Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
“Pereka ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.”—MIY. 16:3.
1-3. (a) Kodi achinyamata amakumana ndi vuto liti, nanga zimenezi tingaziyerekezere ndi chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi achinyamata angatani kuti athane ndi vutoli?
TIYEREKEZE kuti muli pa ulendo wokachita zinthu zina zofunika kwambiri m’tauni ina yakutali. Ulendowo ndi wa pa basi ndipo ukutengerani nthawi yaitali. Mutafika kumalo okwerera basi mukupeza kuti kwadzaza anthu ndipo kuli mabasi ambirimbiri. Ngati mukudziwa bwino kumene mukupita, mukhoza kukwera basi yoyenera ndipo simungasokonezeke. Koma ngati mungakwere basi ina iliyonse, mukhoza kupita kumalo kolakwika.
2 Achinyamata masiku ano ali ngati munthu wa pa ulendo. Ulendo wake si wongoyenda pa basi, koma ndi wa moyo wawo wonse. Nthawi zina amavutika kuti asankhe bwino zochita ndipo anthu ambiri amawauza zinthu zosiyanasiyana zoti achite pa moyo. Koma ngati ali kale ndi cholinga pa moyo wawo, savutika kusankha zochita. Ndiye kodi ndi zolinga ziti zimene angakhale nazo?
3 Nkhaniyi iyankha funso limeneli ndipo isonyeza kuti achinyamata ayenera kukhala ndi cholinga chosangalatsa Yehova. Izi zikutanthauza kuti ayenera kuganizira zimene Yehova amafuna akamasankha zinthu pa Miyambo 16:3.
nkhani zokhudza maphunziro, ntchito, banja komanso zinthu zina. M’mawu ena tingati ndi bwino kukhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. Achinyamata amene amayesetsa kuti akwaniritse zolinga zawo pa nkhani yotumikira Yehova amadalitsidwa kwambiri.—WerenganiN’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA NDI ZOLINGA ZAUZIMU?
4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
4 Kunena zoona ndi nzeru kukhala ndi zolinga zauzimu munthu adakali wamng’ono. Tikutero pa zifukwa zitatu. Zifukwa ziwiri zoyambirira zikusonyeza kuti kuchita zimenezi kumathandiza kuti ubwenzi wa munthuyo ndi Mulungu ulimbe pomwe chifukwa chomaliza chikusonyeza kuti munthu akachita zimenezi ali wamng’ono zimamuthandiza kuti azisankha bwino zochita pa moyo wake.
5. Kodi chifukwa chachikulu chokhalira ndi zolinga zauzimu n’chiyani?
5 Chifukwa chachikulu chokhalira ndi zolinga zauzimu n’chakuti timafuna kusonyeza kuti timayamikira chikondi cha Yehova komanso zonse zimene watichitira. Pa nkhani imeneyi, wolemba masalimo ananena kuti: “Ndi bwino kuyamika inu Yehova . . . Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu. Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.” (Sal. 92:1, 4) Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kuganizira zinthu zambirimbiri zimene Yehova wakupatsani. Mwachitsanzo, wakupatsani moyo, mfundo zimene mumakhulupirira, Baibulo, mpingo komanso chiyembekezo chabwino kwambiri. Munthu akamaika zinthu zauzimu pamalo oyamba amasonyeza kuti akuyamikira zinthu zonse zimene Mulungu watipatsa ndipo zimathandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba.
6. (a) Kodi zolinga zauzimu zimakhudza bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova? (b) Kodi achinyamata angakhale ndi zolinga ziti adakali aang’ono?
6 Chifukwa chachiwiri chokhalira ndi zolinga zauzimu n’chakuti munthu akamayesetsa kukwaniritsa zolingazo amakhala akupanga mbiri yabwino pamaso pa Yehova. Izi zimathandiza kuti ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova uzilimba. Paja mtumwi Paulo ananena kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Choncho musaganize kuti ndinu wamng’ono moti simungakhale ndi zolinga zauzimu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina dzina lake Christine. Ali ndi zaka 10 anali ndi cholinga choti aziwerenga nkhani zofotokoza mbiri ya moyo wa abale ndi alongo okhulupirika. Mnyamata wina dzina lake Toby anali ndi cholinga choti amalize kuwerenga Baibulo asanabatizidwe. Pa nthawiyi n’kuti Toby ali ndi zaka 12 zokha. Mnyamata wina dzina lake Maxim anabatizidwa ali ndi zaka 11 ndipo mchemwali wake dzina lake Noemi anabatizidwa ali ndi zaka 10. Onse anali ndi zolinga zoti akatumikire pa Beteli ndipo ankayesetsa kuti akwaniritse cholinga chawochi. Pofuna kuti asamaiwale cholingachi, anakhoma fomu yofunsira utumiki wa pa Beteli pakhoma la nyumba yawo. Kodi inuyo ndi zolinga ziti zimene mungakonde kukhala nazo, nanga mungachite chiyani kuti muzikwaniritse?—Werengani Afilipi 1:10, 11.
