Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 46

Mmene Yehova Anatsimikizira Lonjezo Lake la Paradaiso

Mmene Yehova Anatsimikizira Lonjezo Lake la Paradaiso

“Aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu amene amanena zoona.”—YES. 65:16.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi ndi uthenga wotani womwe Yesaya ankafotokozera Aisiraeli anzake?

 MNENERI Yesaya ananena kuti Yehova ndi “Mulungu amene amanena zoona.” Mawu amene anawamasulira kuti “zoona” angatanthauze “ame.” (Yes. 65:16 mawu a m’munsi.) Mawu akuti “ame” amatanthauza “zikhale momwemo.” Mawuwa akamagwiritsidwa ntchito m’Baibulo ponena za Yehova ndi Yesu, amatsimikizira kuti zinazake ndi zoona. Choncho uthenga umene Yesaya ankauza Aisiraeli anzake ndi wakuti zimene Yehova amanena nthawi zonse zimakhala zodalirika. Yehova wakhala akusonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona pokwaniritsa malonjezo ake onse.

2. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira malonjezo a Yehova okhudza Paradaiso, nanga tikambirana mafunso ati?

2 Kodi ifenso tingadalire zimene Yehova analonjeza kuti adzachita m’tsogolo? Patapita zaka pafupifupi 800 kuchokera mu nthawi ya Yesaya, mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake malonjezo a Mulungu amakhala odalirika nthawi zonse. Paulo anati: “N’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheb. 6:18) Kasupe sangatulutse madzi abwino komanso amchere pa nthawi imodzi. Mofanana ndi zimenezi, Yehova yemwe ndi Mwiniwake wa choonadi sanganame. Choncho tingadalire chilichonse chimene Yehova amanena kuphatikizapo zimene amalonjeza zokhudza m’tsogolo. Munkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi Mulungu watilonjeza zinthu ziti m’tsogolo? Nanga watitsimikizira bwanji kuti adzakwaniritsa malonjezo akewa?

KODI YEHOVA WATILONJEZA CHIYANI?

3. (a) Kodi ndi lonjezo liti limene atumiki a Mulungu amalikonda? (Chivumbulutso 21:​3, 4) (b) Kodi anthu ena amati bwanji tikamawafotokozera za lonjezoli?

3 Tikambirana lonjezo limene atumiki a Mulungu padziko lonse amalikonda. (Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.) Yehova analonjeza kuti “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.” Ambirife tikamalalikira timakonda kuwerengera anthu lemba lolimbikitsali powafotokozera mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. Kodi anthu ena amati bwanji tikawafotokozera lonjezo limeneli? Iwo anganene kuti, “Lonjezoli ndi labwino koma ndi lovuta kulikhulupirira.”

4. (a) Kodi Yehova ankadziwiratu mfundo iti? (b) Kuwonjezera pa kulonjeza, kodi Yehova anachitanso chiyani?

4 Pamene anauzira mtumwi Yohane kulemba lonjezo lokhudza Paradaisoli, Yehova ankadziwa kuti tizidzauza ena lonjezoli polalikira uthenga wa Ufumu. Ankadziwanso kuti anthu ambiri azidzavutika kukhulupirira lonjezo la “zinthu zatsopano.” (Yes. 42:9; 60:2; 2 Akor. 4:3, 4) Ndiye kodi tingatsimikizire bwanji kuti lonjezo la pa Chivumbulutso 21:3, 4 lidzakwaniritsidwadi? Yehova atapereka lonjezoli, anaperekanso zifukwa zomveka zotichititsa kuti tizilikhulupirira. Kodi anapereka zifukwa ziti?

YEHOVA ANATSIMIKIZIRA KUTI ADZAKWANIRITSA ZIMENE ANALONJEZA

5. Kodi ndi zifukwa ziti zomwe zimatichititsa kukhulupirira lonjezo la Mulungu lokhudza Paradaiso, nanga timazipeza kuti?

5 M’mavesi otsatira muli zifukwa zotichititsa kukhulupirira lonjezo la Yehova lokhuza Paradaiso. M’mavesiwo timawerenga kuti: “Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.’ Ananenanso kuti: ‘Lemba, chifukwa mawu amenewa ndi odalirika komanso oona.’ Iye anandiuza kuti: ‘Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto.’”—Chiv. 21:5, 6a.

