MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muzipeza Malo Abwino Ophunzirira
Kodi mukufuna muzipindula kwambiri mukamaphunzira panokha? Mungayese mfundo zotsatirazi:
-
Muzisankha malo abwino. Ngati n’kotheka, muzipeza malo aukhondo komanso pamene pali kuwala kokwanira. Mukhoza kugwiritsa ntchito desiki kapena tebulo apo ayi mutha kupeza malo abwino alionse panja.
-
Muzikhala panokha. Yesu anasankha kukapemphera “m’mawa kwambiri” komanso “kumalo kopanda anthu.” (Maliko 1:35) Ngati n’zosatheka kukhala panokha, mungathe kuuza anthu a m’banja lanu kapena amene mumakhala nawo nthawi imene mumaphunzira, n’kuwapempha kuti asakusokonezeni.
-
Muziika maganizo pa zimene mukuphunzira. Muzipewa zinthu zimene zingakusokonezeni. Ngati mumagwiritsa ntchito foni kapena tabuleti pophunzira, muziitchera m’njira yoti isakusokonezeni. Mukaganizira zinthu zina zoti muchite, muzingolemba mwachidule penapake kuti mudzazichite nthawi ina. Ngati mukuona kuti maganizo anu ayamba kuyendayenda mukhoza kupuma kaye, kuyenda pang’ono kapena kudziwongolawongola.