7, 8. (a) Kodi kukhala ndi zolinga kumathandiza bwanji posankha zochita? (b) N’chifukwa chiyani mtsikana wina anakana kupita kuyunivesite?
7 Chifukwa chachitatu chokhalira ndi zolinga zauzimu n’chakuti zimatithandiza posankha zochita pa moyo wathu. Achinyamata amafunika kusankha zochita pa nkhani monga maphunziro, ntchito komanso zinthu zina. Munthu akamasankha zochita amakhala ngati wafika pa mphambano ndipo akusankha msewu woti adutse. Ngati munthu akudziwa msewu umene ungakamufikitse kumene akupita, savutika kusankha. Nayenso munthu amene akudziwa zolinga zimene ali nazo savutika kusankha zochita. Lemba la Miyambo 21:5 limanena kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” Choncho munthu akakhala ndi zolinga adakali wamng’ono zinthu zimamuyendera bwino mwamsanga. Izi n’zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Damaris pa nthawi imene ankafunika kusankha zochita ali mtsikana.
8 Damaris anakhoza bwino kwambiri kusekondale.
Iye anapatsidwa mwayi woti alipiriridwe kukaphunzira zamalamulo kuyunivesite koma iye anasankha kukagwira ntchito kubanki. Anachita zimenezi chifukwa chakuti anasankha kale ali wamng’ono kuti adzachite upainiya. Choncho anafunika kusankha ntchito imene ingamamupatse mpata. Mlongoyu akanapita kuyunivesite n’kupeza digiri ya zamalamulo akanapeza ntchito yandalama zambiri koma si bwenzi ikumupatsa mpata. Panopa Damaris wakhala akuchita upainiya kwa zaka 20. Kodi iye amaona kuti anasankha bwino? Mlongoyu anati: “Kubanki kumene ndimagwira ntchito ndimakumana ndi maloya ambiri. Iwo amagwira ntchito imene ineyo ndikanagwira zikanakhala kuti ndalola kukaphunzira zamalamulo. Koma ambiri mwa iwo sasangalala ndi ntchito yawo. Upainiya umene ndinasankha wandithandiza kuti ndisamadandaule ndi ntchito yanga koma ndizisangalala chifukwa chotumikira Yehova kwa zaka zambiri.”9. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira achinyamata athu?
9 M’mipingo yambiri muli achinyamata amene akuchita bwino ndipo ayenera kuyamikiridwa kwambiri. Iwo anadzipereka kwa Yehova ndipo akuyesetsa kukwaniritsa zolinga zawo zauzimu. Achinyamatawa amasangalala komanso amaphunzira kutsatira mfundo za Yehova pa zonse zimene amachita. Amaganizira zimene Yehova amafuna posankha maphunziro, ntchito komanso nkhani zokhudza banja. Paja Mfumu Solomo analemba kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miy. 3:5, 6) Achinyamata m’mipingo yachikhristu ndi amtengo wapatali pamaso pa Yehova ndipo Yehovayo amawakonda kwambiri, kuwateteza, kuwatsogolera komanso kuwadalitsa.
MUZIKHALA OKONZEKA MOKWANIRA KUCHITIRA UMBONI
10. (a) N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira iyenera kukhala pamalo oyamba? (b) Kodi tingatani kuti tizilalikira mogwira mtima?
10 Wachinyamata amene amafunitsitsa kusangalatsa Yehova amaganizira kwambiri za utumiki. Paja Yesu Khristu ananena kuti “uthenga wabwino uyenera ulalikidwe choyamba.” (Maliko 13:10) Popeza ntchito yolalikira ndi yofunika kugwiridwa mwamsanga, tiyenera kuiika pamalo oyamba. Ndiye kodi inuyo mungayesetse kuwonjezera nthawi imene mumalalikira? Nanga kodi mungachite upainiya? Kodi mungatani ngati panopa simusangalala kwenikweni ndi ntchito yolalikira? Kodi mungatani kuti muzilalikira mogwira mtima? Pali zinthu ziwiri zimene mungachite. Choyamba, muyenera kukonzekera bwino ndipo musamagwe ulesi pa nkhani yophunzitsa anthu mfundo zachoonadi zimene mukudziwa. Mukhoza kudabwa kuona mmene mungasangalalire polalikira.