6. Kodi zimene timawerenga pa Chivumbulutso 21:​5, 6, zimatithandiza bwanji kukhulupirira lonjezo la Mulungu?

6 Kodi mawu amenewa amatithandiza bwanji kuti tizikhulupirira lonjezo la Mulungu? Ponena za mawu a m’mavesiwa, buku lakuti Mapeto a Chivumbulutso limanena kuti: “Zimenezi zili ngati kuti Yehova akusainira yekha chikalata chotsimikizira kuti anthu okhulupirika adzalandiradi madalitso m’tsogolomu.” b Lonjezo la Mulungu lili pa Chivumbulutso 21:3, 4, koma mu vesi 5 ndi 6, muli Mawu a Yehova okhala ngati akusainira kuti zimene walonjezazo zidzakwaniritsidwadi. Tsopano tiyeni tione mawu amene Yehova anagwiritsa ntchito potsimikizira lonjezoli.

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu oyamba pa Chivumbulutso 21:5 ndi ochititsa chidwi, nanga tikuphunzira chiyani pa mawuwa?

7 Vesi 5, limayamba ndi mawu akuti: “Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu anati.” (Chiv. 21:5a) Imeneyi ndi imodzi mwa nthawi zitatu pamene Yehova analankhula yekha m’masomphenya m’buku la Chivumbulutso. Choncho apa Yehova akutsimikizira yekha, osati kudzera mwa mngelo wamphamvu kapenanso Yesu. Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti mawu otsatirawo ndi odalirika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova “sanganame.” (Tito 1:2) Izi zikusonyeza kuti zimene timawerenga pa Chivumbulutso 21:5, 6 ndi zodalirika kwambiri.

“ZINTHU ZONSE ZIMENE NDIKUPANGA NDI ZATSOPANO”

8. Kodi Yehova anatsimikizira bwanji kuti lonjezo lake lidzakwaniritsidwa? (Yesaya 46:10)

8 Tsopano tiyeni tikambirane mawu akuti: “Taonani.” (Chiv. 21:5) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “taonani” atchulidwa mobwerezabwereza m’buku la Chivumbulutso. Buku lina limafotokoza kuti mawuwa amagwiritsidwa ntchito “pofuna kuthandiza munthu amene akuwerenga kuti achite chidwi ndi mawu otsatira.” Ndiye kodi mawu otsatirawo ndi oti chiyani? Mulungu akunena kuti: “Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” N’zoona kuti Yehova akufotokoza zinthu zatsopano zimene adzachite m’tsogolo, koma kwa iye zimenezi n’zosakayikitsa moti akufotokoza ngati kuti zikuchitika.—Werengani Yesaya 46:10.

9. (a) Kodi mawu akuti “zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano,” akusonyeza kuti Yehova adzachita zinthu ziwiri ziti? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire “kumwamba” ndi “dziko lapansi” zomwe zilipozi?

9 Tiyeni tikambirane mawu otsatira omwe akupezeka pa Chivumbulutso 21:5 akuti: “Zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” M’chaputalachi mawuwa akufotokoza zinthu ziwiri zimene Yehova akuchita zomwe ndi kusintha komanso kubwezeretsa. Choyamba, kodi iye akusintha chiyani? Pa Chivumbulutso 21:1 timawerenga kuti: “Kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka.” Kumwamba kwakale kukuimira maboma a anthu omwe amachita zinthu motsogoleredwa ndi Satana ndi ziwanda zake. (Mat. 4:8, 9; 1 Yoh. 5:19) Ndipo Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko lapansi” ponena za anthu. (Gen. 11:1; Sal. 96:1) Choncho “dziko lapansi lakale” likuimira anthu oipa omwe ali padzikoli. Sikuti Yehova adzangokonza zina ndi zina zokhudza “kumwamba” ndi “dziko lapansi” zomwe zilipozi. M’malomwake adzasintha, kapena kuti kuzichotseratu n’kubweretsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zomwe zikuimira boma latsopano komanso anthu olungama.

10. Kodi n’chiyani chomwe Yehova adzapange kukhala chatsopano?

10 Pa Chivumbulutso 21:​5, timawerengapo zimene Yehova ananena zokhudza zinthu zimene adzazipange kukhala zatsopano. Yehova ananena kuti, “Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” Apatu zinali ngati iye akunena kuti “Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.” Yehova adzasintha dzikoli komanso adzachititsa kuti anthu akhale atsopano powathandiza kuti akhale angwiro. Mogwirizana ndi zimene Yesaya ananena, dziko lonse lidzakhala lokongola ngati munda wa Edeni. Munthu aliyense payekha adzathandizidwanso kuti akhale watsopano. Olumala, amene ali ndi vuto losaona komanso losamva adzachiritsidwa ndipo ngakhale amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo.—Yes. 25:8; 35:1-7.

“MAWU AMENEWA NDI ODALIRIKA KOMANSO OONA. . . . ZAKWANIRITSIDWA!”

