NKHANI YOPHUNZIRA 20
NYIMBO NA. 7 Yehova Ndi Mphamvu Yathu
Muzidalira Yehova Kuti Azikutonthozani
“Atamandike . . . Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.”—2 AKOR. 1:3.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana zimene tikuphunzira kwa Yehova pa zimene anachita potonthoza Ayuda ku ukapolo.
1. Kodi zinthu zinali bwanji kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo?
KODI mukuganiza kuti Ayuda ankamva bwanji pamene anali ku ukapolo ku Babulo? Iwo anali ataona dziko lawo likuwonongedwa. Anatengedwa kuchoka kudziko lawo kupita kudziko lachilendo chifukwa cha machimo awo komanso a makolo awo. (2 Mbiri 36:15, 16, 20, 21) N’zoona kuti ku Babulo, akapolo anali ndi ufulu wochita zinthu zawo za tsiku ndi tsiku. (Yer. 29:4-7) Koma moyo sunali wophweka ndipo ku Babulo si kumene akanakonda kukhala. Ndiye kodi iwo anamva bwanji ndi zimene zinawachitikirazi? Taonani zimene munthu wina wokhulupirika yemwe anapita nawo ku ukapolowo ananena: “Tinakhala pansi m’mphepete mwa mitsinje ya ku Babulo. Tinalira titakumbukira Ziyoni.” (Sal. 137:1) Anthu amene anali ku ukapolowa anali ndi chisoni, koma kodi ndi ndani amene akanawalimbikitsa?
2-3. (a) Kodi Yehova anawachitira chiyani Ayuda omwe anali ku ukapolo? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.” (2 Akor. 1:3) Iye ndi Mulungu wachikondi ndipo amasangalala kutonthoza anthu amene ali pa ubwenzi wabwino ndi iye. Yehova ankadziwa kuti ena mwa Ayuda amene anapita ku ukapolowo, adzavomereza chilangocho n’kubwerera kwa iye. (Yes. 59:20) Kutatsala zaka zoposa 100 kuti apite ku ukapolowo, iye anauzira mneneri Yesaya kuti alembe buku limene limadziwika ndi dzina lake. Pofotokoza cholinga cha bukuli Yesaya anati: “‘Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,’ akutero Mulungu wanu.” (Yes. 40:1) Kudzera m’zimene mneneriyu analemba, Yehova ananena mawu olimbikitsa omwe Ayuda amene anali ku ukapolowo ankafunikira.
3 Mofanana ndi Ayuda omwe anali ku ukapolo, ifenso timafunika kulimbikitsidwa nthawi ndi nthawi. Munkhaniyi tiona mmene Yehova analimbikitsira akapolowo m’njira zitatu: (1) Iye analonjeza kuti adzakhululukira anthu olapa, (2) anapereka chiyembekezo kwa anthu ake, komanso (3) anawathandiza kuti asamachite mantha. Tikamakambirana nkhaniyi, tiona mmene Yehova amatilimbikitsira m’njira zimenezi.
YEHOVA AMATIKHULULUKIRA MWACHIFUNDO
4. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi Mulungu wachifundo? (Yesaya 55:7)
4 Yehova ndi “Bambo wachifundo chachikulu.” (2 Akor. 1:3) Iye anasonyeza kuti ndi wachifundo pamene analonjeza kuti adzakhululukira akapolo omwe alapa. (Werengani Yesaya 55:7.) Ananena kuti: “Chifukwa cha chikondi changa chokhulupirika chimene sichidzatha ndidzakuchitira chifundo.” (Yes. 54:8) Kodi Yehova akanawachitira bwanji chifundo? Ngakhale kuti Ayudawo akanavutika chifukwa cha zotsatira za machimo awo, Yehova analonjeza kuti iwo sadzakhala ku Babulo mpaka kalekale. M’kupita kwa nthawi iwo akanadzabwerera kwawo. (Yes. 40:2) Mawu amenewa ayenera kuti anatonthoza komanso kulimbikitsa anthu olapa amene anali ku ukapolowo.
