NKHANI YOPHUNZIRA 17
Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Polimbana ndi Mizimu Yoipa
‘Tikulimbana . . . ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.’—AEF. 6:12.
NYIMBO NA. 55 Musawaope
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Malinga ndi Aefeso 6:10-13, kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amatiganizira? Fotokozani.
NJIRA imodzi imene Yehova wasonyezera kuti amatiganizira ndi yakuti amatithandiza polimbana ndi adani athu. Adani athu oopsa kwambiri ndi Satana ndi ziwanda. Yehova amatichenjeza za adani amenewa ndipo amatipatsa zinthu zotithandiza polimbana nawo. (Werengani Aefeso 6:10-13.) Tikamadalira kwambiri Yehova n’kumalola kuti atithandize, tikhoza kupambana polimbana ndi Mdyerekezi. Tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro ngati chimene anali nacho mtumwi Paulo. Paja analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?”—Aroma 8:31.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Akhristufe sitimachita chidwi kwambiri ndi Satana komanso ziwanda. Chimene timafuna kwambiri ndi kuphunzira za Yehova komanso kumutumikira. (Sal. 25:5) Ngakhale zili choncho, timafunika kudziwa zimene Satana amachita. Zimenezi zingathandize kuti asatipusitse. (2 Akor. 2:11) Munkhaniyi, tikambirana njira yaikulu imene Satana ndi ziwanda zake amagwiritsa ntchito popusitsa anthu. Tikambirananso zimene tingachite kuti tisagonje polimbana nawo.
KODI MIZIMU YOIPA IMAPUSITSA BWANJI ANTHU?
3-4. (a) Kodi kukhulupirira mizimu n’kutani? (b) Kodi kukhulupirira mizimu n’kofala bwanji?
3 Njira yaikulu imene Satana ndi ziwanda amagwiritsa ntchito popusitsa anthu ndi kukhulupirira mizimu. Anthu amene amakhulupirira mizimu amanena kuti angathe kuchita *
zinthu zodabwitsa. Mwachitsanzo, ena amanena kuti angathe kudziwa zam’tsogolo pogwiritsa ntchito matsenga kapena kungoona mmene nyenyezi zikuonekera. Ena amachita zinthu zosonyeza kuti amatha kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Pomwe ena amachita zamatsenga ndi ufiti moti amati akhoza kulodza munthu.4 Kodi kukhulupirira mizimu n’kofala bwanji? Kafukufuku amene anachitika m’mayiko 18 a ku Latin America ndi ku Caribbean anasonyeza kuti munthu mmodzi pa anthu atatu alionse amakhulupirira zamatsenga ndi ufiti. Ndipo anthu ambiri amakhulupirira kuti n’zotheka kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Kafukufuku wina anachitika m’mayiko 18 a ku Africa ndipo anasonyeza kuti pa anthu 10 alionse, anthu oposa 5 amachita kapena kuopa zaufiti. Koma kaya ifeyo timakhala kuti, tiyenera kusamala kuti tisayambe kukhulupirira mizimu. Tizikumbukira kuti cholinga cha Satana n’chakuti asocheretse “dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Chiv. 12:9.
5. Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu akukhulupirira mizimu?
5 Yehova ndi “Mulungu wa choonadi.” (Sal. 31:5) Ndiye kodi amamva bwanji akaona anthu akukhulupirira mizimu? Zimamunyansa kwambiri. Paja Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deut. 18:10-12) Akhristu sayendera Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli. Koma maganizo a Yehova pa nkhani yokhulupirira mizimu sanasinthe.—Mal. 3:6.
6. (a) Kodi Satana amapusitsa bwanji anthu? (b) Mogwirizana ndi Mlaliki 9:5, kodi n’chiyani chimachitika munthu akamwalira?
6 Yehova amatichenjeza pa nkhani yokhulupirira mizimu chifukwa amadziwa kuti imeneyi ndi njira imene Satana akupusitsira anthu. Satana amagwiritsa ntchito njirayi pofuna kuti anthu azikhulupirira kuti munthu akafa amakakhalanso ndi moyo kwinakwake. (Werengani Mlaliki 9:5.) Kukhulupirira mizimu kumachititsanso kuti anthu azikhala mwamantha n’kusiya kutumikira Yehova. Cholinga cha Satana n’chakuti anthu azidalira mizimu yoipa m’malo modalira Yehova.
KODI TINGALIMBANE BWANJI NDI MIZIMU YOIPA?
7. Kodi Yehova amatiuza zinthu zotani?
7 Monga tanena kale, Yehova amatiuza zinthu zimene zingatithandize kuti tisapusitsidwe ndi Satana komanso ziwanda. Tiyeni tsopano tikambirane zimene tingachite kuti tisapusitsidwe.
8. (a) Tchulani chinthu chofunika kwambiri chimene chingatithandize kuti tisapusitsidwe ndi mizimu yoipa. (b) Kodi lemba la Salimo 146:4 limasonyeza bwanji kuti Satana amanamiza anthu pa nkhani ya imfa?
