Muzithandiza Ana Anu Kuti Akhale Ndi Chikhulupiriro Cholimba
‘Anyamata ndi anamwali atamande dzina la Yehova.’—SAL. 148:12, 13.
NYIMBO: 88, 115
1, 2. (a) Kodi makolo amakumana ndi vuto lotani, nanga angathane nalo bwanji? (b) Kodi tikambirana mfundo 4 ziti?
BANJA lina la ku France linati: “Timakhulupirira Yehova, koma zimenezi sizikutanthauza kuti ana athunso azimukhulupirira. Chikhulupiriro si chinthu chomwe munthu amangotengera kwa makolo ake. Ana amayamba kukhala ndi chikhulupiriro pang’onopang’ono.” M’bale wina wa ku Australia analemba kuti: “Kuthandiza ana kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba ndi ntchito yovuta kwambiri. Ndipo muyenera kuchita zonse zimene mungathe. Nthawi zina mungaganize kuti mwayankha bwino funso limene mwana wakufunsani. Koma pakapita nthawi, mumangodabwa kuti akufunsanso funso lomwe lija. Zimenezi zikusonyeza kuti mayankho amene angamufike pa mtima lero, pakapita nthawi angakhale osamukhutiritsa. Choncho nkhani zina muyenera kukambirana nawo mobwerezabwereza.”
2 Ngati ndinu kholo, kodi nthawi zina mumaona kuti simungakwanitse udindo wophunzitsa ana anu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba? N’zoona kuti sitingakwanitse ndi nzeru zathu zokha. (Yer. 10:23) Koma tingakwanitse ngati tingadalire Yehova kuti atithandize. Tiyeni tione mfundo 4 zimene zingakuthandizeni. (1) Muyenera kuwadziwa bwino ana anu. (2) Muziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama kuti muzipeza zowaphunzitsa. (3) Muzigwiritsa ntchito zitsanzo. (4) Muzipemphera komanso muzikhala oleza mtima.
MUZIWADZIWA BWINO ANA ANU
3. Kodi makolo angatsanzire bwanji Yesu pophunzitsa ana awo?
3 Yesu ankafunsa otsatira ake kuti adziwe zimene amakhulupirira. (Mat. 16:13-15) Inunso mungachite bwino kufunsa ana anu kuti azifotokoza maganizo awo. Muzikambirana nawo zinthu zimene zimawadetsa nkhawa. Mnyamata wina wazaka 15 wa ku Australia analemba kuti: “Nthawi zambiri bambo anga ankakonda kundifunsa zimene ndimakhulupirira ndipo ankandithandiza kuti ndiziganiza kwambiri. Ankandifunsa mafunso ngati akuti: ‘Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?’ ‘Kodi iweyo umakhulupirira zimene Baibulo limanenazi?’ ‘N’chifukwa chiyani umakhulupirira zimenezi?’ Iwo ankafuna kuti ndiziyankha m’mawu angaanga osati kumangobwereza zimene iwowo kapena amayi ankanena. Pamene ndinkakula ndinayamba kumayankha zomveka.”
4. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuona kuti mafunso a ana awo ndi ofunika kwambiri? Perekani chitsanzo.
4 Ngati mwana wanu akukayikira mfundo zina, musamafulumire kumukalipira kapena kumutsutsa. Muyenera kukambirana naye moleza mtima. Bambo wina anati: “Muziona kuti mafunso amene ana anu amafunsa ndi ofunika kwambiri ndipo musamawanyalanyaze. Komanso musamapewe kukambirana nkhani poganiza kuti simungamasuke kukambirana nawo nkhaniyo.” Akafunsa mafunso okhudza nkhani inayake ndiye kuti akufuna kuimvetsa bwino. Musaiwale kuti Yesu ali ndi zaka 12 ankafunsa mafunso anzeru. (Werengani Luka 2:46.) Mnyamata wina wa ku Denmark wazaka 15 anati: “Nditafunsa makolo anga ngati chipembedzo chathu chilidi choona, sanandiyankhe mwaukali ngakhale kuti mwina anada nkhawa ndi funso langali. Iwo anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo.”
5. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhaledi ndi chikhulupiriro?
5 Yesetsani kuti muwadziwe bwino ana anu. Muyenera kudziwa zimene amaganizira, zimene zimawasangalatsa komanso zomwe zimawadetsa nkhawa. Musaganize kuti ali ndi chikhulupiriro chifukwa choti amapezeka pamisonkhano ndiponso amalalikira. Mukamachita nawo zinthu tsiku ndi tsiku, muzipezanso mpata wokambirana nawo zinthu zauzimu. Muzipemphera nawo komanso muziwapempherera. Muziyesetsanso kudziwa mayesero amene akukumana nawo ndipo muziwathandiza kuthana ndi mayeserowo.