5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira chifundo cha Yehova kuposa Ayuda amene anali ku ukapolo?
5 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova ndi wokonzeka kukhululukira atumiki ake ndi mtima wonse. Mosiyana ndi Ayudawo, masiku ano tili ndi chifukwa chachikulu chotichititsa kukhulupirira mfundo imeneyi. N’chifukwa chiyani tikutero? Panopa timamvetsa chifukwa chake n’zotheka kuti Yehova azitikhululukira. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene Yesaya analemba ulosi umenewu, Yehova anatumiza Mwana wake wokondedwa padzikoli kuti adzapereke dipo lowombola anthu onse omwe alapa. Chifukwa cha nsembe imeneyi, n’zotheka ‘kufafaniziratu’ machimo onse. (Mac. 3:19; Yes. 1:18; Aef. 1:7) Kunena zoona timatumikira Mulungu wachifundo.
6. Kodi kuganizira chifundo cha Yehova kumatithandiza bwanji? (Onaninso chithunzi.)
6 Mawu a Yehova a pa Yesaya 55:7 angatitonthoze tikamadziimba mlandu. Enafe timapitirizabe kudziimba mlandu pa zimene tinalakwitsa ngakhale kuti tinalapa. Izi zikhoza kuchitika makamaka ngati tikukumana ndi zotsatira za zimene tinalakwitsa. Koma ngati titavomereza n’kulapa, tisamakayikire kuti Yehova watikhululukira. Ndipo Yehova akakhululuka amaiwala nkhaniyo. (Yerekezerani ndi Yeremiya 31:34.) Choncho ngati Yehova samangokhalira kuganizira zimene tinalakwitsa, ifenso tizichita zomwezo. Yehova amaganizira kwambiri zimene tikuchita panopa osati zimene tinalakwitsa m’mbuyomo. (Ezek. 33:14-16) Ndipo posachedwapa, Bambo wathu yemwe ndi wachifundo chachikuluyu, adzathetseratu mavuto onse amene timakumana nawo chifukwa cha zimene tinalakwitsa.
Yehova amaganizira kwambiri zimene tikuchita panopa osati zimene tinalakwitsa m’mbuyomo (Onani ndime 6)
7. N’chiyani chingatilimbikitse kupempha thandizo kwa akulu ngati takhala tikubisa tchimo?
7 Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati chikumbumtima chathu chikutivutitsa chifukwa chakuti tabisa tchimo lalikulu? Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipempha akulu kuti atithandize. (Yak. 5:14, 15) Komabe sizimakhala zophweka kuvomereza zomwe talakwitsa. Koma kulapa kudzatilimbikitsa kuti tikafotokozere amuna okhulupirikawa. Chimene chingatithandize ndi kukumbukira kuti Yehova ndi amuna amene wawasankhawa adzatisonyeza chifundo. Taganizirani mmene chifundo cha Yehova chinathandizira m’bale wina dzina lake Arthur, a yemwe chikumbumtima chake chinkamuvutitsa kwambiri. Iye anati: “Pafupifupi kwa chaka ndinakhala ndikuonera zolaula. Koma nditamvetsera nkhani yokhudza chikumbumtima, ndinafotokozera mkazi wanga komanso akulu za vuto langali. Nditachita zimenezi ndinayamba kumva bwino koma ndinkakhumudwabe chifukwa cha tchimo limene ndinachitalo. Akuluwo ananditsimikizira kuti Yehova amafunabe kuti ndikhale mnzake. Iye amatilanga chifukwa chakuti amatikonda. Mawu awo achikondiwa anandikhazika mtima pansi ndipo anandithandiza kuona kuti Yehova anandikhululukira.” Panopa Arthur ndi mpainiya wokhazikika komanso mtumiki wothandiza. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amatichitira chifundo tikalapa.
