Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 32

Muzikhulupirira Kwambiri Mlengi

Muzikhulupirira Kwambiri Mlengi

“Chikhulupiriro ndicho . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.”​AHEB. 11:1.

NYIMBO NA. 11 Chilengedwe Chimatamanda Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi munaphunzitsidwa zotani zokhudza Mlengi wathu?

NGATI munakulira m’banja la Mboni za Yehova, muyenera kuti munayamba kuphunzira za Yehova muli wamng’ono. Munaphunzitsidwa kuti iye ndi Mlengi, ali ndi makhalidwe abwino komanso ali ndi cholinga chabwino chokhudza anthu.​—Gen. 1:1; Mac. 17:24-27.

2. Kodi anthu ena amawaona bwanji anthu amene amakhulupirira zoti kuli Mlengi?

2 Anthu ambiri sakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso kuti iye ndi amene analenga zinthu zonse. M’malomwake, iwo amakhulupirira kuti moyo unangokhalapo wokha ndipo pang’ono ndi pang’ono zamoyo zosavuta kumvetsa zinasintha n’kukhala zamoyo zovuta kumvetsa. Ena mwa anthu amene amakhulupirira zimenezi ndi ophunzira kwambiri. Iwo angamanene kuti sayansi imasonyeza kuti Baibulo si lolondola komanso kuti anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mlengi ndi osaphunzira, opanda nzeru komanso osavuta kuwapusitsa.

3. N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti tizilimbitsa chikhulupiriro chathu?

3 Kodi zimene anthu ena otchuka amanena ziyenera kusokoneza zimene timaphunzira zoti Yehova ndi Mlengi wathu wachikondi? Zingadalire kudziwa chifukwa chake timakhulupirira kuti Yehova ndi Mlengi. Kodi timakhulupirira zimenezi chifukwa choti tinangouzidwa, kapena tinafufuza patokha n’kupeza umboni? (1 Akor. 3:12-15) Kaya takhala a Mboni za Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe timafunika kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tikamachita zimenezi, sitingasocheretsedwe ndi “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake,” zomwe anthu otsutsa mawu a Mulungu amaphunzitsa. (Akol. 2:8; Aheb. 11:6) Pofuna kutithandiza kuti tisasocheretsedwe, munkhaniyi tikambirana (1) chifukwa chake anthu ambiri sakhulupirira kuti kuli Mlengi, (2) zimene tingachite kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova Mlengi wathu, komanso (3) zimene tingachite kuti tipitirizebe kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMBIRI SAKHULUPIRIRA KUTI KULI MLENGI

4. Mogwirizana ndi Aheberi 11:1, kodi Baibulo limati chikhulupiriro ndi chiyani?

4 Anthu ena amaganiza kuti kukhala ndi chikhulupiriro kumatanthauza kukhulupirira zinthu zimene zilibe umboni. Koma malinga ndi zimene Baibulo limanena, chimenecho si chikhulupiriro chenicheni. (Werengani Aheberi 11:1.) Lembali likusonyeza kuti munthu amakhulupirira zinthu zosaoneka zomwe ndi zenizeni monga Yehova, Yesu komanso Ufumu wakumwamba chifukwa choti ali ndi umboni wotsimikizirika. (Aheb. 11:3) Wa Mboni wina yemwe ndi katswiri wasayansi ananena kuti: “Zomwe timakhulupirira zili ndi umboni ndipo sizitsutsana ndi sayansi.”

5. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakhulupirira kuti zinthu sizinachite kulengedwa?

5 Mwina tingafunse kuti, ‘Ngati pali umboni wotsimikizirika woti kuli Mlengi, n’chifukwa chiyani anthu ambiri sakhulupirira kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zamoyo?’ Chifukwa china n’choti anthu ena sanafufuze paokha kuti apeze umboniwo. Robert yemwe panopa ndi wa Mboni za Yehova ananena kuti: “Popeza kusukulu sankaphunzitsa kuti zinthu zinachita kulengedwa, ndinkaganiza kuti zinangokhalako zokha. Ndinkakhulupirira zimenezi mpaka pamene ndinakumana ndi a Mboni za Yehova omwe anandifotokozera mfundo zomveka bwino za m’Baibulo zotsimikizira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Pa nthawiyo n’kuti ndili ndi zaka za m’ma 20.” *​—Onani bokosi lakuti, “ Malangizo kwa Makolo.”