11. Kodi Yehova anapatsa Yohane lamulo liti komanso pachifukwa chiti?

11 Kodi Mulungu anatsimikiziranso bwanji kuti zimene ananena zidzachitikadi? Iye anauza Yohane kuti: “Lemba, chifukwa mawu amenewa ndi odalirika komanso oona.” (Chiv. 21:5) Sikuti Yehova anangomulamula kuti “lemba,” koma anafotokozanso chifukwa chake. Iye anati: “Chifukwa mawu amenewa ndi odalirika komanso oona,” kapena kuti mawu a Mulungu si okayikitsa ndipo ndi olondola. Timayamikira kuti Yohane anamvera lamulo lakuti ‘alembe.’ Pa chifukwa chimenechi, tingathe kuwerenga lonjezo la Mulungu lokhudza Paradaiso komanso kumaganizira madalitso amene tikuyembekezera.

12. N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti Yehova ananena kuti: “Zakwaniritsidwa!”?

12 Kenako Mulungu ananena kuti, “Zakwaniritsidwa!” (Chiv. 21:6) Apa Yehova akulankhula ngati kuti zonse zomwe ananena zokhudza lonjezo la Paradaiso zakwaniritsidwa kale. Ndipotu n’zomveka kuti iye angathe kulankhula chonchi chifukwa palibe chomwe chingamulepheretse kukwaniritsa cholinga chake. Yehova ananenanso mawu ena otsimikizira kuti zimene analonjeza zidzakwaniritsidwadi. Kodi anati chiyani?

“INE NDINE ALEFA NDI OMEGA”

13. N’chifukwa chiyani Yehova ananena kuti: “Ine ndine Alefa ndi Omega”?

13 Monga mmene tafotokozera kale, Yehova analankhula yekha maulendo atatu m’masomphenya opita kwa Yohane. (Chiv. 1:8; 21:5, 6; 22:13) Pa maulendo onsewa, Yehova ankanena kuti: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” Mawu akuti alefa amapezeka kumayambiriro kwa afabeti ya Chigiriki ndipo mawu akuti omega amapezeka kumapeto. Pogwiritsa ntchito mawu akuti “Alefa ndi Omega,” Yehova anasonyeza kuti akayamba kuchita chinthu sasiya mpaka chitatheka.

Yehova akayamba kuchita zinazake, sasiya mpaka zitatheka (Onani ndime 14, 17)

14. (a) Perekani chitsanzo cha nthawi imene zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa,” nanga ndi liti pomwe zidzakhale ngati akunena kuti “Omega”? (b) Kodi ndi mawu ati a pa Genesis 2:​1-3 omwe amatsimikizira kuti Yehova adzakwaniritsa cholinga chake?

14 Atangolenga Adamu ndi Hava, Yehova anafotokoza cholinga chake polenga dziko komanso anthu. Baibulo limati: “Komanso, Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi ndipo muziliyang’anira.’” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyi zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Apa iye anafotokoza momveka bwino cholinga chake. Cholingacho chinali choti pakapita nthawi, ana a Adamu ndi Hava omwe akanakhala angwiro komanso omvera adzaze dzikoli n’kulikonza kukhala Paradaiso. Pa nthawi imeneyi m’pamene zikanakhala ngati wanena kuti “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi komanso zonse zimene zili mmenemo,” ananena mawu otsimikizira kuti cholinga chake chidzatheka. Mawuwo ali pa Genesis 2:​1-3. (Werengani.) Yehova ananena kuti tsiku la 7 linali lopatulika. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Apa Yehova ankatsimikizira kuti cholinga chake chokhudza dziko komanso anthu sichidzalephereka. Cholingachi chikanakwaniritsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.

15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinkaoneka ngati Satana walepheretsa cholinga cha Mulungu?

15 Adamu ndi Hava atachimwa anapatsira ana awo uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Apa zinkaoneka ngati Satana walepheretsa cholinga cha Mulungu choti padzikoli pakhale anthu angwiro komanso omvera. Zinali ngati Satana walepheretsa Yehova kunena kuti “Omega.” Satana ayenera kuti ankaganiza kuti Yehova sangakwaniritsenso cholinga chake. Iye ankaona kuti Mulungu apha Adamu ndi Hava n’kulenganso banja lina kuti akwaniritse cholinga chake chokhudza anthu. Koma ngati Mulungu akanachita zimenezi, ndiye kuti Mdyerekezi akananena kuti Mulunguyo ndi wabodza. Chifukwa chiyani? Chifukwa mogwirizana ndi Genesis 1:​28, Yehova anali atauza Adamu ndi Hava kuti ana awo adzadzaza dziko lapansi.

