KALE LATHU
Anayamba Kufesa Mbewu za Ufumu ku Portugal
PAMENE George Young ankadutsa nyanja ya Atlantic kupita ku Europe, ankasangalala kwambiri podziwa kuti wafesa mbewu za Ufumu ku Brazil. * Koma kenako anayamba kuganizira kwambiri za ku Spain ndi ku Portugal kumene anatumizidwa kuti akayambe kufesanso mbewu za Ufumu. Ankaganiza kuti akafika, adzakonza zoti M’bale J. F. Rutherford adzabwere kudzakamba nkhani. Ankaganizanso kuti padzakhale ntchito yogawira timapepala tokwana 300,000.
Koma atafika mumzinda wa Lisbon mu 1925, M’bale Young anapeza kuti zinthu sizili bwino. Zinthu zinali zitasintha kwambiri pa nkhani zandale kuyambira mu 1910 ndipo tchalitchi cha Katolika chinali chitasiya kukhala ndi mphamvu zambiri. Anthu anali pa ufulu wambiri komabe ziwawa zinkachitikachitika.
Pa nthawi imene M’bale Young ankakonza zoti anthu adzamvetsere nkhani ya M’bale Rutherford, boma la Portugal linakhazikitsa lamulo lokhwima chifukwa choti anthu ena ankafuna kulanda boma. Munthu wina amene anali ndi udindo m’bungwe linalake anachenjeza M’bale Young kuti asamale chifukwa atsutsidwa kwambiri. Koma M’bale Young anapempha chilolezo kuti anthu akamvetsere nkhaniyo paholo ina yakusekondale ya Camões ndipo anapatsidwa chilolezocho.
Anakonza zoti anthu amvetsere nkhaniyi pa 13 May ndipo tsikuli litafika anthu ankayembekezera mwachidwi. Mutu wa nkhaniyi unali wakuti “Kodi Tingatani Kuti Tidzakhale Padzikoli Mpaka Muyaya?” ndipo unaikidwa pa zikwangwani m’nyumba zambiri komanso kulengezedwa munyuzipepala. Koma anthu ena achipembedzo analembanso munyuzipepala mawu ochenjeza anthu kuti kwabwera “aneneri onyenga.” Ndiyeno achipembedzowo ankagawa timabuku tawo pakhomo lolowera muholoyo. Timabukuto tinkatsutsa mfundo zimene M’bale Rutherford ankaphunzitsa.
Ngakhale zinali choncho, anthu 2,000 analowa n’kudzaza moti ena 2,000 anauzidwa kuti abwerere. Anthu ena anakwera m’malo osiyanasiyana kuti amvetsere nkhaniyo.
Sikuti zonse zinayenda bwino. Anthu otsutsa ankasokosa komanso kumenyetsa mipando. Koma M’bale Rutherford sanatekeseke, m’malomwake anangokwera patebulo kuti azimveka bwino. Atamaliza nkhani yake usiku kwambiri, anthu oposa 1,200 anapereka mayina awo kuti azilandira mabuku othandiza pophunzira Baibulo. Tsiku lotsatira, nyuzipepala ina (O Século) inalemba za nkhani ya M’bale Rutherford.
Pofika mu September 1925, Nsanja ya Olonda yachipwitikizi inayamba kutuluka ku Portugal. (Magazini yachilankhulochi inali itayamba kale kutuluka ku Brazil.) Pa nthawi imeneyi, Virgílio Ferguson yemwe anali Wophunzira Baibulo ku Brazil anayamba kuganiza zopita ku Portugal kuti akathandize pa ntchito yolalikira. M’mbuyomo,
m’baleyu anagwirapo ntchito ndi M’bale Young kunthambi ya ku Brazil imene inali yaing’ono. Pasanapite nthawi yaitali, M’bale Virgílio ndi mkazi wake dzina lake Lizzie anapita n’kumakatumikira limodzi ndi M’bale Young. Tingati M’bale Ferguson anafika pa nthawi yabwino chifukwa pasanapite nthawi yaitali M’bale Young anachoka n’kupita kukatumikira kumayiko ena monga ku Soviet Union.Zinthu zitasintha pa nkhani zandale ku Portugal, abale ndi alongo anayamba kutsutsidwa kwambiri. Koma M’bale Ferguson anachita zinthu molimba mtima kuti ateteze kagulu ka Ophunzira Baibulo komanso kuwathandiza kuti azigwirabe ntchito yawo. Iye anapita kukapempha chilolezo kuti misonkhano izichitikira kunyumba kwake. Chilolezochi chinaperekedwa mu October 1927.
Chaka chimene mavuto anayamba ku Portugal, anthu pafupifupi 450 analembetsa kuti azilandira Nsanja ya Olonda. Mabuku ndi timapepala zinathandizanso kuti uthenga ufike m’madera onse olamulidwa ndi dziko la Portugal monga ku Angola, Azores, Cape Verde, East Timor, Goa, Madeira ndi ku Mozambique.
Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1920, mlimi wina dzina lake Manuel da Silva Jordão anafika ku Lisbon. Iye anamva nkhani ya M’bale Young pa nthawi imene anali ku Brazil. Atangomva nkhaniyi anazindikira kuti ndi choonadi ndipo ankafunitsitsa kuthandiza M’bale Ferguson pa ntchito yolalikira. Choncho anayamba kuchita upainiya womwe pa nthawiyo unkatchedwa ukopotala. Mabuku ofotokoza Baibulo atayamba kusindikizidwa komanso kufalitsidwa bwinobwino, mpingo watsopano wamumzinda wa Lisbon unayamba kukula kwambiri.
Mu 1934, M’bale ndi Mlongo Ferguson anabwerera ku Brazil koma anali atafesa mbewu za choonadi m’dzikoli. Pa nthawi ina zinthu zinkavuta kwambiri ku Europe chifukwa cha nkhondo yapachiweniweni ku Spain komanso nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Koma abale okhulupirikawa ku Portugal ankayesetsa kutumikirabe Yehova. Abalewa anali ngati makala a moto omwe anayamba kuyakanso kwambiri mu 1947. Pa nthawiyi, mmishonale woyamba wochokera ku Giliyadi dzina lake John Cooke anafika m’dzikoli. Kuyambira nthawi imeneyi, chiwerengero cha ofalitsa chinkawonjezereka kwambiri. Ngakhale pamene boma linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova mu 1962, chiwerengero cha ofalitsa chinkawonjezerekabe. Mu December 1974, boma linavomereza ntchito ya Mboni za Yehova ndipo m’dzikoli munali ofalitsa oposa 13,000.
Panopa ku Portugal komanso kuzilumba kumene chilankhulo chachikulu ndi Chipwitikizi, monga kuzilumba za Azores ndi Madeira kuli ofalitsa oposa 50,000. Ofalitsa ena ndi zidzukulu za anthu amene anapezeka pa nkhani yosaiwalika imene M’bale Rutherford anakamba mu 1925 ija.
Timathokoza kwambiri Yehova komanso abale ndi alongo oyambirira aja amene anali okhulupirika komanso ankagwira ntchito molimba mtima monga ‘antchito a Khristu Yesu, otumikira anthu a mitundu ina.’—Aroma 15:15, 16.—Nkhaniyi yachokera ku Portugal.
^ ndime 3 Onani nkhani yakuti “Ntchito Yokolola Idakalipo Yambiri” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2014, tsamba 31-32.