MUZIYAMBA INUYO KUPHUNZIRA KUTI MUPEZE ZOWAPHUNZITSA
6. Kodi makolo akamakonda kuphunzira za Yehova, zimathandiza bwanji kuti aziphunzitsa bwino ana awo?
6 Yesu ankaphunzitsa mogwira mtima chifukwa ankakonda Yehova, Mawu ake komanso anthu. (Luka 24:32; Yoh. 7:46) Inunso mukamachita zimenezi, mungathe kuphunzitsa ana anu mogwira mtima. (Werengani Deuteronomo 6:5-8; Luka 6:45.) Choncho muzikonda kuphunzira Baibulo ndiponso mabuku athu. Muzichita chidwi ndi zinthu zachilengedwe. Muzikondanso kuwerenga nkhani za m’mabuku athu zofotokoza zinthu zosiyanasiyana zomwe Mulungu analenga. (Mat. 6:26, 28) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mudziwe zambiri, muzikonda Yehova komanso kuti muthe kuphunzitsa bwino ana anu.—Luka 6:40.
7, 8. Kodi chimachitika n’chiyani mukaphunzira mfundo yosangalatsa m’Baibulo? Perekani chitsanzo.
7 Mukaphunzira mfundo yosangalatsa m’Baibulo, mumafuna kuuza ana anu zimene mwaphunzirazo. Ndi bwino kukambirana nawo nthawi iliyonse osati pokonzekera misonkhano pokha kapena pa kulambira kwa pabanja. Zimakhalanso bwino ngati mukukambirana nawo momasuka
osati mowakakamiza. Makolo ena a ku United States amakonda kukambirana ndi ana awo pamene akudya chakudya chinachake kapena akamaona zachilengedwe. Makolowa anati: “Timakumbutsa ana athu kuti Mulungu anasonyeza chikondi komanso nzeru pa zinthu zimene analenga.” Banja lina la ku South Africa likamalima m’dimba ndi ana awo awiri, limakonda kuwafotokozera zinthu zodabwitsa zimene zimachitika kuti mbewu zimere komanso zikule. Banjali linati: “Timayesetsa kuwaphunzitsa kuti aziyamikira mphatso ya moyo chifukwa zinthu zamoyo zinapangidwa mogometsa.”8 Bambo wina wa ku Australia anapita ndi mwana wake wazaka 10 kumalo ena osungirako zinthu zochititsa chidwi. Iye anagwiritsa ntchito mpatawu ndipo anathandiza mwana wakeyo kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu komanso kuti zinthu zinachita kulengedwa. Bamboyu anati: “Tinaona nyama zina zamakedzana, zimene kalelo zinkapezeka m’nyanja. Tinachita chidwi kwambiri kuona kuti nyama zimenezi zinkakhala zokongola, zogometsa komanso zikuluzikulu. Ndiye ndinadzifunsa kuti, ‘Ngati zamoyo zimasintha n’kukhala zinthu zogometsa, n’chifukwa chiyani nyama zakale chonchi zinali zogometsa?’ Ndinaphunzira zambiri pa nyama zimenezi ndipo ndinakambirana ndi mwana wanga zokhudza nyamazi.”
MUZIGWIRITSA NTCHITO ZITSANZO
9. Kodi zitsanzo zimathandiza bwanji? Perekani chitsanzo.
9 Yesu ankawafika pamtima anthu chifukwa ankakonda kugwiritsa ntchito zitsanzo pophunzitsa. Zitsanzo zinkathandizanso anthu kuganiza komanso kuti asaiwale zimene aphunzira. (Mat. 13:34, 35) Ana amatha kuona zinthu m’maganizo mwawo. Choncho muzigwiritsa ntchito zitsanzo powaphunzitsa. Izi ndi zimene mayi wina wa ku Japan ankachita pophunzitsa ana ake awiri. Mwana wina anali wazaka 10 ndipo wina anali ndi zaka 8. Pa nthawi ina ankafuna kuwaphunzitsa zokhudza zinthu zimene Yehova anaika mlengalenga. Ndiyeno anawapatsa mkaka, shuga ndi khofi n’kuwauza kuti amupangire khofi. Mayiyu anati: “Aliyense anayesetsa kuti apange khofi wabwino. Nditawafunsa kuti n’chifukwa chiyani anachita zimenezo anati ankafuna kuti khofiyo akhale wofanana ndi amene ndimakonda. Kenako ndinawafotokozera kuti Mulungu anaonetsetsa kuti wasakaniza bwino mpweya mlengalenga n’cholinga choti ifeyo tizisangalala ndi moyo padzikoli.” Chitsanzo chimenechi chinali chogwirizana ndi msinkhu wa anawa ndipo chinawathandiza kwambiri. Ayenera kuti sanaiwale zimene anaphunzirapo.