6. N’chifukwa chiyani anthu ena amatsutsa zoti kuli Mlengi?

6 Anthu ena sakhulupirira kuti kuli Mlengi chifukwa amanena kuti amakhulupirira zinthu zokhazo zimene amaona. Komabe anthu amenewa amakhulupirira zinthu zina zosaoneka monga mphamvu yokoka, yomwe pali umboni woti ilipodi. Mtundu wa chikhulupiriro chomwe chatchulidwa m’Baibulo, umakhalanso ndi umboni wa “zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheb. 11:1) Timafunika khama komanso nthawi yophunzira kuti tipeze umboni umenewu patokha. Koma anthu ambiri safuna kuchita zimenezi. Munthu amene safufuza kuti apeze umboni angamanene kuti kulibe Mulungu.

7. Kodi anthu onse ophunzira, amatsutsa zoti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse? Fotokozani.

7 Pambuyo pofufuza umboni, asayansi ena atsimikizira kuti Mulungu analenga zinthu zonse. * Mofanana ndi Robert yemwe tamutchula kale uja, mwina ena ankangoganiza kuti kulibe Mlengi chifukwa choti ali kuyunivesite sanaphunzitsidwe kuti zinthu zinachita kulengedwa. Komabe, asayansi ambiri aphunzira zokhudza Yehova ndipo amamukonda. Mofanana ndi asayansi amenewa, tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizilimbitsa chikhulupiriro chathu, kaya ndife ophunzira kapena ayi ndipo palibe angatichitire zimenezi.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI KUTI KULI MLENGI

8-9. (a) Kodi tsopano tikambirana funso liti? (b) Kodi kuphunzira zinthu zam’chilengedwe kungatithandize bwanji?

8 Kodi tingatani kuti ifeyo tizikhulupirira kuti kuli Mlengi? Tiyeni tikambirane njira 4.

9 Tiziphunzira zinthu zam’chilengedwe. Tingalimbitse chikhulupiriro chathu tikamachita chidwi ndi zinthu monga nyama, zomera komanso nyenyezi. (Sal. 19:1; Yes. 40:26) Mukamaphunzira kwambiri zokhudza zinthu zimenezi m’pamenenso mumapeza umboni wokwanira woti Yehova ndi Mlengi. M’mabuku athu mumapezeka nkhani zomwe zimafotokoza zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe. Mukamaphunzira musamadumphe nkhani zimenezi ngakhale mutaona kuti n’zovuta kumvetsa. Muziyesetsa kuti muphunzirepo kenakake. Ndipo musamaiwale kuonera pawebusaiti yathu ya jw.org mavidiyo osangalatsa onena za chilengedwe omwe takhala tikuonera pamisonkhano yachigawo m’zaka zaposachedwapa.

10. Perekani chitsanzo cha mmene zinthu zam’chilengedwe zimasonyezera kuti kuli Mlengi. (Aroma 1:20)

10 Mukamaphunzira zokhudza chilengedwe muziganizira zimene zinthuzo zikukuphunzitsani ponena za Mlengi wathu. (Werengani Aroma 1:20.) Mwachitsanzo, mwina mukudziwa kuti kuwonjezera pa kutulutsa kutentha komwe kumathandiza zamoyo, dzuwa limatulutsanso kuwala komwe kungakhale kowononga. Anthufe timafunika kutetezedwa kuti kuwala kumeneku kusativulaze ndipo timatetezedwadi. Kodi timatetezedwa bwanji? Dziko lathu lili ndi mpweya wina mlengalenga womwe umachepetsa mphamvu ya kuwala kumeneku. Kuwala kowonongaku kukamawonjezereka, mpweyawonso umawonjezereka. Ndiye pamenepa, kodi simukuvomereza kuti pali winawake amene amachititsa zimenezi, yemwe ndi Mlengi wanzeru komanso wachikondi?

11. Kodi mungapeze kuti mfundo zokuthandizani kukhulupirira kwambiri kuti zinthu zinachita kulengedwa? (Onani bokosi lakuti, “ Zinthu Zotithandiza Kulimbitsa Chikhulupiriro Chathu.”)

11 Mungapeze mfundo zambiri zokuthandizani kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa mu Watch Tower Publications Index komanso pofufuza pawebusaiti yathu ya jw.org. Mwina mungakonde kuyamba ndi kuwerenga nkhani komanso kuonera mavidiyo akuti, “Kodi Zinangochitika Zokha?” Mavidiyo komanso nkhani zimenezi zimakhala zazifupi ndipo zimafotokoza mfundo zochititsa chidwi zokhudza nyama komanso zolengedwa zina. Mulinso zitsanzo za zinthu zimene asayansi apanga potengera zinthu zam’chilengedwe.

12. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tiyenera kuziganizira tikamaphunzira Baibulo?