16. N’chiyani chikanachititsa Satana kunena kuti Yehova ndi wolephera?

16 Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene Satana ankaganiza kuti Mulungu angachite? Mwina ankaganiza kuti Yehova adzalola kuti Adamu ndi Hava akhale ndi ana omwe sizidzatheka kuti akhale angwiro. (Mlal. 7:20; Aroma 3:23) Apa ndiye kuti Mdyerekezi akananena kuti Yehova ndi wolephera. Chifukwa chiyani? Chifukwa njira imeneyi sikanakwaniritsa cholinga cha Mulungu choti padzikoli pakhale ana a Adamu ndi Hava angwiro komanso omvera.

17. Kodi Yehova anathetsa bwanji nkhani yomwe Satana komanso Adamu ndi Hava anayambitsa, nanga zotsatira zake zidzakhala zotani? (Onaninso chithunzi.)

17 Yehova anathetsa nkhani imene inayambitsidwa ndi Satana komanso anthu oyambirirawa m’njira yoti Satanayo analibenso mawu. (Sal. 92:5) Polola Adamu ndi Hava kuti akhale ndi ana, Yehova anasonyeza kuti amanena zoona osati zabodza. Anasonyezanso kuti akanena kuti achita chinachake, palibe chimene chingamulepheretse. Yehova anaonetsetsa kuti cholinga chake chikwaniritsidwe popereka “mbadwa” yoti ipulumutse ana omvera a Adamu ndi Hava. (Gen. 3:15; 22:18) Satana ayenera kuti anagoma ndi zimene Yehova anakonza zokhudza dipo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa zinasonyeza kuti Yehova ali ndi chikondi chopanda dyera. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16) Satana alibe khalidwe limeneli chifukwa iye ndi wadyera. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene zidzachitike chifukwa cha dipo? Kumapeto kwa Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000, ana angwiro komanso omvera a Adamu ndi Hava adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi mogwirizana ndi cholinga cha Yehova choyambirira. Pa nthawi imeneyo zidzakhala ngati Yehova wanena kuti “Omega.”

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI LONJEZO LA YEHOVA LOKHUDZA PARADAISO

18. Kodi Yehova anatsimikizira m’njira zitatu ziti kuti adzakwaniritsa malonjezo ake? (Onaninso bokosi lakuti “ Zifukwa Zitatu Zotichititsa Kukhulupirira Lonjezo la Yehova.”)

18 Mogwirizana ndi zimene taphunzira, kodi tingathandize bwanji anthu amene amakayikira lonjezo la Mulungu lokhudza paradaiso? Choyamba, amene wapereka lonjezoli ndi Yehova. Buku la Chivumbulutso limati: “Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.’” Iye ali ndi nzeru komanso mphamvu ndipo amafunitsitsa atakwaniritsa malonjezo ake. Chachiwiri, n’zosakayikitsa kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa ndipo kwa Yehova zili ngati lakwaniritsidwa kale. Mpake kuti iye anati: “Mawu amenewa ndi odalirika komanso oona. . . . Zakwaniritsidwa!” Chachitatu, mawu akuti, “Ine ndi Alefa ndi Omega,” akutsimikizira kuti Yehova akayamba kuchita chinthu sasiya mpaka chitatheka. Zimene Yehova adzachite zidzasonyeza kuti Satana ndi wabodza komanso wolephera.

19. Kodi mungawauze chiyani anthu amene amakayikira lonjezo la Mulungu lokhudza Paradaiso?

19 Dziwani kuti nthawi iliyonse pamene mukulalikira n’kumatsimikizira kuti zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa, zimakuthandizani inunso kuti muzikhulupirira malonjezo a Yehova. Ndiye mukadzawerengera munthu wina lonjezo lolimbikitsa lokhudza Paradaiso la pa Chivumbulutso 21:​4, munthuyo n’kunena kuti, “Zikumveka zabwino koma n’zovuta kuzikhulupirira,” kodi mudzamuuza kuti chiyani? Mungadzamuwerengere vesi 5 ndi 6 n’kumufotokozera zimene Yehova ananena potsimikizira lonjezolo, zomwe zinali ngati akusainira mawu ake.—Yes. 65:16

NYIMBO NA. 145 Mulungu Watilonjeza Paradaiso

a Munkhaniyi, tikambirana zimene Yehova ananena pofuna kutsimikizira kuti zimene analonjeza zokhudza Paradaiso zidzakwaniritsidwa. Nthawi iliyonse imene timauza anthu ena zimenezi, zimatithandiza ifenso kuti tizikhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova.

b Onani buku lakuti Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Ayandikira tsamba 303-304, ndime 8-9.