10, 11. (a) Kodi mungagwiritse ntchito zitsanzo ziti pothandiza ana anu kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu? (Onani chithunzi m’munsimu.) (b) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene mwaona kuti n’zothandiza?
10 Mukhozanso kugwiritsa ntchito chitsanzo cha kuphika pothandiza mwana wanu kuti azikhulupirira Mulungu. Mwachitsanzo, mungamuuze mwana kuti pophika mandasi pamafunika zinthu zosiyanasiyana komanso kutsatira malangizo enaake. Kenako mungamupatse chipatso n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti amene anapanga chipatsochi anafunika kukhala ndi zinthu zosiyanasiyana komanso kutsatira malangizo?” The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, tsamba 10 mpaka 20.
Kenako mungadule chipatsocho pakati n’kumusonyeza nthanga. Ndiyeno mungamuuze kuti malangizo analembedwa munthangayo koma kalembedwe kake n’kovuta kwambiri kusiyana ndi mmene timalembera papepala. Pamapeto pake mungamufunse kuti: “Ngati anthu amalemba malangizo a kaphikidwe ka mandasi, kodi ndani analemba malangizo ovuta a kapangidwe ka zipatso?” Ngati mwanayo ndi wamkulu mungamuuze kuti malangizo opangira mtengo ndi zipatso amapezeka mu DNA. Ndiyeno ngati n’zotheka mungaone limodzi kabuku kachingelezi kofotokoza mmene moyo unayambira.—11 Makolo ena amakonda kukambirana ndi ana awo nkhani zimene zimapezeka mu Galamukani! zakuti, “Kodi Zinangochitika Zokha?” Nthawi zina amagwiritsa ntchito nkhanizi pofuna kuphunzitsa ana aang’ono nkhani zina zosavuta. Mwachitsanzo, banja lina la ku Denmark linayerekezera ndege ndi mbalame. Linauza ana awo kuti: “Ndege zimafanana ndi mbalame eti? Koma kodi ndege ingaikire mazira n’kuswa anapiye a ndege? Nanga kodi mbalame zikamatera zimafuna bwalo loti ziterepo? Kodi phokoso la ndege lingafanane ndi kulira kosangalatsa kwa mbalame? Ndiye kodi wopanga ndege ndi wopanga mbalame, wanzeru kwambiri ndani?” Mfundo ngati zimenezi komanso mafunso abwino zingathandize ana kuti aziganiza bwino komanso azikhulupirira kwambiri Mulungu.—Miy. 2:10-12.
12. Kodi zitsanzo zingathandize bwanji kuti ana azikhulupirira kwambiri Baibulo?
12 Zitsanzo zabwino zingathandizenso ana kuti azikhulupirira kuti Baibulo ndi lolondola. Mwachitsanzo, mungakambirane nawo lemba la Yobu 26:7. (Werengani.) Kodi mungatani kuti mwana wanu azikhulupirira zoti Yehova ndi amene anauzira Yobu kuti anene mawuwa? Si bwino kungomuuza mfundoyi koma muyenera kumuthandiza kuiganizira kwambiri. Mungamuuze kuti Yobu anakhala ndi moyo pa nthawi yomwe kunalibe zipangizo zoonera zakuthambo. Mwanayo azifotokoza mfundo zosonyeza kuti n’zosatheka kuti chinthu chachikulu ngati dziko chikhale m’malere. Mwina angagwiritse ntchito mpira kapena mwala posonyeza kuti chinthu cholemera chimafunika kukhala penapake osati m’malere. Kenako mungamuuze kuti nthawi ya Yobu anthu sankakhulupiriranso zoti dziko lili m’malere. Izi zingathandize mwanayo kuona kuti m’Baibulo munalembedwa zinthu zolondola pa nthawi yomwe anthu anali asanazitulukire.—Neh. 9:6.
MUZIWAPATSA ZITSANZO ZOSONYEZA KUTI MFUNDO ZA M’BAIBULO NDI ZOTHANDIZA
13, 14. Kodi makolo angatani kuti ana awo aziona kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza?