8 Tiziwerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu. Zimenezi n’zofunika kwambiri kuti tisapusitsidwe ndi mabodza amene ziwanda zimafalitsa. Mawu a Mulungu ali ngati lupanga limene limaduladula mabodza a Satana. (Aef. 6:17) Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amatsutsa bodza lakuti anthu amoyo akhoza kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. (Werengani Salimo 146:4.) Amatiuzanso kuti Yehova yekha ndi amene angathe kulosera zoona zokhazokha. (Yes. 45:21; 46:10) Tikamawerenga komanso kusinkhasinkha Mawu a Mulungu nthawi zonse, tikhoza kupewa ndiponso kudana ndi mabodza a Satana ndi ziwanda.
9. Kodi tiyenera kupewa zinthu ziti zokhudza kukhulupirira mizimu?
9 Tizipewa kuchita chilichonse chokhudzana ndi mizimu yoipa. Akhristufe timapewa kuchita chinthu chilichonse chokhudza kukhulupirira mizimu. Mwachitsanzo, timapewa kupita kwa anthu amene amati amalankhulana ndi anthu amene anamwalira. Monga tinaonera munkhani yapita ija, timapewa kuchita miyambo yokhudza kukhulupirira kuti munthu akafa amakhalabe ndi moyo kwinakwake. Sitiyesanso kudziwa zam’tsogolo pogwiritsa ntchito anthu olosera kapena okhulupirira nyenyezi. (Yes. 8:19) Timadziwa kuti zonsezi ndi zoopsa chifukwa zingachititse kuti tizigwirizana ndi Satana komanso ziwanda.
10-11. (a) Kodi Akhristu a ku Efeso anatani ataphunzira choonadi? (b) Malinga ndi 1 Akorinto 10:21, n’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Akhristu oyambirira, nanga tingawatsanzire bwanji?
10 Tizitaya chinthu chilichonse chokhudzana ndi matsenga. Anthu ena amene ankakhala ku Efeso nthawi ya atumwi ankachita zamizimu. Koma ataphunzira choonadi anasiya. Baibulo limanena kuti: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” (Mac. 19:19) Anthuwa anaona kuti m’pofunika kusiyiratu kuchita zamizimu. Mabuku awo anali odula kwambiri. Koma m’malo mopatsa anthu ena kapena kuwagulitsa, anawawononga. Iwo ankaganizira kwambiri zosangalatsa Yehova osati mtengo wa mabukuwo.
11 Kodi tingatsanzire bwanji Akhristu amenewa? Ndi bwino kutaya chinthu chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. Apa tikutanthauza zinthu monga zithumwa, mankhwala otsirikira 1 Akorinto 10:21.
kapena chinthu chilichonse chimene anthu amavala kapena kukhala nacho pofuna kudziteteza ku mizimu yoipa.—Werengani12. Kodi tingadzifunse mafunso ati pa nkhani ya zosangalatsa?
12 Tizisankha bwino zosangalatsa. Tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimawerenga mabuku, magazini kapena nkhani za pa intaneti zokhudzana ndi matsenga? Nanga bwanji nyimbo zimene ndimamvetsera, mavidiyo amene ndimaonera kapena masewera apakompyuta amene ndimakonda? Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda zimakhudzana ndi zamizimu? Kodi zimakhala zokhudza mavampaya, mizukwa kapena zinthu zina zamatsenga? Kodi zimandichititsa kuganiza kuti zinthu zokhudzana ndi matsenga, kulodzana kapena kutembererana zilibe vuto?’ N’zoona kuti pali zosangalatsa zina zimene zimasonyeza zinthu zongopeka zomwe sizikhudzana ndi zamizimu. Koma tikamasankha zosangalatsa tiyenera kupewa chilichonse chimene Yehova amadana nacho. Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti ‘tisapalamule chilichonse kwa Mulungu.’—Mac. 24:16. *
13. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani?
13 Tizipewa kufotokoza nkhani zokhudza ziwanda. Tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani imeneyi. (1 Pet. 2:21) Iye asanabwere padzikoli anali kumwamba ndipo amadziwa zambiri zokhudza Satana ndi ziwanda zake. Koma sankakamba zimene mizimu yoipayi yachita. Yesu ankafuna kukhala mboni ya Yehova osati mneneri wa Satana. Ifenso tizimutsanzira popewa kufalitsa nkhani zokhudza ziwanda. M’malomwake, zolankhula zathu zizisonyeza kuti mtima wathu ‘wagalamuka ndi nkhani yosangalatsa’ yomwe ndi mfundo za choonadi.—Sal. 45:1.
14-15. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa ziwanda? (b) Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yehova amateteza anthu ake masiku ano?