YEHOVA AMATIPATSA CHIYEMBEKEZO
8. (a) Kodi Yehova anapatsa Ayuda omwe anali ku ukapolo chiyembekezo chotani? (b) Mogwirizana ndi Yesaya 40:29-31, kodi chiyembekezo chinathandiza bwanji Ayuda omwe analapa?
8 Anthu ena ankaona kuti zinali zosatheka kuti Ayuda omwe anali ku ukapolo adzamasulidwe n’kubwerera kwawo. Ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Babulo unkadziwika kuti sunkamasula akapolo ake. (Yes. 14:17) Koma Yehova anapatsa anthu ake chiyembekezo. Iye analonjeza kuti adzamasula anthu ake ndipo palibe chimene chikanalepheretsa zimenezi. (Yes. 44:26; 55:12) Kwa Yehova, Ababulo anali ngati fumbi. (Yes. 40:15) Munthu ukangopeperera pamene pali fumbi, nthawi yomweyo fumbilo limachoka. Ndiye kodi chiyembekezo chikanathandiza bwanji Ayudawo? Chikanawalimbikitsa, koma chikanawathandizanso m’njira ina. Yesaya analemba kuti: “Anthu amene amayembekezera Yehova adzapezanso mphamvu.” (Werengani Yesaya 40:29-31.) Choncho chiyembekezo chikanawapatsa mphamvu, ndipo akanatha ‘kuulukira m’mwamba ngati kuti ali ndi mapiko a chiwombankhanga.’
9. Kodi Ayuda omwe anali ku ukapolo anali ndi zifukwa ziti zowachititsa kukhulupirira malonjezo a Yehova?
9 Yehova anapatsanso Ayuda amene anali ku ukapolowo chifukwa china chokhulupirira malonjezo ake. Taganizirani za maulosi omwe anali atakwaniritsidwa kale pa nthawiyo. Mwachitsanzo, iwo ankadziwa kuti Asuri anali atagonjetsa kale ufumu wakumpoto wa Isiraeli n’kutenga anthu ake kupita nawo ku ukapolo. (Yes. 8:4) Analinso ataona Ababulo atawononga Yerusalemu n’kuwatenga kupita nawo ku ukapolo. (Yes. 39:5-7) Anaonanso Mfumu Zedekiya atachititsidwa khungu n’kutengedwa kupita ku Babulo. (Yer. 39:7; Ezek. 12:12, 13) Zonse zimene Yehova ananeneratu zinakwaniritsidwa. (Yes. 42:9; 46:10) Zonsezi ziyenera kuti zinalimbitsa chikhulupiriro chawo chakuti malonjezo a Yehova, akuti adzawamasula, adzakwaniritsidwa.
10. N’chiyani chingatithandize kuti tikhale ndi chiyembekezo champhamvu m’masiku otsirizawa?
10 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikafooka, chiyembekezo chingatilimbikitse komanso kutithandiza kuti tipezenso mphamvu. Tikukhala m’nthawi yovuta ndipo pali adani amphamvu amene amatitsutsa. Koma tisataye mtima. Yehova watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri, cha moyo wosatha, pomwe tidzakhale otetezeka komanso pamtendere weniweni. Nthawi zonse tiziganizira za chiyembekezo chimenechi. Kupanda kutero, chiyembekezo chathu chikhoza kukhala ngati tikuyang’ana malo okongola kudzera pawindo lomwe galasi lake ndi losatsuka. Ndiye kodi tingatani kuti tiziona bwinobwino zimene tikuyembekezera? Nthawi zonse tingachite bwino kumaganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Tikhoza kuwerenga nkhani, kuonera mavidiyo komanso kumvetsera nyimbo zomwe zimafotokoza za chiyembekezo chathu. Tikhozanso kumufotokozera Yehova m’pemphero za malonjezo amene tikufunitsitsa kudzawaona akukwaniritsidwa.