11, 12. (a) Kodi achinyamata angakonzekere bwanji kuti azilalikira mogwira mtima? (b) Kodi mnyamata wina anagwiritsa ntchito bwanji mpata umene unapezeka kuti alalikire kusukulu?
11 Mwina poyambira pabwino pangakhale kukonzekera yankho la funso limene anzanu ambiri kusukulu amakonda kufunsa, monga lakuti, “N’chifukwa chiyani umakhulupirira zoti kuli Mulungu?” Pa webusaiti yathu pali nkhani zothandiza achinyamata kuti asamavutike kuyankha funso ngati limeneli. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA. Mukapita pamenepa mudzapeza zochita pa nkhani yakuti “N’chifukwa chiyani ndimakhulupirira zoti kuli Mulungu?” Mfundo zimene zili pamenepo zingakuthandizeni kukonzekera zimene mungayankhe. Pali lemba la Aheberi 3:4, Aroma 1:20 ndi Salimo 139:14, ndipo onsewa angakuthandizeni kufotokoza molimba mtima zimene mumakhulupirira. Ndiye mungagwiritse ntchito zinthu ngati zimenezi poyankha mafunso osiyanasiyana.—Werengani 1 Petulo 3:15.
12 Mpata ukapezeka, muzilimbikitsa anzanu kuti apite pawebusaiti ya jw.org. Izi n’zimene mnyamata wina dzina lake Luca anachita. Tsiku lina anthu m’kalasi yake ankakambirana za zipembedzo ndipo iye anaona kuti m’buku limene ankagwiritsa ntchito munali mfundo zolakwika zokhudza Mboni za Yehova. Ngakhale kuti poyamba ankachita mantha, anapempha kuti afotokoze zoona zake pa Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? Luca anasangalala kwambiri kuona kuti wakwanitsa kuchitira umboni bwinobwino.
nkhaniyo ndipo aphunzitsi ake anamulola. Luca anafotokoza zimene amakhulupirira komanso anasonyeza kalasi yonse webusaiti yathu. Pomaliza, aphunzitsi anauza ana onse m’kalasiyo kuti akaonere vidiyo yamakatuni yakuti13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwa ulesi tikakumana ndi mavuto?
13 Musataye mtima ngati nthawi zina mungakumane ndi mavuto poyesetsa kulalikira. (2 Tim. 4:2) Mukakumana ndi vuto muzikumbukira zolinga zanu ndipo musasinthe. Pamene mlongo wina dzina lake Katharina anali ndi zaka 17, anali ndi cholinga choti azilalikira munthu aliyense amene amagwira naye ntchito. Munthu wina anamunyoza kwambiri maulendo angapo koma iye sanagwe ulesi. Munthu wina dzina lake Hans ataona kuti mlongoyu akusonyezabe makhalidwe abwino ngakhale pamene akunyozedwa anachita chidwi kwambiri. Anayamba kuwerenga mabuku athu kenako kuphunzira Baibulo mpaka anafika pobatizidwa. Katharina anasamuka kuderali ndipo sanadziwe kuti zimene zachitika n’zimenezi. Patadutsa zaka 13, iye ali m’Nyumba ya Ufumu ndi banja lake anangomva kuti Hans ndi amene wabwera kudzakamba nkhani. Katharina anasangalala kwambiri kuona kuti sanasinthe cholinga chake cholalikira anzake akuntchito.
MUSALOLE KUTI ZINTHU ZINA ZIKUSOKONEZENI
14, 15. (a) Kodi achinyamata ayenera kukumbukira mfundo ziti akakumana ndi mayesero? (b) Kodi achinyamata angatani kuti asasokonezedwe ndi anzawo?
14 Mundime zapitazi takambirana kuti muyenera kukhala ndi cholinga chosangalatsa Yehova nthawi zonse. Taona kuti izi zingatheke ngati mutakhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. Mwina mumaona achinyamata ena amene amangoganizira zonjoya basi ndipo nthawi zina amafuna kuti muzichita nawo zimene amachita. Choncho mungafunike kusonyeza kuti muli ndi zolinga zanu zimene mukufunitsitsa kuzikwaniritsa. Musalole kuti anzanu akusokonezeni. Kumbukirani chitsanzo cha kumalo okwerera basi chija. Simungakwere basi yopita kulikonse chifukwa chongoona kuti anthu amene ali m’basiyo akuoneka kuti akusangalala kwambiri.
15 Pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni kuti musasokonezedwe ndi anzanu. Choyamba, ndi bwino kupewa kupezeka pamalo amene mungayesedwe. Miy. 22:3) Muzikumbukiranso mavuto amene mungakumane nawo chifukwa chongotengera makhalidwe oipa a anzanu. (Agal. 6:7) Chinthu china chimene chingakuthandizeni n’kuzindikira kuti mumafunika malangizo. Ngati ndinu odzichepetsa mudzalola kuti makolo anu kapena abale ndi alongo odziwa zambiri akupatseni malangizo.—Werengani 1 Petulo 5:5, 6.
