa patapita nthawi anthuwo anafanso. Paulo ananena kuti Yesu anali “chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” N’chifukwa chiyani ananena kuti Yesu anali chipatso choyambirira? Chifukwa choti anali woyamba kuukitsidwa ndi thupi lauzimu komanso anali woyamba kupita kumwamba.—1 Akor. 15:20; Mac. 26:23; werengani 1 Petulo 3:18, 22.
ANTHU AMENE ‘ADZAPATSIDWE MOYO’
13. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti Adamu anali wosiyana ndi Yesu?
13 Kodi imfa ya munthu mmodzi ingathandize bwanji kuti anthu mamiliyoni adzakhale ndi moyo? Paulo anayankha funso limeneli momveka bwino. Iye anasiyanitsa zimene zikuchitikira anthu chifukwa cha zomwe Adamu anachita ndi zimene zidzachitikire anthu chifukwa cha nsembe ya Khristu. Ponena za Adamu, Paulo analemba kuti: “Imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi.” Adamu atachimwa anabweretsa mavuto pa iyeyo ndi ana ake onse. Panopa tikupitiriza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha kusamvera kwake. Koma popeza kuti Mulungu anaukitsa mwana wake, tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. “Kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi,” yemwe ndi Yesu. Paulo ananenanso kuti: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akor. 15:21, 22.
14. Kodi Adamu adzaukitsidwa? Fotokozani.
14 Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti “mwa Adamu onse akufa”? Paulo ankanena za anthu onse amene anatengera uchimo kuchokera kwa Adamu ndipo amafa. (Aroma 5:12) Adamu sali m’gulu la anthu amene ‘adzapatsidwe moyo.’ Iye sangapindule ndi nsembe ya Khristu chifukwa anali wangwiro koma anasankha dala kuti asamvere Mulungu. Zimene zinachitikira Adamu ndi zomwe zidzachitikirenso anthu amene “Mwana wa munthu” adzawaweruze kuti ndi “mbuzi,” kutanthauza kuti adzapita ku “chiwonongeko chotheratu.”—Mat. 25:31-33, 46; Aheb. 5:9.
15. Kodi “onse” amene ‘adzapatsidwe moyo’ akuphatikizapo ndani?
15 Onani kuti Paulo ananenanso kuti “mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akor. 15:22) Iye analembera kalatayi Akhristu odzozedwa a ku Korinto amene ankayembekezera kudzaukitsidwa n’kupita kumwamba. Akhristu amenewo ‘anayeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi kuitanidwa kuti akhale oyera.’ Paulo anatchula za “anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu.” (1 Akor. 1:2; 15:18; 2 Akor. 5:17) M’kalata yake ina analemba kuti ‘amene anagwirizana naye [Yesu] pokhala ndi imfa yofanana ndi yake,’ ‘adzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana ndi iye.’ (Aroma 6:3-5) Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu ndipo anapita kumwamba. Zimenezi ndi zomwe zidzachitike kwa onse amene “ali ogwirizana ndi Khristu” kapena kuti Akhristu onse odzozedwa.
16. Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Yesu ndi “chipatso choyambirira”?
16 Paulo analemba kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa n’kukhala “chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” Kumbukirani kuti anthu ena ngati Lazaro anaukitsidwa n’kukhala ndi moyo padziko lapansi. Koma Yesu anali woyamba kuukitsidwa ndi thupi lauzimu n’kupatsidwa moyo wosatha. Tingamuyerekezere ndi zipatso zoyambirira kukolola zimene Aisiraeli ankapereka kwa Mulungu. Komanso ponena kuti Yesu ndi “chipatso choyambirira,” Paulo ankatanthauza kuti pambuyo pake anthu enanso adzaukitsidwa n’kupita kumwamba. Patapita nthawi atumwi ndi ena amene “ali ogwirizana ndi Khristu,” anaukitsidwa n’kupita kumwamba mofanana ndi Yesu.