13 Makolo ayeneranso kuthandiza ana kuti azindikire ubwino wa mfundo za m’Baibulo. (Werengani Salimo 1:1-3.) Pali njira zambiri zochitira zimenezi. Mwachitsanzo, mungauze ana anu kuti: ‘Tiyerekeze kuti mukupita pachilumba penapake ndiye mukusankha anthu oti mukakhale nawo. Kuti muzikakhala mwamtendere, kodi mungasankhe anthu otani?’ Kenako mungakambirane nawo malangizo abwino amene ali pa Agalatiya 5:19-23.
14 Izi zingathandize anawo kumvetsa mfundo ziwiri. Yoyamba, mfundo za Mulungu zimathandiza kuti anthu azikhala mwamtendere komanso mogwirizana. Yachiwiri, Yehova akutiphunzitsa kuti tikonzekere moyo wa m’dziko latsopano. (Yes. 54:13; Yoh. 17:3) Ndiyeno kuti amvetse mfundozi, mungawapatse chitsanzo cha m’mabuku kapena magazini athu. Mwina mungasankhe nkhani ya munthu wina mu Nsanja ya Olonda pamutu wakuti, “Baibulo Limasintha Anthu.” Kapena ngati mumpingo wanu muli munthu amene anasiya makhalidwe oipa kuti asangalatse Yehova, mungamuitane kuti adzafotokoze. Zitsanzo ngati zimenezi zingathandize ana anu kuona kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwambiri.—Aheb. 4:12.
15. Tchulani mfundo yofunika kuiganizira mukamaphunzitsa ana anu?
15 Mwachidule tingati mukamaphunzitsa ana anu, musamangogwiritsa ntchito njira imodzimodzi nthawi zonse. Muziganizira njira zosiyanasiyana ndipo muziwathandiza kuganiza. Zimene mukuwaphunzitsazo zizikhala zogwirizana ndi msinkhu wawo, zosangalatsa komanso zolimbitsa chikhulupiriro. Bambo wina anati: “Muziyesetsa kupeza njira zatsopano zofotokozera nkhani zimene munakambirana nawo kale.”
MUZIKHALA OKHULUPIRIKA, OLEZA MTIMA KOMANSO MUZIKONDA KUPEMPHERA
16. N’chifukwa chiyani kuleza mtima n’kofunika pophunzitsa ana? Perekani chitsanzo.
16 Mzimu woyera ndi umene umathandiza kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro. (Agal. 5:22, 23) Koma pamatenga nthawi kuti chikhulupirirocho chilimbe. Choncho muzikhala oleza mtima komanso muzichita khama pophunzitsa ana anu. Bambo wina wa ana awiri wa ku Japan anati: “Ine ndi mkazi wanga timayesetsa kupeza nthawi yokwanira yocheza ndi ana athu. Kungoyambira ali aang’ono, tinkaphunzira nawo kwa 15 minitsi tsiku lililonse, kupatula masiku a misonkhano yampingo. Zinali zosavuta kuti tizipeza 15 minitsi yokha yowaphunzitsa komanso anawo sankatopa.” Woyang’anira dera wina anati: “Ndili mnyamata, ndinali ndi mafunso ambirimbiri moti ena sindinkatha kufunsa. Koma patapita nthawi, ambiri mwa mafunsowa ankayankhidwa pamisonkhano, pa kulambira kwa pabanja kapena ndikamaphunzira pandekha. N’chifukwa chake makolo amafunika kupitirizabe kuphunzitsa ana awo.”
17. Kodi chitsanzo chabwino cha makolo chingathandize bwanji ana? Perekani chitsanzo.
17 Chofunika kwambiri ndi chitsanzo chanu. Ana anu amaona kwambiri zimene mumachita. Choncho muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba. Ana anu aziona kuti mumadalira kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, makolo ena a ku Bermuda akakumana ndi mavuto, ankapemphera limodzi ndi ana awo kuti Yehova awatsogolere. Ankalimbikitsanso ana awowo kuti nawonso azipemphera paokha. Iwo anati: “Tinauzanso mwana wathu wamkazi kuti ‘azidalira kwambiri Yehova, azichita khama pomutumikira ndiponso asamade nkhawa kwambiri.’ Ataona zotsatira zake, anadziwa kuti Yehova akutithandiza. Zimenezi zinapangitsa kuti ayambe kumukhulupirira kwambiri komanso kukhulupirira Baibulo.”
18. Kodi makolo ayenera kukumbukira mfundo iti?
18 Komabe muzikumbukira kuti simungakakamize ana anu kuti akhale ndi chikhulupiriro. Ntchito yanu ndi yongodzala ndi kuthirira ndipo Mulungu ndi amene amakulitsa. (1 Akor. 3:6) Choncho muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera ndipo muzichita khama pophunzitsa ana anu. Mukamachita zimenezi, Mulungu adzakudalitsani kwambiri.—Aef. 6:4.