(16. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti mtima wodzichepetsa ndi wothandiza.
16 Mtima wodzichepetsa unathandiza m’bale wina dzina lake Christoph kuti alandire malangizo abwino. Iye atangobatizidwa kumene, anayamba kupita kukachita masewera olimbitsa thupi pamalo enaake. Ndiyeno anyamata ena kumene ankachitira masewerawo anamuuza kuti alowe kagulu kenakake. Atakambirana nkhaniyi ndi mkulu wina, anamuuza kuti aganizire mavuto amene angakumane nawo akalowa m’kaguluko. Mwachitsanzo, anamuuza kuti akhoza kuyamba mtima wokonda mpikisano. Koma Christoph sanamvere ndipo analowabe m’kaguluko. Pasanapite nthawi yaitali, anazindikira kuti masewerowo anali angozi ndipo anthu ankachitirana nkhanza. M’baleyu anakambirananso ndi akulu ena amene anamupatsa malangizo a m’Malemba. Pomaliza Christoph anati: “Yehova anandipatsa alangizi abwino kwambiri ndipo ndinamvera, kungoti ndinamvera mochedwa.” Kodi inuyo muli ndi mtima wodzichepetsa moti mungamvere malangizo abwino?
17, 18. (a) Kodi Yehova amafuna kuti achinyamata azichita chiyani masiku ano? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene achikulire ena amadandaula nazo, nanga ife tingazipewe bwanji? Perekani chitsanzo.
17 Paja Baibulo limati: “Mnyamatawe [kapena mtsikanawe], sangalala ndi unyamata wako, ndipo mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako.” (Mlal. 11:9) Yehova amafuna kuti achinyamata azisangalala. Ndiyeno nkhaniyi yasonyeza zimene zingathandize achinyamata kuti azisangalala. Ndi bwino kukhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa ndiponso kuika Yehova patsogolo posankha zochita. Mukachita zimenezi mwamsanga, mudzaonanso mwamsanga kuti Yehova akukutsogolerani, akukutetezani komanso akukudalitsani. Ndi bwino kuganizira malangizo onse amene timapeza m’Mawu a Mulungu n’kumatsatira mfundo yakuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”—Mlal. 12:1.
18 Tisaiwale kuti palibe amene angakhale wachinyamata kwa nthawi yaitali. Paja anthufe sitichedwa kukula n’kukalamba. Zimakhala zomvetsa chisoni kuona achikulire akudandaula zimene analakwitsa chifukwa chosankha molakwika ali achinyamata, ndipo ena amazindikira kuti analibe n’komwe zolinga zilizonse. Koma achinyamata amene amakhala ndi zolinga zauzimu n’kumazikwaniritsa sanong’oneza bondo ngakhale atakula. Izi n’zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Mirjana. Mlongoyu ali wachinyamata ankadziwa bwino masewera enaake moti anapemphedwa kuti akachite nawo mpikisano wotchuka kwambiri. Koma iye sanalole zimenezi, m’malomwake anayamba upainiya. Panopa papita zaka 30 kuchokera nthawi imeneyo ndipo mlongoyu akuchitabe utumiki wa nthawi zonse limodzi ndi mwamuna wake. Iye anati: “Kukhala ndi zolinga zoti titchuke, tizilemekezedwa, tikhale ndi udindo kapena tilemere n’kosathandiza chifukwa zonsezi n’zakanthawi. Chinthu chofunika kwambiri komanso chimene chingatithandize mpaka m’tsogolo ndi kukhala ndi zolinga zokhudza kutumikira Mulungu ndiponso kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu.”
19. Kodi kukhala ndi zolinga zauzimu ukadali wamng’ono n’kothandiza bwanji?
19 Achinyamata amene tili nawo mumpingo ayenera kuyamikiridwa kwambiri chifukwa chokhala ndi mtima wofuna kutumikira Yehova ndi moyo wawo wonse. Achinyamata amakwanitsa kuchita zimenezi ngati ali ndi zolinga zauzimu komanso ngati amaika patsogolo ntchito yolalikira. Amayesetsanso kuti asamasokonezedwe ndi dzikoli. Achinyamata oterewa sayenera kukayikira zoti Yehova sadzaiwala zimene akuchita. Azikumbukira kuti pali abale ndi alongo amene ali kumbali yawo ndipo akamaika Yehova patsogolo, zolinga zawo zonse zidzakwaniritsidwa.