17. Kodi anthu amene “ali ogwirizana ndi Khristu” anayamba liti kuukitsidwa n’kupita kumwamba?
17 Pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Akhristu a ku Korinto, anthu amene “ali ogwirizana ndi Khristu” anali asanayambe kuukitsidwa n’kupita kumwamba. Paulo anasonyeza kuti zimenezi zidzachitika m’tsogolo. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akor. 15:23; 1 Ates. 4:15, 16) Panopa, tikukhala mu “nthawi ya kukhalapo” kwa Khristu imene Paulo ananenayi. Atumwi komanso Akhristu ena odzozedwa amene anamwalira ankafunika kuyembekezera nthawi ya kukhalapo imeneyi kuti alandire mphoto yawo yakumwamba ndi ‘kugwirizananso ndi Yesu poukitsidwa mofanana ndi iye.’
SITIKUKAYIKIRA KUTI ZIMENE TIKUYEMBEKEZERA ZIDZACHITIKA
18. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti pambuyo pa kuukitsidwa kwa opita kumwamba padzakhalanso kuuka kwina? (b) Mogwirizana ndi 1 Akorinto 15:24-26, kodi n’chiyani chidzachitike kumwamba?
18 Koma kodi chidzachitike n’chiyani kwa Akhristu onse okhulupirika amene sakuyembekezera kupita kumwamba n’kukakhala ndi Khristu? Nawonso akuyembekezera kuti adzaukitsidwa. Baibulo limanena kuti Paulo ndi ena opita kumwamba amaukitsidwa pa “kuuka koyambirira kuchokera kwa akufa.” (Afil. 3:11) Zimenezitu zikusonyeza kuti pambuyo pake padzakhalanso kuuka kwina. Ndipo izi n’zogwirizana ndi zomwe Yobu ankakhulupirira kuti zidzamuchitikira m’tsogolo. (Yobu 14:15) Ndiyeno “ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake” adzakhala ali ndi Yesu kumwamba pamene azidzathetsa maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. “Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” N’zoona kuti anthu amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba, sadzafanso. Koma kodi n’chiyani chidzachitikire anthu ena onse?—Werengani 1 Akorinto 15:24-26.
19. Kodi anthu amene adzakhale padziko lapansi akuyembekezera zotani?
19 Kodi anthu amene adzakhale padziko lapansi akuyembekezera zotani? Zimene akuyembekezera zikupezeka m’mawu a Paulo akuti: “Ine ndili ndi chiyembekezo . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) N’zodziwikiratu kuti anthu osalungama sangapite kumwamba, choncho mawuwa akunena za kuukitsidwa kwa anthu padziko lapansi m’tsogolo.
20. Kodi chiyembekezo chanu chakuti kudzakhala kuuka chalimbikitsidwa bwanji?
20 Sitikukayikira kuti “kudzakhala kuuka.” Ndipo amene adzaukitsidwe padziko lapansi akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha. Muzikhulupirira kuti lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa. Zimene tikuyembekezerazi zingatitonthoze tikamaganizira za achibale athu amene anamwalira. Iwo adzaukitsidwa Khristu ndi anzake akamadzalamulira “monga mafumu . . . zaka 1,000.” (Chiv. 20:6) Inunso musamakayikire kuti mudzaukitsidwa ngati mungafe Yesu asanayambe ulamuliro wake wa zaka 1,000. ‘Chiyembekezo chathu sichingatikhumudwitse.’ (Aroma 5:5) Chiyembekezochi chingatithandize kuti tikhale olimba panopa komanso kuti tizisangalala potumikira Mulungu. Munkhani yotsatira, tidzaona kuti pali zambiri zimene tingaphunzire muchaputala 15 cha buku la 1 Akorinto.
NYIMBO NA. 147 Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha
^ ndime 5 Muchaputala 15 cha buku la 1 Akorinto, Paulo anafotokoza za kuuka kwa akufa. Kodi nkhani ya kuuka kwa akufa ndi yofunika bwanji kwa ife, nanga n’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti Yesu anauka? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa ndi enanso ofunika okhudza kuuka kwa akufa.
^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu anali woyamba kupita kumwamba. (Mac. 1:9) Ena mwa ophunzira ake amene anapitanso kumwamba anali Tomasi, Yakobo, Lidiya, Yohane, Mariya ndi Paulo.
^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’baleyu mkazi wake amene anatumikira naye kwa nthawi yaitali anamwalira. Iye akukhulupirira kuti adzaukitsidwa choncho akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika.