Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Paulo Anateteza Uthenga Wabwino kwa Akuluakulu a Boma

Paulo Anateteza Uthenga Wabwino kwa Akuluakulu a Boma

“MUNTHU ameneyu ndi chiwiya changa chochita kusankhidwa chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina komanso kwa mafumu.” (Mac. 9:15) Mawu amenewa ananena ndi Ambuye Yesu ndipo ankanena za Myuda wina amene anali atatsala pang’ono kukhala Mkhristu. Kenako iye anayamba kudziwika kuti mtumwi Paulo.

Mmodzi mwa “mafumu” amenewa anali mfumu ya Aroma dzina lake Nero. Kodi inuyo mungamve bwanji mutapezeka pamaso pa mfumu ngati imeneyi kuti mukafotokoze za chikhulupiriro chanu? Chifukwatu Akhristufe timalimbikitsidwa kuti tiyenera kutsanzira Paulo. (1 Akor. 11:1) Choncho tiyenera kutsanziranso zimene iye anachita pamene ankaimbidwa milandu yosiyanasiyana.

Aisiraeli komanso Ayuda onse odzipereka amene ankakhala m’madera osiyanasiyana ankatsatira Chilamulo cha Mose. Koma pambuyo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., atumiki a Yehova sankafunikanso kutsatira Chilamulochi. (Mac. 15:28, 29; Agal. 4:9-11) Komabe Paulo ndi Akhristu ena sankanyoza Chilamulo. Choncho ankatha kuuza anthu uthenga wabwino m’madera ambiri a Ayuda. (1 Akor. 9:20) Ndipotu nthawi zambiri Paulo ankapita kumasunagoge n’kumakalalikira anthu amene ankadziwa kale Mulungu wa Abulahamu. Ankathanso kukambirana nawo kuchokera m’Malemba Achiheberi.—Mac. 9:19, 20; 13:5, 14-16; 14:1; 17:1, 2.

Atumwi ankakhala ku Yerusalemu ndipo ankayang’anira ntchito yolalikira. Nthawi zambiri iwo ankaphunzitsa m’kachisi. (Mac. 1:4; 2:46; 5:20) Pa nthawi ina Paulo atapita ku Yerusalemuko, anthu anamugwira n’kumumanga. Ichi chinali chiyambi cha milandu imene inakamufikitsa ku Roma.

ANAGWIRITSA NTCHITO MALAMULO A AROMA

Kodi akuluakulu a boma la Aroma ankaona bwanji mfundo zimene Paulo ankalalikira? Kuti tiyankhe funsoli, tiyenera kukambirana kaye maganizo a Aroma pa nkhani ya zipembedzo zosiyanasiyana. Iwo sankakakamiza anthu kuti asiye zipembedzo zawo pokhapokha ngati akuona kuti angaukire boma kapena kusokoneza makhalidwe abwino.

Aroma ankapereka ufulu kwa Ayuda m’madera onse amene ankalamulira. Buku lina lofotokoza za Akhristu oyambirira linati: “Ayuda ankalemekezedwa mu ulamuliro wa Aroma. . . . Ankaloledwa kulambira Mulungu wawo ndipo sankakakamizidwa kulambira milungu ya Aroma. Iwo ankatsatira malamulo awo kulikonse kumene ankakhala.” Ayuda sankakakamizidwanso kuti azikamenya nawo nkhondo. * Paulo anagwiritsa ntchito ufulu umene Aroma ankapatsa Ayuda pofotokoza zimene amakhulupirira kwa olamulira achiroma.

Koma panali anthu ena amene ankakopa anthu wamba komanso akuluakulu a boma kuti azidana ndi Paulo. (Mac. 13:50; 14:2, 19; 18:12, 13) Mwachitsanzo, akulu a mumpingo wa ku Yerusalemu anamva zoti Ayuda ena akunena kuti Paulo ankaphunzitsa zinthu zosemphana ndi Chilamulo cha Mose. Mabodza amenewa akanatha kuchititsa Ayuda amene anangolowa kumene Chikhristu kuganiza kuti Paulo salemekeza zimene Mulungu ananena. Zikanachititsanso kuti Khoti Lalikulu la Ayuda linene kuti Akhristu akutsutsana ndi Chiyuda. Pamapeto pake, Ayuda amene ankalowa Chikhristu akanazunzidwa kwambiri. Zikanachititsanso kuti iwo azisalidwa komanso asamaloledwe kukalalikira kukachisi kapena m’masunagoge. Choncho akulu analangiza Paulo kuti achite zinthu zimene zikanathandiza anthu kuona kuti mphekeserazo ndi zabodza. Zimene anamuuzazo si zimene Mulungu ankafuna koma popeza zinalibe vuto lililonse, Paulo analolera.—Mac. 21:18-27.

Zimene Paulo anachitazi zinathandiza kuti iye ‘ateteze ndiponso kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.’ (Afil. 1:7) Pa nthawi ina Paulo ali kukachisi, Ayuda anayambitsa chipolowe ndipo ankafuna kumupha. Ndiyeno mkulu wa asilikali achiroma anamutenga n’kukamutsekera. Atangotsala pang’ono kumukwapula, Paulo ananena kuti iye ndi Mroma. Izi zinachititsa kuti apite naye ku Kaisareya kumene kunkakhala Aroma olamulira ku Yudeya. Kumenekonso anali ndi mwayi wolalikira kwa akuluakulu a boma. Zimenezi zinathandiza kuti anthu ena amene sakanalalikiridwa akhalenso ndi mwayi womva zambiri zokhudza Chikhristu.

Nkhani ya pa Machitidwe chaputala 24 imasonyeza kuti Felike, yemwe ankalamulira Yudeya, ndi amene ankaweruza mlandu wa Paulo. Felike anali atamva kale zinthu zina zimene Akhristu amakhulupirira. Ayuda ananena kuti Paulo anaphwanya malamulo achiroma m’njira zitatu. Ananena kuti iye ankalimbikitsa Ayuda kuti aziyambitsa chisokonezo, ankatsogolera gulu lampatuko komanso kuti ankaipitsa kachisi amene Aroma ankamuteteza. (Mac. 24:5, 6) Milandu imene ankamunamizirayi ikanachititsa kuti aphedwe.

Masiku ano, Akhristu ayenera kuganizira zimene Paulo anachita pamene ankazengedwa milandu imeneyi. Mtima wake unali m’malo ndipo ankayankha mwaulemu. Iye anafotokoza za Chilamulo komanso Aneneri ndipo ananena kuti anali ndi ufulu wolambira ‘Mulungu wa makolo ake.’ Ufulu umene ankanenawu ndi womwe Aroma ankapatsa Ayuda onse. (Mac. 24:14) Zitatero, mlanduwu unapitirira mpaka kukafika kwa Porikiyo Fesito kenako kwa Mfumu Herode Agiripa.

Ndiyeno pofuna kuti aweruzidwe mwachilungamo, Paulo ananena kuti: “Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!” (Mac. 25:11) Pa nthawiyo, Kaisara anali wolamulira wamphamvu padziko lonse.

MLANDU WA PAULO KUKHOTI LA KAISARA

Pa nthawi ina, mngelo anauza Paulo kuti: “Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara.” (Mac. 27:24) Mfumu ya Roma dzina lake Nero atangoyamba kulamulira ananena kuti saziweruza yekha milandu yonse. Choncho pa zaka 8 zoyambirira za ulamuliro wake, iye ankapempha anthu ena kuti aziweruza milandu. Koma buku lina lofotokoza za mtumwi Paulo linanena kuti Nero akavomera kuweruza mlandu ankauweruzira m’nyumba yake yachifumu. Linanenanso kuti iye anali ndi alangizi ambiri otchuka komanso odziwa kuweruza milandu.—The Life and Epistles of Saint Paul.

Baibulo silifotokoza ngati Nero anaweruza yekha mlandu wa Paulo kapena ngati anapempha anthu ena, anthuwo n’kungomupatsa lipoti. Kaya zinali bwanji, chomwe sitikukayikira n’chakuti Paulo ananena kuti ankalambira Mulungu wa Ayuda ndipo ankalimbikitsa anthu kuti azilemekeza boma. (Aroma 13:1-7; Tito 3:1, 2) Zikuoneka kuti mlandu wa Paulo unayenda bwino moti khoti la Kaisara linamupeza wopanda mlandu.—Afil. 2:24; Filim. 22.

NAFENSO TIYENERA KUTETEZA UTHENGA WABWINO

Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.” (Mat. 10:18) Ndi mwayi waukulu kuimira Yesu. Nthawi zina tikamateteza uthenga wabwino kukhoti timawina milandu. Komabe sikuti anthu angathe “kukhazikitsa mwalamulo” ntchito yolalikira uthenga wabwino moti mavuto alionse okhudza ntchitoyi n’kutheratu. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto onse n’kubweretsa chilungamo.—Mlal. 8:9; Yer. 10:23.

Tikamayesetsa kuteteza uthenga wabwino Yehova amatamandidwa. Koma tizichita zimenezi modekha, moona mtima komanso motsimikiza ngati mmene Paulo ankachitira. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza, chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.”—Luka 21:14, 15; 2 Tim. 3:12; 1 Pet. 3:15.

Akhristu akamateteza uthenga wabwino pamaso pa akuluakulu a boma, zimathandiza kuti anthu amene sakanamva uthenga wathu, aumve. Nthawi zina akhoti amagamula zotikomera ndipo izi zimapangitsa kuti malamulo ena asinthidwe. Zikatere pamakhala ufulu wolankhula komanso wolambira. Koma kaya agamula zotikomera kapena ayi, Mulungu amasangalala atumiki ake akamasonyeza kulimba mtima pa nthawi zoterezi.

Tikamayesetsa kuteteza uthenga wabwino Yehova amatamandidwa

^ ndime 8 Wolemba mbiri wina dzina lake James Parkes anati: “Ayuda . . . anali ndi ufulu wochita zikondwerero zawo zonse. Ufulu umenewu sunkaperekedwa kwa Ayuda okha. Tikutero chifukwa chakuti Aroma ankayesetsa kupereka ufulu kwa anthu okhala m’madera osiyanasiyana amene ankalamulira.”