Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muziphunzira Mlungu Uliwonse
KODI zimakuvutani kuti muziphunzira Baibulo panokha mlungu uliwonse komanso kuti muzisangalala pophunzirapo? Tonsefe zimenezi nthawi zina zimatichitikira. Koma taganizirani zinthu zina zomwe timachita nthawi zonse, monga kusamba. Kuti munthu asambe pamafunika nthawi komanso khama koma akasamba amamva bwino. Kuphunzira Baibulo tingakuyerekezere ndi ‘kusamba m’madzi a Mawu a Mulungu.’ (Aef. 5:26) Tiyeni tione mfundo zina zomwe zingatithandize pa nkhaniyi.
Muzipanga ndandanda. Kuphunzira Baibulo ndi chimodzi mwa ‘zinthu zofunika kwambiri’ zimene Mkhristu sayenera kunyalanyaza. (Afil. 1:10) Kuti muzitsatira ndandanda yanu, muziika pamalo amene mungamaone mosavuta monga pakhoma kapena pafiriji. Kapenanso mungatchere alamu pachipangizo chanu chamakono kuti izilira nthawi yophunzira ikatsala pang’ono.
Muzisankha nthawi komanso njira yophunzirira yomwe ingakhale yabwino kwa inuyo. Kodi mungakonde kuphunzira kamodzi pa mlungu kwa nthawi yaitali kapena maulendo angapo moduladula? Mukhoza kukonza zoti muziphunzira mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Ngati mumaona kuti mumagwa ulesi nthawi yophunzira ikafika, mungayese kumangophunzira kwa 10 minitsi yokha. Kuphunzira kwa nthawi yochepa chonchi kungakuthandizeni kwambiri kusiyana ndi kungokhala osaphunzira. Ndipo mwina mukayamba kuphunzira mudzalimbikitsidwa kuti mupitirize.—Afil. 2:13.
Muzisankhiratu nkhani zoti muphunzire. Mukakhala pansi n’kumaganizira zoti muphunzire nthawi yomweyo, simungagwiritse ntchito bwino nthawi yanu. (Aef. 5:16) Mungachite bwino kusankhiratu nkhani zimene mukufuna kuphunzira n’kuzilemba penapake. Funso linalake likabwera m’maganizo mwanu muzililemba. Mukamaliza kuphunzira ulendo uliwonse muziwonjezera zinthu zimene mukufuna kudzaphunzira.
Muzikhala okonzeka kusintha. Muziyesa kusintha zinthu zina pandandanda yanu monga kuchuluka kwa nthawi kapena nkhani zimene mungaphunzire. Chofunika si tsiku, kuchuluka kwa nthawi kapena nkhani zimene mungaphunzire koma kuti muziphunzira mlungu uliwonse.
Timapindula kwambiri tikamaphunzira mlungu uliwonse. Ubwenzi wathu ndi Yehova umalimba, timachita zinthu mwanzeru komanso timalimbikitsidwa.—Yos. 1:8.