12 Tiziphunzira Baibulo. Katswiri wasayansi yemwe tamutchula mundime 4 uja, poyamba sankakhulupirira kuti kuli Mlengi. Koma patapita nthawi, iye anayamba kukhulupirira. Iye ananena kuti, “Sikuti ndinayamba kukhulupirira chabe chifukwa chongophunzira zinthu zasayansi, koma chifukwa choti ndinaphunziranso Baibulo mosamala.” N’kutheka kuti mukudziwa kale zinthu zolondola zimene Baibulo limaphunzitsa. Komabe kuti muzikhulupirira kwambiri Mlengi, muyenera kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu. (Yos. 1:8; Sal. 119:97) Mwachitsanzo, muziganizira mmene Baibulo limafotokozera molondola zinthu zimene zinachitika kalekale. Muziganiziranso maulosi komanso kugwirizana kwa nkhani zake. Kuchita zimenezi kungathandize kuti muzikhulupirira kwambiri kuti tinalengedwa ndi Mlengi wachikondi komanso wanzeru, yemwenso anachititsa kuti Baibulo lilembedwe. *​—2 Tim. 3:14; 2 Pet. 1:21.

13. Kodi ndi chitsanzo chimodzi chiti chomwe chikusonyeza kuti timapeza nzeru m’Mawu a Mulungu?

13 Mukamaphunzira Mawu a Mulungu mudzaona kuti malangizo ake ndi othandiza kwambiri. Mwachitsanzo, kale kwambiri Baibulo linachenjeza kuti kukonda ndalama n’koopsa ndipo kumabweretsera munthu “zopweteka zambiri.” (1 Tim. 6:9, 10; Miy. 28:20; Mat. 6:24) Kodi chenjezo limeneli likugwirabe ntchito masiku ano? Buku lina lomwe limafotokoza za maganizo a anthu linanena kuti: “Anthu ambiri omwe amakonda ndalama sakhala osangalala komanso amavutika maganizo kwambiri. Ngakhalenso anthu amene amalakalaka atakhala ndi ndalama zambiri, amachita zinthu mosaganiza bwino ndipo amakhala ndi mavuto ambiri okhudza thanzi lawo.” Pamenepatu tingaone kuti zimene Baibulo limatichenjeza kuti tisamakonde ndalama n’zothandiza. Kodi ndi mfundo zina ziti za m’Baibulo zomwe mwaona kuti ndi zothandiza? Tikamayamikira kwambiri malangizo a m’Baibulo, m’pamenenso timadalira kwambiri nzeru za Mlengi wathu wachikondi zomwe zimakhala zothandiza nthawi zonse. (Yak. 1:5) Tikamachita zimenezi, tidzakhala osangalala kwambiri.​—Yes. 48:17, 18.

14. Kodi mukamaphunzira Baibulo mungadziwe zotani zokhudza Yehova?

14 Muziphunzira ndi cholinga choti mudziwe Yehova. (Yoh. 17:3) Mukamaphunzira Malemba mudzayamba kuona makhalidwe omwe ali nawo, omwenso amaonekera bwino m’zinthu zimene analenga. Kuphunzira makhalidwe a Yehova kumatithandiza kutsimikizira kuti iye alipodi. (Eks. 34:6, 7; Sal. 145:8, 9) Mukamamudziwa bwino Yehova, m’pamenenso mumamukhulupirira kwambiri, kumukonda kwambiri komanso ubwenzi wanu ndi iye umalimba.

15. Kodi kuuza ena zomwe mumakhulupirira n’kothandiza bwanji?

15 Muziuza ena zimene mumakhulupirira zokhudza Mulungu. Mukamachita zimenezi chikhulupiriro chanu chimalimba. Nanga bwanji ngati munthu amene mwamulalikira atakufunsani kuti mumufotokozere umboni woti Mulungu alipo koma simukudziwa mmene mungayankhire? Muzifufuza yankho lake m’mabuku athu ndipo kenako muzikambirana ndi munthuyo. (1 Pet. 3:15) Mukhoza kupemphanso Mkhristu amene amadziwa zambiri kuti akuthandizeni. Kaya munthuyo avomereza zimene Baibulo limanena kapena ayi, inuyo mukhoza kupindula ndi zimene mwafufuzazo. Chikhulupiriro chanu chidzalimba ndipo simudzasokonezedwa ndi mabodza a anthu omwe amaoneka ngati ophunzira komanso anzeru, amene amanena kuti kulibe Mlengi.