11. Kodi n’chiyani chinathandiza mlongo wina amene akudwala matenda aakulu kuti apezenso mphamvu?
11 Taganizirani mmene chiyembekezo chinalimbikitsira mlongo wina dzina lake Joy, yemwe akudwala matenda aakulu. Iye anati: “Ndikakhala ndi nkhawa, ndimamufotokozera Yehova mmene ndikumvera chifukwa ndimadziwa kuti amandimvetsa. Yehova amayankha pemphero langa pondipatsa ‘mphamvu yoposa yachibadwa.’” (2 Akor. 4:7) Joy amadziyerekezeranso ali m’dziko latsopano, momwe “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ine ndikudwala.’” (Yes. 33:24) Ifenso tikamamufotokozera Yehova mmene tikumvera komanso kuganizira za chiyembekezo chathu tingapeze mphamvu.
12. Kodi tili ndi zifukwa ziti zotithandiza kukhulupirira malonjezo a Yehova? (Onaninso chithunzi.)
12 Mofanana ndi mmene anachitira ndi Ayuda omwe anali ku ukapolo, Yehova watipatsanso zifukwa zambiri zotichititsa kukhulupirira malonjezo ake. Taganizirani za maulosi amene akukwaniritsidwa panopa. Mwachitsanzo, tikuona ulamuliro wamphamvu padziko lonse, womwe ‘pa zinthu zina ndi wolimba koma pa zinthu zina ndi wosalimba.’ (Dan. 2:42, 43) Komanso timamva za “zivomerezi m’malo osiyanasiyana” ndiponso timagwira nawo ntchito yolalikira kwa “anthu amitundu yonse.” (Mat. 24:7, 14) Maulosi amenewa ndi enanso ambiri amalimbitsa chikhulupiriro chathu kuti malonjezo a Yehova akwaniritsidwa posachedwapa.
Maulosi amene akukwaniritsidwa masiku ano amatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova (Onani ndime 12)
YEHOVA AMATITHANDIZA KUTI TISAMACHITE MANTHA
13. (a) Kodi Ayuda anakumana ndi mavuto ati pa nthawi imene ankamasulidwa? (b) Mogwirizana ndi Yesaya 41:10-13, kodi Yehova analimbikitsa bwanji Ayuda amene anali ku ukapolo?
13 Ngakhale kuti Yehova analimbikitsa Ayuda amene anali ku ukapolo powapatsa chiyembekezo chabwino, ankadziwa kuti iwo adzakumana ndi mavuto pa nthawi imene akumasulidwa. Yehova anali ataneneratu kuti chakumapeto kwa ukapolowo, mfumu ina yamphamvu idzaukira mitundu yozungulira ndipo kenako idzaukira Babulo. (Yes. 41:2-5) Kodi Ayudawo ankafunika kuchita mantha ndi zimenezi? Izi zisanachitike, Yehova anali atawalimbikitsa powauza kuti: “Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe. Usade nkhawa chifuwa ine ndine Mulungu wako.” (Werengani Yesaya 41:10-13.) Kodi ankatanthauza chiyani pomwe ananena kuti “Ine ndine Mulungu wako”? Apa sikuti iye ankawakumbutsa Ayudawo kuti azimulambira chifukwa iwo ankadziwa kale kuti ayenera kuchita zimenezo. Koma ankawakumbutsa kuti iye adzapitiriza kukhala kumbali yawo.—Sal. 118:6.
