Zokolola N’zochuluka
YESU anauza ophunzira ake kuti zokolola zidzakhala zochuluka nthawi ya mapeto ino. (Mat. 9:37; 24:14) Mawu amenewa akukwaniritsidwa mwapadera ku Transcarpathia, m’dziko la Ukraine. M’matauni atatu okha akumeneku, muli mipingo 50 ndipo ofalitsa alipo oposa 5,400. * Pa anthu 4 alionse a m’matauniwa mmodzi ndi wa Mboni za Yehova.
Kodi ntchito yolalikira imayenda bwanji m’gawo limeneli? M’bale wina wakumeneko dzina lake Vasile anati: “Anthu ake amalemekeza kwambiri Baibulo, amakonda chilungamo, amagwirizana kwambiri ndi achibale awo komanso amafunitsitsa kuthandizana.” M’baleyu anapitiriza kuti: “Si nthawi zonse pamene amagwirizana ndi zimene timakhulupirira. Koma ukawasonyeza mfundo ya m’Baibulo amamvetsera mwachidwi.”
Abale ndi alongo akumeneku amakumana ndi mavuto ena polalikira chifukwa choti anthu amene ayenera kuwalalikira ndi ochepa. Mwachitsanzo, mpingo wina uli ndi ofalitsa 134 koma kuli nyumba 50 zokha zimene angalalikireko. Ndiye kodi ofalitsawo amatani?
Abale ndi alongo ambiri amayesetsa kupita kukalalikira kumadera amene kulibe ofalitsa ambiri. M’bale wina wazaka 90 dzina lake Ionash anati: “Mumpingo wathu, wofalitsa aliyense ali ndi nyumba ziwiri zokha zimene angalalikireko. Panopa ndimangolalikira m’gawo la mpingo wathu. Koma m’mbuyomu thupi langa lisanafooke, ndinkayenda mtunda wa makilomita 160 kukalalikira kudera lina la anthu olankhula Chihangare.” Ofalitsa amafunika kudzipereka kwambiri kuti azikalalikira m’madera akutali. Ionash anati: “Ndinkadzuka 4 koloko m’mawa kuti ndikakwere sitima ndipo ndinkalalikira mpaka m’ma 6 koloko madzulo pamene sitima inkabwerera. Ndinkachita zimenezi kawiri kapena katatu pa mlungu.” Kodi iye anaona kuti zimene ankachitazi zinali zothandiza? Inde, chifukwa anati: “Ndinkasangalala kwambiri ndi utumikiwu ndipo ndinali ndi mwayi wothandiza banja lina lakudera lakutalili kuti liphunzire choonadi.”
N’zoona kuti si aliyense m’mipingo ya m’derali amene angakwanitse kukalalikira kudera lakutali. Koma aliyense, kuphatikizapo achikulire, amayesetsa kuti alalikire mokwanira m’gawo lampingo wawo. Zotsatira zake n’zakuti chaka cha 2017, anthu amene anafika pa Chikumbutso anali pafupifupi kuwirikiza kawiri chiwerengero cha ofalitsa a m’matauniwa. Tingati hafu ya anthu a m’matauniwo anafika pa Chikumbutso. Apa zikuonekeratu kuti kulikonse kumene tili, tikhoza kukhala ndi “zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.
^ ndime 2 Matauniwa ndi oyandikana ndipo mayina ake ndi Hlybokyy Potik, Serednye Vodyane ndi Nyzhnya Apsha.