14 Tisamaope mizimu yoipa. M’dzikoli zinthu zoipa zikhoza kutichitikira. Mwachitsanzo, tingakumane ndi ngozi, matenda kapena imfa yadzidzidzi. Koma tisamaganize kuti mizimu yoipa ndi imene yachititsa. Baibulo limanena kuti “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera” aliyense. (Mlal. 9:11) Yehova wasonyeza kale kuti ndi wamphamvu kuposa ziwanda. Mwachitsanzo, Mulungu sanalole Satana kuti aphe Yobu. (Yobu 2:6) Munthawi ya Mose, Yehova anasonyeza kuti ndi wamphamvu kuposa amatsenga a ku Iguputo. (Eks. 8:18; 9:11) Yesu atapita kumwamba, Yehova anamupatsa mphamvu zambiri moti anathamangitsako Satana ndi ziwanda zake. Posachedwapa, iwo adzaponyedwanso m’phompho ndipo pa nthawiyo sadzavutitsanso aliyense.—Chiv. 12:9; 20:2, 3.
15 Tili ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Yehova amateteza anthu ake masiku ano. Mwachitsanzo, tikutha kulalikira komanso kuphunzitsa anthu choonadi padziko lonse. (Mat. 28:19, 20) Tikamachita zimenezi timathandiza anthu kudziwa ziwembu za Satana. Satana akanakhala ndi mphamvu zambiri akanatha kuletseratu ntchito yathu, koma sangathe. Ndiye tisamaope mizimu yoipa. Paja “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Ngati ndife okhulupirika kwa Yehova, ziwanda sizingatiwonongeretu.
ANTHU AMENE AMALOLA KUTI YEHOVA AWATHANDIZE AMADALITSIDWA
16-17. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti pamafunika kulimba mtima kuti tikane zamizimu.
16 Pamafunika kulimba mtima kuti tikane zamizimu, makamaka ngati anzathu kapena achibale akutitsutsa. Koma Yehova amadalitsa anthu amene amalimba mtima pa nthawi
ngati imeneyi. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira mlongo Erica wa ku Ghana. Mlongoyu anayamba kuphunzira Baibulo ali ndi zaka 21. Bambo ake anali wansembe ndipo ankachita zamizimu. Ndiye ankafuna kuti mlongoyu azichita nawo mwambo wodya nyama imene inkaperekedwa nsembe kwa milungu ya bambo akewo. Erica atakana, banja lake lonse linaona kuti wanyoza milungu yawo. Onse ankakhulupirira kuti milunguyo iwalanga powadwalitsa misala kapena matenda ena.17 Anthu a m’banja lakelo anamukakamiza kwambiri koma iye sanalole. Kenako anamuthamangitsa kunyumba kwawo moti ankasungidwa ndi a Mboni ena. Apa tingati Yehova anadalitsa Erica pomupatsa banja latsopano ndipo ankakhala nawo ngati achibale ake enieni. (Maliko 10:29, 30) Ngakhale kuti achibale ake anamukana komanso kumuwotchera katundu, Erica anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Iye anabatizidwa ndipo panopa akuchita upainiya wokhazikika. Erica saopa ziwanda. Pofotokoza za achibale ake, Erica anati: “Ndimapemphera tsiku lililonse kuti nawonso adziwe Yehova n’kupeza ufulu umene munthu amakhala nawo akamatumikira Mulungu wachikondi.”
18. Kodi timapeza madalitso otani tikamadalira Yehova?
18 Sikuti tonsefe tingakumane ndi mayesero ngati amenewa. Ngakhale zili choncho, tonsefe tiyenera kukana zamizimu n’kumadalira Yehova. Tikatero, tidzadalitsidwa kwambiri ndipo sitidzapusitsidwa ndi mabodza a Satana. Komanso sitingasowe mtendere chifukwa choopa ziwanda. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tidzalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Paja Yakobo analemba kuti: “Gonjerani Mulungu, koma tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani. Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yak. 4:7, 8.
NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke
^ ndime 5 Chifukwa chotikonda, Yehova watichenjeza za mizimu yoipa komanso mmene ingatisocheretsere. Kodi mizimu yoipa imasocheretsa bwanji anthu? Nanga tingalimbane nayo bwanji? Munkhaniyi tikambirana mmene Yehova amatithandizira kuti tisasocheretsedwe.
^ ndime 3 MATANTHAUZO A MAWU ENA: Kukhulupirira mizimu kumatanthauza kukhulupirira kapena kuchita zinthu zokhudzana ndi ziwanda. Anthu okhulupirira mizimu amakhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umakhalabe ndi moyo ndipo tikhoza kulankhula naye kudzera mwa anthu ena. Amathanso kuchita zinthu zodabwitsa, zamatsenga komanso zokhudza ufiti. Ena amati akhoza kutemberera munthu, kulodza kapena kuchesula.
^ ndime 12 Akulu alibe udindo wopanga malamulo pa nkhani ya zosangalatsa. Mkhristu aliyense ayenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo posankha nkhani zoti awerenge, mavidiyo oti aonere kapena masewera oti achite. Anthu omwe ndi mitu ya mabanja ayenera kuonetsetsa kuti banja lawo likutsatira mfundo za m’Baibulo posankha zosangalatsa.—Onani nkhani ya pa jw.org® yakuti, “Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?” Pitani pamene alemba kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI.
^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi chosonyeza Yesu ali Mfumu yamphamvu kumwamba ndipo akutsogolera gulu la angelo. Pamwamba pawo pali mpando wachifumu wa Yehova.