PITIRIZANI KULIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU

16. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titasiya kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

16 Kaya takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tikutero chifukwa ngati sitingasamale, chikhulupiriro chathu chikhoza kufooka. Tizikumbukira kuti chikhulupiriro chimaphatikizapo umboni wa zinthu zenizeni zomwe n’zosaoneka. N’zosavuta kuiwala zinthu zimene sitikuziona. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti kusowa chikhulupiriro ndi “tchimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Ndiye kodi tingatani kuti tisakodwe mumsampha umenewu?​—2 Ates. 1:3.

17. Kodi n’chiyani chingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

17 Choyamba, tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera ndipo tizichita zimenezi pafupipafupi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chikhulupiriro ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho sitingathe kulimbitsa chikhulupiriro chathu popanda kuthandizidwa ndi mzimu wake woyera. Yehova angatipatse mzimuwu ngati titapitiriza kumupempha. (Luka 11:13) Tingathenso kumupempha mwachindunji kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”​—Luka 17:5.

18. Mogwirizana ndi Salimo 1:2, 3, kodi masiku ano tili ndi mwayi wotani?

18 Komanso muziphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. (Werengani Salimo 1:2, 3) Pamene salimoli linkalembedwa, ndi Aisiraeli ochepa okha omwe anali ndi buku lonse la Chilamulo. Komabe mfumu ndi ansembe ankakhala ndi buku la Chilamulo. Ndiponso pambuyo pa zaka 7 zilizonse ankasonkhanitsa “amuna, akazi, ana” komanso alendo okhala mu Isiraeli kuti amvetsere Chilamulo chikamawerengedwa. (Deut. 31:10-12) Munthawi ya Yesunso, mipukutu inkangopezeka ndi anthu ochepa okha komanso m’masunagoge. Mosiyana ndi zimenezi, masiku ano anthu ambiri akhoza kupezeka ndi Baibulo lonse kapena mbali yake. Umenewutu ndi mwayi waukulu. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi umenewu?

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipitirize kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

19 Tingasonyeze kuti timayamikira mwayi wokhala ndi Mawu a Mulungu tikamawawerenga nthawi zonse. Sitiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu mwamwayi pamene taona kuti tili ndi nthawi. Tikamayesetsa kuti tiziphunzira Baibulo nthawi zonse, tingalimbitse chikhulupiriro chathu.

20. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 Mosiyana ndi “anthu anzeru ndi ozindikira” a m’dzikoli, ifeyo tili ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa cha zimene timaphunzira m’Baibulo. (Mat. 11:25, 26) Zimene zili m’buku lopatulikali zimatithandiza kudziwa chifukwa chake zinthu zikuipiraipirabe padzikoli komanso zimene Yehova achite posachedwapa. Choncho tiyeni tipitirizebe kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso kuthandiza anthu ambiri kuti azikhulupirira Mlengi wathu. (1 Tim. 2:3, 4) Komanso tiyeni tipitirize kuyembekezera pa nthawi yomwe anthu onse padzikoli adzanene mawu opezeka pa Chivumbulutso 4:11, akuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu . . . , kulandira ulemerero . . . , chifukwa munalenga zinthu zonse.”

NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndinu Yehova

^ ndime 5 Malemba amaphunzitsa momveka bwino kuti Yehova Mulungu ndi Mlengi. Koma anthu ambiri sakhulupirira zimenezi. Iwo amanena kuti moyo unangoyamba wokha. Zimene amanenazi sizingatisokoneze ngati timachita khama kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu komanso Baibulo. Nkhaniyi itithandiza kudziwa mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 5 M’masukulu ambiri, aphunzitsi saphunzitsa ngakhale pang’ono kuti zinthu zinachita kulengedwa. Iwo amanena kuti kuchita zimenezi kungakhale ngati kukakamiza ophunzira kuti azikhulupirira kuti kuli Mulungu.

^ ndime 7 Mungapeze mfundo zimene ananena anthu ena ophunzira kwambiri oposa 60, kuphatikizaponso asayansi omwe amakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa, mu Watch Tower Publications Index. Pamutu wakuti, “Science” pitani pamene alemba kuti “scientists expressing belief in creation.” Mfundo zina mungazipeze mu Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Pamutu wakuti “Sayansi ndi Luso la Zopangapanga,” pitani pomwe alemba kuti, “Kucheza ndi Munthu Wina.” (Nkhani za mu Galamukani!)

^ ndime 12 Mwachitsanzo, onani nkhani yakuti, “Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?” yomwe ili mu Galamukani! ya February 2011 komanso nkhani yakuti, “Zimene Yehova Amalosera Zimakwaniritsidwa” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008.