14. Kodi Yehova anathandizanso bwanji Ayuda omwe anali ku ukapolo kuti asamachite mantha?
14 Yehova anathandizanso Ayuda omwe anali ku ukapolo kuti asamachite mantha powakumbutsa za nzeru zake komanso mphamvu zake zopanda malire. Iye anauza Ayudawo kuti ayang’ane nyenyezi zakumwamba. Anawauza kuti sikuti iye anangolenga nyenyezizo koma amadziwanso dzina la nyenyezi iliyonse. (Yes. 40:25-28) Choncho iye sangalephere kudziwa dzina la mtumiki wake aliyense. Ndipo ngati Yehova ali ndi mphamvu zolenga nyenyezi ndiye kuti alinso ndi mphamvu zothandiza anthu ake. Apatu Ayuda amene anali ku ukapolowo sankafunika kuda nkhawa kapena kuchita mantha.
15. Kodi Mulungu anawakonzekeretsa bwanji Ayuda omwe anali ku ukapolo pa zinthu zomwe ankayembekezera?
15 Yehova anauzanso anthu ake zoyenera kuchita nthawi yoti amasulidweyo ikafika. Chakumayambiriro kwa buku la Yesaya, Mulungu anauza anthu ake kuti: “Inu anthu anga, pitani mukalowe mʼzipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwu kuyenera kuti kunachitika pa nthawi imene Mfumu Koresi anagonjetsa Babulo. Wolemba mbiri wina wa Chigiriki ananena kuti Koresi atangolowa mu Babulo “analamula [asilikali ake] kuti akaphe aliyense amene anali panja.” Anthu a ku Babulo ayenera kuti anachita mantha ndi zimenezi. Koma Ayuda ayenera kuti anatetezeka chifukwa chotsatira malangizo a Yehova.
16. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudera nkhawa kwambiri za m’tsogolo? (Onaninso chithunzi.)
16 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Posachedwapa tikuyembekezera chisautso chachikulu chomwe sichinachitikepo. Chisautsochi chikadzayamba, anthu m’dzikoli adzasokonezeka ndipo adzachita mantha. Koma anthu a Yehova sadzachita nawo mantha. Tikudziwa kuti Yehova ndi Mulungu wathu. Tidzaimirira ndi kutukula mitu yathu podziwa kuti ‘chipulumutso chathu chayandikira.’ (Luka 21:28) Ngakhale pamene mgwirizano wa mayiko udzatiukire, tidzakhalabe olimba. Yehova adzatithandiza pogwiritsa ntchito angelo komanso malangizo otithandiza kuti tipulumuke. Kodi adzatipatsa bwanji malangizowa? Panopa sitikudziwa, komabe n’kutheka kuti mwina tidzapatsidwa malangizowa kudzera m’mipingo. Tingati mipingoyi idzakhala ngati ‘zipinda zamkati’ zoti tidzabisalemo n’kutetezeka. Kodi tingakonzekere bwanji zimene zichitike m’tsogolo? Tiyenera kumagwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo athu, kumvera malangizo a gulu la Yehova komanso kumakhulupirira kuti Yehova akutsogolera gulu lathu.—Aheb. 10:24, 25; 13:17.
Kuganizira kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso angatipulumutse, kungadzatithandize kuti tisadzade nkhawa kwambiri pa nthawi ya chisautso chachikulu (Onani ndime 16) b
17. Kodi mungatani kuti muzidalira kwambiri Yehova kuti akulimbikitseni?
17 Ngakhale kuti Ayuda omwe anali ku ukapolo ankakumana ndi mavuto, Yehova ankawalimbikitsa komanso kuwathandiza. Ifenso adzatichitira zofananazo. Choncho kaya mukumana ndi zotani, pitirizani kudalira Yehova kuti azikulimbikitsani. Muzikhulupirira kuti iye ndi Mulungu wachifundo chachikulu. Muzikhala ndi chiyembekezo cholimba. Muzikumbukira kuti chifukwa choti Yehova ali kumbali yanu, palibe chimene muyenera kuopa.
NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu ndi Chiyembekezo Chathu Ndipo Timakudalirani
a Mayina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kagulu ka abale ndi alongo kasonkhana m’nyumba. Iwo sakukayikira kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso kuti akhoza kuteteza anthu ake kulikonse komwe ali padzikoli.